Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 12/1 tsamba 22-25
  • Mmene Yehova Amapititsira Patsogolo Ntchito Yake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Yehova Amapititsira Patsogolo Ntchito Yake
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • “Kodi Ndalamazo Zimachokera Kuti?”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mpatsi wa “Mphatso Iliyonse Yabwino”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Mmene Ena Amapatsira Zopereka ku Ntchito Yolalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 12/1 tsamba 22-25

Mmene Yehova Amapititsira Patsogolo Ntchito Yake

M’ZAKA makumi ambiri zaposachedwapa Mboni za Yehova zapeza chiwonjezeko chachikulu. M’zaka khumi zokha zapita, izo zawonjezeka kuchokera pamipingo 42,600 kufikira chiwonkhetso chonse pamodzi cha 60,192 m’maiko 212. Polingalira ichi, ena afunsa kuti: Kodi ntchito ya Mboniyi imachilikizidwa bwanji mwandalama? Watch Tower Society njosangalatsidwa kuliyankha funsoli ndi ena olingana nalo m’nkhani ino.

Kodi Mboni za Yehova zimapereka chachikhumi?

Ayi. Mu Israyeli wakale, kupereka chachikhumi kunalamulidwa pansi pa Chilamulo cha Mose kuchilikiza antchito pakachisi wa Mulungu, Alevi ndi ansembe. (Numeri 18:21, 24-29) Awa analibe maiko a fuko lawo kuposa mizinda yakutiyakuti, chotero anafunikira chilikizo lapaderali. Kuwonjezera apa, Aisrayeli okhulupirika anali aufulu kupatsa zopereka modzifunira kaamba ka ntchito zapadera, monga ngati kumangidwa kwa guwa lansembe ndipo, pambuyo pake kachisi.​—Eksodo 25:1-8; 1 Mbiri 29:3-7.

Komabe, pamene Yesu anamwalira, Baibulo limati ‘iye anachotsa . . . mawu a chilamulo cha kutchulako malangizo.’ (Aefeso 2:15; Akolose 2:13, 14) Kufotokoza m’mawu ena, Chilamulo m’maso mwa Mulungu sichinali kugwiranso ntchito pa Ayuda kapena Akristu. Chotero, limodzi ndi mbali zina za Chilamulo, zonga ngati kupereka nsembe kokhazikika pakachisi, kupereka chachikhumi sikunafunikiresno kwa okhulupirika.

Kwa Akristu, kuperekako kumasonkhezeredwa ndi chikondi, osati ndi chilamulo. Mtumwi Paulo analifotokoza lamulo lamakhalidwe abwinoli pamene ankalinganiza zopereka kaamba ka Akristu osoŵa m’Yudeya. Iye anati: ‘Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.’ (2 Akorinto 9:7) Njira Yamalemba imeneyi ya kupereka kwaufulu ndiyo ikuchitidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi mumapanga mapwando osonkhetsera ndalama, maenevulupu a zopereka, kupemphapempha ndalama, ndi njira zina zokundikira ndalama zofanana ndi izi?

Ayi, Akristu owona safunikira kukakamizidwa kapena kunyengereredwa kuti achite zopereka mwa kuwalonjeza mphotho. Magulu achipembedzo amene amachita bingo, kugulitsa zinthu zoyenera kuperekedwa kwa osauka, njuga, maseŵera osangulutsa, kuchititsa lendi zipinda zina za tchalitchi, kapena kupititsa mbale ya zopereka amavumbula kuti sanawapatse anthu awo chakudya chauzimu, ndipo chotero mzimu wa Mulungu sumawasonkhezera anthu awowo kuti apereke ndalama mwaufulu. Chofananachi chinganenedwe kwa anthu omwe amatenga kachitidwe kakalekale ka kupereka chachikhumi.​—Mateyu 10:8.

Kodi ntchito zomanga Nyumba Zaufumu zatsopano ndi maofesi anthambi mumazilipirira motani, limodzinso ndi kufutukuka kwanu pamalikulu m’Brooklyn ndi ku Patterson, New York?

Yehova amatsanulira mzimu wake woyera pa Mboni zake, kuzitheketsa ‘kuchita zabwino, nachuluka ndi ntchito zabwino, nakondwera kugawira ena, nayanjana; nadzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.’ (1 Timoteo 6:18, 19) Mzimuwu ndiwo umasonkhezera Mboni za Yehova kuchilikiza ntchito Yaufumu m’njira iriyonse.

Mwachitsanzo, mu 1989, Mboni 3,787,188 m’maiko 212 zinawononga maola 835,426,538 zikuphunzitsa ena Mawu a Mulungu. Ndipo zinachititsa maphunziro a Baibulo okhazikika 3,419,745 kwa anthu okondwerera. Zowonongedwa zirizonse zopezedwa m’ntchito imeneyi zinalipiriridwa ndi anthu enieniwo omwe anaichita. Yehova anafupa ntchito imeneyi ya chikondi ndi chiwonjezeko cha Mboni zobatizidwa chatsopano 263,855.

Mzimu wofananawo wa kupatsa ndiwo umafulumiza Mboni ndi anthu okondwerera kuchilikiza ntchitoyi mwandalama. Pambali pa kuthandizira kuchepetsa zowonongedwa zokhazikika za mipingo yakwawo, iwo amachilikiza ntchito yomanga iriyonse yomwe ingakhale yoyenerera, monga ngati kukonzanso kapena kufutukula Nyumba yawo Yaufumu kapena Nyumba Yamsonkhano kapena kumanga yatsopano. Chaka chirichonse, chifukwa cha kukula kofulumira, Nyumba Zaufumu zambiri zimafunikira kumangidwa, zina zimawonongadi mazana ambiri a zikwi za madola. Zowonongedwa zake zimalipiridwa ndi Mboni za kumaloko kupyolera m’zopereka zawo zaufulu ndi ntchito.

Kuwonjezera apa, m’maiko ambiri nyumba zanthambi zosindikizira ndi maofesi limodzinso ndi nyumba zogonamo zinafunikira kuwonjezeredwa​—kapena kumanga zatsopano​—kuti apeze malo ogonamo antchito owonjezereka ndi ziwiya zofunikira ndi gulu lomakulali. Ichi nachonso chimachilikizidwa ndi zopereka zaufulu ndi ntchito, monga mmene imachitidwira ntchito yomanga ndi kukonzanso m’Brooklyn ndi m’Patterson, New York. Zitathekera, Mboni za kumaloko zimalipirira nyumba yomangidwayo. M’zochitika zina, Watch Tower Society imakonzekera nthambi kuti zilandire thandizo​—ponse paŵiri yandalama ndi ogwira ntchito aluso​—kuchokera kumaiko ena. Chotero, motsogozedwa ndi Sosaite, “kulingana” kumachitika.​—2 Akorinto 8:14.

Kodi nchifukwa ninji simumakhala ndi zipatala kapena makiliniki ndikuphatikizidwa m’ntchito yosonkha katundu waufulu ndi ntchito zina zamayanjano monga mmene magulu ena achipembedzo amachitira?

Mboni za Yehova zimathandizira mofulumira kungozi zochitika pambuyo pankhondo kapena tsoka lachilengedwe zitakhala zokhoza kutero. Kwenikweni, iwo kaŵirikaŵiri amakhala pakati pa oyamba kufika pa zochitikazo kupereka zakudya, zovala, ndi antchito aufulu kuthandizira kumanganso. Komabe, Mboni za Yehova sizimayendetsa zipatala kapena makiliniki, monga mmene sizimayendetsera madipatimenti ozima moto kapena a khamu la apolisi, omwe nawonso amakhalako kaamba ka kupulumutsa moyo.

Iwo ali aminisitala odzipereka a uthenga wabwino, ndipo ntchito yawo njakulalikira ndi kuphunzitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu padziko lonse kukhala umboni mapeto asanadze. (Mateyu 24:14) Monga mmene ananenera Yesu, kututa kuchulukadi ndipo antchito ali oŵerengeka. Kukakhala kosakhululukidwa kuleka ntchito yofunikayi ndikuyamba ntchito zina, mosasamala kanthu ndi kutchuka kwake.​—Mateyu 9:37, 38.

Monga mmene zimachitikira, Mboni za Yehova zambiri ziri adokotala, anamwino, ndi othandizira m’chipatala. Koma iwo amailingalira ntchitoyi kukhala yachiŵiri ku ntchito yawo yoyamba, uminisitala Wachikristu.

Kodi aliyense wa maofisala a Watch Tower Society kapena ziŵalo zake amapanga ndalama kuchokera ku ntchito yanu yaikuluyi yosindikiza?

Kunena zowona, ayi! Mwalamulo, Sosaite ndigulu losapanga phindu. Ilibe anthu omwe anaikizamo chuma chawo, simagawa mapindu, osati ngakhale malipiro. Minisitala aliyense pa malikulu, kuphatikizapo pulezidenti wa Sosaite ndi otsogolera, analumbiritsidwa mwalamulo kusakundikamo phindu. Iye amalandira zakudya, pogona, ndi chisamaliro choyenerera chamankhwala, limodzinso ndi ndalama zobwezeretsedwa zochepa kaamba ka zotaika zaumwini. Ngati Mboni yapita paulendo wotumidwa ndi Sosaite, zowonongedwa zake zoyendera kaŵirikaŵiri zimalipiridwa.

Kuwonjezera apa, palibe kulikonse m’dziko lapansi kumene aminisitala athu amalipiritsa kaamba ka kuchititsa mapwando aukwati, ubatizo, kapena maliro. Ndipo sipamakhala ndalama zoloŵera kapena mbale zosonkhetsera pankhani zapoyera kapena misonkhano.

Popeza kuti mbale zosonkhetsera sizimapititsidwa, kodi mipingo ya kumaloko imalandira motani zopereka kuti akwaniritse zotaika?

Mabokosi a zopereka amasungidwa m’Nyumba Zaufumu kotero kuti anthu angapereke zopereka zaufulu ngati akufuna. (2 Mafumu 12:9) Zopereka zonse, kaya zikhale zazikulu kapena zazing’ono, zimayamikiridwa. (Marko 12:42-44) Kamodzi pamwezi, m’minisitala wosamalira maakaunti a mpingo amaŵerenga ndemanga zachidule kumpingo kuŵadziwitsa chiwonkhetso chonse cha zopereka zolandiridwa, zowonongedwa, ndi zopereka zotumizidwa ndi mpingo ku Watch Tower Society kuchilikiza ntchito yolalikira yadziko lonse ndi ntchito zina.

Anthu atamvetsetsa makonzedwewa, iwo ngaufulu kugawanamo ngati angakhumbe kutero, aliyense “monga momwe anapindula.” (1 Akorinto 16:2) Aka ndiko kamakhala kachitidwe m’mipingo yoposa 60,000 padziko lonse.

Pa Pentekoste Akristu oyambirira anachita zonse zodyerana. Kodi Mboni za Yehova zimachita ichi?

Mkhalidwe wangozi udabuka pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E. pamene Ayuda akutali amene anatembenuzidwa posachedwapa ku Chikristu anakhalabe mu Yerusalemu kuti alandire kuwunikira kowonjezereka kwauzimu. Iwo anafunikira pogona pakanthaŵi kochepa ndi zakudya; chotero, Akristu akumaloko anapanga makonzedwe a kugulitsa chuma kwaufulu ndi kugawana kofala kwa mapindu kuti aperekere zakudya za kuyanjana kwanyengo yaitali. (Machitidwe 2:1, 38-47; 4:32-37) Palibe munthu aliyense amene anakakamizidwa kugulitsa kapena kupanga zopereka. (Machitidwe 5:1-4) Kuchita zonse zodyeranaku sikunali chikomyunizimu, monga mmene ena amaganizira. Iko kanali kakonzedwe wamba kosakhalitsa. Pamene Akristu anabwerera kunyumba zawo, iko kanatha.

Kodi mumaphunzitsa kuti kupereka zinthu zakuthupi ndiko njira yolipirira machimo?

Kutalitali! Baibulo limati: ‘Mudziŵa kuti simunawomboledwa ndi zovunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu; koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.’​—1 Petro 1:18, 19.

Mboni za Yehova zimakhulupirira nsembe yadipo ya Yesu kaamba ka chipulumuko. Iwo samapanga zopereka zaufulu nayembekezera kuti kuteroko kudzaŵabweretsera chipulumuko. Komabe, iwo amadziŵa kuti ndalama zokwanira zimafunikira kuti afalitse mbiri yabwino ya dziko latsopano lolungama la Mulungu. (2 Petro 3:13) Ndipo amazindikira kuti kuchita zopereka kukulengezaku ndiko mwaŵi wopatsidwa ndi Yehova.

Popereka chopereka chachikulu ku kachisi wa Yehova amene mwana wake Solomo adati amange, Mfumu Davide anapemphera kuti: ‘Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu . . . Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.’​—1 Mbiri 29:11, 14.

Lerolino, Mboni za Yehova ndi anthu ena okhoterera ku chilungamo amalingalira mofananamo monga mmene anachitira Davide. Iwo ngachimwemwe kukhala ndi mwaŵi wa kupereka zopereka kuchilikiza ntchito yotamanda Yehova, nazindikira kuti chirichonse chimene iwo amapereka kuutumiki wake chimachokeradi kwa iye. Yehova amadalitsa mzimu umenewu, ndipo umu ndimmene amapititsira patsogolo ntchito yake.

[Bokosi patsamba 23]

MMENE ENA AMAPEREKERA KU NTCHITO YAUFUMU

◻ MPHATSO: Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwe ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yakumaloko. Zinthu zonga ngati munda, limodzinso ndi zokometsera kapena zinthu zina zamtengo wapatali, zingaperekedwenso. Kalata yachidule yolongosola kuti zimenezo ziri zopereka zaufulu iyenera kutsagana ndi zopereka zimenezi.

◻ MAKONZEDWE A CHOPEREKA CHOKHALA Ndi MALIRE: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti zisungidwe mwa kuikiziridwa, ndi makonzedwe akuti mwini wake atazifuna, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.

◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe kukhala yodzapindula ndi makonzedwe a inshuwalansi ya moyo kapena makonzedwe a kuleka ntchito/​ndi kulandira penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe aliwonse oterowo.

◻ KUIKIZIRIDWA: Ndalama zosungidwa ku banki mu yotchedwa savings account zingaikiziridwe ku Sosaite. Ichi chitachitidwa, chonde dziŵitsani Sosaite. Ndalama, mapangano, ndi katundu zingaperekedwenso pansi pa makonzedwe opindulitsa woperekayo mkati mwa moyo wake wonse. Njira imeneyi imathetsa ndalama zowonongedwa ndi kusatsimikizirika kwa lamulo lokhudza chuma chamasiye, pamene chikutsimikiziridwa kuti Sosaite idzalandira katunduyo pa imfa.

◻ MAPANGANO A KUGAŴIRA CHUMA CHAMASIYE: Katundu kapena ndalama zingaikiziridwe ku Watch Tower Society kupyolera mwa pangano la kugaŵa katundu loikidwa mwa lamulo. Kope liyenera kutumizidwa ku Sosaite.

Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ndi malangizo onena za nkhani zoterezi, lemberani ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yakumaloko.

[Chithunzi patsamba 24]

Mbali ya chigawo chophunzitsa Baibulo cha Mboni za Yehova chomwe chikumangidwa mu Patterson, New York

[Zithunzi patsamba 25]

Yehova amapititsa patsogolo ntchito yomanga kupyolera mwa anthu ake amene amapanga zopereka zaufulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena