Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 11/8 tsamba 30-31
  • Mankhwala Ogodomalitsa Ngosangulutsira Chifukwa Ninji Ayi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mankhwala Ogodomalitsa Ngosangulutsira Chifukwa Ninji Ayi?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziyambukiro Zovulaza ndi Zakupha
  • Thupi Lanu—‘Nsembe Yamoyo’
  • Kodi Ndani Amagwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—2001
  • Mmene Mankhwala Oletsedwa Amakhudzira Moyo Wanu
    Galamukani!—1999
  • Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo Lingathetsedwe!
    Galamukani!—2001
  • Kulemekeza Mphatso ya Moyo
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 11/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Mankhwala Ogodomalitsa Ngosangulutsira Chifukwa Ninji Ayi?

“COCAINE . . . mwachiwonekere ndiwo mankhwala oletsedwa ndi lamulo ofala amene akugwiritsiridwa ntchito mowanda tsopano . . . ndi osangalalidwa kwenikweni.”

Anatero Dr. Peter Bourne mu 1974. Zaka zinayi pambuyo pake yemwe anali wolangiza pa lamulo laukhondo wa Nyumba Yamalamulo kwa Pulezidenti Jimmy Carter, Dr. Bourne anakakamizidwa kuleka ntchito chifukwa cha milandu ya kugwiritsira ntchito mankwala osaloledwa ndi lamulo. Mofanana ndi ena ambiri, mwinamwake analingalira kuti akalungamitsa kugwiritsidwa ntchito kwa mankhwala ogodomalitsa monga chosangulutsa.

Panthaŵi ina cocaine inali yosavuta kuipeza ndi aliyense pafupifupi kulikonse—ku magolosale, m’bawa, ndi kwa oyendetsa maoda azinthu. M’kati mwa ma 1880 ndi ma 1890, inali kukokedwa mumkhalidwe wa ndudu ya coca-leaf. Inasanganizidwa m’vinyo wosiyanasiyana ndi m’zakumwa zina zozizira. Ngakhale tifitifi Wachingelezi wopeka Sherlock Holmes amasonyezedwa akusuta cocaine “katatu patsiku kwa miyezi yambiri.”—The Sign of Four, yolembedwa ndi Bwana Arthur Conan Doyle.

Cocaine inathokozedwa kaamba ka ziyambukiro zake zokhalitsa ndikuyamikiridwa monga mankhwala a mutu, asima, malungo azilonda, ndi dzino lopweteka. Anawonedwa kukhala mankhwala othandiza ndi anthu ambiri. Mwachitsanzo, mu 1884 wachichepere Sigmund Freud analemba kuti: “Ndalaŵa mphamvu ya coca, imene imathetsa njala, tulo, ndi kutopa kwathupi ndipo imapatsa munthu mphamvu za luntha, kwa ine imatero moŵirikiza nthaŵi zambirimbiri . . . Kuisuta koyamba coca kapena ngakhale kobwerezabwereza sikumachititsa chilakolako champhamvu chofuna kuisutanso.”—Über Coca.

M’zaka zapita, ndemanga zofananazo zinapangidwa ponena za mbanje, zimene zinapangitsa anthu ena kukhulupirira kuti kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa kunali kosavulaza. Komabe, lerolino mungaŵerenge maumboni ambirimbiri a zamankhwala osonyeza zosiyana. Ndithudi, kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa monga ngati mbanje, cocaine, crack (mtundu wina wa cocaine), heroin, amphetamines, ndi barbiturates nkovulaza thupi moopsa.

Ziyambukiro Zovulaza ndi Zakupha

Ofufuza amanena kuti osuta mbanje angayembekezere kubala makanda ang’ono mathupi, ngozi zambiri, ndi mapapo owonongeka. Cocaine ndi zopangidwako zake za crack zagwirizanitsidwa ndi kupenga ndi zizindikiro zina za kusokonezeka maganizo, kupsinjika kwamphamvu, kusoŵa tulo, kusakhala ndi chilakolako chakudya, kusakhoza m’zakugonana, mantha aakulu, njirinjiri, kudwala mtima, kufa ziŵalo, zilonda zapakhungu, matudza, kuduka miyendo ndi zala, kubala mwana wopuduka, kudwala ziwalo zothandiza kupuma, kuleka kununkhiza, ndi imfa. Mogwirizana ndi wolemba wina wasayansi, “ngati kusuta cocaine mkati mwa kukhala ndi pathupi kunali matenda, chiyambukiro chake pa makanda chikanalingaliridwa kukhala vuto ladziko la thanzi la anthu.”

Ogwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa ena amakhalanso paupandu waukulu wa kuyambukiridwa ndi AIDS. Ndipo mavuto athanzi ambiri agwirizanitsidwa ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala opangidwa, monga ngati amphetamines, barbiturates, ochangamula maganizo, ndi “mankhwala achilendo okhutumalitsa.”

Komabe, mosasamala kanthu za ngozi zodziŵika, anthu akulakalakabe kuyesa mankhwala ogodomalitsa. Owagwiritsira ntchito mwamaseŵera amapeza mankhwalawa kukhala osangalatsa. Komabe, ngozizo nzenizeni kwambiri. Ziri ngati kuyendetsa galimoto yonyamula mafuta paphiri logumuka—ngozi njodziŵikiratu.

Thupi Lanu—‘Nsembe Yamoyo’

Lamulo lamakhalidwe abwino lofotokozedwa ndi mtumwi Paulo pa Aroma 12:1 limakhudza nkhaniyi mwamphamvu. Ilo limati: ‘Chifukwa chake ndikupemphererani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.’ Akristu ayenera kupereka nsembe zamtengo woposa nsembe zanyama zimene zinafunikira kuperekedwa ndi mtundu wa Israyeli wakale.

Apadera ndi mawu ogwiritsiridwa ndi Paulo a liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “nsembe yamoyo, yopatulika” (thy·siʹan zoʹsan ha·giʹan). Mogwirizana ndi akatswiri a Baibulo osiyanasiyana, mawuŵa amatanthauza zotsatirazi: Muisrayeli anapereka nyama yophedwera nsembe. Iyo sikaperekedwanso kachiŵiri. Mosiyana, Mkristu ayenera kudzipereka yekha ndi nyonga zake zonse, ‘wamoyo.’ (Mneni Wachigiriki wotembenuzidwa ‘chamoyo’ nthaŵi zina angatanthauze ‘kukhala ndimoyo wathanzi.’) Ndipo monga momwe Muisrayeli analetsedwera kupereka chopunduka kapena cholemala mwamtundu uliwonse, Mkristu amapereka kwa Mulungu nyonga zake zabwino koposa. Ndipo popeza kuti thupi la Mkristu limakhala choyendera cha machitidwe ake, ntchito zake zonse ndi malingaliro limodzi ndi ziwiya zake—thupi lakelo—ziyenera kuperekedwa kotheratu kwa Mulungu. Aka kamakhala kachitidwe ka kudzipereka kotheratu. Iye samadzinenera mwa yekha. Chotero, moyo wake, osati dzoma, ndiwo nsembe yeniyeniyo.

Chotero, Paulo ankalimbikitsa Akristu a mzaka za zana loyamba, pamene adali ndi moyo padziko lapansi, kugwiritsira ntchito nyonga zawo, umoyo wawo, ndi maluso aliwonse kapena mphatso zimene anali nazo kuutumiki wa moyo wonse kwa Mulungu. (Akolose 3:23) Iwo anafunikira kupatsa Yehova zabwino koposa zomwe akatha kupereka kuthupi ndi mwamaganizo. Mulungu akakondweretsedwa kwambiri ndi nsembezo.

Komabe, kodi Mulungu akachitaponji ngati modzifunira anadziloŵetsa m’machitachita amene akazimiriritsa mphamvu yawo yakuthupi kapena yamaganizo ndikuchepetsadi moyo wawo? Kodi Akristu akafuna kuswa lamulo ndi kudziika pachiswe chakuchepetsa kuyenerera kwawo muuminisitala wa Mulungu? Machitachita achidetso angawalepheretse kukhala aminisitala ndipo ngakhale kutulukapo kuchotsedwa kwawo mumpingo Wachikristu.—Agalatiya 5:19-21.

Lerolino, kali kachitidwe kofala kuzungulira dziko lonse kwa anthu kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa. Kodi munthu angagwiritsire ntchito mankhwala oterowo chifukwa cha zosangulutsa ndikuperekabe thupi lake monga “nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu”? Si kufufuza kwa zamankhwala ndi zochitika zosaŵerengeka zokhala ndi zotulukapo zakupha zokha komanso malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo amapereka yankho lomvekera bwino kwambiri lakuti—ayi!

[Chithunzi patsamba 30]

“The Opium Smoker”—by N. C. Wyeth, 1913

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena