Kodi ‘Mukufuna’ Kuthandiza Anthu Ena?
1 Yesu anali woganiziradi anthu ena. Munthu wakhate atamupempha kuti amuthandize, Yesu anatambasula dzanja lake, ndi kumukhudza ndipo anati: ‘Ndifuna; khala wokonzedwa.’ (Marko 1:40-42) Kodi ndi m’njira ziti zimene tingatsanzire mtima wa Yesu wothandiza anthu ena?
2 Anthu Achidwi: Aliyense mu mpingo ali ndi mbali yothandiza anthu achidwi kukhala olambira a Yehova. Anthu atsopano akabwera ku misonkhano, apatseni moni ndipo adziŵeni. Fufuzani njira zimene mungawalimbikitsire. Ayamikireni chifukwa cha mayankho awo. Ayamikireni chifukwa cha kuyesetsa kwawo kugwiritsira ntchito m’moyo wawo mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Athandizeni kuona kuti angapeze mabwenzi enieni mu mpingowo.
3 Okhulupirira Anzathu: Makamaka “a pa banja la chikhulupiriro” ndiwo tikufunika kuwathandiza m’njira zambiri. (Agal. 6:10) Ambiri akuvutika ndi matenda. Mwa kuwayendera kukawalimbikitsa, angapindule ndi mayanjano abwino ndipo mwinanso tingawathandize m’njira zina. N’kutheka kuti ena akukumana ndi mavuto ena m’moyo wawo. Sonyezani chifundo mwa kupatula nthaŵi kuti mumvetsere zonena zawo ndi kuwalimbikitsa. (1 Ates. 5:14) Akulu amafunanso kuti tiwathandize pogwira ntchito yawo. (Aheb. 13:17) Ngati tisonyeza mtima wofunitsitsa kuthandiza, tingakhale ‘chotonthoza mtima’ kwa okhulupirira anzathu.—Akol. 4:11.
4 Am’banja Lathu: Tiyeneranso kuyesetsa kusonyeza mtima wa Yesu kwa anthu a m’banja mwathu. Kukonda kwambiri ana awo kumalimbikitsa makolo ‘kuwalera iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’ (Aef. 6:4) Ananso angachite mbali yawo mwa kukonzeka mofulumira ikakhala nthaŵi ya phunziro la banja, misonkhano ya mpingo, kapena utumiki wakumunda. Ana akuluakulu angasonyeze chifundo cha Yesu mwa kuthandiza mwachikondi makolo awo kulimbana ndi mavuto amene amabwera chifukwa cha ukalamba. Mwa njira zimenezi ndiponso m’njira zina, tonse ‘tingachite ulemu [“tingasonyeze kudzipereka kwa Mulungu,” NW] m’banja lathu.’—1 Tim. 5:4.
5 Tikatsanzira Yesu pothandiza ena, tingathe kuchepetsa mavuto ndipo tingapangitse banja lathu ndiponso mpingo kukhala wogwirizana. Chofunika kwambiri kuposa zonsezi n’chakuti timalemekeza Yehova, “Atate wa zifundo.”—2 Akor. 1:3.