Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 9/1 tsamba 13-18
  • Kondwerani mwa Yehova!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kondwerani mwa Yehova!
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kondwerani​—Chifukwa Ninji Ndipo Motani?
  • Zifukwa Zosaŵerengeka Zokondwerera
  • Kulalikira​—Cholemetsa Kapena Chikondwerero?
  • Tiyeni Tisangalale Limodzi
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kondwerani m’Chiyembekezo cha Ufumu!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Chimwemwe cha Yehova Ndicho Linga Lathu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 9/1 tsamba 13-18

Kondwerani mwa Yehova!

“Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.”​—AFILIPI 4:4.

1. Kodi nchifukwa ninji tingadabwe ndi zimene Paulo anatanthauza pamene ananena kuti Akristu ayenera kukondwera nthaŵi zonse?

MASIKU ano, zifukwa zokondwerera zingaonekere kukhala zochepa ndi zosoŵa. Anthu opangidwa ndi fumbi, ngakhale Akristu enieni, amakumana ndi mikhalidwe imene imadzetsa chisoni​—ulova, kudwaladwala, imfa ya okondedwa, mavuto a kusamvana, kapena chitsutso chochokera ku ziŵalo zabanja zosakhulupirira kapena amene kale anali mabwenzi. Chotero kodi chilangizo cha Paulo chakuti “Kondwerani . . . nthaŵi zonse” tiyenera kuchimva motani? Polingalira za mikhalidwe yosakondweretsa ndi yoyesa imene tonsefe tiyenera kulimbana nayo, kodi zimenezi zingakhaledi zotheka? Kukambitsirana za nkhani yonse ya mawuwa kudzatithandiza kudziŵa bwino nkhaniyi.

Kondwerani​—Chifukwa Ninji Ndipo Motani?

2, 3. Kodi kufunika kwa chikondwerero nkotani, monga momwe kwasonyezedwera m’nkhani ya Yesu ndi Aisrayeli akale?

2 “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.” Zimenezi zingatikumbutse za mawu onenedwa kwa Aisrayeli pafupifupi zaka mazana 24 zapitazo: “Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu,” kapena malinga ndi kunena kwa matembenuzidwe a Moffatt: “Kukondwera mwa Wosathayo ndiko nyonga yanu.” (Nehemiya 8:10) Chimwemwe chimapatsa nyonga ndipo chili ngati linga limene munthu angaloŵemo kaamba ka chitonthozo ndi chitetezero. Chimwemwe chinagwira ntchito m’kuthandiza ngakhale munthu wangwiroyo Yesu kuti apirire. “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Mwachionekere, kukhala wokhoza kukondwera poyang’anizana ndi zovuta nkofunika kaamba ka chipulumutso.

3 Asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeli anali atalamulidwa kuti: “Mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.” Zotulukapo za kulephera kutumikira Yehova mokondwera zikakhala zowopsa. “Matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwawonongeka, . . . Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse.”​—Deuteronomo 26:11; 28:45-47.

4. Kodi nchifukwa ninji tingalephere kukondwera?

4 Chifukwa chake, nkofunika kwambiri kuti otsalira odzozedwa a lerolino ndi mabwenzi awo a “nkhosa zina” akondwere! (Yohane 10:16) Paulo, mwa kubwereza uphungu wake kuti, “ndibwerezanso kutero,” anagogomezera kufunika kwa kukondwera ndi zinthu zonse zabwino zimene Yehova watichitira. Kodi timatero? Kapena kodi timatanganitsidwa kwambiri ndi zochita za moyo watsiku ndi tsiku kwakuti nthaŵi zina timaiŵala zifukwa zathu zambiri zokondwerera? Kodi mavuto amaunjikana kwakuti amaphimba kuona kwathu Ufumu ndi madalitso ake? Kodi timalola zinthu zina​—kusamvera malamulo a Mulungu, kunyalanyaza malamulo a mkhalidwe a Mulungu, kapena kunyalanyaza ntchito Zachikristu​—kutilanda chimwemwe chathu?

5. Kodi nchifukwa ninji munthu wosafatsa amapeza kuti kukondwera kumamuvuta?

5 “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.” (Afilipi 4:5) Munthu wosafatsa amasoŵa uchikatikati. Iye angalephere kusamalira thanzi lake moyenera, akumadzichititsa kukhala pamavuto kapena nkhaŵa zosafunikira. Mwinamwake iye angakhale asanaphunzire kuvomereza zimene sakhoza kuchita ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nazo. Angakhale akumadziikira zonulirapo zapamwamba kwambiri ndiyeno namayesayesa kuzifikira mosasamala kanthu za zimene angatayirepo. Kapena angagwiritsire ntchito zimene sakhoza kuchita kukhala chodzikhululukira cha kubwerera m’mbuyo kapena kuchita ulesi. Posoŵa uchikatikati ndiponso pokhala wosafatsa, amapeza kukondwera kukhala komuvuta.

6. (a) Kodi Akristu anzathu ayenera kuonanji mwa ife, ndipo kodi ndiliti lokha pamene zimenezi zidzakhala choncho? (b) Kodi ndimotani mmene mawu a Paulo pa 2 Akorinto 1:24 ndi Aroma 14:4 amatithandizira kukhala ofatsa?

6 Ngakhale ngati otsutsa atilingalira kukhala otengeka maganizo, nthaŵi zonse Akristu anzathu ayenera kuona kufatsa kwathu. Ndipo iwo adzatero ngati ife tili achikatikati ndipo osayembekezera ungwiro kwa ife eni kapena kwa ena. Kuposa zonse, tiyenera kupeŵa kuika zolemetsa pa ena zimene zimaposa zimene Mawu a Mulungu amafuna. Mtumwi Paulo anati: “Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu.” (2 Akorinto 1:24) Monga amene kale anali Mfarisi, Paulo anadziŵa bwino lomwe kuti malamulo okhwima operekedwa ndi kuumirizidwa ndi okhala ndi ulamuliro akaletsa chikondwerero, pamene kuli kwakuti malingaliro othandiza operekedwa ndi antchito anzake akachiwonjezera. Chenicheni chakuti “Ambuye ali pafupi” chiyenera kukumbutsa munthu wofatsa kuti ‘sitiyenera kuweruza mnyamata wa mwiniwake. Kwa mbuyake aimirira kapena kugwa.’​—Aroma 14:4.

7, 8. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kuyembekezera kukhala ndi mavuto, komabe kodi ndimotani mmene kulili kotheka kwa iwo kupitirizabe kukondwera?

7 “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Lerolino tili mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene Paulo analemba. (2 Timoteo 3:1-5) Chotero Akristu ayenera kuyembekezera kuyang’anizana ndi mavuto. Mawu a Paulo akuti “kondwerani . . . nthaŵi zonse” samatanthauza kuti Mkristu wokhulupirika sangakhale ndi kuthekera kwa nyengo za kutaya mtima kapena kulefulidwa kwa kamodzikamodzi. M’chochitika cha Paulo mwiniyo, iye anavomereza moona kuti: “Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.” (2 Akorinto 4:8, 9) Komabe, chimwemwe cha Mkristu chimachepetsa ndipo potsirizira pake chimachotsa nyengo zakupsinjika kwakanthaŵi ndi chisoni. Chimapereka nyonga yofunikira kupitirizabe kupita patsogolo, osaiŵala konse zifukwa zambiri zokondwerera.

8 Pamene mavuto abuka, kaya akhale otani, Mkristu wokondwera amapempha thandizo la Yehova modzichepetsa mwanjira ya pemphero. Samagonjera nkhaŵa yopambanitsa. Atachita zimene iye mwiniyo angathe kuchita mofatsa kuti athetse vutolo, amasiyira nkhaniyo m’manja mwa Yehova mogwirizana ndi pempho lakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.” Zidakali choncho, Mkristuyo amapitiriza kuthokoza Yehova chifukwa cha ubwino Wake wonse.​—Salmo 55:22; onaninso Mateyu 6:25-34.

9. Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cha choonadi chimaperekera mtendere wa maganizo, ndipo kodi ndi chiyambukiro chabwino chotani chimene zimenezi zili nacho pa Akristu?

9 “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:7) Chidziŵitso cha choonadi cha Baibulo chimamasula maganizo a Mkristu pa chinyengo ndi kumthandiza kukulitsa njira za kuganiza kwabwino. (2 Timoteo 1:13) Motero amathandizidwa kupeŵa khalidwe lolakwa kapena lopusa limene lingawononge maunansi amtendere ndi ena. Mmalo mwa kukhala wogwiritsidwa mwala ndi chisalungamo ndi kuipa, amaika chidaliro chake mwa Yehova kuthetsa mavuto a mtundu wa anthu kupyolera mu Ufumu. Mtendere wamaganizo wotero umatetezera mtima wake, kusunga zolinga zake zili zoyera, ndi kutsogolera maganizo ake m’njira ya chilungamo. Zolinga zoyera ndi maganizo abwino, nazonso, zimapatsa zifukwa zosaŵerengeka za kukondwera, mosasamala kanthu za mavuto ndi zitsenderezo zobweretsedwa ndi dziko lachipwirikitili.

10. Kodi chikondwerero choona chingapezedwe kokha mwa kulankhula kapena kuganiza za chiyani?

10 “Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Mkristu samakondwera ndi kunena kapena kuganiza zinthu zoipa. Zimenezi zimaphatikizapo zambiri za zosangulutsa zimene dziko limapereka. Palibe aliyense angasunge chikondwerero Chachikristu ngati adzaza m’maganizo mwake ndi mu mtima ndi mabodza, kulankhula zopanda pake, ndi nkhani zimene zili zosalungama, zoipa, zopanda ubwino, zovulaza, ndi zonyansa. Kunena mosabisa mawu, palibe amene angapeze chikondwerero choona mwa kudzaza zinthu zonyansa m’maganizo ndi mu mtima mwake. Nkomangirira chotani nanga kudziŵa kuti Akristu ali ndi zinthu zabwino zambirimbiri zoziganiza ndi zokambitsirana m’dziko la Satana loipali!

Zifukwa Zosaŵerengeka Zokondwerera

11. (a) Kodi nchiyani chimene sichiyenera kuonedwa mopepuka, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi nchiyambukiro chotani chimene kufika pamsonkhano wamitundu yonse kunakhala nacho pa nthumwi ina ndi mkazi wake?

11 Pamene tilankhula za zifukwa zokondwerera, tiyeni tisaiŵale za ubale wathu wa padziko lonse. (1 Petro 2:17) Pamene kuli kwakuti magulu a mitundu ndi mafuko a dziko amasonyezana udani waukulu, anthu a Mulungu amayandikirana pamodzi m’chikondi. Umodzi wawo umaonekera makamaka pamisonkhano yamitundu yonse. Ponena za wina umene unachitidwa mu 1993 ku Kiev, mu Ukraine, nthumwi ina ya ku United States inalemba kuti: “Misozi ya chikondwerero, nkhope zachimwemwe, kukumbatirana kosatha konga kwa m’banja, ndi kutumizirana malonje kuchokera kutsidya lina la bwalo lamaseŵero kochitidwa ndi magulu ogwedezerana amwafuli okongola ndi mipango ya m’manja mwachionekere kunali umboni wa umodzi wateokratiki. Mitima yathu imadzazidwa ndi kunyadira zimene Yehova wachita mozizwitsa mu ubale wa padziko lonse. Zimenezi zakhudza kwambiri mtima wanga ndi wa mkazi wanga ndipo zawonjezera tanthauzo latsopano pachikhulupiriro chathu.”

12. Kodi ndimotani mmene Yesaya 60:22 akukwaniritsidwira pamaso pathu penipeni?

12 Nkolimbitsa chikhulupiriro chotani nanga kwa Akristu lerolino kuona maulosi a Baibulo akumakwaniritsidwa pamaso pawo penipeni! Mwachitsanzo, talingalirani za mawu a Yesaya 60:22 akuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” Pakubadwa kwa Ufumu mu 1914, panali 5,100 okha​—wamng’ono​—amene anali kulalikira mokangalika. Koma mkati mwa zaka zisanu zapitazo, ukulu wa ubale wa padziko lonse wakhala ukuwonjezereka pa mlingo wa avareji ya 5,628 ya Mboni zobatizidwa chatsopano mlungu uliwonse! Mu 1993, chiŵerengero chapamwamba cha atumiki okangalika 4,709,889 chinafikiridwa. Tangoganizani! Zimenezi zikutanthauza kuti “wamng’ono” wa mu 1914 ali kwenikweni pafupi kukhala “chikwi”!

13. (a) Kodi nchiyani chimene chakhala chikuchitika chiyambire 1914? (b) Kodi Mboni za Yehova zimasunga motani lamulo la mkhalidwe la mawu a Paulo pa 2 Akorinto 9:7?

13 Chiyambire 1914 Mfumu Yaumesiya yatuluka kukagonjetsa pakati pa adani ake. Ulamuliro wake wachirikizidwa ndi otsatira aumunthu ofunitsitsa amene amapereka nthaŵi, nyonga, ndi ndalama kuchita ntchito ya kulalikira ya padziko lonse ndiponso mkupiti wa kumanga kwa padziko lonse. (Salmo 110:2, 3) Mboni za Yehova zimakondwera kuti ndalama zikuperekedwa kuti ntchito imeneyi imalizidwe, ngakhale kuti ndalamazo sizimatchulidwa kaŵirikaŵiri pa misonkhano yawo.a (Yerekezerani ndi 1 Mbiri 29:9.) Akristu oona safunikira kuumirizidwa kupatsa chopereka; iwo amakulingalira kukhala mwaŵi kuchirikiza Mfumu yawo kufikira kumlingo umene mikhalidwe yawo ikulola, aliyense “monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza.”​—2 Akorinto 9:7.

14. Kodi ndi mkhalidwe wotani umene waonekera pakati pa anthu a Mulungu chiyambire 1919, ukumawapatsa chifukwa chotani chokondwerera?

14 Kubwezeretsedwa kwa kulambira koona pakati pa anthu a Mulungu konenedweratuko kwalenga paradaiso wauzimu. Chiyambire 1919 wafutukula malire ake mopita patsogolo. (Salmo 14:7; Yesaya 52:9, 10) Chotulukapo chake? Akristu oona ‘akusangalala ndi kukondwa.’ (Yesaya 51:11) Kukhalapo kwa zipatso zabwino kuli umboni wa zimene mzimu woyera wa Mulungu ukhoza kuchita kupyolera mwa anthu opanda ungwiro. Thamo lonse ndi ulemu zimamka kwa Yehova, koma kodi ndi mwaŵi wina wokulirapo wotani umene ungakhalepo koposa kukhala antchito anzake a Mulungu? (1 Akorinto 3:9) Yehova n’ngwamphamvudi kwakuti akhoza kuchititsa miyala, ngati pali kufunika kotero, kulengeza uthenga wa choonadi. Komabe, iye waona kukhala koyenera kusatembenukira kunjira imeneyi, koma mmalomwake, kusonkhezera zolengedwa zofunitsitsa zopangidwa ndi fumbi kuchita chifuniro chake.​—Luka 19:40.

15. (a) Kodi ndi zochitika zamakono zotani zimene tikutsatira mwachidwi? (b) Kodi tikuyembekezera chochitika chotani ndi chikondwerero?

15 Ali odzazidwa ndi mantha aulemu, atumiki a Yehova tsopano akutsatira zochitika za dziko pamene zikusonyeza maulosi apadera a Baibulo. Mitundu ikuyesayesa​—koma mosaphula kanthu​—kupeza mtendere weniweni. Zochitika zikuiumiriza kupempha gulu la Mitundu Yogwirizana kuti lichitepo kanthu kumalo a mikangano. (Chivumbulutso 13:15-17) Zidakali choncho, anthu a Mulungu akuyang’ana kale kutsogolo ndi chiyembekezo chachikulu ku chimodzi cha zochitika zokondweretsa koposa chimene sichinachitikepo ndi kale lonse, chimene chikuyandikira tsiku ndi tsiku. “Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.”​—Chivumbulutso 19:7.

Kulalikira​—Cholemetsa Kapena Chikondwerero?

16. Fotokozani mmene kulephera kwa Mkristu kuchita zimene waphunzira kungamulandire chikondwerero chake.

16 “Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.” (Afilipi 4:9) Mwa kuchita zimene aphunzira, Akristu angayembekezere kulandira dalitso la Mulungu. Chimodzi cha zinthu zofunika koposa zimene aphunzira ndicho kufunika kwa kulalikira mbiri yabwino kwa ena. Ndithudi, kodi ndani amene angakhale ndi mtendere wa maganizo kapena kukondwera ngati analeka kupereka chidziŵitsocho kwa anthu oona mtima amene miyoyo yawo yeniyeniyo ikudalira pa kuchimva?​—Ezekieli 3:17-21; 1 Akorinto 9:16; 1 Timoteo 4:16.

17. Kodi nchifukwa ninji ntchito yathu ya kulalikira nthaŵi zonse iyenera kukhala magwero a chikondwerero?

17 Ha, ndi kokondweretsa chotani nanga kupeza anthu onga nkhosa ofunitsitsa kuphunzira za Yehova! Ndithudi, awo amene amatumikira ndi cholinga chabwino nthaŵi zonse adzapeza utumiki wa Ufumuwo kukhala magwero a chikondwerero. Izi zili chifukwa chakuti chifukwa chachikulu chokhalira Mboni ya Yehova ndicho kutamanda dzina Lake ndi kuchirikiza malo Ake monga Mfumu Yolamulira. (1 Mbiri 16:31) Munthu amene amazindikira choonadi chimenechi adzakondwera ngakhale pamene anthu mopanda nzeru akana mbiri yabwino imene amawabweretsera. Iye amadziŵa kuti kulalikira anthu osakhulupirira kudzatha tsiku lina; kutamanda dzina la Yehova kudzapitirizabe kosatha.

18. Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera Mkristu kuchita chifuniro cha Yehova?

18 Chipembedzo choona chimasonkhezera awo amene amachichita ndi kuchita zinthu zofunidwa ndi Yehova, osati chifukwa chakuti ayenera kutero, koma chifukwa chakuti amafuna kutero. (Salmo 40:8; Yohane 4:34) Anthu ambiri amaona zimenezi kukhala zovuta kumvetsetsa. Mkazi wina panthaŵi ina anauza Mboni imene inamfikira kuti: “Mukudziŵa, ndiyenera kukuyamikirani. Ine ndithudi sindingathe kulalikira kunyumba ndi nyumba ponena za chipembedzo changa monga momwe mukuchitira.” Mboniyo momwetulira inayankha kuti: “Ndikumvetsetsa mmene mukumvera. Ndisanakhale mmodzi wa Mboni za Yehova, simukanatha kundichititsa kumka kukalankhula ndi anthu ena za chipembedzo. Koma tsopano ndimafuna kutero.” Mkaziyo anasinkhasinkha kwakanthaŵi ndiyeno pomaliza anati: “Mwachionekere chipembedzo chanu chimapereka kanthu kena kamene sikamaperekedwa ndi changa. Mwinamwake ndiyenera kufufuza.”

19. Kodi nchifukwa ninji tsopano ili nthaŵi ya kukondwera kuposa ndi kale lonse?

19 Lemba lachaka cha 1994, losonyezedwa poyera m’Nyumba zathu Zaufumu, limatikumbutsa nthaŵi zonse kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” (Miyambo 3:5) Kodi pangakhale chifukwa chinanso chachikulu chokondwerera kuposa cha kukhala wokhoza kukhulupirira Yehova, linga lathu limene timabisalamo? Salmo 64:10 limafotokoza kuti: “Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye.” Inoyo sinthaŵi ya kukayikakayika kapena kuleka. Mwezi uliwonse umene ukupita umatidzetsa pafupi ndi chenicheni cha zimene atumiki a Yehova analakalaka kuona chiyambire masiku a Abele. Tsopano ndiyo nthaŵi ya kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, tikumadziŵa kuti sitinakhalepo ndi kale lonse ndi zifukwa zambirimbiri zotere zokondwerera!

[Mawu a M’munsi]

a Chidziŵitso chachifupi chosonyeza ndalama zopereka zaufulu zimene zinalandiridwa ndiponso zinthu zimene zinagulidwa chimaŵerengedwa pamisonkhano yaikulu ndiponso kamodzi pamwezi m’mipingo. Panthaŵi ndi nthaŵi makalata odziŵitsa za mmene zoperekazo zikugwiritsidwira ntchito amatumizidwa. Motero aliyense amakumbutsidwa za mkhalidwe wa ndalama za ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji, malinga ndi kunena kwa Nehemiya 8:10, tiyenera kukondwera?

◻ Kodi ndimotani mmene Deuteronomo 26:11 ndi 28:45-47 amasonyezera kufunika kwa kukondwera?

◻ Kodi ndimotani mmene Afilipi 4:4-9 amatithandizira kukondwera nthaŵi zonse?

◻ Kodi ndi chifukwa chotani chokondwerera chimene lemba lachaka cha 1994 limatipatsa?

[Chithunzi patsamba 16]

Mboni za ku Russia ndi za ku Germany zikukondwera kukhala mbali ya ubale wa padziko lonse

[Chithunzi patsamba 17]

Kuuza ena choonadi kuli chochititsa chikondwerero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena