“Ayesedwe”—Motani?
1 Chifukwa chakuti anthu m’gulu la Yehova akupitirira kuwonjezereka, pakufunikabe abale oyeneretsedwa kuti atumikire monga atumiki otumikira. Abale ambiri kuphatikizapo achinyamata amene pakalipano sanasankhidwe amafuna kwambiri kutumikira mu mpingo. Pamene apatsidwa ntchito yochuluka, amadzimva kuti akugwiritsidwa ntchito ndipo amakhala osangalala. Kupita kwawo patsogolo kwambiri kumadalira pa ‘kuyesedwa.’ (1 Tim. 3:10) Kodi zimenezi zimachitika motani?
2 Udindo wa Akulu: Monga mbali ya kuyesa mbale mwa ziyeneretso za Malemba za atumiki otumikira zopezeka pa 1 Timoteo 3:8-13, akulu ayenera kuyesa mbale ngati akuyenera kusamalira maudindo. Angam’patse ntchito zothandiza ngati kugaŵa magazini ndi mabuku, kusamalira zokuzira mawu, kusamalira Nyumba ya Ufumu, ndi zina zotero. Akulu adzaona mmene amachitira akauzidwa zimenezi ndiponso mmene akugwirira ntchitozo. Adzayang’ana mikhalidwe ya kudalirika, kusunga nthaŵi, khama, kudzichepetsa, mzimu wofunitsitsa, ndiponso kukhala bwino ndi ena. (Afil. 2:20) Kodi ali wachitsanzo chabwino m’kavalidwe ndi kapesedwe kake? Kodi ali ndi nzeru za uchikulire? Akufuna kuona mu “mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.” (Yak. 3:13) Kodi amayesetsadi kuthandiza mu mpingo? Kodi amamvera lamulo la Yesu la “phunzitsani anthu” mwakuchita nawo mwachangu utumiki wakumunda?—Mat. 28:19; onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1990 masamba 18-28.
3 Ngakhale kuti Baibulo siliika malire azaka zofunika kuti munthu asankhidwe kukhala mtumiki wotumikira, limatcha abale oterowo kukhala ‘iwo [“amuna,” NW] akutumikira.’ Sitingayembekezere kuti iwo akhale azaka zoyambira pa 13 mpaka 19, makamaka chifukwa chakuti akutchula kuti atha kukhala ndi mkazi ndi ana. (1 Tim. 3:12, 13) Amuna ameneŵa sayenera kuvomereza “zilakolako za unyamata” koma ayenera kukhala amakhalidwe abwino, a unansi wabwino ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi anthu.—2 Tim. 2:22.
4 Ngakhale kuti luso lachibadwa n’lofunika, maganizo a munthu ndi mtima wake n’zimene zili zofunika kwambiri. Kodi mbaleyo modzichepetsa amafuna kutamanda Mulungu ndiponso kutumikira abale ake? Ngati ndi choncho, Yehova adzadalitsa kuyesetsa kwake kupita patsogolo mu mpingo.