Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/15 tsamba 30
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kukhala Olinganizidwa Kaamba ka Kupulumuka Kuloŵa m’Zaka Chikwi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Chipulumutso Zimene Chimatanthauza Kwenikweni
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kupulumutsidwa Amoyo Kupyola Chisautso Chachikulu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/15 tsamba 30

Kodi Mumakumbukira?

Kodi munalingalirapo mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati nditero, mwinamwake mudzakhala okhoza kukumbukira zotsatirazi:

◻ Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Paulo akugwiritsira ntchito liwu lakuti “nkhoswe” polozera kwa Yesu pa 1 Timoteo 2:5, 6?

Mlemba limeneli, Paulo akugwiritsira ntchito liwu Lachigriki me·siʹtes kaamba ka “nkhoswe,” liwu lokhala ndi kudziŵika kwalamulo, chotero iye sakugwiritsira ntchito liwu limeneli m’lingaliro lalikulu lofala m’zinenero zambiri. Chotero, Paulo sakunena kuti Yesu ali Nkhoswe pakati pa Mulungu ndi mtundu onse wa anthu. M’malomwake, iye akulozera kwa Kristu kukhala Nkhoswe yalamulo ya pangano latsopano, limene linayala maziko kaamba ka atsatiri odzozedwa a Kristu kugawana naye mu Ufumu wakumwamba. (2 Akorinto 5:1, 5; Aefeso 1:13, 14; Ahebri 8:7-13)​—8/15, masamba 30, 31.

◻ Pa Mateyu 25:34, kodi Yesu akutanthauzanji pamene anena kwa onga nkhosa kuti: “Loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi”?

Yesu sanatanthauze kuti onga nkhosa ameneŵa adzalamulira limodzi naye kumwamba. M’malomwake, nkhosazo zidzalandira malo a pa dziko lapansi a Ufumuwo wokonzedwera iwo “pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi” la mtundu wa anthu wowomboledwa. Mwanjira imeneyi iwo amakhala ana a pa dziko lapansi a “Atate [wawo] Wosatha,” Mfumuyo, Kristu Yesu. (Yesaya 9:6, 7)​—9/1, tsamba 20.

◻ Kodi chikakhala choyenera kwa otsalira odzozedwa kukhalabe amoyo pa dziko lapansi kudzalandira okhulupirika owukitsidwa amene anamwalira 33 C.E. isanafike?

Ayi, chimenechi sichikakhala chofunikira. Unyinji wa a khamu lalikulu amene adzapulumuka chisautso chachikulu akuphunzitsidwa tsopano kusamalira mathayo a gulu. Chotero, iwo akukhala okhoza kusamalira mkhalidwe umenewo ndi kuzoloŵeretsa owukitsidwawo ku “dziko latsopano” pansi pa “miyamba yatsopano.” (2 Petro 3:13)​—9/1, masamba 20, 21.

◻ Kodi ndi zinthu zotani zoloŵetsedwamo mu “kupulumuka”? (Machitidwe 16:30)

Chofunikira chachikulu nchakuti: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka.” (Machitidwe 16:31) Izi zimaloŵetsamo kupeza chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu ndi njira yake ya chipulumutso. Ndiyeno tiyenera kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu monga Mkulu wa chipulumutso. (Yohane 3:16; Tito 2:14) Zimenezi zimaika Mkristu mu mkhalidwe wopulumutsidwa, koma tsopano ayenera kupirira kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kupitirizabe kumamatira ku ziyeneretso zonse za Mulungu kwa moyo wake wonse. Kokha mwakutero ndi pamene adzapulumuka kupeza moyo wamuyaya. (Mateyu 24:13)​—9/15, tsamba 7.

◻ Kodi ndimotani mmene chikhulupiriro cha Nowa chinatsutsira dziko? (Ahebri 11:7)

Chimvero cha Nowa ndi machitidwe a chilungamo zinasonyeza kuti ena ake pambali pa iye ndi banja lake akanakhoza kupulumuka Chigumulacho ngati anali ofunitsitsa kusintha njira yawo yamoyo. Mosasamala kanthu za zididikizo za thupi lake lopanda ungwiro, dziko lomuzinga, ndi Mdyerekezi, Nowa anatsimikizira kuti kunali kotheka kukhala ndi moyo umene unakondweretsa Mulungu.​—10/1, tsamba 11.

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchenjera ndi miseche wamba?

Ife tingapange ndemanga yosakonzedwera kuvulaza wina, koma miseche yowoneka kukhala yopanda chifukwa ingakhale yovulaza pamene ibwerezedwa, kukometseredwa, kapena kupotozedwa, kotero kuti imawononga mbiri ya munthu wolankhulidwayo, kumbera dzina lake labwino. (Miyambo 20:19)​—10/15, tsamba 13.

◻ Kodi pali maubwino otani pamene okwatirana amangidwa m’goli lolingana?

Mwamuna ndi mkazi ali m’malo a kulimbikitsana kulambira Mulungu wawo. Ndiponso, iwo angapite ku Malemba kaamba ka chitsogozo m’kuthetsa mikangano yawo.​—11/1, tsamba 20.

◻ Kodi ndimotani mmene Malamulo Khumi angatithandizire lerolino?

Iwo amavumbula kawonedwe ka Yehova pa nkhani ndi kutumikira monga zotikumbutsa thayo lathu la kukonda Mulungu ndi mnansi. (Mateyu 22:37-39; 2 Timoteo 3:16, 17)​—11/15, masamba 5, 6.

◻ Kodi ndi pa zochitika zitatu ziti pamene Mulungu analankhula kwa Yesu anthu akumva?

Chochitika choyamba chinali pa nthaŵi ya ubatizo wa Yesu wochitidwa ndi Yohane Mbatizi (Mateyu 3:17); chachiŵiri chinali pamene Yesu anasandulizika pamaso pa Yakobo, Yohane, ndi Petro (Mateyu 17:5); ndipo chachitatu chinali pa Nisani 10, masiku anayi imfa ya Yesu isanachitike, pamene liwu la Mulungu linamvedwa ndi khamu loimirira m’kachisi. (Yohane 12:28)​—12/1, tsamba 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena