Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 12/1 tsamba 4-8
  • Achinyamata Okhala ndi Tsogolo Labwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata Okhala ndi Tsogolo Labwino
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Aukali”
  • Kuukiridwa
  • Funafunani Ndipo Mudzapeza
  • Chiphunzitso Chaumulungu Chipindulitsa
  • Funitsitsani Maziko Abwino a Mtsogolo
  • Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Tsokalo Lidzatha Liti?
    Galamukani!—1995
  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mmene Mungapambanire Paunyamata Wanu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 12/1 tsamba 4-8

Achinyamata Okhala ndi Tsogolo Labwino

“KUNALI [kugwirira mkazi] koopsa ndi koipitsitsa koposa”​—ndimo mmene woweruza wina anafotokozera upanduwo pozenga mlandu posachedwapa. Gulu la achinyamata asanu ndi atatu, azaka zakubadwa 14 mpaka 18, analalira mkazi wina wodzaona malo mkati mwenimweni mwa mzinda wa London, kumgwira ndi kumgona mobwerezabwereza, ndiye kenako kumponya mumfuleni wa madzi umene unali pafupi ngakhale ananena kuti satha kusambira. Ndipo akuti amayi wa mmodzi wa achinyamatawo ananena kuti anadwala ataona panyuzi ya pa TV zimene mwana wawo anachita.

Mwachisoni, chochitikachi chikusonyeza zimene zikuchitika pakati pa anthu lerolino. Nkhanza yakhala chizoloŵezi, kaya pochita zaupandu, m’mikangano yapanyumba, kapena m’mikangano yamafuko ku maiko a ku Balkan, maiko a pakati ndi a kumadzulo kwa Afirika, ndi kumadera ena. Achinyamata amakulira m’mikhalidwe imeneyi, kapena nthaŵi zambiri amamva nkhani zimenezi. Ndiye chifukwa chake ambiri amakhala opanda chifundo, amasonyeza kukhala “opanda chikondi chachibadwidwe,” ndiponso ali “osakhoza kudziletsa.”​—2 Timoteo 3:3.

“Aukali”

Pamene mtumwi wachikristu Paulo analemba kalata yake yachiŵiri kwa mkulu mnzake Timoteo, Roma anali ulamuliro wa dziko lonse. Nkhanza ndi kupanda chifundo zinali zofala m’mabwalo amaseŵero achiroma. Komabe, Paulo anachenjeza kuti mtsogolo, nthaŵi zidzakhala “zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1, NW) Chosangalatsa nchakuti liwu lachigiriki lofotokoza nthaŵi zino kukhala “zovuta kuchita nazo” limaphatikizapo lingaliro la kukhala ‘zaukali.’ Chochitika china mu utumiki wa padziko lapansi wa Yesu zaka zoposa 30 kalatayi isanalembedwe chikusonyeza chimene nthaŵi zina chinkachititsa ukali m’nthaŵi yake.

Yesu anali atangofika kumene pagombe lakummaŵa la Nyanja ya Galileya pabwato. Atafika pagombepo, amuna aŵiri anakomana naye. Kaonekedwe kawo koopsa ndi kufuula kwawo zinasonyeza poyera kuti panali kena kake kolakwika kwambiri ndi amunawo. Iwo anali “aukali ndithu,” kwenikweni, anali ogwidwa ndi ziŵanda.a Zomwe anali kufuula zinali kuchokera kwa mizimu yoipa yomwe inali kuwachititsa chiwawa. “Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu?” anafuula motero amunawo. “Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthaŵi yake siinafike?” Mizimu yoipa yomwe inagwira aŵiriwo inadziŵa bwino lomwe kuti Mulungu anali ataika kale nthaŵi yopereka chiŵeruzo chake pa ziŵanda. Kumeneku kudzakhala kuwonongedwa kwawo kotheratu. Koma nthaŵiyo isanafike izo zidzakhala zikugwiritsira ntchito mphamvu yawo yauzimu kuyambitsa chiwawa choopsa. Chozizwitsa cha Yesu chochotsa ziŵanda ndicho chinadzetsa mpumulo kwa amuna aŵiriwo.​—Mateyu 8:28-32; Yuda 6.

Pamene anthu lerolino, kuphatikizapo achinyamata, achita zinthu moyaluka, tingachite bwino kukumbukira chochitikacho. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’zaka za zana lino la 20, tili pangozi yofananayo, monga momwe buku lomaliza la m’Baibulo, Chivumbulutso, likufotokozera kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Chonde, onani kuti kutsitsidwa kumeneku kwa Satana kwampangitsa kuti akhale ndi “udani waukulu” chifukwa chakuti akudziŵa kuti nthaŵi yamthera.

Kuukiridwa

Monga momwe magazini ino imatchulira nthaŵi zambiri, m’chaka cha 1914 Kristu Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Nthaŵi yomweyo Yesu anachitapo kanthu kwa mdani wamkulu wa Mulungu, Satana. Chotero, Mdyerekezi ndi ziŵanda zake analetsedwa kuti asaloŵenso kumwamba, ndipo tsopano asumika maganizo awo padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-9) Pokhala kuti malo ake a ntchito anachepetsedwa kwambiri, Satana “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Kodi ndani yemwe iye amagwira mosavuta? Kodi sizomveka kuti kwenikweni ndi awo omwe samadziŵa zambiri m’moyo ndi maunansi a anthu? Chotero achinyamata lerolino akhala chandamale cha Mdyerekezi. Mwa nyimbo zawo zambiri ndi kulondola kwawo zosangulutsa, iwo amaseŵerera m’manja mwenimwenimo mwa wolamulira zochita zawo wamachenjera ameneyu.​—Aefeso 6:11, 12.

Ngakhale pamene achinyamata ayesa kukhala ndi moyo wabwino, amapeza kuti pali zowalepheretsa. Chithere Nkhondo Yadziko II, anthu m’maiko ambiri momwe kale munali nkhondo akonzera mabanja awo moyo wapamwamba poyesa kulipsira mavuto a nkhondowo. Katundu wakuthupi, kusanguluka mosadziletsa, ndi zosangulutsa zina zakhala zinthu zofunika kwambiri. Chotsatirapo chake nchakuti ambiri avutika. “Iwo akufuna kukhala achuma,” Paulo anachenjeza Timoteo motero, “amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka . . . Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba . . . [a]nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Ndithudi, timaona kuti anthu amakono okondetsa chuma amapyozedwa ndi zoŵaŵa za mkhalidwe wa zachuma, ndalama, ndi maganizo. Pakati pawo pali achinyamata ambiri omwe akuvutika ndi machenjera ameneŵa a mdani wamkulu wa Mulungu.

Komabe, mwamwaŵi pali uthenga wabwino. Ndipo ukunena za achinyamata, awo amene ali ndi tsogolo labwino. Kodi nzotheka motani?

Funafunani Ndipo Mudzapeza

Achinyamata ambiri ali ndi malingaliro apamwamba kwambiri. Iwo amakana mikhalidwe yonyonyosoka imene ili pakati pa akuluakulu ambiri. Iwo amanyansidwa ndi kupanda chilungamo ndi chifundo kwa andale ndi amalonda osirira mphamvu zaulamuliro. Ngati ndinu wachinyamata, mwina mumamva chonchi.

Talingalirani za Cedric, wachinyamata wazaka pafupifupi 20 zakubadwa, amene chokumana nacho chake sichachilendo.b Pamene anali mwana, anali kuopa zinthu zambiri, kuphatikizapo imfa. Anali kufuna kudziŵa chifuno cha moyo. Posapeza mayankho a mafunso ake atakwanitsa zaka 15 zakubadwa, iye anangoyamba kusinkhasinkha za moyo limodzi ndi achinyamata ena amalingaliro apamwamba kwambiri. “Tinali kusuta chamba ndi kungokhala pansi kukambitsirana kwa maola ambiri,” akukumbukira motero. “Unali kuona monga kuti onse ali ndi malingaliro ofanana ndi ako, koma palibe yemwe anali ndi mayankho.”

Cedric, monga achinyamata ambiri, analakalaka kusangalala. Kungomwa mankhwala osokoneza bongo sikunamkhutiritse. Posapita nthaŵi anayamba kuba ndi kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo. Koma anafunabe zinthu zina zomsangalatsa. Anayamba kulandira maoda okaba katundu wakutiwakuti. “Zinandisangalatsa kwambiri zimenezi,” akuvomereza motero. “Koma sindinali kubera munthu wamba. Ndikaba galimoto, ndinali kuisiya ili yosawonongeka. Ndikathyola nyumba ya malonda, ndinali kuchita zimenezo kwa okhawo amene ndadziŵa kuti ali ndi inshuwalansi. Zinandithandiza kuona monga ndili ndi chifukwa chabwino chochitira zimenezo.” Monga momwe mungayembekezere, Cedric anaponyedwa m’ndende.

Cedric akukumbukira kuti: “Mark, wandende mnzanga, anandilankhula. Ataona kuti ndinali ndi mtanda waukulu wodindidwa pamkono wanga, anandifunsa chifukwa chake ndinali ndi mtandawo. Anaganiza kuti ndinaudindapo chifukwa cha chipembedzo.” Patapita milungu ingapo, Mark anapatsa Cedric kope la buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.c “‘Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha’​—mawu ochepa amenewo anandichititsa chidwi nthaŵi yomweyo. Zimenezi nzimene tinali kukambitsirana nthaŵi zonse, koma sitinapezepo choonadi chake.” Atakambitsirana nthaŵi zambiri ndi mmodzi wa Mboni za Yehova yemwe anali kuchezera ndendeyo, Cedric anazindikira kuti kunali kotheka kupeza zomwe analakalaka​—koma m’njira ya Mulungu yokha.

“Nditasiya kuyanjana ndi mabwenzi anga akale, ndinapita patsogolo mwamsanga,” Cedric akutero. Kumvetsa kwake zinthu ndi kupeza chimwemwe kwakhala kovuta. “Ndikuyesetsabe kuwongolera,” iye akutero. “Ndimayenera kusamala pa zimene ndimalingalira.” Inde, Cedric tsopano akudziŵa kuti kukhala ndi malingaliro apamwamba kunamloŵetsa mumsampha wa Mdyerekezi, polingalira kuti adzakwanitsa zolinga zake kokha mwa kuchita zinthu zomsangalatsa.

Ubwino wake ngwakuti ndi kale pamene Cedric anamasulidwa kundende, ndipo akusangalala ndi kuyanjana nthaŵi zonse ndi enanso amene anapeza chimene anali kufunafuna. Iye tsopano ndi mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo iyenso ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo m’Paradaiso pano padziko lapansi. Iye akuyembekezeranso kutha kwa chisonkhezero cha Satana cha mitundu yake yonse yosiyanasiyana.

Zoonadi, si achinyamata okha onga Cedric amene ali ndi tsogolo labwino; ena aleredwa ndi makolo oopa Mulungu, amene anazika mwa ana awo chikondi cha choonadi cha Baibulo.

Chiphunzitso Chaumulungu Chipindulitsa

“Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo,” Mfumu Solomo yanzeru yakaleyo inalemba motero. (Miyambo 22:6) Zakhaladi choncho kwa achinyamata ambiri omwe asankha kutsatira malamulo a Baibulo ndi mtima wonse.

Sheila, Gordon, ndi Sarah anachita zimenezi. Iwo akukumbukira kuti makolo awo anali kugogomezera kwambiri kumvera lamulo la Kristu la ‘kumka ndi kuphunzitsa anthu’ mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) “Pazosankha zilizonse zomwe tinafunikira kupanga, Amayi ndi ineyo tinali kufunsana kuti, ‘Kodi zimenezi zidzagwirizana motani ndi ntchito yolalikira?’” akukumbukira motero Sheila. “Tinasiya ntchito zambiri chifukwa cha maganizo ameneŵa,” akuvomereza motero, nawonjezera kuti, “koma si madalitso ake amene tinapeza!” Ngakhale atamaliza kuchezera anthu ambirimbiri m’nyumba zawo ndi uthenga wabwino, Sheila ndi amake anali kubwerera kunyumba akuimba mosangalala. “Ndinali ndi chimwemwe chachikulu kwambiri,” iye akutero. “Ndikudzimva motero tsopano.”

Gordon akukumbukira masiku ambiri pa Loŵeruka madzulo pamene ankasangalala. “Akulu a mumpingo anali kundiitana kunyumba zawo, kumene tinali kuchita maseŵero ofunsana mafunso ndi kukambitsirana zinthu zopindulitsa. Anatilimbikitsa kuloŵeza mavesi a m’Baibulo, kulankhula mwaufulu pankhani za m’Malemba, kusimba chokumana nacho cha mu ulaliki, ndi kuona momwe ntchito ya Ufumu inali kukulira,” akukumbukira motero Gordon. “Zonsezi zinandithandiza kukhala ndi chiyambi chabwino ndi kukulitsa chikondi cha pa Yehova Mulungu.”

Sarah amakumbukira masiku ambiri osangalatsa pamene anali kuchezera Mboni madzulo. “Tinali kudya chakudya limodzi. Ndiyeno pamapeto ake, tinali kuliza piyano, motsagana ndi oimba nyimbo za Ufumu wa Mulungu. Nyimbo zinatithandizadi kwambiri, makamaka pazaka zomwe tinali pasukulu, chifukwa chakuti zinali kutichititsa kuchitira zinthu pamodzi monga banja.”

Nzoona kuti si achinyamata onse ofuna kukondweretsa Yehova omwe mabanja awo ali mumkhalidwe wabwino. Komabe, kuyanjana kwambiri ndi mabanja ena a Mboni mumpingo kumawachititsa kukhala otetezereka ndi kukhala paubwenzi wathithithi.

Funitsitsani Maziko Abwino a Mtsogolo

Achinyamata lerolino ayenera kusankha. Akhoza kupitiriza ndi dziko loipali pamene likuyandikira mofulumira ku chiwonongeko pa “chisautso chachikulu” chimene Yesu ananeneratu. Kapena akhoza ‘kukhala ndi chiyembekezo chawo kwa Mulungu, . . . kusunga malamulo ake,’ monga momwe wamasalmo wouziridwa Asafu anaimbira. Kumvera Mulungu kudzawatetezera kuti asakhale “mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wawo, ndi mzimu wawo sunakhazikika ndi Mulungu.”​—Mateyu 24:21, NW; Salmo 78:6-8.

M’mipingo 80,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, mudzapeza achinyamata ambiri omwe adzakusangalatsani. Iwo alabadira uphungu wa Paulo kwa Timoteo wachinyamatayo “kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugaŵira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi.” Chotero, iwo tsopano ‘agwira moyo weniweniwo.’ (1 Timoteo 6:18, 19) Fufuzani zowonjezereka ponena za Akristu enieni ameneŵa mwa kufika pamisonkhano yawo. Ndiye inunso mudzakhala ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino.

[Mawu a M’munsi]

a Liwu limodzimodzi lachigiriki logwiritsiridwa ntchito pa Mateyu 8:28 ndi pa 2 Timoteo 3:1 latembenuzidwa kuti “aukali.”

b Maina asinthidwa.

c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 7]

Mizimu yoipa ndiyo inali kusonkhezera amuna “aukali ndithu” amene Yesu anachiritsa

[Chithunzi patsamba 8]

Kumanga “maziko okoma a kunyengo ikudzayi”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena