Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/15 tsamba 8-13
  • Chiphunzitso Chothandiza M’nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiphunzitso Chothandiza M’nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro Lochokera m’Mbiri Yakale
  • Ulosi Wonena za Nthaŵi Zathu
  • Patani Mapindu Olemeretsa
  • Kodi Tikukhaladi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
    Dikirani!
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/15 tsamba 8-13

Chiphunzitso Chothandiza M’nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa

“Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. . . . Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”​—2 TIMOTEO 3:1, 13.

1, 2. Kodi nchifukwa ninji tifunikira kupenda ziphunzitso zimene tikuzitsatira?

KODI mukuthandizidwa, kapena mukupwetekedwa? Kodi mavuto anu akuthetsedwa kapena kodi akukulitsidwa? Kodi chikuwathetsa kapena kuwakulitsa nchiyani? Ndizo ziphunzitso. Inde, ziphunzitso zikhoza kuyambukira kwambiri moyo wanu mwa njira yabwino kapena yoipa.

2 Maprofesa atatu anafufuza zimenezi posachedwapa ndipo anapereka zimene anapeza m’magazini otchedwa Journal for the Scientific Study of Religion. Zowona, iwo mwinamwake sanafufuze za inu kapena banja lanu. Komabe, zimene anapeza zimasonyeza kuti pali kugwirizana kotsimikizirika pakati pa ziphunzitso ndi chipambano cha munthu, kapena kulephera kwake, pochita ndi nthaŵi zathu zoŵaŵitsa. M’nkhani yotsatira, tidzapenda zimene anapeza.

3, 4. Kodi pali maumboni ena ati osonyeza kuti tikukhala m’nthaŵi zoŵaŵitsa?

3 Komabe choyamba, talingalirani funso ili: Kodi mukuvomereza kuti tikukhala m’nthaŵi zovuta kuchita nazo? Ngati mukutero, pamenepo muyenera kuona kuti umboni umasonyeza kuti zino zilidi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Anthu amayambukiridwa mwanjira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mwinamwake inu mukudziŵa maiko amene tsopano akugaŵanika ndi chipwirikiti pamene magulu osiyanasiyana akumenyanira ulamuliro wandale. Ku maiko enanso, kuli kuphana kaamba ka kusamvana kwa zipembedzo kapena mafuko. Asilikali sindiwo okha amene amavulazidwa. Talingalirani za akazi ndi atsikana osaŵerengeka amene achitiridwa nkhanza kapena nkhalamba zimene zamanidwa chakudya, kufunda, ndi nyumba. Anthu osaŵerengeka akuvutika momvetsa chisoni zedi, zikumachititsa kuchuluka kowopsa kwa othaŵa kwawo ndi mavuto ena ambiri.

4 Nthaŵi zathu zadzalanso ndi mavuto a zachuma, omwe achititsa kutsekedwa kwa mafakitale, ulova, kutayikiridwa ndi ziwongola dzanja zapantchito, mapenshoni, kutha mphamvu kwa ndalama, ndi kuchepa kapena kusoŵa kwa chakudya. Kodi mungawonjezere zina pa ndandandayo? Mwinamwake mungatero. Mamiliyoni ena kuzungulira dziko lonse akuvutika ndi kupereŵera kwa chakudya ndi matenda. Mwachionekere, mwaona zithunzithunzi zochititsa kakasi zochokera ku East Africa zosonyeza amuna, akazi, ndi ana otsala mafupa okhaokha ndi olenguka ndi njala. Mamiliyoni a anthu m’maiko a ku Asia akuvutika mofananamo.

5, 6. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti matenda nawonso ali mbali yowopsa ya nthaŵi zathu zoŵaŵitsa?

5 Tonsefe tamva za matenda owopsa amene akuwonjezereka tsopano. Pa January 25, 1993, The New York Times inati: “Mliri wa AIDS wa ku Latin America ukufalikira mofulumira pakati pa anthu achiwerewere, mosasamala kanthu za njira zochinjirizira zakanthaŵi ndi zongoyesa, ukumapitirira uja wa United States . . . Chiŵerengero chomakula mofulumira kwambiri chili pakati pa . . . akazi.” Mu October 1992, U.S.News & World Report inati: “Pangopita zaka makumi aŵiri pamene dokotala wina wa ku United States, pothokoza chipambano china cha thanzi la anthu chimene sichinapezedwepo chikhalire, analengeza kuti nthaŵi inafika ‘yakuleka kudera nkhaŵa ndi matenda oyambukira.’ Koma bwanji tsopano? “Zipatala zadzalanso ndi anthu okanthidwa ndi miliri ya matenda amene anayenera kukhala atagonjetsedwa. . . . Tizilombo topatsa matenda tikukhalapo m’thupi la munthu mwanjira zovuta kwambiri kuzindikira kwakuti timakula pa liŵiro lofulumira kwambiri kuposa la kupangidwa kwa mankhwala atsopano. . . . ‘Tikuloŵa m’nyengo yatsopano ya matenda oyambukira.’”

6 Monga chitsanzo chimodzi chokha, Newsweek ya pa January 11, 1993, inanena kuti: “Tizilombo topatsa malungo tsopano tikuyambukira anthu pafupifuppi 270 miliyoni chaka chilichonse, tikumapha ofika ku 2 miliyoni . . . ndi kuchititsa pafupifupi anthu 100 miliyoni kudwala kwakayakaya. . . . Panthaŵi imodzimodziyo, nthendayo ikukhala yovutirapo nthaŵi zonse kuchiritsidwa ndi mankhwala amene kale anali kuichiritsa. . . . Mitundu ina ya malungo posachedwapa idzakhala yosachiritsika.” Zimachititsa mantha kwambiri.

7. Kodi ambiri lerolino akuchita motani ponena za nthaŵi zovuta zino?

7 Mwina mwaona kuti m’nthaŵi zoŵaŵitsa zino, ambiri akufunafuna chithandizo cha kuthetsa mavuto awo. Mwachitsanzo, talingalirani za awo amene amatembenukira ku mabuku onena za mmene munthu angachitire ndi kupsinjika maganizo kapena nthenda ina yatsopano. Ena mothedwa nzeru amafunafuna uphungu kaamba ka ukwati wawo umene ukulephera, kusamalira ana, uchidakwa kapena mankhwala oledzeretsa, kapena mmene angalinganizire zofuna za ntchito ndi zitsenderezo zapanyumba. Inde, amafunikiradi chithandizo! Kodi inuyo mukulimbana ndi vuto laumwini kapena mavuto ena ochititsidwa ndi nkhondo, njala, kapena tsoka? Ngakhale ngati vuto losautsa lingaoneke kukhala losakhoza kutha, muyenera kufunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji tafika pa mkhalidwe wovuta kwambiri choncho?’

8. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupita ku Baibulo kaamba ka chidziŵitso ndi chitsogozo?

8 Tisanadziŵe njira yabwino yolimbanira nazo ndi kupeza chikhutiritso m’moyo tsopano ndi mtsogolo, tifunikira kudziŵa chifukwa chake tikuyang’anizana ndi nthaŵi zovuta motero. Kunena zowona, zimenezo zimapatsa aliyense wa ife chifukwa chopendera Baibulo. Kodi nchifukwa ninji tikutchula Baibulo? Chifukwa chakuti ilo lokhalo lili ndi ulosi wolondola, mbiri yolembedwa pasadakhale, imene imasonyeza zifukwa za mkhalidwe umene tilimowu, pamene tili, ndi kumene tikupita.

Phunziro Lochokera m’Mbiri Yakale

9, 10. Kodi ulosi wa Yesu pa Mateyu chaputala 24 unakwaniritsidwa motani m’zaka za zana loyamba?

9 Nsanja ya Olonda ya February 15, 1994, inapereka mapendedwe a ulosi wa Yesu wofunikira kuudziŵa woonekera bwino pa Mateyu chaputala 24. Ngati mutsegula Baibulo lanu pachaputala chimenecho, mukhoza kuona m’vesi 3 kuti atumwi a Yesu anafunsa za chizindikiro cha kukhalapo kwake kwa mtsogolo ndi cha chimaliziro cha dongosolo la zinthu. Kenako, m’mavesi 5 mpaka 14, Yesu ananeneratu za a Kristu onama, nkhondo, kupereŵera kwa chakudya, kuzunzidwa kwa Akristu, kusayeruzika, ndi kulalikira mofalikira Ufumu wa Mulungu.

10 Mbiri yakale imatsimikizira kuti zinthu zimenezo zinachitikadi mkati mwa chimaliziro cha dongosolo la zinthu Lachiyuda. Ngati mukadakhalako panthaŵiyo, kodi nthaŵi zimenezo sizikadakhala zovuta kwa inu? Komabe, zinthu zinali kufika pachimake, chisautso chosayerekezereka pa Yerusalemu ndi dongosolo Lachiyuda. M’vesi 15 tiyamba kuŵerenga zimene zinachitika pamene Aroma anaukira Yerusalemu mu 66 C.E. Zochitikazo zinathera m’chisautso chimene Yesu anatchula m’vesi 21​—kupasulidwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E., chisautso choipitsitsa chimene sichinayambe chagwerapo mzindawo. Chikhalirechobe, mudziŵa kuti mbiri sinathere pamenepo, ndipo Yesu sananene kuti ikatero. M’mavesi 23 mpaka 28, iye anasonyeza kuti pambuyo pa chisautso cha mu 70 C.E., zinthu zina zikachitika.

11. Kodi kukwaniritsidwa kwa m’zaka za zana loyamba kwa Mateyu chaputala 24 kumagwirizana motani ndi tsiku lathu?

11 Ena lerolino anganyalanyaze zimenezi mwa kunena kuti, ‘Kodi nanga zili ndi kufunika kwanji zimenezo?’ Kumeneko kukakhala kulakwa. Kukwaniritsidwa kwa ulosi kalelo nkofunika kwambiri. Chifukwa ninji? Eya, nkhondo, njala, zivomezi, miliri, ndi zizunzo mkati mwa chimaliziro cha dongosolo la zinthu Lachiyuda zinafunikira kuonekera m’kukwaniritsidwa kwakukulu pambuyo pa kutha kwa “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu” mu 1914. (Luka 21:24, NW) Ambiri okhala ndi moyo tsopano anali mboni zoona ndi maso za Nkhondo Yadziko ya I pamene kukwaniritsidwa kwamakonoku kunayamba. Koma, ngakhale ngati munabadwa pambuyo pa 1914, inuyo mwaona ulosi wa Yesu ukukwaniritsidwa. Zochitika za m’zaka za zana lino la 20 zimatsimikizira mosakayikiritsa konse kuti tikukhala m’chimaliziro cha dongosolo loipa lilipoli.

12. Malinga ndi kunena kwa Yesu, kodi tingayembekezere kuonabe chiyani?

12 Zimenezi zimatanthauza kuti ‘chisautso’ cha pa Mateyu 24:29 chili patsogolo pathupa. Chidzaloŵetsamo chochitika chakumwamba chimene sichingayerekezeredwe konse. Vesi 30 limasonyeza kuti pamenepo anthu adzaona chizindikiro chosiyana​—chotsimikiziritsa kuti chiwonongeko chayandikira. Mogwirizana ndi cholembedwa chofanana cha pa Luka 21:25-28, panthaŵi yamtsogolo imeneyo ‘anthu adzakomoka ndi mantha ndi zinthu zoyembekezeredwa kudza padziko lapansi.’ Cholembedwa cha Luka chimanenanso kuti Akristu panthaŵiyo adzatukula mitu yawo chifukwa chakuti chipulumutso chawo chidzakhala pafupi kwambiri.

13. Kodi ndimfundo zazikulu ziŵiri zotani zimene zikufunikira chisamaliro chathu?

13 Mwina inu munganene kuti, ‘Eya, ndivomereza ndi kukhulupirira zimenezo, koma nanga funso paja silakuti kodi ndingamvetsetse motani ndipo ndingalimbane nazo motani nthaŵi zoŵaŵitsa zimenezi?’ Mwalondola. Mfundo yathu yoyamba ndiyo kuzindikira mavuto aakulu ndi kuona mmene tingawapeŵere. Yogwirizana nayo ndiyo mfundo yachiŵiri, mmene ziphunzitso Zamalemba zingatithandizire kusangalala ndi moyo wabwinopo tsopano lino. Pamfundo zimenezi, chonde tsegulani Baibulo lanu pa 2 Timoteo chaputala 3, ndipo onani mmene mawu a mtumwi Paulo angakuthandizireni kulimbana ndi nthaŵi zoŵaŵitsa zimenezi.

Ulosi Wonena za Nthaŵi Zathu

14. Kodi nchifukwa ninji pali chifukwa chokhulupirira kuti kupenda 2 Timoteo 3:1-5 kungatipindulitse?

14 Mulungu anauzira Paulo kulembera Mkristu wokhulupirika Timoteo uphungu wabwino kwambiri umene unamthandiza kukhala ndi moyo wachipambano ndi wachimwemwe chachikulu. Zina za zimene Paulo analemba zinali kudzakwaniritsidwa kwenikweni m’tsiku lathu. Ngakhale ngati mukuganiza kuti mumazidziŵa bwino lomwe, tsatirani mosamalitsa tsopano mawu aulosiwo a pa 2 Timoteo 3:1-5. Paulo analemba kuti: “Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”

15. Kodi nchifukwa ninji lemba la 2 Timoteo 3:1 lingakhale lapadera kwa ife tsopano?

15 Chonde onani kuti pandandalikidwa zinthu 19. Tisanazipende zimenezi ndi kuona mmene tingapindulire, imani kaye ndi kumvetsetsa ulosi wonsewo. Yang’anani pa vesi 1. Paulo ananeneratu kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” “Masiku otsiriza” ati? Pakhala masiku otsiriza ambiri, monga masiku otsiriza a mzinda wamakedzana wa Pompeii kapena masiku otsiriza a mfumu kapena banja lolamulira. Ngakhale Baibulo limatchula masiku otsiriza angapo, monga masiku otsizira a dongosolo Lachiyuda. (Mac. 2:16, 17) Komabe, Yesu anatiyalira maziko akuti tizindikire kuti “masiku otsiriza” amene Paulo anatchula ndiwo nthaŵi yathu ino.

16. Kodi ndimkhalidwe wotani umene fanizo la tirigu ndi namsongole linaneneratu ponena za nthaŵi yathu?

16 Yesu anachita zimenezo m’fanizo lonena za tirigu ndi namsongole. Mbewuzi zinabzalidwa m’munda ndi kusiidwa kuti zikule. Iye anati tirigu ndi namsongole zikuimira anthu​—Akristu owona ndi onyenga. Tikutchula fanizo limeneli chifukwa chakuti limasonyeza kuti panayenera kupita nyengo yaitali yanthaŵi chimaliziro cha dongosolo lonseli chisanadze. Pamene chimalizirocho chikafika, chinthu china chikakhala chikukula ndi kuwonjezereka. Nchiyani chimenecho? Mpatuko, kapena kupambuka pa Chikristu chowona, ukumabala mbewu zambiri za kuipa. Maulosi ena a Baibulo amatsimikizira kuti zimenezi zikachitika mkati mwa masiku otsiriza a dongosolo loipa la zinthu. Mpamene tili lerolino, m’chimaliziro cha dongosolo la zinthu.​—Mateyu 13:24-30, 36-43.

17. Kodi ndichidziŵitso chofanana chotani chimene lemba la 2 Timothy 3:1-5 limapereka ponena za chimaliziro cha dongosolo la zinthu?

17 Kodi mukuona kufunika kwa zimenezi? Lemba la 2 Timoteo 3:1-5 limatipatsa chisonyezero chofanana chakuti mkati mwa chimaliziro cha dongosolo, kapena masiku otsiriza, Akristu akazingidwa ndi zipatso zoipa. Paulo sanali kunena kuti zinthu 19 zondandalikidwazo zikakhala njira yaikulu yotsimikizirira kuti masiku otsiriza afika. Mmalomwake, iye anali kuchenjeza ponena za zimene tikayenera kulimbana nazo mkati mwa masiku otsiriza. Vesi 1 likunena za “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Mawuwo akuchokera ku Chigiriki, ndipo m’lingaliro lenileni amatanthauza “nthaŵi zoikidwiratu zowopsa.” (Kingdom Interlinear) Kodi simukuvomereza kuti liwulo “zowopsa” limalongosola bwino zimene tikuyang’anizana nazo lerolino? Uthenga wouziridwa umenewu ukupitiriza kutipatsa chidziŵitso chaumulungu ponena za nthaŵi yathu ino.

18. Kodi tiyenera kusumika maganizo pachiyani pamene tiphunzira mawu aulosi a Paulo?

18 Chidwi chathu muulosi umenewu chiyenera kutilola kuzindikira zitsanzo zatsoka zosonyeza mmene nyengo yathu iliri yovuta, kapena yowopsa. Kumbukirani mfundo zathu zazikulu ziŵiri zija: (1) kuzindikira mavuto amene akuchititsa nthaŵi zathu kukhala zovuta ndi kuona mmene tingawapeŵere; (2) kutsatira ziphunzitso zogwiradi ntchito ndi zimene zingatithandize kusangalala ndi moyo wabwinopo. Chotero, mmalo mogogomezera zoipa zokhazokha, tidzasumika maganizo pa ziphunzitso zimene zingatithandize ife ndi mabanja athu m’nthaŵi zino zovuta kuchita nazo.

Patani Mapindu Olemeretsa

19. Kodi ndiumboni wotani umene mwaona wakuti anthu alidi odzikonda okha?

19 Paulo akuyamba ndandanda yake mwa kulosera kuti m’masikuwo, “anthu adzakhala odzikonda okha.” (2 Timoteo 3:2) Kodi anatanthauzanji? Mudzakhala wolondola kunena kuti m’mbiri yonse pakhala amuna ndi akazi odzigangira mwadyera. Komabe, sizokayikiritsa konse kuti chifooko chimenechi nchowanda lerolino. Ndipo chimakhala chachikulu mwa anthu ambiri. Chili kwenikweni mkhalidwe m’ndale zadziko ndi m’malonda. Amuna ndi akazi amafunafuna mphamvu ndi kutchuka mwanjira iliyonse. Kaŵirikaŵiri kumakhala mwa kudyera masuku pamutu anthu ena mwanjira iliyonse, popeza kuti odzikonda okha ameneŵa samasamala mmene amavulazira anthu ena. Amakhala ofulumira kupereka ena kukhoti kapena kuwanyenga. Mungaone chifukwa chake ambiri amatcha unowu kukhala “mbadwo wa dziŵa zako.” Anthu odzitukumula ndi odzigangira akuchulukadi.

20. Kodi uphungu wa Baibulo ngwosiyana motani ndi mzimu wofala wa kudzikonda?

20 Sititofunikira kukumbutsidwa za zochitika zopweteketsa mtima zimene takumana nazo pochita ndi anthu “odzikonda okha.” Komabe, nzowona kuti mwa kudziŵikitsa vutoli mosabisa, Baibulo likutithandiza, popeza kuti likutiphunzitsa mmene tingapeŵere msampha umenewu. Ilo limati: “Musachita kalikonse ndi chikhumbo chadyera kapena ndi chikhumbo choipa cha kudzikuza, koma khalani odzichepetsa kwa wina ndi mnzake, nthaŵi zonse onani ena kukhala okuposani. Ndipo funani zabwino za wina ndi mnzake, osati zanu zokha.” “Musadziganizire nokha modzikweza kuposa mmene muyenera kuchitira. M’malo mwake, khalani odekha m’kuganiza kwanu.” Uphungu wabwino koposa umenewo ukupezeka pa Afilipi 2:3, 4 ndi Aroma 12:3, malinga ndi mamasulidwe a Today’s English Version.

21, 22. (a) Kodi pali umboni waukulu wotani wakuti uphungu woterowo ungakhaledi wothandiza lerolino? (b) Kodi nchiyambukiro chotani chimene uphungu wa Mulungu wakhala nacho pa anthu amaganizo abwino?

21 Wina angatsutse kuti, ‘Zimenezotu zikumvekera zabwino, koma sizotheka.’ Eya, izo nzotheka kumene. Zikhoza kugwira ntchito, ndipo zimaterodi kwa anthu amaganizo abwino lerolino. Mu 1990 wofalitsa wa Oxford University anasindikiza buku lotchedwa The Social Dimensions of Sectarianism. Mutu 8 unali wakuti “Mboni za Yehova m’Dziko la Akatolika,” ndipo linalongosola kufufuza kochitidwa m’Belgium. Tikuŵerenga kuti: “Kuyang’ana pa mbali yokhumbirika yakukhala Mboni, kuwonjezera pa mbali yokopa ya ‘Chowonadi’ chenichenicho, ofunsidwawo anatchulanso mikhalidwe ingapo. . . . Chifundo, ubwenzi, chikondi, ndi kugwirizana ndiyo mikhalidwe inatchulidwa nthaŵi zonse, koma kuwona mtima, ndi kudzisungira ‘mogwirizana ndi malamulo a Baibulo’ inalinso mikhalidwe imene Mbonizo zinaisamala.”

22 Tingafanizire malongosoledwewo ndi chithunzithunzi chojambulidwa ndi kamera yokhala ndi lens yojambula zambiri; ngati mmalo mwake, mukanagwiritsira ntchito lens ya zoom, kapena ya telephoto, mukanaona pafupi, zochitika zenizenizo zambiri. Zimenezi zikanaphatikizapo amuna amene kale anali amwano, odzitukumula, ndi odzigangira mwadyera koma amene tsopano ali ofatsa kwambiri, akumakhala amuna ndi atate amene amasonyeza chikondi chachikulu ndi chifundo kwa akazi awo, ana awo, ndi anthu ena. Chikanaphatikizaponso akazi amene anali opondereza kapena opanda chifundo koma amene tsopano amathandiza ena kuphunzira njira ya Chikristu chenicheni. Pali mazanamazana a zitsanzo zoterozo. Tsopano, chonde khalani owona mtima. Kodi simungakonde kukhala pakati pa anthu oterowo m’malo mwa kumayang’anizana nthaŵi zonse ndi amuna ndi akazi amene amadzikonda okha koposa? Kodi zimenezo sizikakupangitsa kukhala kopepukirapo kuchita ndi nthaŵi zathu zoŵaŵitsa? Chotero, kodi kutsatira ziphunzitso za Baibulo zoterozo sikungakupatseni chimwemwe chachikulu?

23. Kodi nchifukwa ninji kudzakhala koyenerera kupereka chisamaliro chowonjezereka pa 2 Timoteo 3:2-5?

23 Komabe, tangokambitsirana chinthu choyamba chokha pa ndandanda ya Paulo yolembedwa pa 2 Timoteo 3:2-5. Bwanji ponena za zinazo? Kodi kuzipenda kwanu kosamalitsa sikungakuthandizeninso kuzindikira mavuto aakulu a nthaŵi zathu kuti mukhale okhoza kuwapeŵa ndi kudziŵa njira imene idzapatsa inuyo ndi okondedwa anu chimwemwe chokulira? Nkhani yotsatira idzakuthandizani kuyankha mafunso ameneŵa ndi kupata madalitso olemeretsa.

Mfundo Zokumbukira

◻ Kodi pali maumboni ena ati osonyeza kuti tikukhala m’nthaŵi zoŵaŵitsa?

◻ Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti tikukhala m’masiku otsiriza?

◻ Kodi ndimfundo zazikulu ziŵiri ziti zimene tingapeze mwa kuphunzira 2 Timoteo 3:1-5?

◻ Mkati mwa nthaŵi ino pamene anthu ochuluka kwambiri ali odzikonda okha, kodi ndimotani mmene ziphunzitso za Baibulo zathandizira anthu a Yehova?

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Chithunzi pamwamba kumanzere: Andy Hernandez/​Sipa Press; chithunzi pamwamba kulamanja: Jose Nicolas/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena