Kodi Tikukhala m’Masiku Otsiriza?
MAWU akuti “nthaŵi zoŵaŵitsa” atembenuzidwa kuchokera ku mawu Achigiriki akuti kai·roiʹ kha·le·poiʹ. (2 Timoteo 3:1) Liwu lakuti kha·le·poiʹ ndilo kuchulukitsidwa kwa liwu limene kwenikweni limatanthauza “chititsa mantha” ndipo lili ndi lingaliro la kuwopseza ndi ngozi. Wothirira ndemanga Baibulo wina akunena kuti liwulo limanena za “kukantha kwakukulu kwa zoipa.” Chotero, pamene kuli kwakuti nyengo zina zapapitazo zinali ndi zipwirikiti, “masiku otsiriza” akakhala auchinyama kwambiri. Monga momwe 2 Timoteo 3:13 akunenera, “anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.”
Kodi zimenezi zikulongosola za tsiku lathu? Tiyeni tipende ena a maumboni apadera olembedwa pa 2 Timoteo 3:2-5 kuti tione ngati umenewu umasonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza.
“Anthu adzakhala . . . okonda ndalama.”—2 Timoteo 3:2.
Chinyengo chakhala “upandu wosalamulirika m’zachuma,” monga momwe U.S.News & World Report ikuchitchera. Mu United States, ndalama zobedwa zolipirira chisamaliro cha mankhwala chokha zili pakati pa $50 biliyoni ndi $80 biliyoni chaka chilichonse. Mwachisoni, kusaona mtima kotero kumachitika kaŵirikaŵiri. Monga momwe Gary Edwards, pulezidenti wa Ethics Resource Center akunenera, tili ndi “chitaganya chimene nthaŵi zina chimalemekeza kusaona mtima.” Iye akulongosola: “Anthu amene ali apandu, andale, anthu amalonda amene amanyenga boma mosaimbidwa mlandu timawayesa ngwazi.”
“Odzikuza.”—2 Timoteo 3:2.
Munthu wodzikuza amachitira chipongwe ena. Zimenezi nzooneka kwambiri chotani nanga m’kusankhana mafuko lerolino! “Mafuko onse aang’onoang’ono ndiwo amene ali chandamale,” ikutero The Globe and Mail ya ku Toronto, Canada. “Chiwawa cha mafuko chikukula mu Germany, gulu la Ku Klux Klan lili lokangalika mu United States ndipo maswastika akuwononga njira za m’mbali mwa misewu ya ku Toronto ndi masunagoge omwe.” Irving Abella, pulezidenti wa Canadian Jewish Congress, akuti: “Tikuona zimenezi kulikonse: ku Sweden, ku Italy, ku Holland ndi ku Belgium ndiponso ku Germany.”
“Osamvera akuwabala.”—2 Timoteo 3:2.
“Anthu obadwa pambuyo pa nkhondo ya dziko yachiŵiri akunenedwa ndi ambiri kuti akulera mbadwo wa ana olongolola, amakani, ndi opanda ulemu,” ikutero The Toronto Star. Kupanduka kumene kumayambira panyumba kaŵirikaŵiri kumaloŵerera m’sukulu. Mphunzitsi wina wachikazi akunena kuti ana ausinkhu waung’ono wa zaka zinayi amayankha mwachipongwe. “Aphunzitsi amathera nthaŵi yambiri pa kulimbana ndi khalidwe loipa kuposa pa kuphunzitsa,” iye akutero. Zoonadi, si achichepere onse amene ali opanduka. Komabe, “monga khalidwe,” akutero mphunzitsi wina wa nthaŵi yaitali wa kusekondale Bruce MacGregor, “iwo amaonekera kukhala ndi ulemu wochepa kwambiri wa chinthu chilichonse.”
“Opanda chikondi chachibadwidwe.”—2 Timoteo 3:3.
Masiku otsiriza akakhala ndi kuwonongeka kwa banja—mmene, chikondi chachibadwidwe chiyenera kukhala nthaŵi zonse, kuposa kwina kulikonse. The New York Times ikusimba kuti “chiwawa cha panyumba ndicho chochititsa chachikulu cha kuvulala ndi imfa kwa akazi a ku America, chovulaza anthu ambiri kuposa ngozi za galimoto, kugwirira chigololo ndi umbala zitaikidwa pamodzi.” Kugona ana kochuluka kumachitidwa ndi ziŵalo za banja zodaliridwa. Mlingo waukulu wa chisudzulo, kuchitira nkhanza okalamba, ndi kutaya mimba nazonso zimapereka umboni wakuti ambiri “alibiretu . . . chikondi chaumunthu chachibadwa.”—Phillips.
“Aukali, osakonda abwino.”—2 Timoteo 3:3.
“Akupha achichepere amangopha popanda chifukwa,” akulemba motero Bob Herbert wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala. “Achichepere ochuluka amakondwera kukhala ndi lingaliro la kupha munthu wina ‘popanda chifukwa.’” Ngakhalenso makolo ena amaoneka kukhala opanda lingaliro la makhalidwe abwino. Pamene kagulu kena ka anyamanta achichepere kanaimbidwa mlandu wa kuchita mpikisano wa kufuna kuona amene anagonana ndi asungwana ambiri, atate wina anati: “Mwana wanga anangochita chinthu chimene mnyamata wina aliyense Wachimereka wokwana angachite pausinkhu wake.”
“Okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:4.
Malinga ndi kuyerekezera kwina, achichepere amathera maola 15 pa mawailesi ndi mawailesi akanema mosiyana ndi ola limodzi limene amathera ali ndi kagulu ka chipembedzo. “Lerolino,” ikusimba motero Altoona Mirror, “makhalidwe oulutsidwa kwambiri m’masitolo ndi m’malikole a sukulu amalamulira moyo wa achichepere. Ndiyeno pamadza banja. Pamapeto pa mpambowo [pali] tchalitchi.” Mirror ikusimbanso kuti, “ngati palibe makolo, ndipo tchalitchi chatonthola, pamenepo zofalitsira nkhani zimasonkhezera kwambiri achichepere.”
“Akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”—2 Timoteo 3:5.
Choonadi cha Baibulo chili ndi mphamvu yosintha miyoyo. (Aefeso 4:22-24) Koma machitidwe ena opanda umulungu amachitidwa m’dzina la chipembedzo. Chitsanzo china chomvetsa chisoni ndicho kugona ana kwa atsogoleri achipembedzo. Malinga ndi kunena kwa The New York Times, loya wina mu United States “akunena kuti ali ndi milandu 200 imene ikumyembekezera m’maboma 27 ya anthu amene akunena kuti anagonedwa ndi ansembe.” Zoona, mpangidwe uliwonse kapena kuyerekezera kulikonse kwa kupembedza kumene atsogoleri achipembedzo ameneŵa amasonyeza kumavumbulidwa kukhala chinyengo chabe ndi ntchito zawo zoipa.
MAUMBONI ENA A MASIKU OTSIRIZA
2 TIMOTEO 3:2-4 AMANENANSO KUTI ANTHU ADZAKHALA . . .
□ Odzitamandira
□ Amwano
□ Osayamika
□ Osayera mtima
□ Osayanjanitsika
□ Akudyerekeza
□ Osakhoza kudziletsa
□ Achiwembu
□ Aliuma olimbirira
□ Otukumuka mtima
“CHIZINDIKIRO CHA KUKHALAPO KWANU”
Imfa yake ili pafupi kuchitika, Yesu anafunsidwa kuti: “Kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthuli?” (Mateyu 24:3, NW ) Yesu anatchula mikhalidwe ndi zochitika zimene zikasonyeza masiku otsiriza. Tiyeni tipende zina za izo.
“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.”—Mateyu 24:7.
“Zaka za zana la 20—ngakhale kuti zawongolera kakhalidwe ka anthu ambiri ndi kukulitsa kusonyeza nkhaŵa kwa boma kaamba ka miyoyo ya osauka—zalamuliridwa ndi mfuti zachiwaya, akasinja, ndi ndege za B-52, mabomba a nyukliya ndipo, potsirizira pake, mabomba a makina. Zakhala za nkhondo zokhetsa mwazi kwambiri ndi zowononga kwambiri kuposa za m’nyengo ina iliyonse.”—Milestones of History.
“Zivomezi m’malo akutiakuti.”—Mateyu 24:7.
Mkati mwa zaka za zana lino, zivomezi zoyambira pa 7.5 kufikira pa 8.3 pa mpimo wa Richter zachitika ku Chile, China, India, Iran, Italy, Japan, Peru, ndi Turkey.
“Kudzakhala zowopsa.”—Luka 21:11.
Chifukwa cha zochitika zowopsa m’zaka zaposachedwapa, mwinamwake mantha ndiwo mkhalidwe umodzi waukulu koposa m’miyoyo ya anthu. Anthu amawopa nkhondo, upandu, kuipitsa, nthenda, kukwera mtengo kwa zinthu, ndi zinthu zina zambiri zimene zimawopseza chisungiko chawo ndi miyoyo yawo yeniyeniyo.
“Njala.”—Mateyu 24:7.
“Njala Ikuwopseza Pamene Magulu Othandiza Akukangana,” ukulengeza motero mutu wina wankhani mu magazini a New Scientist. Malinga ndi kunena kwa yemwe kale anali pulezidenti wa United States, njala ikuwopseza kusakaza pulanetiyi mkati mwa zaka makumi aŵiri. “Ngakhale kuti pali kuneneratu kowopsa kotero,” nkhaniyo ikutero, “kuchuluka kwa thandizo limene maiko olemera akupereka kaamba ka chitukuko cha ulimi m’maiko osatukuka kukuchepa mofulumira.”
“Miliri m’malo akutiakuti.”—Luka 21:11.
Malinga ndi kunena kwa kagulu kena ka akatswiri, kulimbana ndi AIDS kwa boma la United States—kodya $500 miliyoni pa chaka—kwatchedwa kulephera komvetsa chisoni. “Tikutaya mbadwo wonse wa anthu chifukwa cha AIDS,” Dr. Donna Sweet, amene amasamalira odwala oyambira pa 200 kufikira pa 300 akuchenjeza motero. Ku United States, AIDS tsopano ndiyo chochititsa chachikulu cha imfa pakati pa amuna a misinkhu yoyambira pa 25 kukafika pa 44.
“Kuchuluka kwa kusayeruzika.”—Mateyu 24:12.
Kufufuza kwina kwa ku United States pa achichepere 2,500 kunasonyeza kuti 15 peresenti inanyamulapo mfuti pa nthaŵi ina yake mkati mwa masiku 30 apitawo, 11 peresenti inawomberedwa mkati mwa chaka chapita ndipo 9 peresenti inawombera munthu wina ndi mfuti panthaŵi ina.
KODI NCHIYANI CHIMENE CHILI PATSOGOLOPA?
Monga momwe taonera, anthu atayika, ali kutali kwambiri ndi dziko la mtendere. Ponena za ukulu wake, mikhalidwe yotchulidwayo njosayerekezera ndi ina. Indedi, banja la munthu lili m’dera limene lili lachilendo. Likupyola m’nyengo yotchedwa kuti masiku otsiriza.
Kodi nchiyani chimene chidzatsatira pambuyo pa nyengo imeneyi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Michael Lewis/Sipa Press