Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 10-15
  • Makolo, Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo, Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisamaliro cha Tsiku ndi Tsiku Kuyambira Paukhanda
  • Chisamaliro Chapadera Chofunikira
  • Yamikirani Nthaŵi Imene Mukhala Pamodzi
  • Mphotho Yaulemerero
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo—Fikirani Mtima wa Mwana Wanu Kuyambira ku Ubwana
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ana—“Cholandira cha kwa Yehova”
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Makolo, Kondwerani mwa Ana Anu
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 10-15

Makolo, Ana Anu Amafunikira Chisamaliro Chapadera

“Ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.”​—SALMO 128:3.

1. Kodi kulera ana kungayerekezeredwe motani ndi kulima mbewu?

KAŴIRIKAŴIRI, ana amakula ndi kukhwima mofanana ndi mbewu. Chifukwa chake, sikodabwitsa pamene Baibulo limanena za mkazi wa mwamuna kuti ali “mpesa wopatsa” ndipo limafanizira ana ake ndi “timitengo ta azitona pozinga podyera [pake].” (Salmo 128:3) Mlimi angakuuzeni kuti kukulitsa mbewu zazing’ono sikofeŵa, makamaka pamene mphepo ndi nthaka sizili bwino. Mofananamo, mu “masiku otsiriza” ano oŵaŵitsa, kuli kovuta kwambiri kulera ana kuti akule bwino, nakhale achikulire owopa Mulungu.​—2 Timoteo 3:1-5.

2. Kodi nchiyani chimakhala chofunika kaŵirikaŵiri kuti munthu akolole zochuluka?

2 Kuti akolole zipatso zochuluka, mlimi amafunikira nthaka yachonde, dzuŵa, ndi madzi. Kuwonjezera pa kulima ndi kupalira, iye afunikira kuikamo mankhwala ophera tizilombo ndi njira zina za chisamaliro. Nthaŵi zina zinthu zimakhala zovuta, mpaka kufika nthaŵi yokolola. Zimakhala zachisoni chotani nanga pamene zipatsozo zilephera kucha bwino! Komabe, mlimiyo amakhala wokhutiritsidwa chotani nanga pamene akolola zipatso zocha bwino, chifukwa cha kugwira ntchito kwake kwamphamvu!​—Yesaya 60:20-22; 61:3.

3. Kodi kufunika kwa mbewu ndi kwa ana kuli kotani pokuyerekezera, ndipo kodi nchisamaliro cha mtundu wanji chimene ana ayenera kuchilandira?

3 Ndithudi, moyo wa munthu wachipambano ndi wopindulitsa uli wamtengo wapatali kuposa zotuta za mlimi. Nchifukwa chake sizodabwitsa kuti kulera mwana mwachipambano kukhoza kutenga nthaŵi yaitalidi ndi kuyesayesa kokulira kuposa kukulitsa mbewu zochuluka. (Deuteronomo 11:18-21) Mwana wamng’ono wobzalidwa m’munda wa moyo, ngati athiriridwa ndi kupaliridwa ndi chikondi ndi kuikiridwa malire oyenerera, akhoza kukula ndi kukhwima mwauzimu ngakhale m’dzikoli lodzaza ndi makhalidwe onyansa. Koma ngati sasamaliridwa bwino kapena atsenderezedwa, mwanayo adzafota mkati mwake ndipo mwinamwake kufa mwauzimu. (Akolose 3:21; yerekezerani ndi Yeremiya 2:21; 12:2.) Indetu, ana onse amafunikira chisamaliro chapadera!

Chisamaliro cha Tsiku ndi Tsiku Kuyambira Paukhanda

4. Kodi ana amafunikira chisamaliro cha mtundu wanji “kuyambira ukhanda”?

4 Makolo ayenera kupereka chisamaliro chosalekeza kwa khanda lobadwa kumene. Komabe, kodi khandalo limangofunikira chisamaliro chakuthupi chokha cha tsiku ndi tsiku? Kwa Timoteo, mtumiki wa Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso.” (2 Timoteo 3:15) Chotero chisamaliro chaukholo chimene Timoteo anachilandira, kuyambiradi paukhanda weniweni, chinalinso cha mtundu wauzimu. Koma kodi ukhanda umayamba liti?

5, 6. (a) Kodi Baibulo limanenanji za mwana wosabadwa? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti makolo ayenera kudera nkhaŵa za ubwino wa mwana wosabadwa?

5 Liwu Lachigiriki limene Paulo anagwiritsira ntchito panopa lakuti (breʹphos) limagwiritsiridwanso ntchito kwa mwana wosabadwa. Elizabeti, amayi wa Yohane Mbatizi, anauza wachibale wake Mariya kuti: “Pamene mawu a kulankhula kwako analoŵa m’makutu anga, mwana [“khanda,” NW] [breʹphos] anatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga.” (Luka 1:44) Chifukwa chake, ngakhale ana osabadwa amatchedwa makanda, ndipo Baibulo limasonyeza kuti iwo akhoza kumva zochitika za kunja kwa mimba. Pamenepo, kodi chisamaliro cha mwana wosabadwa, chimene kaŵirikaŵiri chimalimbikitsidwa lerolino, chiyenera kuphatikizapo kusamalira mkhalidwe wauzimu wa khanda losabadwa?

6 Imeneyi ndi nkhani yofunika kuipenda, chifukwa chakuti maumboni amasonyeza kuti ana osabadwa akhoza kupindula kapena kuyambukiridwa moipa ndi zimene amamva. Mlangizi wina wa nyimbo anapeza kuti maimbidwe osiyanasiyana omwe ankayeseza anamveka ozoloŵereka kwa iye modabwitsa, makamaka choimbira chotchedwa cello. Pamene anatchula maina a nyimbozo kwa amayi ake omwe anali katswiri woimba choimbira chotchedwa cello, iwo anati amenewo ndi maimbidwe omwe ankayeseza pamene anali ndi pathupi pa mwanayo. Mofananamo, makanda osabadwa akhoza kuyambukiridwa moipa ngati amayi awo amaonerera nthaŵi zonse akanema opitirizabe a pa TV. Chifukwa chake, magazini a zamankhwala analankhula za “kumwerekera ndi kanema kwa mluza.”

7. (a) Kodi ndimotani mmene makolo ambiri aikira chisamaliro pa ubwino wa mwana wawo wosabadwa? (b) Kodi ndi kukhoza kotani kumene mwana ali nako?

7 Pozindikira ubwino wa zinthu zakunja zoyambukira makanda m’njira yabwino, makolo ambiri amayamba kuŵerenga, kulankhula, ndi kuimba kwa mwana wawo ngakhale asanabadwe. Mukhoza kuchita zofananazo. Ngakhale kuti khanda lanulo silingazindikire mawuwo, mwachionekere lidzapindula ndi liwu lanu lotonthozalo ndi mamvekedwe ake achikondi. Atabadwa, mwanayo adzayamba kuzindikira mawu anu, mwina mwake mofulumira kwambiri kuposa mmene mungaganizire. M’zaka ziŵiri kapena zitatu zokha, mwana amaphunzira chilankhulo chovutacho mwa kungochimvetsera. Khanda likhozanso kuyamba kuphunzira “chinenero choyera” cha choonadi cha Baibulo.​—Zefaniya 3:9, NW.

8. (a) Kodi umboni umasonyeza kuti Baibulo limatanthauzanji pamene limati Timoteo anadziŵa malembo opatulika “kuyambira ukhanda”? (b) Kodi nchiyani chinatsimikizirika kukhala choona ponena za Timoteo?

8 Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati Timoteo anali ‘atadziŵa malembo opatulika kuyambira ukhanda’? Umboni umasonyeza kuti iye anatanthauza kuti Timoteo anali atalandira chiphunzitso chauzimu kuyambira paukhanda, osati kuyambira chabe pamene anali mwana wamng’ono. Zimenezi nzogwirizana ndi tanthauzo la liwu Lachigiriki lakuti breʹphos, limene kaŵirikaŵiri limatanthauza khanda lobadwa kumene. (Luka 2:12, 16; Machitidwe 7:19) Timoteo analangizidwa mwauzimu ndi amayi wake Yunike ndi agogo ake aakazi a Loisi kuyambira paubwana weniweni. (2 Timoteo 1:5) Mwambi wakuti, ‘Mmene mphukira yaing’ono imasamaliridwira, ndimmenenso mtengo udzakulira’ unagwiradi ntchito kwa Timoteo. Iye anali ‘ataphunzitsidwa m’njira yake,’ ndipo, monga chotulukapo, anakhala mtumiki wabwino wa Mulungu.​—Miyambo 22:6; Afilipi 2:19-22.

Chisamaliro Chapadera Chofunikira

9. (a) Kodi nchiyani chimene makolo ayenera kupeŵa kuchita, ndipo nchifukwa ninji? (b) Pamene mwana akukula, kodi nchiyani chimene makolo ayenera kuchita, ndipo nchitsanzo chotani chimene ayenera kutsanzira?

9 Ana nawonso ali ngati mbewu m’njira yakuti si onse ali ndi mikhalidwe yofanana, ndiponso si onse amene amatsatira mofanana chisamaliro choperekedwacho. Makolo anzeru adzazindikira kusiyanako ndipo adzapeŵa kuyerekezera mwana mmodzi ndi wina. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:4) Ngati ana anu ati akule kukhala achikulire anzeru, mufunikira kuzindikira mikhalidwe yawo yosiyanasiyana, mukumakulitsa yabwino ndi kuzulamo yoipa. Bwanji ngati muona chifooko china kapena khalidwe losayenera, mwinamwake kusaona mtima, kukondetsa chuma chakuthupi, kapena dyera? Ziwongolereni mokoma mtima, monga momwedi Yesu anawongolerera zifooko za atumwi ake. (Marko 9:33-37) Makamaka, thokozani mwana aliyense nthaŵi zonse kaamba ka zimene amakhoza ndi mikhalidwe yake yabwino.

10. Kodi ana amafunikiranji makamaka, ndipo kodi chingaperekedwe motani?

10 Chimene ana amafunikira kwambiri ndicho chisamaliro chaumwini chachikondi. Yesu anapatula nthaŵi yopereka chisamaliro chapadera choterocho kwa ana aang’ono, ngakhale m’masiku otanganidwa omalizira a utumiki wake. (Marko 10:13-16, 32) Makolonu, tsatiranitu chitsanzo chimenecho! Mopanda dyera patulani nthaŵi yokhala pamodzi ndi ana anu. Ndipo musachite manyazi kuwasonyeza chikondi chenicheni. Afungatireni, monga momwe Yesu anachitira. Ayangateni ndi kuwapsompsona mwachikondi. Pamene makolo a achichepere okula msinkhu olangizidwa bwino anafunsidwa za uphungu umene angapereke kwa makolo ena, mayankho operekedwa kaŵirikaŵiri anali akuti: ‘Akondeni kwambiri,’ ‘therani nawo nthaŵi,’ ‘kulitsani kulemekezana,’ ‘amvetsereni kwenikweni,’ ‘perekani chitsogozo osati mawu,’ ndipo ‘chitani moona mtima.’

11. (a) Kodi makolo ayenera kuona motani kuperekedwa kwa chisamaliro chapadera kwa ana awo? (b) Kodi nliti pamene makolo angasangalale ndi makambitsirano opindulitsa ndi ana awo?

11 Kupereka chisamaliro chapadera choterocho kungakhale kosangalatsa. Kholo lina lachipambano linalemba kuti: “Pamene anyamata athu aŵiri anali aang’ono, mchitidwe wa kuwakonzekeretsa kugona, kuwaŵerengera, kuwafunda, ndi kupemphera nawo unali wosangalatsa.” Nthaŵi yochitira zinthu pamodzi yoteroyo imapereka mpata wa kulankhulana kumene kungakhale kolimbikitsa ponse paŵiri kwa kholo ndi mwana yemwe. (Yerekezerani ndi Aroma 1:11, 12.) Okwatirana aŵiri ena anali kumamvetsera pamene mwana wawo wa zaka zitatu anapempha Mulungu kudalitsa “Wally.” Iye anapempherera “Wally” kwa mausiku otsatizana, ndipo makolo ake analimbikitsidwa kwambiri pamene anazindikira kuti iye anatanthauza abale a m’Malaŵi, omwe ankazunzidwa panthaŵiyo. Mkazi wina anati: “Pamene ndinali ndi zaka zinayi zokha zakubadwa, amayi anga anandithandiza kuloŵeza malemba ndi kuimba nyimbo za Ufumu pamene ndinkaimirira pampando ndikumapukuta mbale zomwe amayi ankatsuka.” Kodi mungaganizire za nthaŵi zimene mukhoza kusangalala ndi makambitsirano olimbikitsana ndi ana anu?

12. Kodi nchiyani chimene makolo Achikristu mwanzeru angalinganizire ana awo, ndipo kodi ndi njira iti imene ingagwiritsiridwe ntchito?

12 Makolo Achikristu anzeru amalinganiza programu yophunzira yokhazikika. Ngakhale kuti mungagwiritsire ntchito njira yozoloŵereka ya mafunso ndi mayankho, kodi mungathe kuwonjezera pa ukoma wa kukambitsiranako mwa kukhala ndi mbali za kuyeseza kuphunzira, makamaka kaamba ka ana aang’ono? Mukhoza kuphatikizapo kujambula zithunzithunzi za malo a Baibulo, kusimba nkhani za Baibulo, kapena kumvetsera lipoti limene munapempha mwanayo kukonzekera. Chititsani Mawu a Mulungu kukhala okoma kwambiri kwa ana anu kotero kuti adziwalakalaka. (1 Petro 2:2, 3) Atate wina anati: ‘Pamene anawo anali aang’ono, tinakwaŵa nawo pansi ndi kuseŵera zochitika za m’mbiri zoloŵetsamo anthu a m’Baibulo. Anawo anakonda kwambiri zimenezo.’

13. Kodi mbali za kuyeseza zili ndi phindu lanji, ndipo kodi mungayeseze chiyani m’mbali zimenezi?

13 Mbali za kuyeseza zimachititsanso makambitsirano opindulitsa chifukwa chakuti zimathandiza achichepere kukonzekera mikhalidwe yeniyeni ya moyo. Mmodzi wa ana a banja la a Kusserow​—onsewo 11 omwe anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu m’nthaŵi ya chizunzo cha Nazi​—anati ponena za makolo ake: “Anatisonyeza mmene tingachitire ndi mmene tingadzichinjirizire ndi Baibulo. [1 Petro 3:15] Kaŵirikaŵiri tinkachita mbali za kuyeseza, kufunsa mafunso ndi kupereka mayankho.” Bwanji osachita zofananazo? Mukhoza kuyeseza maulaliki, ndi kholo likukhala mwininyumba. Kapena mbali ya kuyesezayo ikhoza kukhala ya ziyeso za m’moyo. (Miyambo 1:10-15) “Kuyeseza mikhalidwe yovuta kungakulitse maluso a mwana ndi chidaliro,” anafotokoza motero munthu wina. “Kuyesezako kungaphatikizepo kuchita monga bwenzi limene likuyesa kupatsa mwana wanu ndudu, moŵa kapena anamgoneka.” Mbali zimenezi zingakuthandizeni kuzindikira mmene mwana wanu angachitire m’mikhalidwe yoteroyo.

14. Kodi nchifukwa ninji makambitsirano achikondi ndi achifundo pamodzi ndi ana anu ali ofunika kwambiri?

14 Mkati mwa kukambitsirana ndi mwana wanu, mchonderereni mwachifundo monga momwe anachitira wolemba mawu aŵa: “Mwananga, usaiŵale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.” (Miyambo 3:1, 2) Kodi zimenezo sizikhoza kugwira mtima wa mwana wanu ngati mufotokoza mwachikondi kuti mukufuna kuti akhale womvera chifukwa chakuti kudzamchititsa kukhala ndi mtendere ndi masiku ambiri​—ndipotu, moyo wosatha m’dziko latsopano lamtendere la Mulungu? Lingalirani za umunthu wa mwanayo pamene mukukambitsirana Mawu a Mulungu. Chitani zimenezi mwa pemphero, ndipo Yehova adzadalitsa zoyesayesa zanu. Makambitsirano achikondi ndi achifundo ozikidwa pa Baibulo oterowo ali othekera kukhala ndi zotulukapo zabwino ndi kudzetsa mapindu osatha.​—Miyambo 22:6.

15. Kodi makolo angathandize motani ana awo kuthetsa mavuto?

15 Ngakhale ngati kukambitsirana koteroko sikuchitika panyengo yolinganizidwa ya phunziro lanu, musachenjenekedwe ndi zinthu zina. Mvetserani mosamalitsa osati chabe zimene mwana wanu akunena komanso mmene akulongosolera lingalirolo. “Penyani mwana wanuyo,” anatero katswiri wina. “Ikani maganizo onse pa iye. Mufunikira kumvetsetsa, osati kumva chabe. Makolo amene amachita kuyesayesa kowonjezereka koteroko akhoza kuwongolera kwambiri miyoyo ya ana awo.” Ana lerolino kaŵirikaŵiri amakumana ndi mavuto aakulu pasukulu ndi kwina kulikonse. Monga kholo, chititsani mwanayo kulankhula za kukhosi, ndipo mthandizeni kuona zinthu mogwirizana ndi lingaliro la Mulungu. Ngati simuli wotsimikiza mmene mungathetsere vutolo, fufuzani m’Malemba ndi zofalitsidwa zogaŵiridwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Mulimonse mmene mungakhozere, patsani mwana wanu chisamaliro chonse chapadera chofunikira kuthetsa vutolo.

Yamikirani Nthaŵi Imene Mukhala Pamodzi

16, 17. (a) Kodi nchifukwa ninji achichepere makamaka amafunikira chisamaliro chapadera ndi chilangizo lerolino? (b) Kodi ana amafunikira kudziŵa chiyani pamene alangidwa ndi makolo awo?

16 Achichepere amafunikira chisamaliro chapadera chachikulu lerolino kuposa ndi kalelonse chifukwa chakuti tikukhala mu “masiku otsiriza,” ndipo zinozi ndizo “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-14) Makolo ndi ana omwe afunikira chitetezo cha nzeru yoona imene “isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Popeza kuti nzeru yaumulungu imaloŵetsamo kugwiritsira ntchito moyenera chidziŵitso chozikidwa pa Baibulo, ana amafunikira chilangizo cha nthaŵi zonse m’Mawu a Mulungu. Chifukwa chake, phunzirani Malemba ndi ana anu. Auzeni za Yehova, fotokozani mosamalitsa zofuna zake, ndipo kulitsani mwa iwo chiyembekezo chokondweretsa cha kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake aakulu. Lankhulani zinthu zotero panyumba, pamene muyenda panjira ndi ana anu​—inde, panthaŵi iliyonse yoyenera.​—Deuteronomo 6:4-7.

17 Alimi amadziŵa kuti si mbewu zonse zimakula bwino m’mikhalidwe imodzimodzi. Mbewu zimafuna chisamaliro chapadera. Mofananamo, mwana aliyense ali wosiyana ndipo amafunikira chisamaliro chapadera, chilangizo chapadera, ndi chiphunzitso chapadera. Mwachitsanzo, nkhope yokha ya kholo yosonyeza kusavomereza ingaletse mwana wina kuchita cholakwa, pamene kuli kwakuti mwana wina angafunikire chilango champhamvu ndithu. Koma ana anu onse amafunikira kudziŵa chifukwa chake simumakondwera ndi mawu kapena machitidwe ena, ndipo makolo onse aŵiri ayenera kugwirizana kotero kuti chilango chikhale chosasintha. (Aefeso 6:4) Kuli kofunika makamaka kwa makolo Achikristu kupereka chitsogozo choonekera bwino chogwirizana ndi Malemba.

18, 19. Kodi ndi thayo lotani limene makolo Achikristu ali nalo pa ana awo, ndipo chothekera kutulukapo nchiyani ngati ntchitoyo ichitidwa bwino?

18 Mlimi ayenera kuchita ntchito ya kubzala ndi kupalira panthaŵi yoyenera. Ngati achedwa kapena anyalanyaza mbewu zake, adzakolola zochepa kapena osakolola kalikonse. Eya, ana anu ali “mbewu” zomakula zofunikira chisamaliro chapadera tsopano lino, osati mwezi wamaŵa kapena chaka chamaŵa. Musaphonye mipata yabwino kwambiri yosonkhezerera kukula kwawo kwauzimu mogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndi ya kuzulamo malingaliro adziko amene angawafotetse ndi kufa mwauzimu. Yamikirani maola ndi masiku amene muli nawo okhala pamodzi ndi ana anu, chifukwa chakuti nthaŵi zimenezi zimatha mofulumira. Gwirani ntchito zolimba kukulitsa mwa ana anu mikhalidwe yaumulungu yofunikira kaamba ka moyo wachimwemwe monga atumiki okhulupirika a Yehova. (Agalatiya 5:22, 23; Akolose 3:12-14) Imeneyi si ntchito ya munthu wina aliyense; ndi ntchito yanu, ndipo Mulungu akhoza kukuthandizani kuichita.

19 Patsani ana anu choloŵa chauzimu chaulemerero. Phunzirani nawo Mawu a Mulungu, ndipo sangalalani nawo pamodzi ndi zosangulutsa zoyenera. Tengerani ana anu ku misonkhano Yachikristu, ndipo khalani nawo m’ntchito yolalikira Ufumu. Kulitsani mwa ana anu okondedwawo umunthu wovomerezedwa ndi Yehova, ndipo mothekera kwambiri iwo adzakuchititsani chisangalalo chachikulu m’moyo wa mtsogolo. Ndithudi, “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.”​—Miyambo 23:24, 25.

Mphotho Yaulemerero

20. Kodi n’chiyani chimene chili mfungulo ya kukhala kholo lachipambano la achichepere?

20 Kulera ana kuli ntchito yovuta ndi ya nthaŵi yaitali. Kukulitsa ‘timitengo ta azitona pozinga podyera panu’ timeneti kuti tikhale achikulire owopa Mulungu obala zipatso za Ufumu kwatchedwa kuti projekiti ya zaka 20. (Salmo 128:3; Yohane 15:8) Projekiti imeneyi kaŵirikaŵiri imakhala yovutirapo pamene ana afika zaka 13 mpaka 19, pemene zitsenderezo pa iwo kaŵirikaŵiri zimawonjezereka ndipo makolo amakuona kukhala kofunikira kukulitsa zoyesayesa zawo. Koma mfungulo ya chipambano imakhalabe imodzimodzi​—kukhala wosamala, wachikondi, ndi womvetsetsa. Kumbukirani kuti ana anu amafunikiradi chisamaliro chaumwini. Mungawapatse chisamaliro choterocho mwa kusonyeza nkhaŵa yeniyeni yachikondi kaamba ka ubwino wawo. Kuti muwathandize, muyenera kudzipereka inu eni mwa kugaŵira nthaŵi, chikondi, ndi chisamaliro zimene amafunikiradi.

21. Kodi nchiyani chingakhale mfupo ya kupatsa ana chisamaliro chapadera?

21 Mphotho ya zoyesayesa zanu za kusamalira zipatso zamtengo wakezo zimene Yehova waikizira kwa inu ingakhale yokhutiritsa kwambiri kuposa zokolola zochuluka zilizonse za mlimi. (Salmo 127:3-5) Chotero makolonu, pitirizani kupatsa ana anu chisamaliro chapadera. Chitani motero kaamba ka ubwino wawo ndi ulemerero wa Atate wathu wakumwamba, Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi kulima mbewu ndi kulera ana kungayerekezeredwe motani?

◻ Kodi nchisamaliro chotani chimene mwana ayenera kulandira tsiku ndi tsiku kuyambira paukhanda?

◻ Kodi nchisamaliro chapadera chotani chimene ana amafunikira, ndipo kodi chingaperekedwe motani?

◻ Kodi nkupatsiranji ana anu chisamaliro chapadera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena