Zaka za Kuumbika—Pamene Chithandizo Chanu Chimafunika Koposa
ANA amanenedwa kukhala “cholandira cha kwa Yehova.” Amanenedwa kukhala ngati “timitengo ta azitona pozinga podyera pako.” (Salmo 127:3; 128:3) Makolo akulangizidwa kuti ‘awalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova.’—Aefeso 6:4.
Ngati muti muchititse mitengo ya azitona kubereka zipatso zabwino, nthaŵi ya kuchita zimenezo iri pamene iri ‘ngati timitengo podyera panu.’ Mmene mphukira yaing’ono imasamaliridwira, ndimmenenso mtengowo udzakulira. Ngati muti muphunzitse ana anu kukhala ogwirizana ndi njira za Mulungu, nthaŵi yabwino koposa kuchita zimenezo ndiyo kuyambira paukhanda wawo. “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6; 2 Timoteo 3:15) Paukhanda ubongo umatsopa chidziŵitso paliŵiro lalikulu, mofulumira kuposa mmene udzachitira panthaŵi ina iriyonse. Ndinthaŵi yanu ya mwaŵi wa kuchita zimene mungathe kwa ana anu.
Masaru Ibuka, woyambitsa Sony Corporation, analemba bukhu lotchedwa Kindergarten Is Too Late! (Kuyembekezera Sukulu Yanasale Nkuchedwa!) Pachikuto chake panali mawu aŵa: “Kuthekera kwa kuphunzira kwa mwana wanu nkwakukulu m’zaka ziŵiri kapena zitatu zoyamba za moyo. Chotero, musayembekezere . . . Kuyembekezera Sukulu Yanasale Nkuchedwa!”
M’mawu ake oyamba Glenn Doman, mkulu wa The Institutes for the Achievement of Human Potential, akunena zotsatirazi: “Bukhu labwino kwambiri ndi lolemekezeka la a Ibuka limenelo silimalengeza kanthu kena kodabwitsa ka mtundu uliwonse. Iwo akungopereka lingaliro lakuti ana aang’ono ali ndi mphamvu ya kuphunzira pafupifupi chirichonse pamene akali aang’ono. Akupereka lingaliro lakuti zimene amaphunzira mosavuta pamsinkhu wa zaka ziŵiri, zitatu, kapena zinayi zingangophunziridwa ndi kuyesayesa kwakukulu, kapena sizingaphunziridwe nkomwe pambuyo pake m’moyo. Akupereka lingaliro lakuti zimene achikulire amaphunzira movutikira ana amaziphunzira mosangalala. Akupereka lingaliro lakuti zinthu zimene achikulire amaphunzira pamlingo wochedwa kwambiri, ana aang’ono amaziphunzira mwamsanga. Akupereka lingaliro lakuti nthaŵi zina achikulire amapeŵa kuphunzira zinthu, pamene kuli kwakuti ana aang’ono angakonde kuphunzira kuposa kudya.”
Chifukwa chimene Ibuka akuperekera lingaliro lakuti kuyembekezera sukulu ya nasale nkuchedwa kwambiri nchakuti podzafika nthaŵiyo zaka zabwino koposa za kuphunzira kwa mwanayo zimakhala zitapita. Koma palinso chifukwa china. M’masiku ano kunyonyotsoka kwa makhalidwe kwaloŵerera m’sukulu zanasale, ndipo mwanayo asanafike kumeneko, makolo afunikira kukhomereza mwa mwanayo malamulo amakhalidwe abwino amphamvu kumtetezera pakuipitsidwa.
Chofunika chimenechi chikusonyezedwa ndi lipoti lonenedwa ndi makolo a mnyamata wina wa zaka zisanu ndi chimodzi amene anali atangoloŵa kumene sukulu yanasale. “Mkati mwa mlungu woyamba pasukulu yanasale, mwana wathuyo anali kunyengereredwa m’zakugonana ndi mnyamata wina mkati mwa mphindi 15 zimene amayenda ulendo m’basi ya kusukulu. Zimenezi zinachitikabe kwa masiku angapo. Sanali maseŵera chabe koma kuti zinali zachilendo, khalidwe loluluzika.
“Ana ambiri m’kalasi la mwana wathuyo amawonerera akanema oluluzika ndi makolo awo. Mwinamwake makolowo amalingalira kutengera anawo kumeneko kukhala kotetezereka koposa kuwasiya ndi wolera mwana wokayikitsa. Ana ena amawonerera akanema oluluza kaya kupyolera mwa cable television kapena pa akanema amene makolo awo amasunga panyumba.
“Phindu la kukhomereza malamulo a makhalidwe abwino mwa mwana wathu m’zaka zake za kuumbika, kuyambira paukhanda kumkabe mtsogolo, linagogomezeredwa pa ife ndi chochitika choipa m’nyumba mwathu mwenimwenimo. Kamsungwana ka zaka zinayi, kanadza limodzi ndi alendo ena achikulire. Iko ndi mwana wathu wamwamuna, amene anali atalangizidwa mosamalitsa kuti kugonana kunali kwa anthu achikulire okwatirana okha, anali m’chipinda chake choseŵerera. Kamsungwanako kanafuna kuti kaseŵere za kutomerana ndipo kanafotokoza kuti mwana wamwamunayo agone pansi. Pamene anachita motero mosadziŵa, kamsungwanako kanagona pamwamba pake. Mwana wathuyo anachita mantha ndi kuufula kuti: ‘Zimenezitu nza anthu okwatirana okha!’ Pamene anapokonyoka ndi kuthaŵa moseŵereramo, kamsungwanako kanafuula kuti: ‘Usauze aliyense!’”—Yerekezerani ndi Genesis 39:12.
Zotsatirazi ndizo zinthu zina zimene zikuchitika m’mizinda ndi m’milaga momwe—zinthu zimene ana anu ayenera kutetezeredwa kuyambira paukhanda kumkabe mtsogolo.
Anyamata aŵiri azaka zisanu ndi ziŵiri anaimbidwa mlandu wa kugwirira chigololo msungwana wazaka zisanu ndi chimodzi m’chimbudzi pasukulu ina ya boma. Anyamata atatu, amisinkhu ya zaka zisanu ndi chimodzi, zisanu ndi ziŵiri, ndi zisanu ndi zinayi, anagona msungwana wina wa zaka zisanu ndi chimodzi. Mnyamata wina wa zaka zisanu ndi zitatu anachita mathanyula pamwana wina wa sukulu yanasale. Mnyamata wina wa zaka 11 anaimbidwa mlandu wa kugwirira chigololo kamsungwana ka zaka ziŵiri. Akatswiri ena ochiritsa amanenetsa kuti kaŵirikaŵiri opalamula milandu otero anali mikhole ya kuchitiridwa moipa mwa kugonedwa pamene anali achichepere.
Zimenezi zinatsimikiziridwa munkhani ya mnyamata wina wachichepere. Pamene anali khanda, amake aang’ono a zaka 20 ankagonana naye m’kamwa. Kuyambira pamiyezi 18 ya usinkhu kufikira kumiyezi 30, anachitiridwa choipa cha kugonana chimenechi. Zaka ziŵiri kapena zitatu pambuyo pake iye anali kunyenga asungwana achichepere. Pamene anayamba sukulu, anapitirizabe mchitidwe umenewu ndipo anathamangitsidwa mugiredi loyamba ndiponso m’giredi lachiŵiri.
Kufunika kwa Kuphunzitsa Poyambirira
Kulephera kwa makolo kupereka maphunziro oyenerera m’zaka za kuumbika kumatsegulira njira ya kupulupudza, kumene kungatsegulire njira ya maupandu ena aakulu kwambiri: kuwononga zinthu mwadala, kuphwanya nyumba ndi cholinga cha kuba, ndi kuchita mbanda. Zotsatirazi ndizo zitsanzo zoŵerengeka za zinthu zimenezo.
Ana atatu a zaka zisanu ndi chimodzi anagubidiza m’nyumba ya mnzawo wina, akumawononga mwadala zinthu pafupifupi m’chipinda chirichonse. Wowononga zinthu mwadwala wina wa zaka zisanu ndi zinayi anaimbidwa mlandu wa upandu wa kuwononga zinthu motsutsa lamulo, kuphatikizapo kuphwanya nyumba ndi cholinga cha kuba, kuwopseza mwana wina ndi mpeni, ndi kutentha tsitsi la msungwana wina. Anyamata aŵiri a zaka 11 analoŵetsa volovolo ya mamilimitala asanu ndi anayi m’kamwa mwa mnyamata wa zaka 10 ndi kumubera wotchi. Mnyamata wina wa zaka khumi anawombera ndi kupha msungwana wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamkangano wa seŵero la vidiyo. Mnyamata wina wa zaka khumi anawombera mnzake ndi kubisa mtembo wake m’nyumba. Mnyamata wina wa zaka zisanu anakankhira pansi khanda lina kuchokera pachipinda chapamwamba chachisanu ndipo anafa. Mnyamata wina za zaka 13 anagwirizana ndi achichepere ena aŵiri m’kufwamba mwana wa zaka zisanu ndi ziŵiri kuti apeze ndalama kwa makolo ake, koma ngakhale pamene anali asanalizire telefoni banja lake kufuna ndalama zomuombolera, anamkwirira mnyamatayo akali moyo.
Pamenepo, monga kulingaliridwa kotsiriza, pali chochititsa mantha cha timagulu ta achichepere, tonyamula mfuti, toyendayenda m’makwalala, tikumenyana ndi mfuti, zipolopolo ziri mkati, zikumapha osati kokha wina ndi mnzake komanso ana opanda liwongo ndi achikulire opezereredwa m’kuomberanako. Tikusakaza madera ambiri okhala anthu m’mizinda yaikulu—m’chigawo cha Los Angeles chokha, “muli ziŵalo zoposa 100,000 za timagulu todziŵika toposa 800.” (Seventeen, August 1991) Ambiri a iwo ngochokera m’mabanja osweka. Kaguluko kamakhala banja lawo. Ambiri amaloŵa m’ndende. Ambiri amafa. Mawu ogwidwa m’makalata atatu olembedwa kundende aŵa ali mkhalidwe wake weniweniwo.
Oyamba: ‘Ndiri m’ndende chifukwa cha kuyesa kuba. Tinali anayi. Ndiyeno apolisi anadza. Anzanga aŵiri anathaŵa, ineyo ndi mnzanga wina tinathaŵira kwina, koma osati mwamsanga koposa agalu apolisi a mtundu wa Jeremani amene anatipeza ndi kutigwira. Pamene ndituluka, ndikhulupirira kuti tsiku lina ndidzakhala munthu wina wapadera. Nthaŵi zonse kumka kusukulu ndi kupeza magiredi abwino kunali kondivuta kwambiri. Komatu, bwanawe, sunawonepo chinthu chovuta monga kukhala m’ndende!’
Achiŵiri: ‘Pamene ndinafika kuchokera ku Mexico poyamba, ndinali wa zaka zisanu ndi zitatu zokha. Pamene ndinafika zaka 12, ndinaloŵa m’kagulu ka apandu. Pamene ndinafika zaka 15, ndinali wokangalikadi. Ndinkaombera anthu ndiri m’galimoto. Nthaŵi zonse ndinali ndi mfuti. Pamene ndinali ndi zaka 16, ndinawomberedwa ndipo ndinali pafupifupi kufa. Ndipo ndimathokoza Ambuye kuti sanandifune panthaŵiyo chifukwa ndinali wosakonzekera kukakhala naye. Pakali pano ndiri ndi ziboo za zipolopolo m’miyendo. Chotero kulangiza kwanga nkwakuti musakhale chiŵalo cha kagulu ka apandu!!! mukatero mudzakhala nokhanokha ndi wopunduka m’ndende monga ineyo!’
Achitatu: ‘Ndakhala chiŵalo chodziŵika cha kagulu ka apandu kuyambira zaka 11 zakubadwa. Ndabayidwa ndi mpeni kanayi, kuwomberedwa katatu, ndi kutsekeredwa m’ndende ndi kumenyedwa nthaŵi zambiri kwakuti nkovuta kuŵerenga kuti ndikangati. Chinthu chokha chotsalira kwa ine ndicho kufa, koma ndakhala wokonzekera zimenezo tsiku lirilonse chiyambire pamene ndinafika zaka 13, ndipo tsopano ndiri ndi zaka 16. Ndiri muukaidi wa miyezi isanu ndi itatu ndipo m’zaka zoŵerengeka ndidzafa, komatu mungapeŵe zonsezi mwa kusakhala chiŵalo cha kagulu ka apandu.’
Pezani Nthaŵi Yamtengo Wapatali
Tsopanotu, konseku sikunena kuti kulephera kuphunzitsa ana m’zaka za kuumbika kudzachititsa kwenikweni maupandu owopsa ameneŵa. Koma kulephera kuchita motero kungatsogolere kukhalidwe losokonezeka, limene lingakule kukhala kupulupudza, ndipo ngati kulekereredwa, kupulupudza kungakule kukhala khalidwe laupandu, kuloŵa m’ndende, ndi imfa.
Ndipo kuletsedwa zikhoterero zirizonse zotero mwa ana anu kumachitidwa mosavuta m’zaka za kuumbika koposa kuyembekezera kufikira pamene ali m’zaka zawo za ku ma 13 kufikira 19. Kwenikweni, asanafike pausinkhu wopita kusukulu yanasale ndiyo nthaŵi ya kuyamba, pamene mumakhala nawo kwambiri m’zaka za kuumbika, zisonkhezero zakunja zisanaloŵe. Ngati simunayandikane nawo kwambiri kuyambira paukhanda, sadzakulolani kuwayandikira m’zaka zawo za kusinkhuka. Mungatulukire kuti anzawo akuloŵani m’malo. Chotero uphungu kwa makolo ngwakuti, Musanyalanyaze ana anu m’zaka za kuumbika zimenezi pamene chithandizo chanu choposa kwa iwo chidzabala ubwino, wanu ndi wawo.—Yerekezerani ndi Mateyu 7:16-20.