Phunzitsani Mwana Wanu M’njira Yabwino—Ndipo Kuchiteni Kuchokera ku Ukhanda!
“Nthaŵi ya ukhanda iri mosakaikira yolemerera kwenikweni. Ifunikira kugwiritsiridwa ntchito ndi maphunziro m’kuthekera kulikonse ndi njira yophulapo kanthu. Kuwononga kwa nthaŵiyi ya umoyo sikungathe kupezedwanso. M’malo mwa kunyalanyaza zaka zoyambirira, liri thayo lathu kuzilimirira izo ndi kusamala kokulira.”—Dr. Alexis Carrel.
PALI kufunika kwa kukonzekeretsa ponse paŵiri nzeru ndi mtima. Anthu angazizwitsidwe ndi kuwonetsedwa kwa zofikiritsidwa za nzeru, koma Mulungu amawona m’mtima. Chidziŵitso m’mutu chimakhoterera pa kudzitukumula; chiri chikondi m’mtima chimene chimamangirira. Nzeru za luntha zimafunikira mitima ya chikondi, “pakuti m’kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” Kuchokera m’mtima wophiphiritsira umenewu kumabweranso ntchito zabwino ndi zoipa. (Mateyu 12:34, 35; 15:19; 1 Samueli 16:7; 1 Akorinto 8:1) Chotero pamene kuli kwakuti chiri chofunika kudzutsa nzeru za mwana, chiri ngakhale chofunika kwenikweni kulowetsa chikondi m’mitima yawo.
Pamakhala choyambitsa chopangidwira mkati kaamba ka ichi pa kubadwa. Chimatchedwa chomangira. Mayi amanyamula, kuyangata, kugirigisa, ndi kulankhula mofewa kwa khanda lake. Khanda, m’kuyankha, limayang’ana mwachindunji kwa mayi wake. Kumangirira kumatenga malo, chibadwa cha ukholo chimadzutsidwa, ndipo khanda limadzimva losungika. Maulamuliro ena amakhulupirira kuti “pamakhala nyengo yozindikira m’mphindi zochepa zoyambirira ndi maora pambuyo pa kubadwa kwa khanda chimene chiri chokhutiritsa ku kugwirizana kwa khanda ndi kholo.”
Chiyambi chabwino, koma chiri kokha chiyambi. Khanda limakhala lopanda thandizo, limakhala lodalira poyambirirapo kwa amayi wake kaamba ka zofunika zake za mwamsanga—ponse paŵiri zakuthupi ndi zamalingaliro. Popanda zakudya khanda limafa ndi njala; ilo lingafenso ndi njala mwamalingaliro. Kuyangata, kusisita, kumuponya m’mwamba ndi kum’gwiranso, kumuseweretsa, kumkonda—zonsezi zimadzutsa kukula kwa bongo. Kudzutsa kumeneku kwalinganizidwa ku zakudya zopatsa mphamvu za bongo. Popanda izo bongo limakhala ndi njala ndipo limadwala kwa moyo wonse. Ndipo kaamba ka kusasamala kumeneku ilo lingakhalenso lankhanza, losamvera, ndi lachiwawa. Kulera kwa umayi kuli chiyambi chamwana ndi chachitaganya—chofunika kwambiri kuposa ntchito iriyonse yakudziko!
Mbali ya Atate
Atate safunikira kusiyidwa. Ngati iwo akhalapo pakubadwa, kumangirira kwa atate ndi mwana kudzayamba. Pamene milungu ndi miyezi ipita, chisonkhezero cha mbali yawo chimakula mwamsanga, monga mmene chasonyezedwera ndi Dr. T. Berry Brazelton, katswiri m’gawo la kukula kwa mwana.
“Mwana aliyense amafunikira amayi ndi atate,” iye akutero, “ndipo atate aliyense angapange kusiyana. Kwa khanda, kukhala ndi tate wodziphatikizamo mwachangu, sikuli kofanana ndi kungokhala ndi kulera kwa umayi.” Iye akugwira mawu ripoti lomwe linasonyeza kusiyana mu njira imene amayi ndi atate amasamalira ana. “Amayi anawonekera kukhala okhazikika ndi a mtima wofatsa ndi makanda awo. Atate, kumbali ina, anali amaseŵera kwenikweni, kunyerenyetsa ndi kujinyajinya makanda awo kuposa ndi mmene amayi anachitira.”
Koma atate amapatsa ana zoposa maseŵera chabe. “Kumene kuli atate wachangu,” iye watero, “mwana amakula kukhala wopita patsogolo kwenikweni pasukulu, kukhala ndi nzeru zabwino za kuzindikira ndi kuyanjana bwino ndi ana ena. Iye amakhulupirira kwambiri mwa iyemwini ndipo ali wosonkhezeredwa bwino kuti aphunzire. Panthaŵi imene ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi kapena zisanu ndi ziŵiri, mphamvu za luntha za mwana zidzakhala zokulira.”
Yehova Mulungu amalamulira unansi wa kuphunzitsa kosamalitsa pakati pa atate ndi ana: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Palibe chiyambi champata wa mbadwo pano!
Kuphunzitsa Kuchokera ku Ubwana
Pali misinkhu kapena mbali mu kukula kwa achichepere m’kupita kwa zaka kuchokera pa kubadwa kufika ku zaka zisanu ndi chimodzi: kugwirizanitsa mphamvu, maluso akalankhulidwe, mitundu ya malingaliro, nzeru za kukumbukira, mphamvu za kuganizira, chikumbumtima, ndi zina. Pamene bongo la mwana likula mofulumira ndipo misinkhu imeneyo ifika m’nthaŵi zake, imeneyo imakhala nthaŵi ya mwaŵi kaamba ka kuphunzitsa maluso osiyanasiyanawa.
Imeneyo ndiyo nthaŵi pamene bongo la mwana ligwiritsira ntchito maluso amenewa kapena mitundu monga mmene chinkhupule chimayamwira madzi. Atakondedwa, amaphunzira kukonda. Atalankhulidwa ndi kuŵerengeredwa, amaphunzira zonse ziŵiri kulankhula ndi kuŵerenga. Ataikidwa kuseŵera pamadzi (skis), amadzakhala katswiri woseŵera pamadzi. Atawunikiridwa ku chilungamo, amamwerekera ndi malamulo abwino. Ngati misinkhu yophunzira yoyenera imeneyi yapita popanda zolowetsedwamo zabwino, michitidwe imeneyi ndi maluso zidzakhala zovuta kwenikweni kuzipeza pambuyo pake.
Baibulo limazindikira ichi, chotero limalangiza makolo kuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo ngakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Kuchitira ndemanga kwa The Keil-Delitzsch kumachiika mwanjirayi: “Patsani mwana malangizo molingana ndi njira zake.” Liwu la Chihebri lotembenuzidwa “kuphunzitsa” limatanthauzanso “kuyambitsa” ndipo pano limasonyeza kuyambitsa kwa malangizo oyambirira a mwana. Aperekeni kulingana ndi njira ya mwana, ogwirizana ndi njira zake, kulingana ndi misinkhu ya kukula kwake komwe iye akupitamo. Iyo ndiyo nthaŵi yoyenera kwa iye kumwerekera mosavuta, ndipo zimene amaphunzira mkati mwa zaka za kukulazi mwachidziŵikire zidzakhalira ndi iye.
Iri ndilo lingalironso la ophunzira ambiri a kukula kwa anthu: “Palibe kulikonse m’kufufuza kwa kukula kwa mwana kumene tasonyeza mlingo wamphamvu wa kuchotsa zizoloŵezi zaumwini zoyambirira, kapena mkhalidwe wa mayanjano woyambirira.” Iwo amavomereza kuti zingachite, koma “kaŵirikaŵiri kuchiritsa sikudzapezedwa.” Kusiyapo kwambiri kumachitika, ngakhale kuli tero, kupyolera mu mphamvu ya chowonadi cha Mulungu kuyambukira masinthidwe.—Aefeso 4:22, 24; Akolose 3:9, 10.
Chinenero chiri chitsanzo chabwino cha kuphunzira kopatsidwa panthaŵi yoyenera. Makanda ali okonzekeretsedwa mwachibadwa kaamba ka malankhulidwe, koma kuti unyinji wamphamvu woterewu wotsekeredwa mu bongo ugwire ntchito pa kuyenera kokulira, wachichepere afunikira kuwunikiridwa ku mawu amalankhulidwe pa msinkhu wabwino wa kukula. Kukula mu magwero akalankhulidwe kumadzawonekera pakati pa miyezi 6 ndi 12 ngati achikulire amalankhula kwa wachichepere kaŵirikaŵiri. Pakati pa miyezi 12 ndi 18 kukula kumeneku kumapitirizabe pamene wachichepere azindikira kuti mawu ali ndi tanthauzo.
Iye akuphunzira mawu asanayambe kuwalankhula iwo. Mkati mwa chaka chachiŵiri cha umoyo, kulandira kumeneku, kapena kochititsidwa ndi zakunja, kwa kusunga unyinji wa mawu kungapitirize kuchoka pa mawu ochepa kufika ku mazana angapo. Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteo kuti “kuyambira ukhanda wako wadziŵa malemba opatulika.” (2 Timoteo 3:15) Tanthauzo lenileni la liwu lakuti “ukhanda” liri “wosalankhula.” Mwachidziŵikire kwenikweni Timoteo anali kuŵerengeredwa Malemba Oyera pamene iye anali khanda, ndipo chotero iye anadziŵa mawu ambiri a Baibulo asanayambe kuwalankhula.
Nsonga iri yakuti, pali nthaŵi zenizeni m’kukula kwa mwana pa zimene zinthu zina zingaphunziridwe mosavuta, chifupifupi mwakumwerekera. Komabe, ngati nthaŵi zimenezo zipita popanda kusonkhezera kofunika, maluso sadzakulitsidwa kotheratu. Ngati, mwachitsanzo, ana samamvera malankhulidwe a mawu aliwonse kufikira zaka zina pambuyo pake, iwo adzawaphunzira mochedwa ndipo movutitsitsa, ndipo kaŵirikaŵiri osachita bwino.
Ŵerengani kwa Mwana Wanu Kuchokera Kuukhanda
Kodi ndi liti pamene mungayambe? Kuchokera pachiyambi. Ŵerengani kwa wobadwa chatsopano wanu. ‘Koma iye sadzakumvetsera iko!’ Kodi ndi liti pamene munayamba kulankhula kwa iye? ‘Nkulekelanji, mwamsanga, ndithudi.’ Kodi iye anamvetsera chimene inu munkanena? ‘Chabwino, ayi, koma . . . ’ Ngati ndi tero bwanji osaŵerenga kwa iye?
Mwakufungata mwana m’manja mwanu, mikono yanu iri yomuzungulira iye, kumufungata iye mwathithithi, amadzimvera wosungika, wokondedwa. Kuŵerenga kwanu kwa iye kuli chokumana nacho chokondweretsa. Kumapanga chisonyezero. Iye amagwirizanitsa kudzimva kwa chisangalalo ndi kuŵerenga. Makanda ali otsanzira, ndipo makolo ali chosonyeza chitsanzo. Iye amafuna kukutsanzirani inu. Amafuna kuŵerenga. Iye amaseŵera kusonyeza kuti akuŵerenga. Pambuyo pake amakumana ndi chisangalalo cha kuŵerenga.
Chifukwa cha ichi pamabweranso kupindula kwina kokulira—iye kaŵirikaŵiri samakhala womwerekera ndi wailesi ya kanema. Iye samakhala mosadziŵa kanthu ndi kupenyerera zikwizikwi za kupyozedwa ndi mpeni, kulasidwa ndi mfuti, kupha anthu, kugwirira chigololo, dama, ndi chigololo. Iye angazime TV; angatsegule bukhu ndi kuliŵerenga. Kukwaniritsa ndithudi m’masiku awa akusaphunzira ndi kumwerekera mu TV!
Chimatenga Nthaŵi kuti Mukonde Mwana
Ndithudi, chimatenga nthaŵi kuŵerenga kwa mwana. Ndipo chimatenga nthaŵi kuseŵera ndi khanda lanu, kuchita maseŵera osangulutsa mwana ndi maseŵera osangulutsa mwa kudzidzimutsa mwana, kumuyang’anira iye pamene akutsanzira, kuyambitsa ntchito, kufunafuna zatsopano, kukwaniritsa chilakolako, ndi kudzutsa mtima wa zopangapanga. Kulera kwa ukholo kumatenga nthaŵi. Ndipo munali ndi chiyambi chabwino pamene ana anu anali makanda. Pamenepo kaŵirikaŵiri ndi pamene mpata wa mbadwo umayamba; iwo amayembekeza mochepera kufikira nthaŵi ya unyamata. Robert J. Keeshan, wowulutsa pa wailesi wa ana monga Captain Kangaroo, akulongosola mmene chingachitikire:
“Mwana wachichepere amayembekeza, chala chake chiri mkamwa, ndi chidoli m’dzanja, ndi kutekeseka, kwa kubwera kwa kholo kunyumba. Iye amalakalaka kulongosola zokumana nazo za maseŵera. Amakhala wosangalatsidwa kugawana zinthu zomwe wadziŵa tsiku limenelo. Nthaŵi imayandikira, ndipo kholo limafika. Mwakutopetsedwa ndi kudidikiza kwa malo antchito kholo kaŵirikaŵiri limangonena kwa mwana wake kuti, ‘Osati nthaŵi ino, wokondedwa. Ndiri wotanganitsidwa, pita ukapenyerere wailesi ya kanema.’ Mawu amene kaŵirikaŵiri amakambidwa m’nyumba zambiri mu America, ‘Ndiri wotanganitsidwa, pita ukapenyerere wailesi ya kanema.’ Ngati sinthaŵi ino, liti? ‘Nthaŵi zina.’ Koma nthaŵi zina kaŵirikaŵiri sizimabwera . . .
“Zaka zimangopita ndipo mwana amakula. Timangomupatsa zidoli ndi zovala. Timampatsa zovala zopangidwa bwino ndi wailesi koma sitimampatsa chimene iye akufuna kwambiri, nthaŵi yathu. Ali wa zaka khumi ndi zinayi, maso ake ali osadziŵa kanthu, iye akufunafuna chinthu china. ‘Wokondedwa, kodi nchiyani chimene chikuchitika? Tangolankhula kwa ine, lankhula kwa ine.’ Kuli kuchedwa. Kulidi kuchedwa. Chikondi chatipitirira. . . .
“Pamene tinena kwa wachichepere kuti, ‘Osati tsopano, nthaŵi zina.’ Pamene tinena kuti, ‘Pita ukapenyerere TV.’ Pamene tinena kuti, ‘Usamafunsa mafunso ambiri.’ Pamene tilephera kupatsa anthu athu achichepere chinthu chimodzi chimene iwo amafuna kwa ife, nthaŵi yathu. Pamene tilephera kukonda mwana. Sitiri osasamala. Ife tiri kokha otanganitsidwa kukonda mwana.”
Nzowona, kukonda mwana wanu kumatenga nthaŵi. Osati kokha nthaŵi ya kudyetsa thupi lake ndi zakudya ndi kumupatsa zovala koma nthaŵi ya kudzaza mtima wake ndi chikondi. Osati chikondi chopimidwa, cholinganizidwa, ndi chamlingo koma chosefukira ndi “chikondi chopanda polekezera,” monga mmene Burton L. White, mkonzi wa bukhu la The First Three Years of Life, anachiitanira icho. Iye ananena kuti: “Chiri chopanda nzeru kwenikweni kwa makolo ogwira ntchito kusinthira ntchito yoyambirira ya kulera mwana kwa winawake, makamaka ku maziko okhazikitsidwa pakati a kulera ana. Tsopano, ndakhala ndikusulizidwa kwambiri ndi kalankhulidweko, koma kudera nkhaŵa kwanga kuli kaamba ka chimene chiri chabwino koposa kwa makanda.” Iye akuwona ichi monga “chimene chiri chabwino koposa kaamba ka makanda.” Komabe kuzindikira kufunika kumeneku sikuli kothekera nthaŵi zonse mwa ndalama pamene mmodzi kapena ngakhale makolo onse aŵiri afunikira kugwira ntchito.
Uphungu—Nkhani Yogwira Mtima!
Kusuliza kwambiri kwaikidwanso pa Baibulo kaamba ka malangizo ake onena za uphungu. “Wobweza nthyole yake akuda mwana wake, koma womkonda amyambiza kumlanga.” (Miyambo 13:24) Pa ndime imeneyi New International Version Study Bible mawu ammunsi amati: “nthyole. Mwinamwake mawu ophiphiritsira a chilango cha mtundu uliwonse.” Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limamasulira “nthyole” monga “ndodo ya mfumu, monga chiphiphiritsiro cha kulamulira.”
Kulamulira kwa makolo kungaphatikizepo kukwapula, koma kaŵirikaŵiri sikumafunikira. Kulingana ndi 2 Timoteo 2:24, 25, Akristu afunikira kukhala “okhazikika kwa onse, . . . ophunzitsa moleza mtima” (NW). Liwu lakuti “kuphunzitsa” likutembenuzidwa pano kuchokera ku liwu la Chigriki lauphungu. Uphungu ufunikira kupatsidwa molingana ndi malingaliro a ana: “Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”—Aefeso 6:4.
Akatswiri a za maganizo mwakupititsa patsogolo kuvomereza amanena kuti ngati mukwapula mwana wanu mumamuda. Zimenezo siziri zowona. Kuvomereza kuli kuda. Iko kwamasula kuswa lamulo kwa achichepere ndi uchifwamba kuzungulira dziko lonse lapansi ndipo kwapangitsa kuthedwa nzeru ku mamiliyoni a makolo. Chiri monga mmene Miyambo 29:15 imanenera: “Mwana wolekereredwa achititsa amake manyazi.” Pansi pa mutu wakuti “Kusamalitsa kutsutsana ndi makolo ovomereza,” Dr. Joyce Brothers ananena kuti:
“Maphunziro aposachedwapa achifupifupi 2,000 okhala m’magredi a chisanu ndi a chisanu ndi chimodzi—ena omwe analeredwa ndi makolo osamalitsa, ena ndi makolo ovomereza—anatulutsa zotulukapo zodabwitsa. Ana amene anapatsidwa uphungu mosamalitsa anali ndi kulemekezedwa kokulira ndipo [anali] okwaniritsa opambana, mwamayanjano ndi mwamaphunziro.” Kodi iwo anali okalipitsidwa ndi makolo awo osamalitsa? Ayi, “iwo anakhulupirira kuti malamulo a ukholo anapangidwa kaamba ka ubwino wa ana—ndipo kunali kusonyezedwa kwa chikondi cha ukholo.”
White akuti ngati muli wosamalitsa ndi mwana wanu, simufunikira kukhala ndi mantha “kuti sadzakukondani kwambiri kuposa ngati inu mukanakhala wolekerera. Ana mu zaka zoyamba ziŵiri za umoyo samakhala olekanitsidwa mosavuta kuchokera ku owasamalira awo oyambirira; ngakhale ngati muwakwapula nthaŵi zonse, inu mudzapeza kuti iwo apitirizabe kubwerera kwa inu.”
Kuphunzitsa Kwabwino Koposa Zonse
Kuli inu. Chitsanzo chanu. Muli chitsanzo chotsatira cha mwana wanu. Iye amamvetsetsa kwambiri ku chimene inu muli kuposa ndi chimene mumanena. Iye amamvetsera mawu anu, koma amatsatira kachitidwe kanu. Mwana wanu ali chinthu chotsanzira. Chotero, kodi mufuna kuti iye akhale wotani? Wokonda, wachifundo, woolowa manja, wa luntha, wa nzeru, wa luso, wophunzira wa Yesu, wolambira wa Yehova? Chirichonse chimene chingakhale, khalani tero inu eni.
Chotero, phunzitsani mwana wanu kuchokera ku ukhanda, pamene bongo lake likukula mofulumira, kusonkhanitsa chidziŵitso ndi malingaliro kaamba ka nzeru ndi mtima. Koma ngati zaka zovuta zimenezo za kakulidwe zapita ndipo umunthu waumulungu sunaikidwe mwa mwana wanu, ndiyeno chiyani? Musataye mtima. Kusintha kungachitikebe ndipo kukuchitika kwa mamiliyoni, ponse paŵiri achichepere ndi achikulire, mwa mphamvu ya Mulungu. “Vulani umunthu wakale limodzi ndi zochita zake,” Mawu a Mulungu amatero, “ndipo muvale umunthu watsopano, umene mwa chidziŵitso cholongosoka ulinkupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanefane cha Uyo amene anaulenga.”—Akolose 3:9, 10, NW.
[Zithunzi patsamba 8]
Ndi atate: Nthaŵi ya kuŵerenga, Nthaŵi ya kusewera
[Chithunzi patsamba 10]
Nthaŵi yosamba ingakhale nthaŵi yoseketsa