Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jd mutu 1 tsamba 5-13
  • Uthenga Umene Yehova Anapereka Kalelo Ndi Wothandizanso Masiku Ano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uthenga Umene Yehova Anapereka Kalelo Ndi Wothandizanso Masiku Ano
  • Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI MABUKU ANG’ONOANG’ONO A ANENERI 12 NDI OTHANDIZADI?
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TINGANENE KUTI MABUKUWA NDI A ANENERI?
  • ZIMENE TINGACHITE KUTI TIPINDULE NDI MABUKUWA
  • Dziwani Yehova Ndipo Mutumikireni
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Mulungu Angakuthandizeni Kukonzekera Tsiku Lake Lalikulu
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Aneneri Amene Uthenga Wawo Ungatithandize
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Mfundo Yaikulu mu Uthenga wa Aneneri 12 Inali Yokhudza Tsiku la Yehova
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
Onani Zambiri
Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
jd mutu 1 tsamba 5-13

MUTU 1

Uthenga Umene Yehova Anapereka Kalelo Ndi Wothandizanso Masiku Ano

1, 2. Kodi anthu ena achita chiyani kuti apeze chuma chobisika, ndipo mungachite chiyani kuti mukhale ndi moyo wosangalala?

KWA zaka zambiri, anthu ambiri akhala akuyesetsa kuti apeze chuma chobisika. Kodi munawerengapo nkhani za anthu osiyanasiyana amene ankafufuza chuma chobisika? Mwina inuyo simungafufuze nawo chuma chobisika ngati chimenechi. Koma kodi mungamve bwanji mutapeza chuma chinachake chamtengo wapatali? N’zodziwikiratu kuti mungasangalale kwambiri ngati chumacho chingakuthandizeni kuti zinthu zikuyendereni bwino pa moyo wanu.

2 Anthu ambiri safufuza chuma chenicheni chobisika, koma pofuna kukhala osangalala, amayesetsa kuti apeze ndalama, akhale ndi thanzi labwino, komanso kuti akhale ndi banja labwino. Anthu ofufuza chuma chobisika amadalira mapu kuti apeze chumacho. Koma palibe mapu enieni amene amathandiza anthu kuti akhale osangalala komanso kuti zinthu ziziwayendera bwino. Choncho anthu amafunika kuchita khama kuti apeze zinthu zimenezi. N’chifukwa chake anthu ambiri amayamikira akapeza malangizo abwino amene angawathandize kukwaniritsa zolinga zawo komanso amene angawathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino n’kumasangalala pa moyo wawo.

3, 4. Kodi malangizo amene angakuthandizeni kukhala ndi moyo wabwino mungawapeze kuti?

3 Inuyo mungapeze malangizo ofunika kwambiri omwe athandiza kale anthu ena kukhala osangalala. M’Baibulo muli malangizo abwino kwambiri othandiza pa moyo wathu, ndipo anthu ambiri aona kuti zimenezi n’zoona. Mwachitsanzo, wolemba mabuku wa ku England dzina lake Charles Dickens, analemba kuti: “Baibulo ndi buku labwino kwambiri kuposa buku lina lililonse padziko lonse lapansi . . . chifukwa lili ndi malangizo abwino amene munthu wina aliyense . . . akhoza kugwiritsa ntchito.”

4 Mfundo imeneyi ndi yosadabwitsa kwa anthu onse amene amaona kuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu. Mwina mumavomereza mfundo imene timaiwerenga pa 2 Timoteyo 3:16, yakuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.” Choncho tinganene kuti Baibulo lili ndi mfundo zabwino kwambiri zimene zingathandize anthu kudziwa mmene angakhalire ndi moyo wabwino m’dziko lamavutoli. Amene amatsatira mfundo za m’Baibulo angakhale ndi moyo wabwino kwambiri komanso wosangalala.

Chithunzi patsamba 12

5-7. Kodi malangizo othandiza angapezekenso kumbali ziti za m’Baibulo?

5 Koma kodi ndi mbali ziti za m’Baibulo zimene mumaona kuti mungapezemo mfundo zothandiza? Ena angaganize za ulaliki wa paphiri, pamene Yesu anapereka malangizo othandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Ndipo ena angakumbukire makalata amene mtumwi Paulo analemba. Aliyense angapeze malangizo ambiri anzeru komanso othandiza m’mabuku a Masalimo ndi Miyambo. Komatu buku lililonse la m’Baibulo ndi lothandiza mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu kapena mavuto amene mukukumana nawo. Mungapeze malangizo othandiza ngakhale m’mabuku amene amafotokoza mbiri yakale monga mabuku amene ayambira pa Yoswa mpaka Esitere. M’nkhani zimene zili m’mabuku amenewa muli zitsanzo zochenjeza aliyense amene akufuna kuti azisangalala potumikira Mulungu. (1 Akorinto 10:11) Zoonadi, m’mabuku onse a m’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino pa moyo wanu ngati mutawagwiritsira ntchito. Kumbukirani mfundo yakuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”​—Aroma 15:4; Yoswa 1:8; 1 Mbiri 28:8, 9.

6 Komabe pali mbali ina ya m’Baibulo imene anthu ambiri sanaiphunzire mozama koma ili ndi chuma chobisika. Mbali imeneyi ili ndi mabuku 12, oyambira ndi buku la Hoseya mpaka la Malaki. M’Mabaibulo ambiri mabuku amenewa amatsatizana ndi mabuku akuluakulu omwe ndi Ezekieli komanso Danieli, tisanapeze buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu. (M’Mabaibulo ambiri mabuku 12 amenewa anatsatizana motere: Hoseya, Yoweli, Amosi, Obadiya, Yona, Mika, Nahumu, Habakuku, Zefaniya, Hagai, Zekariya ndi Malaki.) Taona kale kuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu ndipo ndi lothandiza pophunzitsa, komanso muli malangizo othandiza anthu pa moyo wawo. Koma kodi mabuku 12 amenewa ndi othandizanso?

7 Inde ndi othandiza. Ndipotu m’mabuku amenewa muli mfundo zofunika kwambiri zimene zingatithandize pa moyo wathu masiku ano. Anthu ena amaona kuti mabuku 12 amenewa ndi osafunika kwenikweni chifukwa chakuti ndi afupiafupi. Koma kodi ndi osafunikadi?

KODI MABUKU ANG’ONOANG’ONO A ANENERI 12 NDI OTHANDIZADI?

8. (a) Kodi njira yofunika kwambiri imene Mulungu waperekera malangizo ndi iti? (b) Kodi mabuku 12 amene akuyambira pa Hoseya mpaka Malaki tiyenera kuwaona bwanji?

8 Pamene mtumwi Paulo ankalemba kalata yopita kwa Aheberi, anayamba ndi mawu akuti: “Kalekale, Mulungu analankhula ndi makolo athu nthawi zambiri ndiponso m’njira zambiri kudzera mwa aneneri. Kumapeto kwa masiku ano, iye walankhulanso kwa ife kudzera mwa Mwana wake.” (Aheberi 1:1, 2) Popeza kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito aneneri popereka uthenga wake, sitiyenera kuona aneneri amenewo kapena zimene analemba ngati zosafunika. Ngakhale kuti mabuku a aneneriwa ndi ang’onoang’ono, sikuti nkhani zake n’zosathandiza kwenikweni. Uthenga umene uli m’mabukuwo ndi wofunika kwambiri mofanana ndi uthenga umene uli m’mabuku ena onse a m’Baibulo.

9. N’chifukwa chiyani kufupika kwa buku la m’Baibulo sikusonyeza kuti bukulo ndi losafunika poyerekezera ndi mabuku ena?

9 Buku la m’Baibulo likakhala lalifupi sizitanthauza kuti ndi losafunika kapena silingakuthandizeni. Mwachitsanzo, buku la Rute ndi lalifupi kwambiri kuposa mabuku amene ali pambuyo kapena patsogolo pake, koma mumapezeka mfundo zogwira mtima kwambiri. Bukuli limasonyeza mmene tiyenera kukondera kulambira koona. Limasonyezanso kuti Mulungu amaona kuti akazi ndi ofunika kwambiri komanso limatiuza mfundo zotithandiza kudziwa m’badwo wa makolo a Yesu. (Rute 4:17-22) Chitsanzo china ndi buku la Yuda limene lili chakumapeto kwa Baibulo. Bukuli ndi lalifupi kwambiri moti m’Mabaibulo ena silikwana ngakhale tsamba limodzi. Komabe, m’bukuli muli mfundo komanso malangizo ofunika kwambiri chifukwa limanena zimene Mulungu anachita ndi angelo oipa komanso chilango chimene adzawapatse m’tsogolo. Ndiponso muli chenjezo lakuti anthu oipa adzalowa mwachinyengo mumpingo, ndipo bukuli limatilimbikitsa kuti tiyesetse kumenya nkhondo ya chikhulupiriro chathu. Choncho ngakhale kuti mabuku 12 amenewa ndi afupiafupi, sizikutanthauza kuti ndi osafunika kapena kuti sangakuthandizeni.

N’CHIFUKWA CHIYANI TINGANENE KUTI MABUKUWA NDI A ANENERI?

10, 11. (a) Kodi anthu ena amaganiza chiyani akamva mawu akuti “mneneri”? (b) Malinga ndi Baibulo, kodi mneneri anali ndani ndipo ankachita chiyani?

10 Mfundo ina yofunika kuiganizira ikukhudza mawu akuti “mneneri.” Tikamva mawu amenewa tingaganizire za kulosera zam’tsogolo. Anthu ambiri akamva mawu akuti mneneri amaganiza za munthu amene amalosera zam’tsogolo, mwina polankhula mawu ovuta kuwamvetsa amene anthu angawatanthauzire m’njira zosiyanasiyana. Maganizo amenewa amachititsa kuti anthu aziona mabuku 12 amenewa mosiyanasiyananso.

11 N’zoona kuti mukamawerenga mabukuwa, mumazindikira mwamsanga kuti muli maulosi ambiri, ndipo ambiri mwa iwo ndi okhudza tsiku lalikulu la Yehova limene latsala pang’ono kufika. Zimenezi n’zogwirizana ndi tanthauzo la mawu akuti “mneneri.” Mneneri anali munthu amene anali pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo kawirikawiri ankamugwiritsa ntchito yolengeza zimene zichitike. Kuyambira ndi Inoki, aneneri ambiri otchulidwa m’Baibulo ankaloseradi zam’tsogolo.—1 Samueli 3:1, 11-14; 1 Mafumu 17:1; Yeremiya 23:18; Machitidwe 3:18; Yuda 14, 15.

12. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti ntchito ya mneneri sinali kungolosera zam’tsogolo basi?

12 Komabe tiyenera kukumbukira kuti aneneri a Yehova Mulungu ankagwira ntchito zambiri osati kungonena ulosi wochokera kwa iye basi. Nthawi zambiri Mulungu ankagwiritsa ntchito aneneri kuti azimulankhulira pouza ena zimene iye akufuna. Mwachitsanzo, sitinganene kuti Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ankalosera zam’tsogolo, komabe lemba la Salimo 105:9-15 limawaika m’gulu la aneneri. Nthawi zina Mulungu ankawagwiritsa ntchito kuti anene zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo, monga pa nthawi imene Yakobo ankadalitsa ana ake. Komanso makolo akale amenewa akutchedwa aneneri chifukwa ankauza anthu a m’banja mwawo zimene Yehova ananena zoti iwo adzathandizira pokwaniritsa chifuniro chake. (Genesis 20:7; 49:1-28) Mfundo ina yosonyeza kuti mawu a m’Baibulo akuti “mneneri” amatanthauza zambiri, ndi yakuti Aroni anatumikira monga mneneri wa Mose chifukwa ankalankhula m’malo mwa Moseyo, kapena kuti anali ngati “kamwa” ya Mose.—Ekisodo 4:16; 7:1, 2; Luka 1:17, 76.

13, 14. (a) Perekani zitsanzo zosonyeza kuti aneneri ankachita zambiri kuwonjezera pa kulosera zam’tsogolo. (b) Kodi mungapindule bwanji mukadziwa mfundo yakuti aneneri ankachita zambiri kuwonjezera pa kulosera zam’tsogolo?

13 Taganiziraninso za mneneri Samueli ndi mneneri Natani. (2 Samueli 12:25; Machitidwe 3:24; 13:20) Ngakhale kuti Yehova anagwiritsira ntchito anthu awiri onsewa polosera zam’tsogolo, iwo anatumikira monga aneneri m’njira zinanso. Mwachitsanzo, pogwira ntchito yake monga mneneri, Samueli analimbikitsa Aisiraeli kuti asiye kulambira mafano, n’kuyambiranso kulambira koyera. Komanso iye anapereka uthenga wachiweruzo kwa Mfumu Sauli, ndipo tikaona uthengawo tingaphunzirepo mfundo yakuti Yehova amaona kuti kumvera n’kofunika kwambiri kuposa nsembe. Zoonadi, Samueli ankatchedwanso mneneri chifukwa ankapereka malangizo ochokera kwa Mulungu, amene angathandize anthu kudziwa zimene angachite kuti akhale ndi moyo wabwino. (1 Samueli 7:3, 4; 15:22) Nayenso mneneri Natani analosera zoti Solomo adzamanga kachisi ndiponso kuti ufumu wake udzakhazikika. (2 Samueli 7:2, 11-16) Koma pali zifukwa zinanso zimene zinachititsa kuti Natani azidziwika kuti anali mneneri. Mwachitsanzo, iye anaulula tchimo la chigololo limene Davide anachita ndi Bati-seba komanso tchimo la kupha Uriya. Palibe amene angaiwale fanizo limene Natani anagwiritsa ntchito poulula tchimo la chigololo limeneli. Iye ananena za munthu wolemera amene anatenga kankhosa kamodzi kokhako ka munthu wosauka, komwe mwiniwakeyo ankakakonda kwambiri. Komanso pa nthawi ina Natani anathandiza nawo pokhazikitsa ndondomeko yolambirira Mulungu panyumba yopatulika.​—2 Samueli 12:1-7; 2 Mbiri 29:25.

14 Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti tisamaganize kuti uthenga umene uli m’mabuku a aneneriwa ndi wolosera zam’tsogolo basi. M’mabukuwa mulinso mfundo zambirimbiri zouziridwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, muli mfundo zabwino kwambiri zimene zingatithandize kudziwa zimene anthu a Mulungu kalelo ankayenera kuchita kuti zinthu ziziwayendera bwino, ndipo mfundo zimenezi zingatithandizenso ifeyo. Sitikukayikira zoti mfundo zimene timapeza m’Baibulo, kuphatikizapo m’mabuku 12 a aneneriwa, n’zofunika kwambiri. Mfundozi zingathandize anthu kuti aone zimene angachite kuti akhale ndi moyo wabwino. Mabuku ouziridwawa amatithandiza kuti ‘tikhale anthu amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.’​—Tito 2:12.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIPINDULE NDI MABUKUWA

15, 16. (a) Kodi m’mabuku 12 a aneneri mukupezeka nkhani yotani yophiphiritsa? (b) Kodi nkhaniyo ikuchitira chithunzi chiyani?

15 Tikamawerenga mawu ouziridwa a Mulungu tingapindule m’njira zambiri. Buku lililonse la m’Baibulo ndi lofunika palokha, chifukwa mabuku ena amatiuza zimene zinachitika nthawi inayake ndipo ena analembedwa ngati ndakatulo. M’mabuku ena muli mawu ambiri ophiphiritsa ngati mmene zilili ndi mabuku 12 aulosiwa. Mwachitsanzo, Yesu ankagwiritsa ntchito nkhani ya m’buku la Yona pamene ananena kuti: “M’badwo woipa ndi wachigololo ukufunitsitsabe chizindikiro. Sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse koma chizindikiro cha mneneri Yona chokha. Pakuti monga momwe Yona anakhalira m’mimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, usana ndi usiku, chimodzimodzinso Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku. Anthu a ku Nineve adzaimirira pa chiweruzo limodzi ndi m’badwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona. Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.”​—Mateyu 12:39-41.

16 Apa n’zoonekeratu kuti Yesu anaona kuti m’buku la Yona munali zambiri kuwonjezera pa nkhani yokhudza zimene Mulungu anachita ndi Yona, zimene mneneriyu anachita ku Nineve komanso zimene zinachitika Yona atalengeza uthenga wa Mulungu wochenjeza anthu. Yesu Khristu anazindikira kuti zimene mneneri Yona ankachita zinkachitira chithunzi zimene zidzamuchitikire, monga imfa yake ndi kuukitsidwa pa tsiku lachitatu. Komanso zimene anthu a ku Nineve anachita Yona atawalalikira, n’zosiyana ndi zimene Ayuda anachita atamva uthenga wa Yesu ndi kuona ntchito zake. (Mateyu 16:4) Choncho tikudziwa kuti m’mabuku 12 amenewa muli nkhani zaulosi zimene zikuchitira chithunzi zochita za Mulungu ndi anthu ake masiku ano. Musangalala kuphunzira mabuku amenewa ndipo mupezamo mfundo zothandiza kwambiri.a

17. Kodi buku lino lafotokoza bwanji nkhani za m’mabuku 12?

17 Koma buku limene mukuwerengali silinalembedwe n’cholinga chofotokoza matanthauzo a nkhani zophiphiritsa zopezeka m’buku la Yona kapena m’mabuku ena 11 aja. Komanso silikufotokoza nkhani za m’mabuku amenewa vesi ndi vesi. Koma likufotokoza mfundo za m’mabuku amenewa zimene tingazigwiritse ntchito pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Choncho mukamaphunzira mabukuwa muzidzifunsa kuti: Kodi ndi malangizo kapena uphungu wothandiza uti umene Yehova akundipatsa kudzera m’mabuku 12 amenewa? Kodi mabukuwa angandithandize bwanji ‘kukhala wamaganizo abwino, wachilungamo ndi wodzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino’? Popeza kuti “tsiku la Yehova likubwera ndipo lili pafupi,” kodi mabukuwa akundiphunzitsa chiyani za moyo wachikhristu, makhalidwe abwino, moyo wabanja, komanso makhalidwe a anthu m’nthawi yovuta ino? (Tito 2:12; Yoweli 2:1; 2 Timoteyo 3:1) Mupeza mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa. Mupezanso malemba amene mudzaone kuti angakuthandizeni kwambiri pa moyo wanu, omwenso simunagwiritsirepo ntchito pokambirana ndi ena malangizo a m’Baibulo. Mukamachita zimenezi, mosakayikira mudzadziwa mfundo zambiri zofunika za m’Baibulo.​—Luka 24:45.

18. Kodi buku lino lalembedwa bwanji ndipo mungachite chiyani kuti mupindule nalo?

18 Mitu ya m’buku lino yagawidwa m’zigawo zinayi. Mukamayamba chigawo chilichonse, yesetsani kuganizira zimene muphunzire m’chigawo chimenecho. Kuyambira mutu 2, muzipeza mabokosi awiri m’mutu uliwonse, omwe cholinga chake n’kukuthandizani kukumbukira zimene mwaphunzira. Mafunso amene ali m’mabokosi amenewo akuthandizani kuganizira mozama zimene mwawerenga, kufunika kwake, komanso mmene mungazigwiritsire ntchito. Bokosi loyamba lili chapakati pa mutu uliwonse. Mukafika pabokosi limeneli, muziyesetsa kupeza mayankho a mafunso amene ali mmenemo. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti zimene mwaphunzirazo zikhazikike mumtima mwanu. (Mateyu 13:8, 9, 23; 15:10; Luka 2:19; 8:15) Bokosi lachiwiri lizikuthandizani kuganizira mozama zimene mwawerenga m’mbali yomaliza ya mutuwo komanso kuti muzizikumbukira. Choncho muziyesetsa kupeza nthawi yofufuza mayankho a mafunso amene ali m’mabokosi amenewa. Mafunso amenewa adzakuthandizani kuona mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo.

19. Kodi tidzifunse mafunso ati tisanayambe kuphunzira nkhani za m’mabuku 12 amenewa?

19 Musanayambe kuphunzira nkhani yotsatira, mudzifunse kuti, ‘Kodi ndikudziwa chiyani za nkhani za m’buku lililonse pa mabuku 12 amenewa? Kodi Mulungu anapereka uthengawu kudzera mwa anthu ati, ndipo anthu amenewo anali otani? Kodi anthuwo anakhala ndi moyo pa nthawi iti, ndipo zinthu zinali bwanji pamene ankachita utumiki wawo?b Kodi pa nthawi imene nkhaniyi inkalembedwa, uthenga wake unali wotani ndipo anthu akanaugwiritsa ntchito bwanji pa nthawiyo? Kodi kudziwa zimenezi kungandithandize bwanji kumvetsa nkhaniyi? Mutu wotsatira ukuthandizani kuyankha mafunso amenewa.

a Mwachitsanzo onani mmene Nsanja ya Olonda ya January 1, 1997, inafotokozera buku la Hagai, patsamba 6 mpaka 22, komanso mmene Nsanja ya Olonda ya January 1, 1996, inafotokozera buku la Zekariya, patsamba 8 mpaka 22.

b Tchati chimene chili patsamba 20 ndi 21 chingakuthandizeni kudziwa nthawi imene anthuwo anakhala ndi moyo. Choncho muzigwiritsa ntchito tchati chimenechi nthawi zonse mukamaphunzira mitu yotsatirayi.

MMENE MABUKUWA ANGAKUTHANDIZIRENI

  • Kodi muyenera kupewa maganizo olakwika ati okhudza mabuku ang’onoang’ono 12 a aneneri?​—Aroma 15:4.

  • • N’chifukwa chiyani mukuona kuti mungapindule pophunzira mabuku 12 a aneneri?​—2 Timoteyo 3:16.

  • Kodi mukuyembekezera kuti muphunzira zotani m’mabuku amenewa?—1 Atesalonika 2:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena