-
Kodi Zinachitikadi?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2016 | Na. 2
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAVUTIKA MPAKA KUFA?
Kodi Zinachitikadi?
Kumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., Yesu wa ku Nazareti anaimbidwa mlandu wabodza woukira boma. Anamenyedwa kwambiri ndipo kenako anakhomereredwa pamtengo. Yesu anafa mozunzika kwambiri. Komabe Mulungu anamuukitsa ndipo patatha masiku 40 anabwerera kumwamba.
Nkhani imeneyi imapezeka m’mabuku 4 a Uthenga Wabwino m’Malemba Achigiriki Achikhristu, omwe anthu ambiri amawatchula kuti Chipangano Chatsopano. Koma kodi nkhaniyi inachitikadi? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa ngati zili zabodza, ndiye kuti zimene Akhristu amakhulupirira ndi zopanda phindu, komanso zimene amayembekezera zoti dzikoli lidzakhala Paradaiso ndi maloto chabe. (1 Akorinto 15:14) Koma ngati zinachitikadi, ndiye kuti akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri mtsogolo ndipo inunso mukhoza kudzasangalala ndi zinthu zimenezi. Ndiye funso ndi lakuti, Kodi nkhani zimene zili m’Mabuku a Uthenga Wabwino ndi zoonadi?
UMBONI WOTSIMIKIZIRA KUTI ZINACHITIKADI
Mosiyana ndi nkhani zongopeka zomwe anthu amakhulupirira, nkhani zomwe zili m’Mauthenga Abwino ndi zolondola chifukwa zinafufuzidwa mosamala kwambiri. Mwachitsanzo, nkhanizi zimatchula mayina enieni a malo ndipo ambiri mwa malowa ndi oti anthu amapitako. Zimatchulanso mayina enieni a anthu ndipo olemba mbiri ena amatsimikizira kuti anthuwo anakhalakodi.—Luka 3:1, 2, 23.
Olemba mbiri ena omwe analipo pa nthawiyo analembanso nkhani zina zokhudza Yesu.a Nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zokhudza mmene Yesu anafera, zimagwirizana ndi zimene Aroma ankachita akafuna kunyonga munthu. Komanso zinthu zimene zinachitika zinalembedwa molondola ndipo olembawo sanabise china chilichonse moti analembanso zimene otsatira a Yesu analakwitsa. (Mateyu 26:56; Luka 22:24-26; Yohane 18:10, 11) Mfundo zonsezi zikusonyezeratu kuti amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino analemba zinthu zolondola zokhudza Yesu.
KODI YESU ANAUKITSIDWADI?
Anthu ambiri amavomereza kuti Yesu anakhalako padziko lapansili ndipo kenako anamwalira. Koma pali anthu ena amene amatsutsa zoti anaukitsidwa. Zimenezi n’zimenenso atumwi ake anachita chifukwa sanakhulupirire atangomva kuti Yesu waukitsidwa. (Luka 24:11) Koma Yesu ataonekera kwa atumwiwo ndiponso kwa ophunzira ake ena, m’pamene anakhulupirira kuti waukitsidwadi. Ndipo nthawi ina Yesu anaonekeranso kwa anthu opitirira 500.—1 Akorinto 15:6.
Atumwiwo anayamba kulengeza molimba mtima kuti Yesu waukitsidwa ngakhale kuti ankadziwa kuti akhoza kumangidwa kapenanso kuphedwa chifukwa chochita zimenezi. Iwo ankalengeza uthenga umenewu ngakhale kwa anthu omwe anapha Yesu. (Machitidwe 4:1-3, 10, 19, 20; 5:27-32) Ophunzira a Yesu sakanalimba mtima kumalengeza kuti waukitsidwa pamene sanaukitsidwe. Ndipotu anthu ambiri pa nthawiyo anakhala Akhristu chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu ndipo ndi mmenenso zikuchitikira masiku ano.
Zimene mabuku a Uthenga Wabwino amanena zokhudza imfa ya Yesu komanso kuukitsidwa kwake ndi zenizeni. Mukamaphunzira nkhanizi mwakhama mudzazindikira kuti zinachitikadi. Kenako mudzayamba kumvetsa chifukwa chake zinthu zimenezi zinachitika. Ndipo nkhani yotsatira ifotokoza chifukwacho.
a Mwachitsanzo, katswiri wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Tacitus, yemwe anabadwa cha m’ma 55 C.E., analemba kuti: “Khristu, [dzina limene Akhristu anatengerako dzina lawo] anazunzidwa kwambiri ndi bwanamkubwa wathu Pontiyo Pilato, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Tiberiyo.” Palinso olemba mbiri ena a m’zaka 100 zoyambirira amene anachitira umboni za Yesu monga Seutonius ndi Josephus, wolemba mbiri wachiyuda. Zitatha zaka 100 zoyambirira, Pliny Wamng’ono yemwe anali bwanamkubwa wa mzinda wa Bituniya, nayenso analemba zokhudza Yesu.
-
-
Nchifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2016 | Na. 2
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO
N’chifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?
‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12
Kodi mungayankhe bwanji ngati munthu atakufunsani kuti, “Kodi mukufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale?” Ambiri akhoza kuyankha kuti inde, koma amaona kuti n’zosatheka. Amanena kuti anthufe tinalengedwa kuti tizikhala ndi moyo kwa kanthawi kochepa n’kufa.
Nanga bwanji atakufunsani kuti, “Kodi mumafuna mutafa?” Ambiri angayankhe kuti ayi, chifukwa anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Ndipo n’zimene Baibulo limanena, kuti Mulungu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Mlaliki 3:11.
Komatu anthufe sitikhala ndi moyo mpaka kalekale. Ndiye n’chiyani chinachitika kuti tizifa? Nanga Mulungu anachitapo chiyani pofuna kuthetsa vutoli? Baibulo limayankha mafunsowa komanso limafotokoza chifukwa chimene Yesu anavutikira mpaka kufa.
N’CHIYANI CHINACHITIKA KUTI ANTHU AZIFA?
Machaputala atatu oyambirira a buku la Genesis amatifotokozera kuti Mulungu analenga Adamu ndi Hava kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale. Anawapatsanso malamulo amene anayenera kutsatira kuti asafe. Koma Baibulo limafotokoza kuti anthuwa analephera kumvera malamulowo ndipo anataya mwayi wopitiriza kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Nkhaniyi inalembedwa mwachidule komanso m’njira yosavuta kumva, moti anthu ena amaganiza kuti ndi yongopeka. Koma mofanana ndi Mauthenga Abwino, buku la Genesis ndi lolondola komanso limafotokoza nkhaniyi momveka bwino.a
Kodi zotsatira za kusamvera kwa Adamu ndi zotani? Baibulo limanena kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Adamu anachimwa ndipo n’chifukwa chake anakhala ndi moyo kwa nthawi yochepa, kenako n’kufa. Ifeyo tinatengera uchimo wa Adamu chifukwa tinachokera kwa iyeyo. Zimenezi zinachititsa kuti tizidwala, tizikalamba ndiponso tizifa. Mfundo imeneyi imagwirizana ndi zimene asayansi anapeza zoti ana amatengera zinthu zina kuchokera kwa makolo awo. Koma kodi Mulungu anachitapo zotani kuti athetse mavuto amenewa?
KODI MULUNGU ANACHITAPO CHIYANI?
Adamu atachimwa anachititsa kuti ana ake onse asakhalenso ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Choncho Mulungu anakonza zoti awombole mtundu wa anthu kuti akhalenso ndi mwayi wodzakhala mpaka muyaya. Kodi anachita zotani kuti zimenezi zitheke?
Lemba la Aroma 6:23 limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” Zimenezi zikutanthauza kuti imfa imabwera chifukwa cha uchimo. Adamu anachimwa ndipo anafa. Zimenezi n’zimenenso zimachitikira anthu ochimwafe chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa. Komabe sikuti anthufe timachita kufuna kuti tibadwe ochimwa. N’chifukwa chake Mulungu mwachikondi chake anatumiza Mwana wake Yesu kuti adzatifere ngati njira yolipirira machimo athu. Ndiye zimenezi zimatheka bwanji?
Imfa ya Yesu inathandiza kuti anthu adzakhale ndi moyo mpaka kalekale
Adamu yemwe anali munthu wangwiro anatipatsira uchimo ndi imfa chifukwa cha kusamvera. Choncho panafunikanso munthu wina wangwiro yemwe akanamvera mpaka imfa yake kuti atiwombole ku imfa. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu, ambiri adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) “Munthu mmodziyu” ndi Yesu. Iye anachoka kumwamba n’kudzakhala munthu wangwirob ndipo kenako anatifera. Pa chifukwa chimenechi anthufe timatha kukhala olungama pamaso pa Mulungu ndipo timayembekezera kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale.
N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAVUTIKA MPAKA KUFA?
N’chifukwa chiyani Yesu anafunika kufa? Kodi Mulungu Wamphamvuyonse sakanatha kungokhazikitsa lamulo lina lomwe likanapatsa mwayi ana a Adamu kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale? Ndi zoona kuti ali ndi mphamvu zoti akanatha kuchita zimenezi. Komabe akanachita zimenezi ndiye kuti akanaphwanya lamulo limene anakhazikitsa yekha lakuti malipiro a uchimo ndi imfa. Lamulo limeneli linali lamphamvu komanso logwirizana ndi chilungamo cha Yehova moti sizikanatheka kungolisintha.—Salimo 37:28.
Mulungu akanati anyalanyaze mfundo zake zachilungamo pa nkhaniyi, anthu akanakayikira ngati angachite chilungamo pa zinthu zina. Mwachitsanzo, akanasankha kuti ana ena a Adamu apitirize kukhala ndi moyo mpaka kalekale, kodi chikanakhala chilungamo? Kodi anawo akanakhulupirira kuti Mulungu azikwaniritsa malonjezo ake? N’zosangalatsa kuti Mulungu sananyalanyaze mfundo zake zachilungamo. Ndipo zimene anachita pofuna kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa zimatitsimikizira kuti nthawi zonse amachita zoyenera.
Mulungu anagwiritsa ntchito nsembe ya Yesu kuti apatse anthu mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Pa Yohane 3:16, Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Imfa ya Yesu imasonyeza kuti Mulungu amachita zinthu zachilungamo nthawi zonse. Koposa zonse, imasonyezanso kuti Mulungu amakonda anthu kwambiri.
Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza kuti Yesu anavutika mpaka kufa mozunzika. Kodi n’chifukwa chiyani anafunika kufa mozunzika choncho? Zimene Yesu anachita pololera kuzunzidwa komanso pokhala wokhulupirika zinathandiza kuti atsutse zimene Mdyerekezi ananena zoti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati atakumana ndi mavuto. (Yobu 2:4, 5) Zimene Satana ananenazi zinkaoneka ngati zoona chifukwa anali atachititsa Adamu, yemwe anali wangwiro kuti achimwe. Koma Yesu, yemwenso anali wangwiro anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ambiri. (1 Akorinto 15:45) Apatu n’zoonekeratu kuti Adamu nayenso akanatha kumvera Mulungu. Choncho Yesu anatisiyira chitsanzo kuti ifenso tizipirira tikamakumana ndi mavuto. (1 Petulo 2:21) Mulungu anapatsa Mwana wake Yesu moyo wosakhoza kufa kumwamba, chifukwa chakuti anakhala wokhulupirika mpaka imfa.
KODI INUYO MUNGAPINDULE BWANJI NDI IMFA YA YESU?
Nkhani yoti Yesu anaphedwa ndi yoona ndipo imfa yake ndi imene inathandiza kuti anthu akhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Kodi inuyo mumafuna mutadzakhala ndi moyo mpaka kalekale? Yesu ananena zimene tiyenera kuchita kuti tidzapeze moyo. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.
Amene amafalitsa magaziniyi akukulimbikitsani kuti mudziwe zambiri za Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, komanso Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wake. A Mboni za Yehova am’dera lanu angakonde kukuthandizani. Mungapezenso mfundo zina zothandiza pawebusaiti yathu ya www.jw.org.
a Onani nkhani yakuti, “The Historical Character of Genesis,” m’buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 922. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Mulungu anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Zimenezi zinachititsa kuti Mariya akhale ndi pakati. Ndipo mzimu woyera unateteza Yesu kuti asatengere uchimo kwa Mariya.—Luka 1:31, 35.
-