Amakusoŵanitu!
1 Nthaŵi ndi nthaŵi, tingamalephere kufika pamsonkhano wampingo umodzi kapena ingapo, tikumaganiza kuti ‘palibe yemwe adzandisoŵa; sangaone nkomwe kuti ineyo palibepo.’ Si zoona zimenezo! Monga chiwalo cha thupi lathuli, aliyense amachita mbali yofunika kuti mpingo uziyenda bwino. (1 Akor. 12:12) Tikamasoŵeka pamsonkhano wa mlungu ndi mlungu timadodometsa mtendere wauzimu wa amene amapezekapo. Ngati inu palibepo, dziŵani kuti—amakusoŵanitu!
2 Mbali Yofunika Imene Mumachita: Paulo analakalaka kusonkhana ndi abale ake. Aroma 1:11, 12, amafotokoza chifukwa chake: “Kuti ndikagaŵire kwa inu mtulo wina wauzimu, . . . kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse aŵiri, chanu ndi changa.” Momwemonso, mwa mayankho athu, nkhani zimene timakamba pamsonkhano, ndiponso mwa kungopezekapo, timalimbikitsa ena kuyendabe mokhulupirika.—1 Ates. 5:11.
3 Kodi simumayembekezera mwachidwi kukaona ena pamisonkhano yampingo? Mumatchera khutu iwo akamayankha ndipo mumayamikira mmene amasonyezera chikhulupiriro chawo. Mphatso zawo zauzimu zimathandizira kukulimbikitsani. Ngati iwo sanapezekepo pamsonkhanopo, mumamva kuti pasoŵeka kanthu kena kofunika. Abale anu ndi alongo anu amamvanso choncho ngati inuyo simunapezekepo.
4 Mbali Yofunika Imene Misonkhano Imachita: Panthaŵi ina, Nsanja ya Olonda inafotokoza mmene misonkhano ilili yofunika pakutithandiza kukhalabe amoyo mwauzimu. Inati: “M’dziko lino lodzaza ndi mikangano ndi chisembwere, mpingo Wachikristu ulidi pothaŵirapo pauzimu penipeni . . . , uli phanga la mtendere ndi chikondi. Chotero, khalani wofika pamisonkhano yake yonse wokhazikika.” (w93-CN 8/15 11) Tsiku lililonse, timakumana ndi zothetsa nzeru zomwe zimatilemetsa mwauzimu. Ngati sitisamala, tingamire m’nkhaŵa zathu moti tingaiŵale zinthu zofunika zauzimu. Tonsefe timadalira ena kuti atilimbikitse kuti tikhalebe ogwirizana ndi achangu mu utumiki wa Mulungu.—Aheb. 10:24, 25.
5 Kupezeka pamisonkhano nkofunika. Matenda kapena zina zogwa mwadzidzidzi zingatilepheretse nthaŵi zina. Komabe, tiyeni tizitsimikiza nthaŵi zonse kuti azitiŵerengera pamasonkhano a anthu otamanda Yehova pamodzi!—Sal. 26:12.