Misonkhano Yautumiki ya December
Mlungu Woyambira December 1
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Lankhulani za Yehova Masiku Onse.” Mafunso ndi mayankho. Pokamba za m’ndime 4, phatikizanipo mawu ochokera mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 16, ndime 14-16.
Mph. 20: “Baibulo Nlimene Mulungu Amatsogozera Anthu Onse.” Mkulu akambe nkhaniyi nafotokoze zifukwa zake aliyense ayenera kusonkhezereka kuphunzira Baibulo. (Onani brosha lakuti Buku la Anthu Onse, masamba 30, 32.) Funsani mwachidule ofalitsa aŵiri mmene akonzekerera kugwiritsira ntchito maulaliki amene aperekedwa m’ndime 3, 5, ndi 7. Sonyezani umodzi monga pakufika koyamba ndipo winawo paulendo wobwereza.
Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 8
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 20: “Nkuululiranji Choipa?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1997, masamba 26-30.
Mph. 15: “Amakusoŵanitu!” Mkulu akambitsirane ndi omvetsera. Tchulani maavareji a amene amapezeka pamisonkhano yampingo. Pemphani ena kuti asimbe zifukwa zake amatsitsimulidwa mwa kukhala pamodzi pamisonkhano.
Nyimbo Na. 172 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 15
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Yerekezerani njira zina za mmene tingayankhire mochenjera moni wa holide yakudziko. Fotokozani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda pa December 25 ndi January 1.
Mph. 10: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 25: “Tiyenera Kukhala Aphunzitsi, Osati Alaliki Chabe.” Mafunso ndi mayankho. Pokamba za m’ndime 11, ŵerengani Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 15, ndime 11.
Nyimbo Na. 174 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 22
Mph. 8: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 17: “Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Pendani njira zimene zidzathandiza onse kupindula nayo sukuluyo chaka chikudzacho. Alimbikitseni kuti azitsatira “Ndandanda Yowonjezera ya Kuŵerenga Baibulo” yatsopano mlungu uliwonse.
Mph. 20: Lalikirani Uthenga Wabwino Kulikonse. Kukambitsirana ndi omvetsera m’buku lakuti Uminisitala Wathu, masamba 92-7, mukumafunsa mafunso awa: (1) Nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito mabuku athu pofalitsa uthenga wa Ufumu kumapangitsa anthu kuumva? Nchifukwa ninji tiyenera kumagaŵira mabuku pampata uliwonse? (2) Nchifukwa ninji tiyenera kumakhala maso kuti tizitha kuchitira umboni mwamwaŵi? Kodi njira zina zochitira umboni mwamwaŵi nziti? (Pemphani ena kuti asimbe zimene anakumana nazo pochitira umboni mwamwaŵi.) (3) Kodi nchifukwa ninji mpingo uyenera kulimbikira kufola gawo lake? Ngati pali gawo lalikulu, kodi ubwino wake ngwotani woti munthu akhale ndi gawo lakelake? (4) Kodi timapindula motani mwa kuchitira umboni tili kagulu? Kodi tingalinganize bwanji ntchito yathu yochitira umboni kuti titsimikize kuti tikugwiritsira ntchito bwino nthaŵi yathu?
Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 29
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Akumbutseni onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda. Ngati mpingo wanu udzasintha nthaŵi yamisonkhano m’chaka chatsopano, alimbikitseni bwinobwino onse kuti azisonkhana ndi mpingo nthaŵi zonse panthaŵi zatsopanozo.
Mph. 15: Pendani mabuku ogaŵira m’January. Sonyezani mabuku akale ambiri omwe mpingo uli nawo, ndiye tchulani mfundo zosangalatsa zokambitsirana zimene zingathandize pokonzekera ulaliki. Chitaniponso chitsanzo chimodzi. Tichitebe khama kuti tiziyambitsa maphunziro a Baibulo mwina m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji kapena m’buku la Chidziŵitso.
Mph. 20: “Phunziro la Banja Losangalatsa.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu wokhoza bwino, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1997, masamba 26-9.
Nyimbo Na. 215 ndi pemphero lomaliza.