Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 10/15 tsamba 13-18
  • Chitanipo Kanthu Kuti Banja Lanu Likaloŵe m’Dziko Latsopano la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitanipo Kanthu Kuti Banja Lanu Likaloŵe m’Dziko Latsopano la Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwongolera Kulankhulana
  • ‘M’Chilangizo cha Yehova’
  • Phunziro la Banja Limene Limamangirira
  • “Mphindi Yakuseka”
  • Kupezera Banja Lanu Mtsogolo Mwamuyaya
  • Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Gwirani Ntchito Zolimba Kaamba ka Chipulumutso cha Banja Lanu
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mabanja Aakulu Ogwirizana Potumikira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 10/15 tsamba 13-18

Chitanipo Kanthu Kuti Banja Lanu Likaloŵe m’Dziko Latsopano la Mulungu

“Mudzawasunga, Yehova, mudzawatchinjiriza mbadwo uno ku nthaŵi zonse.”​—SALMO 12:7.

1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene mabanja akuchitira pansi pazitsenderezo za masiku otsiriza? (b) Ndimotani mmene mabanja Achikristu angafunire chipulumutso?

“LERO mtima wanga wakondwa zedi!” anadzuma motero mkulu wina Wachikristu wotchedwa John. Kodi nchiyani chinamkondweretsa? “Ana anga aŵiri, mnyamata wanga wazaka 14 ndi msungwana wazaka 12 abatizidwa,” iye akutero. Koma sizokhazo zomkondweretsa. “Ana anganso aŵiri, mnyamata wazaka 17 ndi msungwana wazaka 16 anali apainiya othandiza chaka chatha,” akuwonjezera motero.

2 Mabanja ambiri pakati pathu akukhala ndi zotulukapo zabwino zofananazo pamene akugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Komabe, ena akukhala ndi mavuto. “Tiri ndi ana asanu,” akulemba motero Akristu ena okwatirana, “ndipo kwakhala kovutirapo nthaŵi zonse kuchita nawo. Tatayikiridwa kale ndi mwana mmodzi m’dongosolo ili lakale. Ana athu akuwonekera kukhala chandamale chachikulu cha Satana pakali pano.” Palinso okwatirana amene akukumana ndi mavuto aakulu a muukwati, nthaŵi zina ochititsa kulekana kapena kusudzulana. Komabe, mabanja amene amakulitsa mikhalidwe Yachikristu akhoza kudzapulumuka “chisautso chachikulu” ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu likudzalo. (Mateyu 24:21; 2 Petro 3:13) Chotero, kodi mungachitenji kuti banja lanu lisungike kaamba ka chipulumutso?

Kuwongolera Kulankhulana

3, 4. (a) Kodi kulankhulana nkofunika motani m’moyo wabanja, ndipo nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri pamabuka mavuto okhudza kulankhulana? (b) Kodi nchifukwa ninji amuna ayenera kuyesetsa kukhala omvetsera abwino?

3 Kulankhulana kwabwino ndiko mwazi wamoyo wa banja logwirizana; pamene kusoŵeka, kukangana ndi kupsinjika zimakula. “Zolingalira zizimidwa popanda upo,” ikutero Miyambo 15:22. Mokondweretsa, mkazi wina amene ndiphungu waukwati anati: “Dandaulo lofala kwambiri limene ndimamva kwa akazi amene ndimapatsa uphungu nlakuti ‘Samalankhula nane,’ ndi kuti ‘Samandimvetsera.’ Ndipo pamene ndiyesa kukambitsirana za dandauloli ndi amuna awo, samandimvetsera ndi inenso.”

4 Kodi nchiyani chimasoŵetsa kulankhulana? Choyamba, amuna ndi akazi amasiyana, ndipo kaŵirikaŵiri amakhala ndi njira zolankhulirana zosiyanasiyana. Nkhani ina inanena kuti mwamuna “amakhala wolunjika ndi wofuna zinthu kuchitika” m’kukambitsirana kwake, pamene kulikwakuti “chimene [mkazi] amafuna koposa china chirichonse ndicho kukhala mvetseri wabwino.” Ngati zimenezi zipereka vuto muukwati wanu, limbikirani pakuwongolera zinthu. Mwamuna Wachikristu angafunikire kulimbikira pakukhala mvetseri wabwinopo. “Munthu aliyense,” akutero Yakobo, “akhale wotchera khutu, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Phunzirani kupeŵa kulankhula molamulira, mopatsa uphungu, kapena mophunzitsa pamene mkazi wanu angofunikira “chifundo” basi. (1 Petro 3:8) “Wopanda chikamwakamwa apambana kudziŵa,” imatero Miyambo 17:27.

5. Kodi ndinjira zina ziti zimene amuna angawongoleremo kumveketsa malingaliro awo ndi kudzimva kwawo?

5 Kumbali ina, pali “mphindi yakulankhula,” ndipo mwina mufunikira kudziŵa kumveketsa bwinopo malingaliro anu ndi kumva kwa mtima. (Mlaliki 3:7) Mwachitsanzo, kodi ndinu wowoloŵa manja mwakuthokoza zochita za mkazi wanu? (Miyambo 31:28) Kodi mumasonyeza kukhala woyamikira ntchito yaikulu imene amachita yokuthandizirani pakusamalira banja? (Yerekezerani ndi Akolose 3:15.) Kapena mwina mufunikira kuwongokera pakukamba “timawu tokoma tachikondi.” (Nyimbo ya Solomo 1:2) Kuchita zimenezo kungawonekere kukhala kosazoloŵereka kwa inu poyamba, koma kungakhale kothandiza kwambiri kuchititsa mkazi wanu kumva wotetezereka m’chikondi chanu pa iye.

6. Kodi nchiyani chimene akazi angachite kuwongolera kulankhulana m’banja?

6 Bwanji za akazi Achikristu? Mkazi wina anagwidwa mawu akunena kuti mwamuna wake amadziŵa kuti iye amamyamikira, chotero sikofunikira kwenikweni kuti auze mwamuna wake zimenezo. Komabe, amuna nawonso amachita bwinopo akamayamikiridwa, kuthokozedwa, ndi kutamandidwa. (Miyambo 12:8) Kodi mufunikira kudziŵa kunena bwinopo zimenezi? Kumbali ina, mwinamwake mufunikira kupereka chisamaliro chokulirapo pakumvetsera kwanu. Ngati mwamuna wanu akupeza kukhala kovuta kukambitsirana momasuka mavuto ake, mantha ake, kapena nkhaŵa zake, kodi mwadziŵa mmene mungamsonkhezerere kutero, mokoma mtima ndi mwaluso?

7. Kodi nchiyani chingabutse mikangano muukwati, ndipo kungatchinjirizidwe motani?

7 Ndithudi, ngakhale okwatirana amene amamvana bwino nthaŵi zina angaleke kulankhulana. Kumva kwa mtima kungaphimbe kulingalira, kapena kukambitsirana kwabata kungasinthe ndi kukhala mkangano waukulu. (Miyambo 15:1) “Timakhumudwa tonse pazinthu zambiri”; komabe, kulongolola sikumatanthauza kutha kwa ukwati. (Yakobo 3:2) Koma “chiwawa, ndi mwano” nzosayenera ndipo zimawononga unansi uliwonse. (Aefeso 4:31) Khalani wofulumira kubwezeretsa mtendere pamene mwakhadzulirana mawu opweteka. (Mateyu 5:23, 24) Kaŵirikaŵiri, kukangana kungatchinjiziridwe ngati nonse aŵirinu mugwiritsira ntchito mawu a Paulo pa Aefeso 4:26 akuti: “Dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” Inde, kambiranani mavuto akali aang’ono ndi olamulirika; musayembekezere kufikira pamene mkwiyo uswa mitima. Kuthera mphindi zingapo tsiku lirilonse mukukambitsirana nkhani zodetsa nkhaŵa kungathandize kwambiri kulimbikitsa kulankhulana ndi kuchinjiriza kumvana molakwa.

‘M’Chilangizo cha Yehova’

8. Kodi nchifukwa ninji achichepere ena angapambuke pachowonadi?

8 Kukuwonekera kuti makolo ena ali okhutiritsidwa kulola ana awo kumangokula popanda chitsogozo chawo kwenikweni. Anawo amapezeka pamisonkhano ndipo amatuluka muutumiki wakumunda, koma kaŵirikaŵiri samakhala atakulitsa unansi wa iwo eni ndi Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi “zilakolako za thupi ndi zilakolako za maso” zikhoza kupambutsa ambiri a achichepere oterowo pachowonadi. (1 Yohane 2:16) Kukakhala kochititsa chisoni chotani nanga kwa makolo kupulumuka Armagedo koma chifukwa cha kunyalanyaza kwakaleko ana awo nkutsala nawonongeka!

9, 10. (a) Kodi kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW],” kumaphatikizapo chiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulola ana kufotokoza malingaliro awo momasuka?

9 Chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” (Aefeso 6:4) Kuti muchite zimenezo, inuyo muyenera kukhala wozoloŵerana bwino lomwe ndi miyezo ya Yehova. Muyenera kupereka chitsanzo choyenera pazinthu zonga kusankha zosangulutsa, phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano, ndi kutuluka muutumiki wakumunda. Mawu a Paulo amatanthauzanso kuti kholo liyenera kukhala (1) woyang’anira watcheru wa ana ake ndi (2) wochirikiza kulankhulana nawo kwabwino. Ndikokha mwakutero pamene mungadziŵe mmene afunikira “chilangizo.”

10 Chiri chibadwa kwa ana amene akusinkhuka kufuna ufulu winawake. Komabe, muyenera kukhala maso ndi zizindikiro zodziŵikiratu za chisonkhezero chadziko m’mawu awo, kalingaliridwe, kavalidwe, kapesedwe, ndi mabwenzi amene amasankha. Atate wanzeru anati m’mawu a pa Miyambo 23:26: “Mwananga, undipatse mtima wako.” Kodi ana anu amadzimva omasuka kukambitsirana nanu malingaliro awo ndi mnene amamverera mumtima? Pamene ana sakuwopa kudzudzulidwa kwapanthaŵi yomweyo, angakhale ofuna kwambiri kuvumbula mmene akumvereradi pankhani monga ngati zochita zina zapasukulu, kupita kocheza, maphunziro apamwamba, kapena chowonadi cha Baibulo chenichenicho.

11, 12. (a) Kodi nthaŵi zachakudya zingagwiritsiridwe ntchito motani kuchirikiza kulankhulana kwa banja? (b) Kodi chingakhale chotulukapo nchiyani ngati kholo lilimbikira pakuchirikiza kulankhulana ndi ana ake?

11 M’maiko ambiri chiri chizoloŵezi cha mabanja kudyera pamodzi. Chotero nthaŵi yakudyera pamodzi ingakhale nthaŵi yabwino kwa ziŵalo zonse za banja kukambitsirana nkhani zomangirira. Kaŵirikaŵiri nthaŵi ya chakudya cha banja imatengedwa ndi TV ndi zocheukitsa zina. Komabe kwa maola ochuluka, ana anu anali atagwidwa muukapolo kusukulu, titero kunena kwake, ndi kukhala pamodzi ndi anthu amalingaliro audziko. Nthaŵi zachakudya zimakhala zabwino kumalankhulana ndi ana anu. “Timagwiritsira ntchito nthaŵi yachakudya kukamba za zinthu zimene zachitika patsikulo,” linatero kholo lina. Chikhalirechobe, nthaŵi zachakudya sizimafunikira kukhala nthaŵi zoperekera zilango zochititsa manyazi kapena nthaŵi zofunsa mafunso opezera zifukwa. Chititsani nthaŵiyo kukhala yampumulo ndi yosangalatsa!

12 Kuchitisa ana kulankhula kwa inu momasuka kumakhala chitokoso ndipo kungafunikire kuleza mtima kwakukulu. Komabe, mkupita kwa nthaŵi, mungawone zotulukapo zosangalatsa. “Mwana wathu wamwamuna wa zaka 14 zakubadwa wakhala wochita tondovi ndi mphwayi,” akukumbukira motero mayi wina wodera nkhaŵa. “Mwa mapemphero athu ndi kulimbikira, iye akuyamba kumasuka ndi kulankhula!”

Phunziro la Banja Limene Limamangirira

13. Kodi nchifukwa ninji kuyambirira kuphunzitsa ana nkofunika kwambiri, ndipo kodi kungachitidwe motani?

13 “Chilangizo” chimenecho chimaphatikizaponso kuphunzitsa kwenikweni kwa Mawu a Mulungu. Monga zinaliri ndi Timoteo, kuphunzitsa koteroko kuyenera kuyambira ‘paukhanda.’ (2 Timoteo 3:15) Kuphunzitsa koyambidwa paubwana kumalimbitsa ana kaamba ka ziyeso za chikhulupiriro zimene zingadze m’zaka za sukulu​—kukondwerera tsiku lakubadwa, mapwando aufuko, kapena maholide achipembedzo. Popanda kukonzekera kaamba ka ziyeso zimenezi, chikhulupiriro cha mwana chingaswedwe. Chifukwa chake tengani mwaŵi wa zida zimene Watch Tower Society yalinganiza kaamba ka ana aang’ono, zonga ngati mabukhu akuti Kumam’mvetsera Mphunzitsi Wamkulu’yo ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a

14. Kodi ndimotani mmene phunziro labanja lingakhalire lokhazikika, ndipo kodi mwachitaponji kuti mukhale ndi phunziro labanja lokhazikika?

14 Mbali ina yofunikira chisamaliro ndiyo phunziro labanja, limene mosavuta likhoza kukhala lodumphadumpha kapena kukhala mchitidwe wosasangalatsa umene umakhala wankhokera ponse paŵiri kwa makolo ndi ana omwe. Kodi mungawongolere motani zinthu? Choyamba, muyenera ‘kuwombola nthaŵi’ kaamba ka phunziro, kusalola kuti itengedwe ndi TV kapena zododometsa zina. (Aefeso 5:15-17) “Kunali kotivuta kupangitsa phunziro lathu labanja kukhala lokhazikika,” ukuvomereza motero mutu wina wa banja. “Tinayesa nthaŵi zosiyanasiyana mpaka pomalizira tinapeza nthaŵi yamadzulo yoyenerera. Tsopano phunziro lathu labanja nlokhazikika.”

15. Kodi ndimotani mmene mungagwirizanitsire phunziro labanja ndi zosoŵa za banja lanu?

15 Chachiŵiri, pendani zosoŵa zakutizakuti za banja lanu. Mabanja ambiri amasangalala kukonzekerera pamodzi phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu. Komabe, nthaŵi ndi nthaŵi, banja lanu lingakhale ndi nkhani zachindunji zimene zifunikira kukambitsirana, kuphatikizapo mavuto opezeka pasukulu. Bukhulo Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza ndi nkhani zina za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zikhoza kukwaniritsa chosoŵachi. “Ngati tiwona maganizo ena mwa ana athu aamuna ofunikira kuwongoleredwa,” akutero atate wina, “timasumika maganizo pa mutu umene umakhudza nkhaniyo m’bukhu la Mafunso Achichepere Akufunsa.” Mkazi wake akuwonjezera kuti: “Timayesa kukhala osinthasintha. Ngati takonzekera kanthu kena kokambitsirana paphunziro, komano pabuka kanthu kena kosiyana kofunikira kukambitsirana, pamenepo timasintha malinga ndi chosoŵacho.”

16. (a) Kodi mungatsimikizire motani kuti ana anu akumvetsetsa zimene amaphunzira? (b) Kodi nchiyani nthaŵi zonse chiyenera kupeŵedwa pochititsa phunziro labanja?

16 Kodi mungatsimikizire motani kuti ana anu akumvetsetsadi zimene amaphunzira? Mphunzitsi Wamkuluyo, Yesu, anafunsa mafunso oitanira lingaliro, onga ngati, “Kodi uganiza bwanji?” (Mateyu 17:25) Mwakuchita zofananazo, yesani kupeza chimene kwenikweni ana anu akulingalira. Limbikitsani mwana aliyense kuyankha m’mawu akeake. Ndithudi, ngati muchitapo kanthu mopambanitsa mwakusonyeza mkwiyo kapena kudabwa pazimene iwo anena mowona mtima, adzakayikakayika kukhaka omasuka kwa inu kachiŵirinso. Chotero khazikani mtima. Peŵani kuchititsa phunziro labanja kukhala nthaŵi yokwapulira ana. Liyenera kukhala lokondweretsa, lomangirira. “Ngati ndiwona kuti mmodzi wa ana anga ali ndi vuto,” akutero atate wina, “ndimachita nalo panthaŵi ina.” “Pamene mwana mumlanga payekha,” akuwonjezera motero amayi wina, “mwanayo samachititsidwa manyazi kwambiri ndipo sikumakhala kovuta kwambiri kwa iye kulankhula momasuka koposa ngati apatsidwa uphungu paphunziro labanja.”

17. Kodi nchiyani chingachitidwe kupangitsa phunziro labanja kukhala lokondweretsa, ndipo kodi nziti zimene zagwira ntchito m’banja lanu?

17 Kuchititsa ana kuyankha paphunziro labanja kungakhale chitokoso, makamaka pamene mukuchita ndi ana a misinkhu yosiyanasiyana. Ana aang’ono angakhale oseŵera, osakhazikika, kapena osatha kupereka chisamaliro kwanthaŵi yotalikirapo. Kodi mungachitenji? Yesani kusungitsa mkhalidwe wa phunzirolo kukhala wosangulutsa. Ngati ana anu satha kupereka chisamaliro kwanthaŵi yaitali, yesani kukhala ndi magawo aafupi koma apafupipafupi. Kumathandizanso ngati mukhala wosangalala. “Iye wakuweruza, aweruze . . . ndi kukondwa mtima.” (Aroma 12:8) Phatikizanimo aliyense. Ana ocheperapo angakhoze kukambapo pazithunzithunzi kapena kuyankha mafunso okhweka. Ana osinkhukirapo angauzidwe kufufuza zowonjezereka kapena kugwiritsira ntchito zimene zikukambitsiridwa.

18. Kodi ndimotani mmene makolo angakhomerezere Mawu a Mulungu panthaŵi iriyonse, ndipo ndi chotulukapo chotani?

18 Komabe, kuphunzitsa kwanu kwauzimu kusakhale kokha kwa ola limodzi limenelo pamlungu. Khomerezani Mawu a Mulungu mwa ana anu panthaŵi iriyonse. (Deuteronomo 6:7) Pezani nthaŵi yakuwamvetsera. Alangizeni ndi kuwatonthoza pamene kuli kofunikira. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:11.) Khalani wokoma mtima ndi wachifundo. (Salmo 103:13; Malaki 3:17) Mukatero, mudzapeza ‘chisangalalo’ mwa ana anu ndipo mudzachirikiza chipulumutso chawo kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu.​—Miyambo 29:17.

“Mphindi Yakuseka”

19, 20. (a) Kodi kuseŵera kosangulutsa kumachita mbali yanji m’moyo wa banja? (b) Kodi ndinjira zina ziti zimene makolo angalinganizire zosangulutsa kaamba ka banja lawo?

19 Pali “mphindi yakuseka . . . , mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:4) Liwu Lachihebri lotembenuzidwa “kuseka” lingatembenuzidwe kutanthauzanso “kukondwera,” “kuseŵera,” “kuchita maseŵera,” kapena ngakhale “kukhala ndi nthaŵi yabwino.” (2 Samueli 6:21; Yobu 41:5; Oweruza 16:25; Eksodo 32:6; Genesis 26:8) Kuseŵera kungakhale kothandiza, ndipo nkofunika kwa ana aang’ono ndi okulirapo. M’nthaŵi za m’Baibulo makolo analinganiza maseŵera ndi zosangulutsa zina kaamba ka mabanja awo. (Yerekezerani ndi Luka 15:25.) Kodi mumachita zofananazo?

20 “Timatenga mwaŵi wa kukhalapo kwa mapaki a anthu onse,” akutero mwamuna Wachikristu. “Timaitanira ena a abale achichepere ndi kuseŵera nawo mpira ndi kuchita pikiniki. Amakhala ndi nthaŵi yabwino ndi kusangalala ndi mayanjano abwino kwambiri.” Kholo lina likuwonjezera kuti: “Timalinganiza zinthu zochitira pamodzi ndi anyamata athu. Timakasambira, kuseŵera mpira, kupita patchuthi. Koma timaika zosangulutsa m’malo ake oyenera. Ndimagogomezera kufunika kwa kukhala achikatikati.” Zosangulutsa zabwino, zonga ngati timapwando toyenerera kapena kukachezera malo osungirako zinyama kapema mamuziyamu, kungathandize kwambiri kuchinjiriza mwana kusakopeka ndi zosangulutsa zadziko.

21. Kodi ndimotani mmene makolo angatchinjirizire ana awo kumva kukhala omanidwa kanthu kena chifukwa cha kusakondwerera maholide akudziko?

21 Nkofunikanso kuti ana anu asadziwone kukhala omanidwa kanthu chifukwa chakuti samakondwerera masiku akubadwa kapena maholide achikunja. Ndi malinganizidwe anu, iwo akhoza kuyang’ana kutsogolo kunthaŵi zosangalatsa zambiri mkati mwa chaka. Eya, kholo labwino silimafunikira kuchita kutenga holide monga chodzikhululukira chosonyezera chikondi mwanjira ya zinthu zakuthupi. Mofanana ndi Atate wake wakumwamba, ilo ‘limadziŵa kupereka mphatso zabwino kwa ana ake’​—mochokera mumtima.​—Mateyu 7:11.

Kupezera Banja Lanu Mtsogolo Mwamuyaya

22, 23. (a) Pamene chisautso chachikulu chikuyandikira, kodi mabanja owopa Mulungu ayenera kukhalanso otsimikiziridwa za chiyani? (b) Kodi mabanja angachitepo kanthu motani kuti akapulumuke kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu?

22 Wamasalmo anapemphera kuti: “Mudzawasunga, Yehova, mudzawachinjirizira mbadwo uno ku nthaŵi zonse.” (Salmo 12:7) Chitsenderezo chochokera kwa Satana nchotsimikizirika kuwonjezereka​—makamaka pamabanja a Mboni za Yehova. Komabe, kuli kothekera kuima nji motsutsana ndi chiukiro chowonjezereka chimenechi. Ndi chithandizo cha Yehova ndi kutsimikizira mtima kwamphamvu ndi kugwira ntchito zolimba kwa amuna, akazi, ndi ana, mabanja​—kuphatikizapo banja lanu​—akhoza kukhala ndi chiyembekezo cha kupulumutsidwa amoyo pachisautso chachikulu.

23 Amuna ndi akazi, chititsani mtendere ndi umodzi muukwati wanu mwakukwaniritsa mbali zanu zopatsidwa ndi Mulungu. Makolo, pitirizani kupereka chitsanzo chabwino kwa ana anu, mukumaiwombola nthaŵi kuwapatsa chiphunzitso ndi chilangizo zimene akuzifunikira koposa. Lankhulani nawo. Amvetsereni. Miyoyo yawo iri paupandu! Ananu, mvetserani ndi kumvera makolo anu. Ndi chithandizo cha Yehova mukhoza kupambana ndi kudzipezera mtsogolo mwamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu likudzalo.

[Mawu a M’munsi]

a Makaseti ake aliponso m’zinenero zina.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi ndimotani mmene amuna ndi akazi angawongolere kulankhulana kwawo?

◻ Kodi ndimotani mmene makolo angalerere ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW]”? (Aefeso 6:4)

◻ Kodi ndinjira zina ziti zochititsira phunziro labanja kukhala lomangirira ndi lokondweretsa kwambiri?

◻ Kodi makolo angachitenji m’kulinganiza maseŵera ndi zosangulutsa kaamba ka mabanja awo?

[Bokosi patsamba 16]

Nyimbo​—Chisonkhezero Champhamvu

Wolemba bukhu lonena za kulera ana anati: “Ngati ndikanati ndiime patsogolo pa omvetsera . . . ndi kuthokoza madzoma a kukhuta moŵa, kuledzera ndi cocaine, chamba, kapena mankhwala alionse opotoza maganizo, akandiyang’ana ndi kudabwa kwakukulu. . . . [Komabe] makolo kaŵirikaŵiri amapatsa ana awo ndalama zogulira malekodi kapena makaseti anyimbo zimene zimachirikiza zinthuzo poyera.” (Raising Positive Kids in a Negative World, lolembedwa ndi Zig Ziglar) Mwachitsanzo, mu United States, mawu a nyimbo zothokoza chisembwere ali pamilomo ya achichepere ambiri. Kodi mumathandiza ana anu kusankha nyimbo kuti apeŵe mbuna zauchiŵanda zoterozo?

[Chithunzi patsamba 15]

Nthaŵi zachakudya zingakhale zosangalatsa zopititsa patsogolo umodzi wa banja ndi kulankhulana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena