Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/15 tsamba 4-7
  • “Mulungu wa Mtendere” Amawasamala Amene Akuzunzika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mulungu wa Mtendere” Amawasamala Amene Akuzunzika
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amakusamalani
  • Mmene Mulungu Athandizira Ozunzika
  • Posachedwapa​—Dziko Lopanda Mazunzo!
  • Chitonthozo kwa Ovutika
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Amene Akuzunzika Adzakhaladi ndi Mtendere?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yehova Amalanditsa Wovutika
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Chotandizira Kupirira Pobvutika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/15 tsamba 4-7

“Mulungu wa Mtendere” Amawasamala Amene Akuzunzika

BAIBULO limafotokoza bwino kuti ngakhale Davide wakale anazunzikapo. Zaka zambiri iye anali wothaŵathaŵa popeza mfumu yoipa ndi yaliuma inamlondalonda kufuna kumupha. Panthaŵi ya nsautso imeneyo, Davide anabisala mtalimtali. Koma anachitanso zina. Anapemphera kwa Yehova mwaphamphu za nsautso yake. “Ndifuula nalo liwu langa kwa Yehova,” ndi mmene analembera za mavuto ake pambuyo pake. “Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake.”​—Salmo 142:1, 2.

Lero, ena angamseke Davide chifukwa cha kudalira kwake Mulungu. Anganene kuti pemphero limangokhazika mtima pansi basi ndi kuti kunena zoona, limangotayitsa nthaŵi. Komabe, Davide sanalakwe kudalira Mulungu, pakuti anagonjetsa adani ake m’kupita kwa nthaŵi. Pokumbukira zimene zinamchitikira, Davide analemba kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m’masautso ake onse.” (Salmo 34:6) Mulungu woona amene Davide anatembenukirako, kwina amatchedwa “Mulungu wa mtendere.” (Afilipi 4:9; Ahebri 13:20) Kodi adzachotsapo mazunzo ndi kubweretsa mpumulo, kutipatsa mtendere?

Yehova Amakusamalani

Yehova sachita mphwayi ndi masauko a anthu ake. (Salmo 34:15) Samangosamala chabe za zosoŵa za atumiki ake monga gulu komanso za munthu yense payekha amene amuopa iye. Popatulira kachisi m’Yerusalemu wakale, Solomo anachonderera Yehova kuti amve ‘pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisrayeli, akadziŵa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake.’ (2 Mbiri 6:29) Monga anatchulira Solomo, munthu yense ali ndi mazunzo ake oti awapirire. Munthu wina angakhale ndi matenda. Wina, nsautso ya mtima. Ena angazunzike chifukwa cha imfa ya wokondedwa wawo. Ulova, mavuto a zachuma, ndi a m’banja alinso mazunzo ofala m’nthaŵi zino zovuta.

Talingalirani kamphindi za ‘chinthenda chanu, ndi chisoni chanu.’ Mwina nthaŵi zina mwamva monga anamvera wamasalmo Davide, amene analemba kuti: “Ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe: ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.” Komabe, dziŵani kuti Mulungu amasamala za mkhalidwe wanu, pakuti pambuyo pake m’salmo limodzimodzilo, Davide analemba kuti: “Yehova amvera aumphaŵi, ndipo sapeputsa am’ndende ake.”​—Salmo 69:20, 33.

Kufutukula lingaliro la mawu a Davide, tikutsimikiza kuti Mlengi wa anthu amamva mapemphero a amene ali m’ndende, kunena mophiphiritsa, chifukwa cha mazunzo awo. Makamaka, amachitapo kanthu pa nsautso yawo. Tapendani mawu otsatira omwe akusonyeza chifundo cha Yehova kwa ozunzika.

“Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo; ndi mkwiyo wanga udzayaka.”​—Eksodo 22:22-24.

“Kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima?”​—Luka 18:7.

“Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzaombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​—Salmo 72:12-14.

“Iye wokhudza inu [anthu a Mulungu padziko lapansi], akhudza mwana wa m’diso lake [“langa,” NW].”​—Zekariya 2:8.

Zitsanzo zingapo zimenezi zikusonyeza nkhaŵa yaikulu imene Mlengi wathu ali nayo paubwino wa anthu ake. Chotero, tili ndi chifukwa chabwino chotsatirira chilangizo cha mtumwi Petro chakuti: ‘Tayani pa Iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.’ (1 Petro 5:7) Koma kodi Mulungu adzatithandiza bwanji panthaŵi ya kuzunzika?

Mmene Mulungu Athandizira Ozunzika

Monga taonera, pamene Davide anazunzika, anapemphera kwa Mulungu mwaphamphu kuti amtsogoze. Panthaŵi imodzimodzi, anayamba ndiye kuchitapo kanthu kuti apeŵe mkhalidwewo, mwa kugwiritsira ntchito luntha kuthaŵa omlondalonda. Choncho, kudalira kwake Yehova pamodzi ndi khama lake zinamthandiza Davide kupirira masauko ake. Kodi tikuphunziraponji pamenepa?

Pamene tili m’mazunzo, sikulakwa ayi ngati tingayambe patokha kuchitako zina kuti tithetse vutolo. Mwachitsanzo, ngati Mkristu amchotsa ntchito, kodi sadzachita khama kuti apeze ntchito ina? Kapena ngati akudwala, kodi sadzapita kuchipatala? Inde, ngakhale Yesu, amene anali ndi mphamvu yochiritsa nthenda yamtundu uliwonse, anavomereza kuti ‘odwala afuna sing’anga.’ (Mateyu 9:12, yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:23.) Zoona, mavuto ena sangachotsedwe; angofuna kuwapirira basi. Ngakhale ndi tero, Mkristu woona samakondwa ndi mavuto ake monga mmene ena samakondwera. (Yerekezerani ndi 1 Mafumu 18:28.) M’malo mwake, amachita zonse zotheka kuti athetse mazunzo ake.

Komanso, zili bwino kutulira Yehova nkhaniyo m’pemphero. Chifukwa? Choyamba, mwa kudalira Mlengi wathu, timathandizidwa ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:10, NW) Mwachitsanzo, pofuna ntchito, kudalira Mulungu mwapemphero kudzatithandiza kusavomera ntchito yoombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Tidzapeŵanso ‘kusochera ndi kutaya chikhulupiriro’ chifukwa cha chikondi cha pandalama. (1 Timoteo 6:10) Ndithudi, pogamula zinthu zazikulu​—zokhudza ntchito kapena mbali iliyonse ya moyo​—tiyenera kutsatira chilangizo cha Davide chakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

Pemphero limatithandizanso kukhala ndi maganizo okhazikika, kuti kuzunzika kwathu kusatilake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Zotsatira zake? “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, mtendere, mtendere wa Mulungu. Mtenderewo “upambana chidziŵitso chonse,” choncho ungatikhazikitse pamene tathodwa ndi zovuta za mtima. ‘Udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu,’ kutithandiza kupeŵa kuchita zinthu mwansontho ndi mopanda nzeru, zimene zingawonjezere kuzunzika kwathu.​—Mlaliki 7:7.

Pemphero lingachitenso zambiri. Lingalamulire mmene mkhalidwewo udzakhalira. Talingalirani chitsanzo cha m’Baibulo. Pamene mtumwi Paulo anali m’ndende ku Roma, analimbikitsa Akristu anzake kumpempherera. Chifukwa? “Ndikudandaulirani koposa kuchita ichi,” anawalembera, “kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.” (Ahebri 13:19) Paulo anadziŵa kuti mapemphero akhama a okhulupirira anzake akanalamulira nthaŵi imene akanamasulidwa.​—Filemoni 22.

Kodi pemphero lingasinthe zotsatira zake za kuzunzika kwanu? Mwinamwake. Komabe, tiyenera kukumbukira kuti si nthaŵi zonse pamene Yehova amayankha mapemphero athu mwanjira imene timafuna. Mwachitsanzo, Paulo anapemphera mobwerezabwereza za “munga m’thupi” mwake​—kapena anali matenda a maso. M’malo mochotsa vutolo, Mulungu anauza Paulo kuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa [“ikukhala yangwiro,” NW] m’ufooko.”​—2 Akorinto 12:7-9.

Chotero mavuto athu nthaŵi zina samachotsedwa. M’malo mwake, timakhala ndi mwaŵi wosonyeza chidaliro chathu mwa Mlengi wathu. (Machitidwe 14:22) Ndiponso, ndife otsimikiza kuti ngakhale ngati Yehova sachotsa chotizunzacho, “adzaikanso populumukirapo, kuti [ti]dzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Inde, chifukwa chake nchomveka chimene Yehova amatchedwera “Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Amatipatsa zimene tifunikira kuti tipirire mwamtendere ndithu.

Posachedwapa​—Dziko Lopanda Mazunzo!

Mlengi akulonjeza kuti kupyolera mwa Ufumu wake, iye posachedwapa adzachotsapo zonse zimene zimazunza munthu. Kodi zimenezi adzazichita motani? Mwa kuchotsapo Satana Mdyerekezi, wosonkhezera mazunzo wamkulu ndi mdani wamkulu wa mtendere, amene Baibulo limamutcha “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Koma posachedwa ulamuliro wake pa anthu udzatha. Kuwonongedwa kwake kudzatsegulira njira madalitso osaŵerengeka kuti adze kwa oopa Mulungu. Baibulo limalonjeza kuti Yehova “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:1-4.

Kodi mukuganiza kuti dziko lopanda mazunzo nlosatheka? Tazoloŵera kwambiri kukhala m’masauko kwakuti zimavuta kuganiza kuti angachoke. Komatu polenga munthu, Mulungu anafuna kuti munthuyo akhale womasuka pamantha, nkhaŵa, ndi tsoka, ndipo chifuno chake chidzapambana.​—Yesaya 55:10, 11.

Sonia, Fabiana, ndi Ana, otchulidwa m’nkhani yotsegulira, anapeza chiyembekezo chimenechi. Sonia, amene ana ake aŵiri anafa ndi AIDS, anapeza mtendere wochuluka m’chiyembekezo chimene Baibulo limapereka​—kuuka kwa olungama ndi osalungama. (Machitidwe 24:15) “Ndikudziŵa chinthu chimodzi,” akutero, “chiyembekezo chathu chiposa zoŵaŵa zilizonse.”

Pamene Ana anali kukhala m’nyumba ya ana amasiye, mmodzi wa Mboni za Yehova anamchezera. “Anandionetsa dzina la Yehova m’Baibulo,” akutero Ana, “ndipo ndinalira ndi chimwemwe. Ndinali kufuna thandizo kwambiri, ndipo ndinaphunzira kuti Mulungu aliko amene amatisamala.” Ana atachoka panyumba ya ana amasiye, analandira phunziro la Baibulo naphunzira zambiri ponena za malonjezo a Yehova. Ndiyeno anapatulira moyo wake kwa Yehova nabatizidwa kusonyeza zimenezo. “Chiyambire nthaŵiyo, ndapitiriza kudalira Yehova mwa pemphero, ndipo chidaliro chakuti adzandithandiza chimanditonthoza.”

Nayenso Fabiana anapeza chitonthozo chochuluka ndi mtendere wa maganizo pamazunzo ake mwa kuphunzira za malonjezo a mtsogolo a Mulungu. “Kuphunzira choonadi m’Baibulo kuli monga kutuluka m’malo amdima wabii ndi kuloŵa m’chipinda chabwino choŵala ngwee.”​—Yerekezerani ndi Salmo 118:5.

Koma kodi ndi motani ndipo ndi liti pamene mtendere weniweni udzakhalapo padziko lonse? Tiyeni tione nkhani zotsatira.

[Bokosi patsamba 6]

Mazunzo Amitundumitundu

▪ Pali ngati gawo limodzi mwa anayi la anthu onse padziko amene ali amphaŵi enieni, ndipo enanso mamiliyoni ali m’mikhalidwe yoipa imene imaika umoyo wawo pangozi.

▪ Ana oposa 200 miliyoni sadya mokwanira.

▪ Chaka chilichonse matenda a kutseguka m’mimba amapha ana osakwanitsa zaka zisanu okwanira ngati mamiliyoni atatu.

▪ Matenda oyambukira anapha anthu ngati 16,500,000 mu 1993 mokha. Popeza kuti maiko ena amafotokoza matenda mosiyanasiyana, chiŵerengero chenicheni chingaposepo kwambiri pamenepa.

▪ Anthu okwanira ngati 500 miliyoni ali ndi nthenda ina yake ya maganizo.

▪ Ziŵerengero za achichepere amene akudzipha zikuwonjezeka mofulumira kwambiri kuposa za amisinkhu ina.

▪ “Njala ndi ulova zakhala miliri padziko,” ikutero magazini yakuti The Unesco Courier. “M’maiko asanu ndi aŵiri olemera koposa padziko muli anthu 35 miliyoni osoŵa ntchito, ndipo ku Brazil kokha kuli antchito 20 miliyoni amene ntchito yawoyo simatanthauza kuti adzakhala ndi chakudya chokwanira.”

[Zithunzi patsamba 7]

Pemphero lingatithandize kusumika maganizo athu pa lonjezo la Mulungu la dziko lopanda mazunzo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena