CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 39-43
Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake
Zedekiya sanamvere zimene Yehova anamuuza zoti akadzipereke yekha kwa mfumu ya Babulo
Ana a Zedekiya anaphedwa iye akuona ndipo kenako anamukolowola maso, anamumanga ndi maunyolo amkuwa n’kukamuika m’ndende ku Babulo mpaka anafera komweko
Ebedi-meleki anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova komanso ankadera nkhawa Yeremiya
Yehova analonjeza kuti adzapulumutsa Ebedi-meleki pamene Yuda azidzawonongedwa
Yeremiya analalikira molimba mtima kwa zaka zambiri Yerusalemu asanawonongedwe
Yehova anateteza Yeremiya pamene mzinda wa Yerusalemu unazunguliridwa ndi adani ndipo anachititsa kuti Ababulo amumasule