CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Chuma Sichipangitsa Munthu Kukhala Wolungama
Zofari ananena kuti Mulungu amalanda chuma anthu oipa ndipo pamenepa ankasonyeza kuti Yobu ayenera kuti anachimwa (Yob 20:5, 10, 15)
Yobu anayankha kuti: ‘N’chifukwa chiyani oipa zimawayendera?’ (Yob 21:7-9)
Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza kuti anthu olungama akhoza kukhala osauka (Lu 9:58)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi munthu wolungama amaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wake n’chiyani, kaya akhale wolemera kapena wosauka?—Lu 12:21; w07 8/1 29 ¶12.