Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 4 tsamba 16-tsamba 17 ndime 2
  • Kaini Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kaini Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Aŵiri a Pachibale Amene Anali ndi Mitima Yosiyana
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mwana Wabwino, ndi Woipa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kupereka Nsembe Zovomerezeka kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 4 tsamba 16-tsamba 17 ndime 2
Kaini wakwiya pamene Abele akupereka nsembe kwa Yehova

MUTU 4

Kaini Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake

Adamu ndi Hava atathamangitsidwa m’munda wa Edeni, anabereka ana ambiri. Mwana wawo woyamba anali Kaini ndipo wachiwiri anali Abele. Kaini anali mlimi koma Abele anali m’busa.

Tsiku lina, Kaini ndi Abele anapereka nsembe kwa Yehova. Kodi ukudziwa kuti nsembe ndi chiyani? Ndi mphatso yapadera. Yehova anasangalala ndi nsembe ya Abele koma sanasangalale ndi ya Kaini. Zimenezi zinamukwiyitsa kwambiri Kaini. Yehova anamuchenjeza kuti asiye kukwiya chifukwa akhoza kuchita zoipa. Koma Kaini sanamvere.

Ndiyeno Kainiyo anauza Abele kuti: ‘Tiye tipite kumunda.’ Ali kumundako, anayamba kumenya m’bale wakeyo mpaka kumupha. Kodi Yehova anatani? Analanga Kaini pomuthamangitsira kutali ndipo sanamulole kuti abwererenso kwawo.

Kaini akupita kumene kuli Abele

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Tikuphunzira kuti nthawi zina tingakhumudwe zinthu zikakhala kuti sizinayende mmene timafunira. Koma tikaona kuti tayamba kukwiya kwambiri kapena ena akatilangiza, tiyenera kusiya kukwiyako, kuopera kuti tingayambe kuchita zosayenera.

Popeza Abele ankakonda Yehova komanso ankachita zabwino, Yehova sanamuiwale. M’tsogolomu adzamuukitsa kuti adzakhale m’paradaiso.

“Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi mʼbale wakoyo. Kenako ukabwerenso nʼkudzapereka mphatso yakoyo.”​—Mateyu 5:24

Mafunso: Kodi ana awiri oyamba a Adamu ndi Hava anali ndani? N’chifukwa chiyani Kaini anapha m’bale wake?

Genesis 4:1-12; Aheberi 11:4; 1 Yohane 3:11, 12

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena