Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 2
  • Kukambirana Mwachibadwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukambirana Mwachibadwa
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Filipo Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Filipo
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Filipo
  • Filipo—Mlaliki Wokangalika
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kulalikira “Uthenga Wabwino Wonena za Yesu”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 2

ULENDO WOYAMBA

Mlaliki Filipo akucheza ndi munthu wa ku Itiyopiya amene akuwerenga mpukutu ali mugaleta lake.

Machitidwe 8:30, 31

PHUNZIRO 2

Kukambirana Mwachibadwa

Mfundo yaikulu: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.”—Miy. 15:23.

Zomwe Filipo Anachita

Mlaliki Filipo akucheza ndi munthu wa ku Itiyopiya amene akuwerenga mpukutu ali mugaleta lake.

VIDIYO: Filipo Analalikira Nduna ya ku Itiyopiya

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 8:30, 31. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Filipo anayamba bwanji kukambirana ndi munthuyo?

  2. N’chifukwa chiyani kuyamba kukambirana mwanjira imeneyi kunali kwachibadwa? Nanga zimenezi zinathandiza bwanji munthuyo kuphunzira mfundo zatsopano za choonadi?

Zomwe Tikuphunzira kwa Filipo

2. Tikamakambirana ndi anthu mwachibadwa, zimawathandiza kukhala omasuka komanso savutika kuti atimvetsere.

Zomwe Mungachite Potsanzira Filipo

3. Muzichita chidwi ndi anthu. Mungathe kudziwa zambiri zokhudza munthuyo pongoona mmene waimira, akulankhulira komanso mmene nkhope yake ikuonekera. Kodi akuoneka kuti ali ndi chidwi kuti mulankhulane? Mungayambe kukambirana mfundo inayake ya m’Baibulo pofunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti . . . ?” Musakakamize munthu amene sakufuna kuti mukambirane.

4. Muzikhala oleza mtima. Musamakhale ndi maganizo ofuna kuyamba pompopompo kukambirana ndi munthu mfundo ya m’Baibulo. Dikirani mpaka patapezeka mpata wabwino kuti muyambe kukambirana mwachibadwa. Nthawi zina zingafunike kudikira mpaka pomwe mungadzachezenso ndi munthuyo.

5. Muzikhala okonzeka kusintha. Munthu akhoza kuyambitsa nkhani ina. Choncho muzikhala okonzeka kukambirana naye mfundo inayake yogwirizana ndi zomwe akufotokoza ngakhale kuti si zomwe munakonzekera.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mlal. 3:1, 7; 1 Akor. 9:22; 2 Akor. 2:17; Akol. 4:6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena