-
Kodi Mumaphunzitsa Ena Kuti Akhalenso Akulu?Nsanja ya Olonda—2015 | April 15
-
-
Kodi Mumaphunzitsa Ena Kuti Akhalenso Akulu?
“Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—MLAL. 3:1.
1, 2. Kodi oyang’anira madera ambiri amafuna kuti akulu azichita chiyani?
PAMENE woyang’anira dera ankatsanzikana ndi akulu mumpingo wina anawayamikira kwambiri. Ankaona kuti ambiri anali akhama ngakhale kuti ena anali achikulire. Koma woyang’anira derayo anali ndi nkhawa ndipo anawafunsa kuti: “Kodi abale mwachita zotani pothandiza ena kuti akhalenso akulu?” Apa akuluwo anakumbukira kuti pa ulendo wapita anauzidwa kuti athandize anthu ena. Kenako mkulu wina anayankha kuti: “Kunena zoona sitinachite zambiri.” Ndiyeno akulu ena onse anavomereza zimene mnzawoyo ananena.
2 Ngati ndinu mkulu n’kutheka kuti zimenezi zinakuchitikirani. Oyang’anira madera ambiri amaona kuti m’pofunika kuphunzitsa abale achinyamata ndi achikulire omwe kuti athandize poweta nkhosa za Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kumavuta nthawi zina?
3. (a) Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kuphunzitsa ena n’kofunika? (b) N’chifukwa chiyani aliyense ayenera kuganizira bwino mfundo za m’nkhaniyi? (Onani mawu am’munsi.) (c) N’chifukwa chiyani akulu ena amavutika kuphunzitsa ena?
3 Ngati ndinu mkulu, mukudziwa kuti kuphunzitsa ena n’kofunika.a Mukudziwa kuti pakufunika akulu ambiri kuti mipingo ikhalebe yolimba ndiponso kuti mipingo yatsopano ikhazikitsidwe. (Werengani Yesaya 60:22.) Mukudziwanso kuti Mawu a Mulungu amakulimbikitsani kuphunzitsa anthu ena. (Werengani 2 Timoteyo 2:2.) Koma n’kutheka kuti nanunso zimakuvutani kupeza nthawi yophunzitsa ena. Mwina mumatanganidwa kwambiri kusamalira banja lanu, kugwira ntchito zina komanso za pampingo. Ngakhale kuti mumatanganidwa chonchi, kuphunzitsa ena n’kofunika kwambiri. Tiyeni tikambirane zifukwa zake.
KUPHUNZITSA ENA N’KOFUNIKA KWAMBIRI
4. N’chifukwa chiyani akulu ena amasiya kuphunzitsa ena?
4 N’chifukwa chiyani akulu ena zimawavuta kupeza nthawi yophunzitsa ena? Mwina amaganiza kuti kuphunzitsa ena n’kosafunika kwambiri poyerekezera ndi ntchito zina zofunika mwamsanga mumpingo. Ena amaganizanso kuti mpingo ukhoza kumayenda bwinobwino ngakhale atasiya kaye kuphunzitsa ena. N’zoona kuti ntchito zambiri pampingo zimafunika kuzigwira mwamsanga, koma kusiya kuphunzitsa ena kungayambitse mavuto.
5, 6. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha kholo limene mwana wake wadwala malungo?
5 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mwana wadwala malungo ndipo makolo ake akuganiza zomupatsa panado m’malo mopita naye kuchipatala. Akuchita zimenezi n’cholinga choti agwire ntchito zina zofunika. Iwo akuganiza kuti mwanayo akhalabe ndi mphamvu ngakhale kuti sanapatsidwe mankhwala a malungo. Kodi zimenezi n’zoopsa bwanji? Ngati makolowo atapitirizabe kuchita zimenezi, matenda a mwanayo angakule kwambiri mwina kufika pokomoka. Zimenezitu zingadzachititse kuti awononge ndalama zambiri kuchipatala. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
6 N’zoona kuti akulu amafunika kugwira ntchito zambiri mwamsanga. Kupanda kutero zikhoza kubweretsa mavuto aakulu mumpingo. Mofanana ndi makolo amene amakhala ndi ntchito zina zofunika, akulu amafunikanso ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ (Afil. 1:10) Komabe akulu ena amatanganidwa ndi ntchito zofunika pampingo n’kufika posiya kuphunzitsa ena. Choncho zili ngati akupereka panado kwa mwana amene wadwala malungo n’cholinga choti agwire ntchito zina. Ngati izi zitachitika, ndiye kuti mpingowo m’tsogolo udzasowa akulu amene angayenerere kugwira ntchito zina.
7. Kodi tiyenera kuwaona bwanji akulu amene amayesetsa kuphunzitsa ena?
7 Izitu zikusonyeza kuti sitiyenera kuona mopepuka udindo wophunzitsa ena. Akulu amene amaphunzitsa ena kuti ayenerere maudindo ndi anzeru ndipo amaganizira zam’tsogolo. Zimene amachita zimathandiza kwambiri abale ndi alongo mumpingo. (Werengani 1 Petulo 4:10.) N’chifukwa chiyani tikunena choncho?
MUZIGANIZIRA ZAM’TSOGOLO
8. (a) Kodi akulu ayenera kuphunzitsa ena pa zifukwa ziti? (b) Kodi akulu amene akutumikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri ayenera kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti “Ntchito Yofunika Kwambiri.”)
8 Akulu, ngakhale atakhala aluso kwambiri, ayenera kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti akadzakalamba sadzakwanitsa kuchita zinthu zina bwinobwino. (Mika 6:8) Ayenera kudziwanso kuti mavuto ogwa “mwadzidzidzi” angawalepheretse kuchita zinthu zina mumpingo. (Mlal. 9:11, 12; Yak. 4:13, 14) Choncho akulu amene amaganizira nkhosa amaphunzitsa anthu ena zinthu zimene iwo aphunzira kwa zaka zambiri.—Werengani Salimo 71:17, 18.
9. Kodi kuphunzitsa anthu ena kudzathandiza kwambiri pa nthawi iti?
9 Kodi akulu amene amaphunzitsa ena amathandizanso bwanji mpingo? Iwo amathandiza kuti mpingo ukhale wotetezeka. Kodi tikutanthauza chiyani pamenepa? Anthu ena akaphunzitsidwa ndiye kuti padzakhala abale ambiri othandiza kuti mpingo ukhale wolimba ndiponso wogwirizana panopa komanso makamaka pa chisautso chachikulu. (Ezek. 38:10-12; Mika 5:5, 6) Choncho ngati ndinu mkulu, tikukupemphani kuti muyambe panopa kuphunzitsa anthu ena mumpingo.
10. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani kuti apeze nthawi yophunzitsa ena?
10 Tikudziwa kuti mumatopa chifukwa cha ntchito zina zofunika kwambiri mumpingo. Koma tikukupemphani kuti pa nthawi imene mumatanganidwayo muzipatulapo ina kuti muphunzitse ena. (Mlal. 3:1) Mukatero mudzasonyeza kuti mukuona zam’tsogolo.
CHOYAMBA, MUZIWATHANDIZA KUKHALA OMASUKA
11. (a) Kodi malangizo ofanana amene akulu ochokera madera osiyanasiyana ananena akusonyeza chiyani? (b) Malinga ndi Miyambo 15:22, kodi kukambirana zimene akuluwa ananena kungatithandize bwanji?
11 Chaposachedwapa, akulu ena amene amayesetsa kuphunzitsa abale kuti ayenerere maudindo mumpingo, anafunsidwa kuti afotokoze zimene amachita.b Ngakhale kuti akuluwa amakhala m’madera osiyanasiyana, malangizo amene ananena ndi ofanana. Izi zikusonyeza kuti kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo n’kothandiza ‘kulikonse ndiponso mumpingo uliwonse.’ (1 Akor. 4:17) Choncho mu nkhaniyi ndiponso yotsatira tikambirana malangizo amene akuluwa anapereka. (Miy. 15:22) Kuti nkhaniyi ikhale yosavuta kumva, akulu tiziwatchula kuti “aphunzitsi” ndipo amene akuwathandiza tiziwatchula kuti “ophunzira.”
12. Kodi mphunzitsi ayenera kuchita chiyani kuti athandize ophunzira?
12 Mphunzitsi amafunika kukhala womasuka kuti athandize ophunzira. Zimenezi n’zofanana ndi zimene mlimi amachita. Iye asanafese mbewu amakonza kaye munda wake. Choncho mphunzitsi ayenera kukonzekeretsa ophunzira ake kuti aphunzire zinthu zatsopano. Kodi mphunzitsi angachite chiyani kuti akonzekeretse ophunzira ake kuphunzira zinthu zatsopano? Chitsanzo cha mneneri Samueli chingathandize pa nkhaniyi.
13-15. (a) Kodi Samueli anapatsidwa ntchito yotani? (b) Kodi Samueli anagwira bwanji ntchito yake? (Onani chithunzi patsamba 3.) (c) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuganizira bwino nkhaniyi?
13 Tsiku lina zaka zoposa 3,000 zapitazo, Yehova anauza Samueli kuti: “Mawa nthawi ngati ino ndikutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini, ndipo udzam’dzoze kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.” (1 Sam. 9:15, 16) Samueli anazindikira kuti udindo wake monga mtsogoleri wafika kumapeto ndipo Yehova akufuna kuti iye adzoze munthu wina wolowa m’malo mwake. Mwina Samueli ankadzifunsa kuti: ‘Kodi munthu ameneyo ndimuphunzitsa bwanji ntchito yakeyo?’ Koma kenako anadziwa zochita.
14 Tsiku lotsatira Samueli anaona Sauli ndipo Yehova anamuuza kuti: “Ameneyu ndiye munthu ndimakuuza uja.” Ndiyeno Samueli anaitana Sauli kuti akadye naye chakudya kumalo okwezeka. Atafika m’chipinda chodyera, Samueli anakonzera Sauli ndiponso mtumiki wake malo apamwamba n’kuwapatsa chakudya chabwino kwambiri. Ndipo Samueli anati: “Tenga, udye chifukwa anasungira iweyo kuti udzaidye pa nthawi ino.” Kenako ananyamuka kupita kunyumba ya Samueli ndipo popita ankacheza. Samueli anachita zonsezi pofuna kuti amasukirane ndi Sauli. Atafika kunyumbako, anapita padenga la nyumba ndipo Samueli “anapitiriza kulankhula ndi Sauli.” Ankachita zimenezi uku akupitidwa kamphepo kayeziyezi kenako anapita kukagona. Ndiyeno tsiku lotsatira Samueli anadzoza Sauli, kumupsompsona ndipo anam’patsa malangizo ena. Kenako Sauli ananyamuka ali wokonzeka kukhala mtsogoleri.—1 Sam. 9:17-27; 10:1.
15 N’zoona kuti kudzoza munthu kuti akhale mfumu n’kosiyana ndi kuthandiza abale kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu mumpingo. Komabe akulu masiku ano angaphunzire zambiri pa zimene Samueli anachita. Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri.
KHALANI APHUNZITSI KOMANSO ANZAWO
16. (a) Kodi Samueli anamva bwanji Aisiraeli atanena kuti akufuna mfumu? (b) Kodi Samueli anatani pamene Yehova anamuuza kuti adzoze Sauli?
16 Muzikhala ndi mtima wofuna kuphunzitsa. Poyamba, Samueli atamva zoti Aisiraeli akufuna mfumu, anakhumudwa ndipo ankaona kuti anthuwo asiya kumukonda. (1 Sam. 8:4-8) Iye sankafuna kuchita zimene anthu ananenazo. Ndiyeno Yehova anamuuza katatu kuti amvere zimene anthuwo akunena. (1 Sam. 8:7, 9, 22) Ngakhale zinali choncho, Samueli sankachitira nsanje munthu womulowa m’maloyo. Yehova atamuuza kuti adzoze Sauli, iye anachita zimenezi ndi mtima wonse osati monyinyirika.
17. (a) Kodi akulu angatsanzire bwanji Samueli? (b) Kodi chimachitika n’chiyani ngati akulu aphunzitsa bwino anthu ena?
17 Masiku anonso, akulu ayenera kukhala ndi mtima wofuna kuphunzitsa anthu. (1 Pet. 5:2) Sayenera kuopa kuphunzitsa ena poganiza kuti awalanda udindo. Aphunzitsi abwino amaona kuti anthu amene akuwaphunzitsa ndi antchito anzawo osati anthu amene akupikisana nawo. (2 Akor. 1:24) Iwo amadziwa kuti anthuwo ndi mphatso zamtengo wapatali mumpingo. (Aheb. 13:16) Kunena zoona aphunzitsi abwinowa amasangalala akaona anthu amene awaphunzitsa akuthandiza kwambiri mumpingo.—Mac. 20:35.
18, 19. (a) Kodi mkulu angathandize bwanji munthu amene akumuphunzitsa kuti amasuke? (b) Kodi kuchita zimenezi n’kothandiza bwanji?
18 Muzipeza mpata wocheza nawo. Kodi mukukumbukira zimene Samueli anachita atakumana ndi Sauli? Iye sanangotenga botolo la mafuta mwamsangamsanga n’kuthira pamutu pa Sauli kenako n’kumuuza kuti azipita. Akanatero sizikanayenda bwino chifukwa akanamudzidzimutsa. Samueli anachita zinthu mokoma mtima komanso mwapang’onopang’ono. Anapita naye kukadya, kenako kuyenda naye ndipo pambuyo poti apuma anamudzoza kukhala mfumu.
Muzipeza mpata wocheza ndi anthu amene mukufuna kuwaphunzitsa (Onani ndime 18 ndi 19)
19 Izi n’zimene mphunzitsi ayenera kuchita. Choyamba ayenera kupeza mpata wocheza ndi wophunzirayo n’cholinga choti amasuke. Zimene mkulu angachite kuti amasukirane ndi munthu zingakhale zosiyana malinga ndi kumene akukhala komanso chikhalidwe chawo. Koma kaya zili bwanji kwanuko, mkulu amene amatanganidwa ayenera kupeza nthawi yocheza ndi anthu amene akufuna kuwaphunzitsa. Akatero zimakhala ngati akuwauza kuti “Ndimaona kuti ndiwe munthu wofunika kwambiri.” (Werengani Aroma 12:10.) Zimenezi zingathandize kwambiri anthu amene mukuwaphunzitsawo ndipo sadzaiwala.
20, 21. (a) Kodi mphunzitsi wabwino amatani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
20 Mfundo imene akulu ayenera kuikumbukira ndi yakuti: Mphunzitsi wabwino amakonda kuphunzitsa komanso amakonda anthu amene akuwaphunzitsawo. (Yerekezerani ndi Yohane 5:20.) Ophunzira amadziwa ngati mphunzitsi wawo amawakonda kapena ayi ndipo ngati aona kuti amawakonda amaphunzira mosavuta. Choncho ngati ndinu mkulu, chonde yesetsani kupeza mpata wocheza ndi anthu kuti muwaphunzitse bwino.—Miy. 17:17; Yoh. 15:15.
21 Munthu amene mukufuna kumuphunzitsayo akamasuka muyenera kuyamba kumuthandiza. M’nkhani yotsatira tidzakambirana njira zimene mungagwiritse ntchito pophunzitsa anthu.
a Nkhaniyi ndiponso yotsatira kwenikweni alembera akulu koma aliyense mumpingo ayenera kuganizira bwino mfundo zake. Tikutero chifukwa chakuti nkhanizi zilimbikitsa m’bale aliyense wobatizidwa kuti aphunzitsidwe n’cholinga choti athandize pa ntchito za mumpingo. Zikatero, aliyense mumpingo adzapindula kwambiri.
b Akulu amene anafunsidwa ndi a ku Australia, Bangladesh, Belgium, Brazil, France, French Guiana, Japan, Korea, Mexico, Namibia, Nigeria, Réunion, Russia, South Africa ndi ku United States.
-
-
Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale AkuluNsanja ya Olonda—2015 | April 15
-
-
Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu
“Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . , uziphunzitse kwa anthu okhulupirika.”—2 TIM. 2:2.
1. (a) Perekani zitsanzo zakale zosonyeza kuti kuphunzitsa ena n’kofunika? (b) N’chifukwa chiyani nafenso masiku ano tiyenera kuphunzitsidwa? (c) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
ATUMIKI a Mulungu amadziwa kuti kuphunzitsa ena n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, Abulamu anakwanitsa kupulumutsa m’bale wake Loti chifukwa choti anali ndi “anyamata ake odziwa kumenya nkhondo” kapena kuti ophunzitsidwa bwino. (Gen. 14:14-16) M’nthawi ya Mfumu Davide, anthu omwe ankaimba m’nyumba ya Mulungu anali “ophunzitsidwa kuimbira Yehova” ndipo izi zinkalemekeza Yehova. (1 Mbiri 25:7) Masiku ano tikumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndi otsatira ake. (Aef. 6:11-13) Komanso tikuyesetsa kuchita zimene tingathe kuti tizitamanda Yehova. (Aheb. 13:15, 16) Choncho nafenso tiyenera kuphunzitsidwa kuti zinthu zizitiyendera bwino. Kuti zimenezi zitheke, Yehova waika akulu m’mipingo kuti aziphunzitsa ena. (2 Tim. 2:2) Mu nkhaniyi tikambirana zimene akulu angachite pophunzitsa ena kuti akhale akulu.
ATHANDIZENI KUTI AZIKONDA KWAMBIRI YEHOVA
2. (a) Kodi mkulu ayenera kuchita chiyani asanayambe kuphunzitsa munthu wina zinthu zatsopano? (b) Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji?
2 Akulu ali ngati mlimi. Nthawi zina, mlimi amayamba wathira manyowa m’munda asanabzalemo mbewu. N’chimodzimodzi ndi kuphunzitsa anthu ena zinthu zatsopano. Choyamba, muyenera kuwathandiza kudya chakudya chabwino chochokera m’Mawu a Mulungu. Izi zimathandiza kuti aphunzire bwino zinthu zatsopanozo.—1 Tim. 4:6.
3. (a) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mawu a Yesu a pa Maliko 12:29, 30? (b) Kodi pemphero lingathandize bwanji munthu amene mukumuphunzitsa?
3 Kodi mungadziwe bwanji ngati mfundo za m’Malemba zikuthandiza munthuyo? Mwina mungamufunse kuti: “Kodi inuyo mutadzipereka kwa Yehova munasintha zinthu ziti?” Funso limeneli likhoza kuthandiza kuti mukambirane mfundo zambiri zolimbikitsa kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse. (Werengani Maliko 12:29, 30.) Pambuyo pokambirana mfundo ngati zimenezi mukhoza kupemphera naye. Ndiyeno m’pempherolo mungapemphe Yehova kuti amupatse mzimu woyera kuti umuthandize kuphunzira zinthu zatsopano. M’baleyo akhoza kusangalala kumva pemphero losonyeza kuti mumamuganizira kwambiri.
4. (a) Kodi mungagwiritse ntchito malemba ati pothandiza munthu kuti azikonda kwambiri Yehova? (b) Kodi akulu amafunitsitsa kuti munthu amene akumuphunzitsa atani?
4 Poyamba kuphunzitsa munthu, muyenera kukambirana naye nkhani zina za m’Baibulo zimene zingamuthandize kukhala ndi mtima wofuna kutumikira, kukhala wodalirika komanso wodzichepetsa. (1 Maf. 19:19-21; Neh. 7:2; 13:13; Mac. 18:24-26) Makhalidwe amene tatchulawa ali ngati manyowa othandiza munthu wophunzirayo. Tikutero chifukwa chakuti amathandiza kuti ayambe mwamsanga kukonda kwambiri Yehova. Mkulu wina wa ku France, dzina lake Jean-Claude, anati: “Chimene ndimafunitsitsa n’kuthandiza wophunzirayo kuti azikonda kwambiri Yehova. Ndimayesetsa kupeza mpata wokambirana naye malemba amene angamutsegule m’maso kuti aone ‘zinthu zodabwitsa’ za m’Mawu a Mulungu.” (Sal. 119:18) Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite pothandiza munthuyo pa mbali imeneyi?
ATHANDIZENI KUKHALA NDI ZOLINGA
5. (a) Kodi kukambirana ndi munthu zolinga zake n’kothandiza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuthandiza achinyamata kukhala ndi zolinga adakali aang’ono? (Onani mawu am’munsi.)
5 Choyamba, tiyenera kufunsa munthu amene tikufuna kumuphunzitsayo zolinga zake. Ngati alibe zolinga zilizonse, muyenera kumuthandiza kukhala ndi zolinga zimene angazikwanitsedi. Mwina mungamufotokozere zolinga zomwe munali nazo ndiponso mmene munamvera mutazikwaniritsa. Zimenezi zingaoneke zazing’ono koma zimathandiza. Chitsanzo ndi m’bale wina wa ku Africa dzina lake Victor. Iye ndi mkulu komanso mpainiya ndipo anati: “Ndili wamng’ono mkulu wina anandifunsa mafunso ochepa okhudza zolinga zanga. Mafunsowo anandithandiza kuyamba kuganizira kwambiri za utumiki wanga.” Akulu enanso omwe amakonda kuphunzitsa ena anafotokoza kuti m’pofunika kuyamba kuphunzitsa achinyamata adakali aang’ono. Ndi bwino kuwapatsa ntchito zina mumpingo zogwirizana ndi msinkhu wawo. Kuphunzitsa achinyamatawa kungawathandize kukhala ndi zolinga isanafike nthawi yomwe angasokonezedwe ndi zinthu zina.—Werengani Salimo 71:5, 17.a
Mukamapempha munthu kuchita zinazake, muzimuuza zifukwa zake ndipo muzimuyamikira ngati wachita bwino (Onani ndime 5 mpaka 8)
6. Kodi Yesu ankaphunzitsa bwanji anthu ena?
6 Pophunzitsa anthu, Yesu ankafotokoza zoyenera kuchita ndiponso zifukwa zake. Mwachitsanzo, asanauze ophunzira ake ntchito yoti agwire, Yesu anawauza chifukwa chake ayenera kumvera. Iye anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kenako ananena kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:18, 19) Pophunzitsa munthu, nanunso muyenera kumufotokozera zimene ayenera kuchita ndiponso zifukwa zake.
7, 8. (a) Kodi akulu masiku ano angatsanzire bwanji Yesu pophunzitsa ena? (b) N’chifukwa chiyani kuyamikira ena n’kothandiza? (c) Kodi akulu angaphunzitse bwanji anthu ena? (Onani bokosi lakuti “Kodi Tingawaphunzitse Bwanji?”)
7 Mukamauza munthu zoyenera kuchita, muzimufotokozera zifukwa zake zochokera m’Malemba. Mukamachita zimenezi mudzamuthandiza kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti mukupempha m’bale kuti ayeretse kanjira kopita ku Nyumba ya Ufumu. Mwina mungakambirane naye lemba la Tito 2:10 ndipo mungafotokoze kuti ntchitoyo idzakometsera “chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.” Mungamufotokozerenso mmene ntchitoyo ingathandizire anthu achikulire mumpingo. Mukamakambirana mwa njira imeneyi, zidzathandiza munthuyo kugwira ntchitoyo ndi mtima wofuna kuthandiza anthu osati mongotsatira malamulo. Iye adzasangalala kwambiri poona kuti ntchito yake yathandiza abale ndi alongo.
8 Muziyamikira munthu amene mukumuthandizayo ngati wayesetsa kutsatira zimene mukumuphunzitsa. Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji? Kuyamikira munthu kuchokera pansi pa mtima kuli ngati kuthirira mbewu kuti zikule bwino.—Yerekezerani ndi Mateyu 3:17.
VUTO LINA
9. (a) Kodi akulu amene amatumikira m’mayiko otukuka amakumana ndi vuto liti? (b) N’chifukwa chiyani achinyamata m’mayiko amenewa saika Yehova pa malo oyamba?
9 Akulu amene akutumikira m’mayiko otukuka amakumana ndi vuto lina. Zimakhala zovuta kwambiri kulimbikitsa achinyamata a zaka za m’ma 20 kapena 30 kuti azichita zambiri mumpingo. Titafunsa akulu amene atumikira nthawi yaitali m’mayiko 20 oterewa, anatiuza chimene chimachititsa vutoli. Chifukwa chimodzi ndi chakuti achinyamatawo amalimbikitsidwa kuphunzira kwambiri kapena kupeza ntchito zapamwamba osati kutumikira Yehova. Achinyamata oterewa saika Yehova pa malo oyamba.—Mat. 10:24.
10, 11. (a) Kodi mkulu angathandize bwanji m’bale amene akuoneka kuti safuna kuchita zambiri mumpingo? (b) Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene angagwiritse ntchito pokambirana naye? (Onani mawu am’munsi.)
10 Pamafunika khama komanso kuleza mtima kuti tithandize wachinyamata amene safuna kuchita zambiri mumpingo. Alimi ena amapeza njira yowongolera mbewu zopindika kuti zikule bwino. Amachita zimenezi mwapang’onopang’ono. N’chimodzimodzi ndi kuthandiza achinyamata kuti asinthe maganizo n’kukhala ndi mtima wofuna kutumikira. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
11 Choyamba muyenera kupeza mpata wocheza nawo. Athandizeni kudziwa kuti ndi anthu ofunika kwambiri mumpingo. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono muzikambirana nawo malemba amene angawathandize kuganizira zimene analonjeza podzipereka kwa Yehova. (Mlal. 5:4; Yes. 6:8; Mat. 6:24, 33; Luka 9:57-62; 1 Akor. 15:58; 2 Akor. 5:15; 13:5) Mwina mungamufunse kuti, ‘Kodi pamene unkadzipereka kwa Yehova unamulonjeza kuti chiyani?’ Kenako mungamufunse kuti, ‘Ukuganiza kuti Yehova anamva bwanji tsiku limene unabatizidwa?’ (Miy. 27:11) ‘Nanga ukuganiza kuti Satana anamva bwanji?’ (1 Pet. 5:8) Dziwani kuti mukawerenga naye malemba oyenerera akhoza kusintha kwambiri.—Werengani Aheberi 4:12.b
MUZIYESETSA KUKHALA OKHULUPIRIKA
12, 13. (a) Kodi Elisa anasonyeza khalidwe lotani pamene ankaphunzitsidwa? (b) Kodi Elisa anadalitsidwa bwanji chifukwa chokhala wokhulupirika?
12 Kodi achinyamata muyenera kuchita chiyani kuti zinthu zikuyendereni bwino? Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tikambirane za munthu wina wakale.
13 Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mneneri Eliya anapempha Elisa kuti akhale mtumiki wake. Nthawi yomweyo iye anavomera ndipo anali wokhulupirika. Ankatumikira Eliya ngakhale pa ntchito zooneka zonyozeka. (2 Maf. 3:11) Ndiyeno patapita zaka 6, Elisa anazindikira kuti kwatsala nthawi yochepa kuti Eliya asiye kutumikira ku Isiraeli. Pa nthawiyi Eliya anali ataphunzitsa Elisa zinthu zambiri ndipo anamuuza katatu kuti asiye kumutsatira. Pa nthawi zonsezi Elisa ankayankha kuti: “Sindikusiyani.” Iye sanafune kusiyana ndi Eliya ngakhale pang’ono. Yehova anadalitsa Elisa chifukwa cha kukhulupirika kwake. Iye anali ndi mwayi woona zinthu zochititsa mantha pa nthawi imene Eliya ankachoka.—2 Maf. 2:1-12.
14. (a) Kodi achinyamata angatsanzire bwanji Elisa? (b) N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera kukhala okhulupirika?
14 Kodi achinyamatanu mungatsanzire bwanji Elisa? Mukapatsidwa ntchito zooneka ngati zonyozeka muzizigwira mokhulupirika. Muziona kuti akulu amene akupatsani ntchitoyo ndi anzanu ndipo asonyezeni kuti mumayamikira kwambiri zimene akuchita pokuthandizani. Mukamatero mudzakhala ngati mukuuza akuluwo kuti: “Sindikusiyani.” N’chifukwa chiyani muyenera kukhala okhulupirika? Mukakhala okhulupirika akulu adzaona kuti Yehova akufuna kuti mupatsidwe maudindo ena mumpingo.—Sal. 101:6; Werengani 2 Timoteyo 2:2.
MUZITSATIRA ZIMENE MWAPHUNZITSIDWA
15, 16. (a) Kodi Elisa anasonyeza bwanji kuti ankatsatira zimene anaphunzitsidwa? (Onani chithunzi patsamba 9.) (b) N’chiyani chinatsimikizira aneneri a ku Yeriko kuti mzimu wa Eliya uli pa Elisa?
15 Nkhani ya Elisa ikusonyezanso zimene abale angachite posonyeza kuti amalemekeza akulu amene atumikira nthawi yaitali. Tsiku lina, Eliya ndi Elisa anakumana ndi ana a aneneri ku Yeriko ndipo kenako anapita kumtsinje wa Yorodano. Atafika, “Eliya anatenga chovala chake chauneneri n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika.” Iwo anawoloka pouma ndipo ankayenda, uku akulankhulana. Pa nthawiyi Elisa sankadzitenga kuti akudziwa zonse. Elisa ankasunga mumtima mawu onse amene Eliya ankamuuza. Ankachita zimenezi mpaka nthawi imene Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Ndiyeno pobwerera Elisa anafikanso pamtsinje paja. Iye anatenga chovala cha Eliya chija n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanikanso.—2 Maf. 2:1-14.
16 Taonani kuti chozizwitsa choyamba chimene Elisa anachita chinali chofanana ndendende ndi chimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani? N’kutheka kuti Elisa sankaganiza kuti ali ndi mphamvu zonse moti akhoza kuchita zosiyana ndi zimene Eliya ankachita. Iye ankatsatira zimene Eliya ankachita potumikira Yehova ndipo izi zinachititsa aneneri a ku Yeriko kutsimikizira kuti mzimu wa Eliya uli pa Elisa. (2 Maf. 2:15) Elisa anagwira ntchito yauneneri kwa zaka 60 ndipo Yehova anamuthandiza kuchita zozizwitsa zambiri kuposa zimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
17. (a) Kodi anthu amene akuphunzitsidwa angatsanzire bwanji Elisa? (b) Kodi Yehova angathandize bwanji anthu okhulupirika amene aphunzitsidwa bwino?
17 Mukapatsidwa udindo mumpingo, musamakhale ndi mtima wofuna kusinthiratu zinthu. Kumbukirani kuti zinthu zimasinthadi mumpingo malinga ndi mmene zinthu zilili kapena malinga ndi malangizo amene gulu lapereka, osati chifukwa cha mtima wanu wofuna kusintha zinthu. Paja aneneri ena aja anatsimikizira zoti Elisa ndi mneneri chifukwa choti ankatsatira zimene Eliya ankachita. Anthu mumpingo adzatsimikiziranso kuti muchita bwino udindo wanu ngati mutsatira njira zimene akulu ena ankatsatira mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. (Werengani 1 Akorinto 4:17.) Pang’ono ndi pang’ono, mudzayamba kudziwa zambiri ndipo mudzathandiza kuti mpingo usinthe zinthu zina n’cholinga choti uzitsatira malangizo a gulu la Yehova. Mukatero, Yehova akhoza kukuthandizani ngati mmene anachitira ndi Elisa ndipo mukhoza kuchita zambiri kuposa aphunzitsi anu.—Yoh. 14:12.
18. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa ena mumpingo n’kofunika kwambiri masiku ano?
18 Tikukhulupirira kuti malangizo amene ali mu nkhaniyi komanso yapita ija athandiza akulu kupeza nthawi yophunzitsa ena. Tikukhulupiriranso kuti anthu ophunzitsidwawo alandira bwino malangizo amene angapatsidwe n’cholinga choti athandize poweta nkhosa za Yehova. Zonsezi zidzathandiza kuti mipingo ikhale yolimba ndiponso kuti aliyense adzakhalebe wokhulupirika pa nthawi yovuta kwambiri imene ikubwerayi.
a Ngati wachinyamata akukonda kwambiri Yehova, ndi wodzichepetsa ndipo akukwaniritsa zimene Malemba amanena, akulu angamuvomereze kukhala mtumiki wothandiza ngakhale kuti sanakwanitse zaka 20.—1 Tim. 3:8-10, 12; onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1989, tsamba 29.
b Mungakambirane naye mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 14 mpaka 16, ndime 8 mpaka 13; ndiponso buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” mutu 16, ndime 1 mpaka 3.
-