-
“Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala ndi Moyo”Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
-
-
MUTU 19
“Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala Ndi Moyo”
MFUNDO YAIKULU: Mmene masomphenya a mtsinje umene ukuchokera m’kachisi anakwaniritsidwira m’mbuyomo, mmene akukwaniritsidwira masiku ano komanso mmene adzakwaniritsidwire m’tsogolo
1, 2. Mogwirizana ndi Ezekieli 47:1-12, kodi Ezekieli anaona komanso kuphunzira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)
EZEKIELI anaonanso chinthu china chodabwitsa m’masomphenyawo. Anaona mtsinje ukuyenda kuchokera m’nyumba yopatulika. Tayerekezerani kuti mukumuona akuyenda kutsatira madzi oyerawo. (Werengani Ezekieli 47:1-12.) Mtsinjewo ukutuluka pakhomo la nyumba yopatulika, kenako ukudutsa pageti lakum’mawa la malo a pakachisipo. Mngelo amene akutsogolera Ezekieli akuchoka naye kukachisiko ndipo akutsatira mtsinjewo n’kumayeza kuzama kwake. Mobwerezabwereza mngeloyo akuuza Ezekieli kuti awoloke mtsinjewo ndipo mneneriyu akuona kuti ukuzama mofulumira. Pasanapite nthawi ukukhala mtsinje woti sangathe kuuwoloka pokhapokha atachita kusambira.
2 Ezekieli anamva kuti mtsinjewo ukukathira m’Nyanja Yakufa. M’nyanja imeneyi munali madzi amchere komanso munalibe chamoyo chilichonse. Koma mtsinjewo utakathira m’nyanjayi, munayamba kukhala nsomba zambiri. Komanso anaona kuti m’mbali mwa mtsinjewo mwamera mitengo yosiyanasiyana. Mwezi uliwonse mitengoyo imabala zipatso zabwino ndipo imaphuka masamba ochiritsa. Ezekieli ataona zonsezi ayenera kuti anapeza mtendere mumtima ndipo zinam’patsa chiyembekezo. Koma kodi mbali imeneyi ya masomphenya a pakachisi inkatanthauza chiyani kwa iyeyo ndi Ayuda ena omwe anali nawo ku ukapolo? Nanga kodi akutanthauza chiyani kwa ife masiku ano?
Kodi Mtsinje Umene Ezekieli Anaona M’masomphenya Unkatanthauza Chiyani kwa Ayuda Omwe Anali ku Ukapolo?
3. N’chifukwa chiyani Ayuda akale sankaona kuti masomphenya a mtsinje amene Ezekieli anaona akunena za zochitika zenizeni?
3 N’zodziwikiratu kuti Ayuda a m’nthawi yakale sankaona kuti zimene Ezekieli anaona m’masomphenyawo zinali zenizeni. N’kutheka kuti lemba limeneli linawakumbutsa ulosi wina wouziridwa wokhudza kubwezeretsa kulambira koyera umene unalembedwa ndi mneneri Yoweli mwina zaka zoposa 200 m’mbuyomo. (Werengani Yoweli 3:18.) Pamene Ayuda amene anali ku ukapolowo ankawerenga mawu a Yoweli, sankayembekezera kuti m’mapiri ‘mungatuluke vinyo wotsekemera’ weniweni kapena m’mapiri ang’onoang’ono ‘mungayende mkaka.’ Komanso sankayembekezera kuti “m’nyumba ya Yehova” mungatuluke kasupe. Mofanana ndi zimenezi, Ayuda anzake a mneneri Ezekieli sankaona kuti uthenga wakewu ukunena za mtsinje weniweni.a Ndiye kodi Yehova ankapereka uthenga wotani? Malemba amatithandiza kumvetsa mbali imeneyi ya masomphenyawa. Koma panopa tikambirana mbali zitatu zomveka bwino kuchokera mu ulosi umenewu zimene zikutipatsa chiyembekezo.
4. (a) Kodi mtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli ukanachititsa kuti Ayuda aziyembekezera madalitso otani kuchokera kwa Yehova? (b) Kodi mmene Baibulo lagwiritsira ntchito mawu akuti “mtsinje” komanso “madzi” zikutitsimikizira bwanji kuti Yehova adzadalitsa anthu ake? (Onani bokosi lakuti “Mitsinje ya Madalitso Ochokera kwa Yehova.”)
4 Mtsinje wa madalitso. M’Baibulo mitsinje komanso madzi amagwiritsidwa ntchito kuimira madalitso opatsa moyo ochokera kwa Yehova. Ezekieli anaona mtsinje ngati umenewu ukuchokera pakachisi. Choncho masomphenyawa akanachititsa kuti anthu a Mulungu aziyembekezera kuti madalitso opatsa moyo ochokera kwa Yehova adzafika kwa iwo ngati angapitirizebe kulambira Yehova m’njira yovomerezeka. Kodi akanalandira madalitso otani? Iwo akanayambiranso kulandira malangizo kuchokera kwa ansembe. Popeza kuti akanayambiranso kupereka nsembe pakachisi, sakanakayikiranso kuti machimo awo aphimbidwa. (Ezek. 44:15, 23; 45:17) Zimenezi zikanapangitsa kuti akhalenso oyera ngati kuti asamba madzi oyera ochokera m’kachisi.
5. Kodi mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya ukuthetsa bwanji nkhawa yakuti mwina m’Paradaiso simudzakhala madalitso okwanira kwa wina aliyense?
5 Kodi zikanakhala zotheka kuti aliyense azilandira madalitso okwanira nthawi zonse? Masomphenyawo akuyankha funso limeneli chifukwa akusonyeza kuti madziwo akuchuluka modabwitsa moti mtsinjewo, womwe unali waung’ono unakula n’kukhala chimtsinje chachikulu pakamtunda kochepa chabe. (Ezek. 47:3-5) N’zoona kuti chiwerengero cha Ayuda amene anabwerera kwawo chikanatha kuwonjezereka, komabe madalitso a Yehova akanapitiriza kuwonjezeka moti aliyense akanapeza zimene akufunikira. Mtsinjewo unkaimira kuti m’dzikomo mudzakhala zinthu zochuluka kwambiri.
6. (a) Kodi masomphenyawa akupereka lonjezo liti lotsimikizika? (b) Kodi masomphenyawa akuperekanso chenjezo lotani? (Onani mawu am’munsi.)
6 Madzi opatsa moyo. M’masomphenya a Ezekieli, mtsinjewo ukukathira m’Nyanja Yakufa n’kuipangitsa kuti ikhale yamoyo. Onani kuti madziwo anapereka moyo kwa nsomba zambiri komanso zosiyanasiyana zofanana ndi zimene zikupezeka m’Nyanja Yaikulu kapena kuti nyanja ya Mediterranean. M’mbali mwa Nyanja Yakufa munkachitika bizinesi yaikulu yogulitsa nsomba pakati pa matauni awiri amene anali motalikirana. Mngeloyo ananena kuti: “Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.” Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti madzi ochokera m’nyumba ya Yehovayo anafika mbali iliyonse ya Nyanja Yakufayo? Ayi. Mngeloyo ananena kuti m’madambo ena simunafike madzi opatsa moyowa. Malo amenewa ‘anakhalabe amchere.’b (Ezek. 47:8-11) Choncho ulosiwu unapereka lonjezo lolimbikitsa lakuti kulambira koyera kudzathandiza kuti anthu akhalebe amphamvu komanso kuti zinthu ziziwayendera bwino. Koma anaperekanso chenjezo lakuti: Si aliyense amene adzalandire madalitso a Yehova kapena kuchiritsidwa.
7. Kodi kupezeka kwa mitengo m’mbali mwa mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya kunalimbikitsa bwanji Ayuda omwe anali ku ukapolo?
7 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Kodi mitengo imene inali m’mbali mwa mtsinjewo inali ya ntchito yanji? Inkathandiza kuti malowo azioneka okongola, si choncho? Komanso mitengoyi inali ndi ntchito ina yofunika. Mosakayikira, Ezekieli ndi Ayuda anzake ayenera kuti ankasangalala akaganizira kuti mitengo imeneyi izidzawapatsa zipatso zokoma mwezi uliwonse. Zimenezi zinawatsimikizira kuti Yehova azidzawadyetsanso mwauzimu. Kodi mitengoyi ikanawathandizanso m’njira ina iti? Onaninso kuti Baibulo likunena kuti masamba a mitengoyo “adzakhala mankhwala.” (Ezek. 47:12) Yehova ankadziwa kuti koposa zonse, Ayuda amene adzabwerere kwawo adzafunika kuchiritsidwa mwauzimu ndipo analonjeza kuti adzawachiritsa. Maulosi ena okhudza kubwezeretsa anafotokoza mmene Mulungu anachitira zimenezi monga mmene Mutu 9 wa buku lino unafotokozera.
8. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti masomphenya a Ezekieli anali oti adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu?
8 Koma mogwirizananso ndi zimene tinaona m’Mutu 9, Ayuda omwe anabwerera kwawo anaona mbali yochepa ya kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa. Zochita za anthuwo ndi zimene zinachititsa kuti asaone ulosiwu ukukwaniritsidwa m’mbali zonse. Kodi Yehova akanawadalitsa bwanji mokwanira pamene mobwerezabwereza ankachita zinthu zoipa, kusamvera komanso kunyalanyaza kulambira koyera? Ayuda okhulupirika zinkawapweteka komanso ankakhumudwa ndi zochita zoipa za Ayuda anzawo. Koma anthu amene ankalambira Yehova mokhulupirika ankadziwa kuti malonjezo ake amakwaniritsidwa nthawi zonse. (Werengani Yoswa 23:14.) Choncho masomphenya a Ezekieli anali oti tsiku lina adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu. Koma kodi akanakwaniritsidwa liti?
Mtsinje Ukuyenda Masiku ano
9. Kodi masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona adzakwaniritsidwa liti m’njira yaikulu?
9 Monga mmene tinaonera m’Mutu 14 wa bukuli, masomphenya a Ezekieli a kachisi akukwaniritsidwa kwambiri “m’masiku otsiriza” ano, nthawi imene kulambira koyera kwakwezedwa kwambiri kuposa kale. (Yes. 2:2) Kodi mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli ikukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
10, 11. (a) Kodi ndi madalitso ati amene akubwera kwa ife ngati mtsinje masiku ano? (b) Kodi madalitso ochokera kwa Yehova awonjezereka bwanji masiku ano kuti afikire anthu ambiri?
10 Mtsinje wa madalitso. Kodi madzi amene akuchokera m’nyumba ya Yehova akutikumbutsa za madalitso ati masiku ano? Akutikumbutsa za zinthu zambiri zimene Yehova amatipatsa zimene zimatithandiza mwauzimu. Chinthu chofunika kwambiri chimene watipatsa ndi nsembe ya dipo ya Khristu imene imatiyeretsa mwauzimu. Nsembe imeneyi imachititsa kuti zikhale zotheka kuti machimo athu akhululukidwe. Choonadi cha m’Mawu a Mulungu amachiyerekezeranso ndi madzi opatsa moyo omwe amayeretsa. (Aef. 5:25-27) Kodi madalitso amenewa tikuwalandira bwanji masiku ano?
11 Mu 1919, panali atumiki a Yehova ochepa kwambiri ndipo ankasangalala kulandira chakudya chauzimu chimene ankafunikira. Pamene zaka zinkapita, chiwerengero chawo chinkawonjezereka. Masiku ano chiwerengero cha anthu a Mulungu chikuposa 8 miliyoni. Kodi onsewa akulandira madzi oyera a choonadi pa nthawi yake? Inde. Pali mfundo zambiri za choonadi zimene panopa tikuzimvetsa bwino. Mwachitsanzo, zaka 100 zapitazi, anthu a Yehova atulutsa Mabaibulo mabiliyoni ambiri, mabuku, magazini, timabuku ndi timapepala. Mofanana ndi mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenyawo, choonadi chafalikira mofulumira kwambiri ndipo chathandiza anthu amene anali ndi ludzu la choonadi padziko lonse. Mabuku osindikizidwa, othandiza pophunzira Baibulo, akhala akupezeka kuyambira kalekale. Koma panopa, mabuku amenewa akupezeka pa webusaiti ya jw.org m’zilankhulo zoposa 900. Kodi madzi a choonadi amenewa amakhudza bwanji anthu amitima yabwino?
12. (a) Kodi taona zotani zosonyeza kuti uthenga wa choonadi wapereka moyo komanso thanzi lauzimu kwa anthu? (b) Kodi masomphenyawa akutipatsa chenjezo lotani la pa nthawi yake masiku ano? (Onaninso mawu am’munsi.)
12 Madzi opatsa moyo. Ezekieli anauzidwa kuti: “Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.” Taganizirani mmene anthu omwe ali m’paradaiso wauzimu wobwezeretsedwa akupezera uthenga wa choonadi. Choonadi cha uthenga wa m’Baibulo chathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Komabe ulosiwu ukuperekanso chenjezo la pa nthawi yake lakuti: Si onse amene adzapitirize kumvetsera uthenga wa choonadi. Mofanana ndi madambo a madzi a m’mbali mwa Nyanja Yakufa, amene Ezekieli anaona m’masomphenya, pali anthu ena amene amakana kumvetsera uthenga wabwino kapena kugwiritsa ntchito mfundo za choonadi pa moyo wawo.c Tisalole kuti zimenezi zitichitikire.—Werengani Deuteronomo 10:16-18.
13. Kodi masiku ano tingaphunzire chiyani pa mitengo imene Ezekieli anaona m’masomphenya?
13 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Kodi mitengo imene inali m’mbali mwa mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya ikutiphunzitsa chiyani masiku ano? Musaiwale kuti mitengoyi ikumabereka zipatso zokoma mwezi uliwonse ndipo masamba ake ndi mankhwala. (Ezekieli 47:12) Zimenezi zikutikumbutsa kuti tikutumikira Mulungu amene amatidyetsa mokwanira komanso kutichiritsa m’njira yofunika kwambiri yomwe ndi yauzimu. Masiku ano dzikoli likudwala mwauzimu ndipo anthu samvetsa mfundo za choonadi. Ndiye yerekezerani zimenezi ndi zimene Yehova akutipatsa. Mutawerenga nkhani m’magazini yathu, kuimba nyimbo yomaliza pamsonkhano wadera kapena wachigawo, kapena mutamaliza kuonera vidiyo, kodi munamva kuti Yehova wakudalitsani pokupatsani chakudya chauzimu chimenecho? Kunena zoona tili ndi chakudya chauzimu chochuluka. (Yes. 65:13, 14) Kodi chakudya chauzimuchi chimatithandiza kukhala olimba mwauzimu? Malangizo amene timalandira omwe amachokera m’Mawu a Mulungu, amatithandiza kulimbana ndi adani amene angasokoneze moyo wathu wauzimu monga chiwerewere, dyera komanso kupanda chikhulupiriro. Yehova wakhazikitsanso njira yothandizira Akhristu kuti azilimbana ndi matenda auzimu amene amabwera chifukwa cha tchimo lalikulu. (Werengani Yakobo 5:14.) Yehova watidalitsadi mogwirizana ndi mmene masomphenya a mitengo amene Ezekieli anaona akusonyezera.
14, 15. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa madambo osachiritsika amene Ezekieli anaona m’masomphenya? (b) Kodi masomphenya a mtsinje amene Ezekieli anaona akutithandiza bwanji masiku ano?
14 Koma pali zinanso zimene tikuphunzira kuchokera pa madambo amene sanachiritsidwe ndi madzi aja. Sitingayese n’komwe kukana kulandira madalitso ochokera kwa Yehova. Zingakhale zomvetsa chisoni ngati titakhala osachiritsika ngati mmene zilili ndi anthu ambiri m’dziko losachiritsikali. (Mat. 13:15) M’malomwake, timasangalala ndi mtsinje wa madalitso amene tikulandira. Tikamamwa madzi oyera a choonadi ochokera m’Mawu a Mulungu, tikamauza ena choonadi pogwira ntchito yolalikira, tikamalandira malangizo achikondi, tikamalimbikitsidwa komanso kuthandizidwa ndi akulu amene aphunzitsidwa ndi kapolo wokhulupirika, timaganizira za mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya. Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita umathandiza kuti anthu akhale ndi moyo komanso kuwachiritsa.
15 Koma kodi chidzachitike n’chiyani masomphenya a mtsinjewa akadzakwaniritsidwa m’tsogolo? M’ndime zakutsogoloku, tiona kuti madzi amtsinjewo adzayenda kwambiri m’Paradaiso amene akubwerayo.
Mmene Masomphenyawa Adzakwaniritsidwire M’Paradaiso
16, 17. (a) Kodi madzi a moyo adzachuluka bwanji m’Paradaiso? (b) Kodi tidzapindula bwanji ndi mtsinje wa madalitsowu m’Paradaiso?
16 Kodi mumayerekezera muli m’Paradaiso limodzi ndi achibale komanso anzanu mukusangalala ndi moyo mokwanira? Kuphunzira masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona kungakuthandizeni kuona kuti zimenezi ndi zenizeni. Kodi zingakuthandizeni bwanji? Ganiziraninso zinthu zitatu zimene tikuzipeza m’masomphenyawa zosonyeza kuti Mulungu amatikonda.
17 Mtsinje wa madalitso. Tinganene kuti mtsinje wophiphiritsawu udzakhala waukulu m’Paradaiso chifukwa choti madalitso ake sadzakhala auzimu okha koma adzakhalanso akuthupi. Mu ulamuliro wa Yesu wa Zaka 1,000, Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu okhulupirika kuti apindule ndi nsembe ya dipo m’njira yaikulu kwambiri. Iwo adzasintha pang’onopang’ono n’kukhala angwiro. Sipadzakhalanso matenda, madokotala, manesi, zipatala kapena kusunga ndalama kuti zidzatithandize tikadzadwala mwadzidzidzi. Anthu mabiliyoni ambiri amene adzapulumuke pa Aramagedo, adzalandira madzi amoyo. Anthu amenewa ndi “khamu lalikulu” limene lidzatuluke mu “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:9, 14) Komabe, mtsinje wa madalitso umenewu ngakhale kuti udzakhala wochititsa chidwi, udzakhala wochepa tikayerekezera ndi zimene zidzabwere pambuyo pake. Monga taonera m’masomphenya a Ezekieli, mtsinjewo udzakula kuti madalitso afikire anthu ambiri.
M’Paradaiso mtsinje wa madalitso udzathandiza kuti aliyense akhale wachinyamata komanso wathanzi (Onani ndime 17)
18. Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” udzakhala bwanji mtsinje wa madzi ambiri mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu?
18 Madzi opatsa moyo. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, “mtsinje wa madzi amoyo” udzakula kwambiri. (Chiv. 22:1) Anthu mamiliyoni osawerengeka kapenanso mabiliyoni adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala m’Paradaiso mpaka kalekale. Madalitso amene Yehova adzatipatse kudzera mu Ufumu wake adzaphatikizapo kuukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira, anthu amene akhala akugona mufumbi kwa nthawi yaitali. (Yes. 26:19) Komabe kodi aliyense amene adzaukitsidwe adzakhala ndi moyo mpaka kalekale?
19. (a) N’chiyani chimene chikusonyeza kuti m’Paradaiso tidzapeza madzi atsopano a choonadi chochokera kwa Mulungu? (b) Kodi anthu ena “adzakhalabe amchere” m’tsogolo m’njira yotani?
19 Aliyense adzayenera kusankha yekha. Pa nthawi imeneyo, mipukutu yatsopano idzatsegulidwa. Choncho madzi otsitsimula ochokera kwa Yehova, adzaphatikizapo mfundo zatsopano za choonadi komanso malangizo atsopano auzimu. Kodi zimenezi si zochititsa chidwi? Komabe anthu ena adzakana kutsatira malangizo atsopanowa ndipo m’malomwake adzasankha kusamvera Yehova. N’kutheka kuti anthu ena adzakhala osamvera m’kati mwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, koma sadzaloledwa kuti azichita zosokoneza m’Paradaiso. (Yes. 65:20) Zimenezi zikutikumbutsa masomphenya a Ezekieli komanso kutichititsa kuganizira za madambo opanda chonde amene “adzakhalabe amchere.” Anthu amene amakana mouma mtima kumwa madzi amtengo wapatali opatsa moyo, ndi opusa kwambiri. Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, gulu la anthu oukira adzakhala kumbali ya Satana. Onse amene adzakane ulamuliro wolungama wa Yehova adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso mpaka kalekale.—Chiv. 20:7-12.
20. Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi padzakonzedwa dongosolo lotani limene likutikumbutsa mitengo imene Ezekieli anaona m’masomphenya?
20 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Yehova sakufuna kuti wina aliyense aphonye mwayi wokapeza moyo wosatha. Pofuna kutithandiza kuti tisaphonye mwayi wamtengo wapatali umene akutipatsawu, adzaonetsetsanso kuti pali dongosolo lofanana ndi mitengo imene Ezekieli anaona. Koma m’Paradaiso madalitso ochokera kwa Yehova adzakhala akuthupi komanso auzimu. Ali kumwamba, Yesu Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000 adzalamulira monga mafumu kwa zaka 1,000. Monga ansembe, a 144,000 adzapereka madalitso obwera chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu ndipo adzathandiza anthu okhulupirika kuti akhale angwiro. (Chiv. 20:6) Dongosolo limeneli, loti anthu achiritsidwe mwauzimu komanso mwakuthupi, likutikumbutsa za mitengo imene Ezekieli anaona m’mbali mwa mtsinje, imene inkabereka zipatso zokoma ndipo masamba ake anali ochiritsa. Masomphenya a Ezekieli akufanana ndi ulosi wina wochititsa chidwi umene unalembedwa ndi mtumwi Yohane. (Werengani Chivumbulutso 22:1, 2.) Masamba a mitengo imene Yohane anaona, “anali ochiritsira mitundu ya anthu.” Anthu mamiliyoni ambirimbiri okhulupirika adzapindula ndi ntchito imene a 144,000 adzagwire monga ansembe.
21. Kodi kuganizira masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona, kukukukhudzani bwanji, nanga m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani? (Onani bokosi lakuti, “Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu.”)
21 Mukamaganizira za masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona, kodi mumtima mwanu simukudzaza mtendere komanso chiyembekezo? Tikuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri kutsogoloku. Tangoganizani, zaka masauzande ambiri zapitazo Yehova anatithandiza kuona chithunzi cha mmene zinthu zidzakhalire ndipo moleza mtima, akutipempha kuti tidzakhalepo pa nthawiyo kuti tidzaone kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi umenewu. Kodi mudzakhalapo? Mwina mungamakayikire kuti kodi malo anga adzakhalapo m’Paradaiso? Tsopano tiyeni tione mmene mavesi omalizira a ulosi wa Ezekieli akutithandizira kuti tisamakayikire lonjezo limeneli.
a Kuwonjezera pamenepo, Ayuda omwe anali ku ukapolo omwe ankakumbukira mmene dziko lawo linalili, ankadziwa kuti mtsinje umenewu sungakhale weniweni. Tikutero chifukwa chakuti mtsinjewu ukuyambira m’kachisi amene ali pamwamba pa phiri lalitali lomwe pamalo amene akufotokozedwawa panalibe. Komanso masomphenyawa angatanthauze kuti mtsinjewu unkalowera ku Nyanja Yakufa ndipo panalibe cholepheretsa chilichonse. Koma malinga ndi mmene dzikolo linalili zimenezinso zinali zosatheka.
b Akatswiri ena oikira ndemanga pa mawu a m’Baibulo, amaona kuti imeneyi ndi nkhani yabwino. Amanena kuti kwa nthawi yaitali kukumba mchere n’kumaugwiritsa ntchito poteteza zinthu kuti zisawonongeke inali bizinesi yaikulu ku Nyanja Yakufa. Koma mungaone kuti nkhaniyi ikunena mosapita m’mbali kuti madambo amenewo “sadzasintha nʼkukhala abwino.” Iwo adzakhala opanda moyo komanso sadzachiritsidwa chifukwa chakuti madzi opatsa moyo ochokera kunyumba ya Yehova sadzafika kumeneko. Choncho zikuoneka kuti pamene lembali likunena kuti madambowo adzakhala amchere, zikutanthauza kuti sadzakhala malo abwino.—Sal. 107:33, 34; Yer. 17:6.
c Mofanana ndi zimenezi, ganizirani fanizo la Yesu la khoka. Khoka limagwira nsomba zambiri koma si zonse zimene zimakhala “zabwino.” Nsomba zoipazo amangozitaya. Choncho Yesu anachenjeza kuti anthu ena amene alowa m’gulu la Yehova, pakapita nthawi, akhoza kusonyeza kuti ndi osakhulupirika.—Mat. 13:47-50; 2 Tim. 2:20, 21.
-
-
‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
-
-
MUTU 20
‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’
MFUNDO YAIKULU: Tanthauzo la kugawana dziko
1, 2. (a) Kodi Ezekieli analandira malangizo otani kuchokera kwa Yehova? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
EZEKIELI anali atangoona masomphenya amene anamupangitsa kuganizira zam’mbuyo, pafupifupi zaka 900 m’masiku a Mose ndi Yoswa. Pa nthawi imeneyo Yehova anauza Mose malire a Dziko Lolonjezedwa ndipo pambuyo pake anauza Yoswa mmene angagawire dzikolo kwa mafuko onse a Isiraeli. (Num. 34:1-15; Yos. 13:7; 22:4, 9) Koma tsopano m’chaka cha 593 B.C.E., Yehova akupereka malangizo kwa Ezekieli ndi Ayuda anzake amene anali ku ukapolo kuti agawenso Dziko Lolonjezedwa kwa mafuko a Isiraeli.—Ezek. 45:1; 47:14; 48:29.
2 Kodi masomphenyawa anali ndi uthenga wotani kwa Ezekieli ndi Ayuda anzake omwe anali ku ukapolo? N’chifukwa chiyani masomphenyawa ali olimbikitsa kwa anthu a Mulungu masiku ano? Kodi masomphenyawa adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu m’tsogolo?
Masomphenyawa Anasonyeza Kuti Padzachitika Zinthu 4
3, 4. (a) Kodi masomphenya omaliza a Ezekieli anapatsa anthu omwe anali ku ukapolo mfundo 4 ziti zolimbikitsa? (b) Kodi m’mutu uno tikambirana mfundo yotsimikizirika iti?
3 Masomphenya omaliza amene Ezekieli anaona akupezeka m’machaputala 9 a buku la Ezekieli. (Ezek. 40:1–48:35) Masomphenyawa anatchula mfundo 4 zolimbikitsa kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo, zosonyeza kuti mtundu wa Isiraeli udzabwezeretsedwa. Kodi mfundo zake ndi ziti? Mfundo yoyamba, kulambira koyera kudzabwezeretsedwa m’kachisi wa Mulungu. Mfundo yachiwiri, ansembe komanso abusa olungama adzatsogolera mtundu wobwezeretsedwawo. Mfundo yachitatu, anthu onse amene adzabwerere ku Isiraeli adzapatsidwa malo. Ndipo mfundo ya 4, Yehova adzakhala nawo kapena kuti adzayambiranso kukhala pakati pawo.
4 M’Mutu 13 ndi 14 wa bukuli, tinakambirana mmene mfundo zoyambirira ziwiri zokhudza kubwezeretsa kulambira koyera komanso kutsogoleredwa ndi abusa olungama zidzakwaniritsidwire. M’mutu uno tikambirana mfundo yachitatu yomwe ndi lonjezo lakuti anthu adzalandira dziko kuti likhale cholowa chawo. M’mutu wotsatira tidzakambirana lonjezo lakuti Yehova adzayambiranso kukhala ndi anthu ake.—Ezek. 47:13-21; 48:1-7, 23-29.
“Dziko Limeneli . . . Ndikulipereka kwa Inu Kuti Likhale Cholowa Chanu.”
5, 6. (a) M’masomphenya a Ezekieli, kodi ndi gawo liti limene linkafunika kugawidwa? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi cholinga cha masomphenya ogawa dziko chinali chiyani?
5 Werengani Ezekieli 47:14. M’masomphenyawa Yehova anaonetsa Ezekieli dziko limene posachedwapa lifanane ndi “munda wa Edeni.” (Ezek. 36:35) Kenako Yehova ananena kuti: “Limeneli ndi dera limene mudzagawire mafuko 12 a Isiraeli ngati cholowa chawo.” (Ezek. 47:13) “Dera” limene ankayenera kuwagawiralo linali dziko la Isiraeli lobwezeretsedwa, limene Ayuda amene anali ku ukapolowo ankayenera kubwererako. Kenako malinga ndi Ezekieli 47:15-21, Yehova anapitiriza kufotokoza mwatsatanetsatane malire akunja adziko lonselo.
6 Kodi cholinga cha masomphenya amenewa okhudza kugawa dziko chinali chiyani? Kufotokoza malire oyezedwa bwino adzikolo kunatsimikizira Ezekieli komanso Ayuda omwe anali nawo ku ukapolo kuti dziko lawo lokondedwa lidzabwezeretsedwadi. Zimene Yehova anafotokozazi ziyenera kuti zinalimbikitsa kwambiri Ayuda amene anali ku ukapolo. Kodi anthu a Mulungu akale analandiradi dziko limene anapatsidwa ngati cholowa chawo? Inde analandiradi.
7. (a) Kodi n’chiyani chimene chinayamba kuchitika mu 537 B.C.E., ndipo zimatikumbutsa chiyani? (b) Kodi choyamba tikambirana funso liti?
7 Mu 537 B.C.E., patadutsa zaka 56 kuchokera pamene Ezekieli anaona masomphenyawa, anthu ambirimbiri amene anali ku ukapolo anayamba kubwerera ku Isiraeli kuti akatenge dzikolo kukhala lawo. Zinthu zochititsa chidwi zimene zinachitika kalelo zikutikumbutsa zinthu zofanana ndi zimenezi, zomwe zachitika pakati pa anthu Mulungu masiku ano. Tinganene kuti nawonso analandira dziko ngati cholowa chawo. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Yehova analola atumiki ake kulowa m’dziko lauzimu n’kulitenga kuti likhale lawo. Pa chifukwa chimenechi, kubwezeretsedwa kwakale kwa Dziko Lolonjezedwa kungatiphunzitse zambiri zokhudza kubwezeretsedwa kwauzimu kwa anthu a Mulungu masiku ano. Koma tisanakambirane mfundo zimenezi, choyamba tiyeni tikambirane funso lakuti, “N’chifukwa chiyani tinganene kuti paradaiso wauzimu alipodi masiku ano?”
8. (a) Kodi Yehova anachititsa kuti mtundu wa Isiraeli weniweni ulowedwe m’malo ndi ndani? (b) Kodi paradaiso wauzimu ndi chiyani? (c) Kodi paradaiso ameneyu anakhalapo liti ndipo ndi ndani amene akukhala mmenemo?
8 Masomphenya amene Yehova anaonetsa Ezekieli m’mbuyomu, anasonyeza kuti ulosi wokhudza kubwezeretsedwa kwa Aisiraeli udzakwaniritsidwa m’njira yaikulu pambuyo poti ‘mtumiki wake Davide,’ yemwe ndi Yesu Khristu, wayamba kulamulira monga Mfumu. (Ezek. 37:24) Zimenezi zinachitika mu 1914 C.E. Pofika nthawi imeneyi, Aisiraeli omwe anali anthu a Mulungu anali atalowedwa m’malo ndi Isiraeli wauzimu amene ndi Akhristu odzozedwa. (Werengani Mateyu 21:43; 1 Petulo 2:9.) Sikuti Yehova anangochititsa kuti mtundu weniweni wa Aisiraeli ulowedwe m’malo ndi Isiraeli wauzimu koma anachititsanso kuti dziko lenileni la Isiraeli lilowedwe m’malo ndi paradaiso wauzimu. (Yes. 66:8) Monga mmene tinaonera m’Mutu 17 wa bukuli, paradaiso wauzimu ndi malo otetezeka auzimu ndipo m’malo amenewa mumachitika zinthu zambiri. Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi akhala akulambira Yehova m’malo amenewa kuyambira mu 1919. (Onani bokosi 9B lakuti, “N’chifukwa Chiyani Tikuti Chinali Chaka cha 1919?”) Pamene nthawi imapita, anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi kapena kuti a “nkhosa zina” nawonso anayamba kukhala m’paradaiso wauzimuyu. (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti paradaiso wauzimuyu akupitiriza kukula masiku ano, madalitso ake tidzasangalala nawo mokwanira pambuyo pa Aramagedo.
Kugawa Dziko Mwachilungamo
9. Kodi Yehova anapereka malangizo atsatanetsatane otani okhudza kugawa dziko?
9 Werengani Ezekieli 48:1, 28. Atamaliza kufotokoza malire akunja a dzikolo, Yehova anafotokoza mwatsatanetsatane mmene akuyenera kuligawira. Iye analamula kuti dzikolo aligawe mofanana pakati pa mafuko 12 aja, kuyambira kumpoto kukafika kum’mwera. Analamula kuti ayambe ndi fuko la Dani kumpoto kwenikweni kwa dzikolo, n’kumaliza ndi fuko la Gadi kum’mwera kwenikweni kwa dzikolo. Malo aliwonse amene fuko lililonse linalandira pa mafuko 12 amenewo, anayambira kumalire akum’mawa adzikolo kukafika ku Nyanja Yaikulu kapena kuti nyanja ya Mediterranean komwe ndi kumadzulo.—Ezek. 47:20.
10. Kodi mbali imeneyi ya masomphenya iyenera kuti inawatsimikizira chiyani Ayuda omwe anali ku ukapolo?
10 Kodi mbali imeneyi ya masomphenya iyenera kuti inalimbikitsa bwanji Ayuda amene anali ku ukapolo? Mmene Ezekieli anafotokozera mwatsatanetsatane mmene dzikolo lidzagawidwire, zinathandiza Ayuda omwe anali ku ukapolo kudziwa kuti dzikolo lidzagawidwa mwadongosolo. Kuwonjezera pamenepo, kugawa dzikolo mofanana kwa mafuko onse 12, kunasonyeza kuti aliyense amene adzabwerere kwawo adzalandira cholowa m’dziko limene lidzabwezeretsedwe. Palibe amene adzabwerere kwawo n’kupezeka kuti alibe malo okhala.
11. Kodi tingaphunzire chiyani pa masomphenya a ulosi okhudza kugawa dziko? (Onani bokosi lakuti “Kugawa Dziko.”)
11 Kodi tikuphunzira chiyani m’masomphenyawa zomwe zikutilimbikitsa masiku ano? Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa linali ndi malo kumene kunkakhala ansembe, alevi komanso atsogoleri. Koma panalinso malo ena kumene kunkakhala anthu ena onse ochokera m’mafuko 12 aja. (Ezek. 45:4, 5, 7, 8) Mofanana ndi zimenezi, sikuti m’paradaiso wauzimu muli malo a odzozedwa okha amene adakali padziko lapansi komanso a “khamu lalikulu” okha amene akutsogolera, koma mulinso malo a anthu ena onse amene ali m’gulu la khamu lalikulu.a (Chiv. 7:9) Ngakhale zitakhala kuti sitichita zambiri m’gulu la Yehova, tili ndi malo komanso ntchito yofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri.
Kaya tili ndi udindo wotani m’gulu la Mulungu, Yehova amasangalala ndi chilichonse chimene tikuchita pomutumikira (Onani ndime 11)
Kodi Kusiyana kwa Malangizo Awiriwa Kukutanthauza Chiyani Masiku ano?
12, 13. Kodi Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali otani, okhudza kugawira malo mafuko?
12 Malangizo ena amene Yehova anapereka kwa Ezekieli okhudza kugawa dzikolo ayenera kuti anamudabwitsa chifukwa chakuti ankasiyana ndi malangizo amene Mulungu anapereka kwa Mose. Tiyeni tione njira ziwiri zimene malangizowa ankasiyanirana. Kusiyana koyamba kunkakhudza dzikolo ndipo kusiyana kwachiwiri kunkakhudza anthu amene ankakhala m’dzikolo.
13 Kusiyana koyamba kokhudza dzikolo. Mose anauzidwa kuti mafuko omwe anali akuluakulu awapatse malo aakulu kusiyana ndi mafuko ang’onoang’ono. (Num. 26:52-54) Koma m’masomphenya a Ezekieli, Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali akuti fuko lililonse lilandire gawo “lofanana ndi la mnzake.” (Ezek. 47:14) Choncho mtunda wochokera kumalire akumpoto a cholowa cha fuko lililonse, kukafika kumalire akumwera, unkayenera kukhala wofanana pa mafuko onse 12 aja. Aisiraeli onse, mosatengera fuko lawo, ankayenera kukhala ndi mwayi wofanana wopeza zinthu zabwino za m’Dziko Lolonjezedwalo.
14. Kodi malangizo a Yehova okhudza alendo anaposa bwanji malangizo amene anapereka m’Chilamulo cha Mose?
14 Kusiyana kwachiwiri kokhudza anthu amene ankakhala m’dzikolo. Chilamulo cha Mose chinkateteza anthu ochokera m’mayiko ena ndipo chinkawalola kuti nawonso azilambira Yehova, koma sankalandira cholowa m’dzikolo. (Lev. 19:33, 34) Koma zimene Yehova akuuza Ezekieli tsopano, zikuposa zimene ananena m’Chilamulo. Yehova akumupatsa malangizo akuti: “Mlendo aliyense muzimupatsa cholowa mʼdera la fuko limene akukhala.” Popereka lamulo limeneli, Yehova anachotsa kusiyana kwakukulu kumene kunalipo pakati pa “nzika za Isiraeli,” ndi alendo amene ankakhala m’dzikolo. (Ezek. 47:22, 23) M’masomphenya a dziko lobwezeretsedwa limene Ezekieli anaona, anthu amene ankakhala m’dzikomo ankachita zinthu zofanana komanso ankalambira limodzi mogwirizana.—Lev. 25:23.
15. Kodi malangizo amene Yehova anapereka okhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo anatsindika mfundo yotani yokhudza Yehova?
15 Malangizo awiri ochititsa chidwi amene Ezekieli analandira okhudza dziko komanso anthu, ayenera kuti analimbikitsa Ayuda omwe anali ku ukapolo. Iwo ankadziwa kuti Yehova adzawapatsa malo ofanana ndi a anthu ena onse kaya ndi nzika za Isiraeli kapena alendo amene ankalambira Yehova. (Ezara 8:20; Neh. 3:26; 7:6, 25; Yes. 56:3, 8) Malangizo amenewa anatsimikizira mfundo yolimbikitsa komanso yosasintha yakuti, kwa Yehova atumiki ake onse ndi ofanana ndiponso ndi a mtengo wapatali. (Werengani Hagai 2:7.) Masiku ano, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, timakhulupirira mfundo zofanana za choonadi.
16, 17. (a) Kodi tikupindula bwanji pophunzira mfundo zokhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo? (b) Kodi tidzaphunzira chiyani m’mutu wotsatira?
16 Kodi kukambirana mfundo zimenezi zokhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo n’kothandiza bwanji? Zikutikumbutsa kuti mgwirizano komanso kuchita zinthu mosakondera zikuyenera kumaonekera mosavuta pakati pa atumiki a Yehova padziko lonse lapansi. Yehova alibe tsankho. Ndiye tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndilibe tsankho mofanana ndi Yehova? Kodi munthu aliyense amene ndikulambira naye Mulungu, ndimamulemekeza kuchokera pansi pamtima, mosaganizira mtundu wake kapena mmene zinthu zilili pa moyo wake?’ (Aroma 12:10) Tikusangalala kuti Yehova watilola tonsefe kuti tikhale m’paradaiso wauzimu, mmene timatumikira Atate wathu wakumwamba ndi mtima wonse ndipo timasangalala ndi madalitso ake.—Agal. 3:26-29; Chiv. 7:9.
Kodi timapewa tsankho ndipo timalemekeza ena kuchokera pansi pa mtima potengera chitsanzo cha Yehova? (Onani ndime 15, 16)
17 Tsopano tiyeni tikambirane mfundo ya 4 yolimbikitsa imene ikupezeka m’mbali yomalizira ya masomphenya a Ezekieli. Mfundo yake ndi yakuti, Yehova adzakhala ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo. Kodi tikuphunzira chiyani kuchokera pa lonjezo limeneli? Tipeza yankho la funso limeneli m’mutu wotsatira.
-
-
“Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
-
-
MUTU 21
“Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”
MFUNDO YAIKULU: Tanthauzo la mzinda komanso chopereka
1, 2. (a) Kodi ndi gawo lapadera liti la dziko, limene ankafunika kulipatula? (Onani chithunzi chapachikuto.) (b) Kodi masomphenyawa anawatsimikizira chiyani anthu omwe anali ku ukapolo?
M’MASOMPHENYA ake omaliza, Ezekieli anauzidwa za gawo lina la malo amene akuyenera kudzapatulidwa kuti adzagwire ntchito ina yapadera. Malo opatulidwawo sanali oti adzaperekedwe kwa fuko lina la Isiraeli ngati cholowa chawo, koma anali oti aperekedwe kwa Yehova ngati chopereka. Ezekieli anauzidwanso za mzinda wina umene unali ndi dzina lochititsa chidwi. Mbali imeneyi ya masomphenya inalimbikitsa kwambiri Ayuda amene anali ku ukapolo chifukwa inawatsimikizira kuti Yehova adzakhala nawo akadzabwerera kudziko lawo limene ankalikonda.
2 Ezekieli anafotokoza momveka bwino za chopereka chimenechi. Tiyeni tikambirane nkhani imeneyi chifukwa ili ndi mfundo zolimbikitsa kwambiri kwa ife amene timalambira Yehova m’njira yovomerezeka.
“Chopereka Chopatulika Ndiponso Malo a Mzinda”
3. Kodi malo amene Yehova anapatula anali ndi mbali 5 ziti, nanga ntchito ya mbali zimenezo inali yotani? (Onani bokosi lakuti “Gawo Loti Likhale Chopereka Chanu.”)
3 Malo apaderawa anali okwana mikono 25,000 (makilomita 13) kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera komanso mikono 25,000 kuchoka kum’mawa kukafika kumadzulo. Malo amenewa anali ofanana mbali zonse ndipo ankatchedwa kuti “malo onse oti aperekedwe.” Malowa anagawidwa m’magawo atatu. Gawo lakumtunda linali la Alevi, gawo lapakati linapatulidwa kuti likhale la kachisi komanso ansembe. Magawo onse awiriwa ndi amene ankapanga “chopereka chopatulika.” Gawo laling’ono limene linali m’munsi kapena kuti “malo otsala,” anali “oti munthu aliyense angagwiritse ntchito.” Malo amenewa anali a mzinda.—Ezek. 48:15, 20.
4. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yokhudza chopereka kwa Yehova?
4 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi yokhudza chopereka kwa Yehova? Yehova anayamba ndi kupatula malo a chopereka chapadera kenako malo a mafuko. Pochita zimenezi iye anasonyeza kuti chofunika kwambiri chinali malo amene amakhudza kulambira koyera. (Ezek. 45:1) Mosakayikira, Ayuda amene anali ku ukapolowo anaphunzira zambiri pa dongosolo limeneli la mmene anagawira dzikoli. Ankayenera kuika patsogolo nkhani yokhudza kulambira Yehova pa moyo wawo. Masiku anonso timaona kuti zinthu zokhudza kulambira, monga kuphunzira Mawu a Mulungu, kupita ku misonkhano ya Chikhristu komanso kugwira nawo ntchito yolalikira ndi zofunika kwambiri. Tikamatsanzira chitsanzo cha Yehova choika zinthu zofunika pamalo oyamba, timasonyeza kuti timaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu ndi kulambira Yehova.
“Mzinda Ukhale Pakati pa Malowa”
5, 6. (a) Kodi mzinda unali wa ndani? (b) Kodi mzindawo sukuimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?
5 Werengani Ezekieli 48:15. Kodi “mzinda” ndi malo ozungulira ankaimira chiyani? (Ezek. 48:16-18) M’masomphenya, Yehova anali atauza Ezekieli kuti: “Malo a mzinda . . . adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.” (Ezek. 45:6, 7) Zimenezi zikutanthauza kuti mzindawo komanso malo onse ozungulira sanali mbali ya “chopereka chopatulika” lomwe linali ‘gawo loti liperekedwe kwa Yehova.’ (Ezek. 48:9) Pamene tikukambirana za kusiyana kumeneku, tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira masiku ano pa dongosolo la mzindali.
6 Kuti tidziwe zimene tikuphunzira pa mzindawu, choyamba tikufunika tidziwe kuti mzinda umenewu sukuimira chiyani. Sukuimira mzinda wa Yerusalemu umene unamangidwanso komanso kachisi wake. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti m’kati mwa mzinda umene Ezekieli anaona m’masomphenya munalibe kachisi. Komanso mzindawu sukuimira mzinda wina uliwonse m’dziko lobwezeretsedwa la Isiraeli. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Ayuda amene anabwerera kwawo komanso mbadwa zawo sanamange mzinda wokhala ndi zinthu zimene zafotokozedwa m’masomphenyawo. Kuwonjezera pamenepo, mzindawu sukuimira mzinda wakumwamba. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mzindawo unamangidwa pamalo amene anasankhidwa kuti akhale “malo wamba” [kapena kuti malo omwe si opatulika]. Zimenezi ndi zosiyana ndi nyumba zimene zinamangidwa pamalo amene anasankhidwa kuti agwiritsidwe ntchito pa kulambira koyera.—Ezek. 42:20.
7. Kodi mzinda umene Ezekieli anaona m’masomphenya ndi uti, nanga zikuoneka kuti ukuimira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)
7 Ndiye kodi mzinda umene Ezekieli anaona unali uti? Kumbukirani kuti iye anaona mzindawu m’masomphenya omwewo amene anaonanso dzikolo. (Ezek. 40:2; 45:1, 6) Mawu a Mulungu akusonyeza kuti dzikolo ndi dziko lophiphiritsa, choncho mzindawo uyenera kuti ukuimiranso mzinda wophiphiritsa. Ndiye tinganene kuti mawu akuti “mzinda” akutanthauza chiyani? Mawuwa akupereka chithunzi cha anthu amene akukhala monga gulu limodzi ndipo gulu lawo ndi logwirizana. Choncho mzinda womangidwa mwadongosolo umene Ezekieli anaona, umene kukula kwake unali wofanana mbali zonse, zikuoneka kuti ukuimira mzinda umene umachita zinthu mwadongosolo.
8. Kodi oyang’anira a mzinda umene umachita zinthu mwadongosolo ntchito yawo amagwirira kuti, nanga n’chifukwa chiyani?
8 Kodi oyang’anira amene amachita zinthu mwadongosolowa ntchito yawo amagwirira kuti? Masomphenya a Ezekieliwa akusonyeza kuti mzindawu uli m’dziko lophiphiritsa. Choncho zimenezi zikusonyeza kuti oyang’anirawa amatsogolera zochita za anthu a Mulungu. Kodi mfundo yoti mzindawu uli pamalo wamba kapena kuti malo omwe si opatulika ikutanthauza chiyani? Ikutikumbutsa kuti ulamulirowo sukuimira mzinda wakumwamba koma wa padziko lapansi umene wakhala ukuthandiza anthu onse amene ali m’paradaiso wauzimu.
9. (a) Kodi oyang’anira amenewa padziko lapansi pano ndi ndani? (b) Kodi Yesu adzachita chiyani mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000?
9 Kodi oyang’anira amenewa ndi ndani? M’masomphenya a Ezekieli, amene akutsogolera mzindawo akutchedwa “mtsogoleri.” (Ezek. 45:7) Iye anali woyang’anira pakati pa anthuwo koma sanali wansembe kapena wa fuko la Levi. Mtsogoleri ameneyu akutipangitsa kuganizira kwambiri za oyang’anira mumpingo masiku ano amene si odzozedwa ndi mzimu. Abusa achikondi amenewa omwe ali m’gulu la “nkhosa zina,” ndi atumiki odzichepetsa a boma lakumwamba lomwe wolamulira wake ndi Khristu. (Yoh. 10:16) Mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000, Yesu adzasankha komanso kuika akulu oyenerera kapena kuti “akalonga padziko lonse lapansi.” (Sal. 45:16) Ufumu wakumwamba udzathandiza akulu amenewa kuti azipereka zinthu zofunika kwa anthu a Mulungu mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu.
“Yehova Ali Kumeneko”
10. Kodi dzina la mzindawo ndi chiyani, nanga zimenezi zikutitsimikizira chiyani?
10 Werengani Ezekieli 48:35. Dzina la mzindawo ndi lakuti “Yehova Ali Kumeneko.” Dzina limeneli linkatsimikizira anthu okhala mumzindawo kuti Yehova adzakhala nawo. Posonyeza Ezekieli mzinda umenewo, umene unali pakati pa dzikolo, zinali ngati Yehova akuuza Ayuda amene anali ku ukapolo kuti: ‘Ndidzakhalanso nanu.’ Zimenezitu zinali zolimbikitsa kwambiri.
11. Kodi tikuphunzira chiyani m’masomphenya a Ezekieli okhudza mzinda ndi dzina lake losangalatsa?
11 Kodi tikuphunzira chiyani pa mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli? Dzina la mzinda umenewu, womwe ukuimira ulamuliro, likutsimikizira atumiki a Mulungu masiku ano kuti panopa Yehova amakhala ndi atumiki ake okhulupirika padziko lapansi ndipo adzakhala nawo mpaka kalekale. Dzina lapaderali likutsindikanso mfundo yofunika ya choonadi yakuti: Sikuti mzindawu ulipo kuti upereke mphamvu kwa munthu aliyense koma kuti uthandize anthu kutsatira njira za Yehova zomwe ndi zachikondi komanso zosavuta kutsatira. Mwachitsanzo, Yehova sanapereke udindo kwa oyang’anirawo kuti agawe dzikolo mmene anthu akufunira, titero kunena kwake. M’malomwake, Yehova amayembekezera kuti oyang’anirawo azilemekeza gawo kapena utumiki uliwonse umene iyeyo wapereka kwa atumiki ake kuphatikizapo ‘onyozeka.’—Miy. 19:17; Ezek. 46:18; 48:29.
12. (a) Kodi chochititsa chidwi ndi chiyani ndi mzinda umenewu, nanga kodi zimenezi zikuimira chiyani? (b) Kodi mbali imeneyi ya masomphenya ikukumbutsa oyang’anira a Chikhristu mfundo yofunika iti?
12 Kodi ndi chinthu china chiti chochititsa chidwi ndi mzinda wodziwika ndi dzina lakuti “Yehova ali Kumeneko”? Mizinda yakale inali ndi mipanda yachitetezo komanso mageti ochepa, koma mzinda uwu uli ndi mageti 12. (Ezek. 48:30-34) Kuchuluka kwa magetiwa (omwe analipo atatu mbali iliyonse ya mzindawo) kukusonyeza kuti oyang’anirawo anali osavuta kuwafikira ndipo mtumiki aliyense wa Mulungu akanatha kuwapeza mosavuta. Kuwonjezera pamenepo, mfundo yakuti mzindawo unali ndi mageti 12 ikusonyeza kuti “anthu a nyumba yonse ya Isiraeli” akanatha kulowa mumzindawo mosavuta. (Ezek. 45:6) Mfundo yoti zinali zosavuta kuti aliyense alowe mumzindawo ikukumbutsa oyang’anira a Chikhristu mfundo yofunika kwambiri. Yehova akufuna kuti anthu azikhala omasuka kufika kwa oyang’anira komanso kuti azipezeka mosavuta kwa onse amene akukhala m’paradaiso wauzimu.
Oyang’anira a Chikhristu amakhala osavuta kuwafikira ndipo amapezeka mosavuta (Onani ndime 12)
Anthu a Mulungu “Alowa Kudzalambira” Ndipo “Akugwira Ntchito Mumzinda”
13. Kodi Yehova anati chiyani za mautumiki osiyanasiyana amene anthu azidzachita?
13 Tiyeni tibwerere m’nthawi ya Ezekieli ndipo tione mfundo zina zimene akufotokoza m’masomphenya ochititsa chidwiwa zokhudza kugawa dziko. Yehova akutchula anthu amene akuchita mautumiki osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ansembe omwe ndi “atumiki apamalo opatulika,” ankayenera kupereka nsembe komanso kuyandikira kwa Yehova n’kumamutumikira. Alevi omwe anali “atumiki apakachisi,” ankayenera kuchita “utumiki wapakachisi ndi zinthu zonse zimene zikuyenera kuchitika mʼkachisimo.” (Ezek. 44:14-16; 45:4, 5) Kuwonjezera pamenepo, antchito ankagwira ntchito zosiyanasiyana pafupi ndi mzindawo. Kodi antchito amenewa ndi ndani?
14. Kodi anthu ogwira ntchito pafupi ndi mzinda akutikumbutsa chiyani?
14 Anthu ogwira ntchito pafupi ndi mzinda ankachokera “mʼmafuko onse a Isiraeli.” Iwo ankagwira ntchito zosiyanasiyana mumzindawo. Ntchito yawo inali yolima mbewu kuti “zizikhala chakudya cha amene akugwira ntchito mumzindawo.” (Ezek. 48:18, 19) Kodi zimenezi zikutikumbutsa mwayi umene tili nawo masiku ano? Inde. Masiku ano onse amene ali m’paradaiso wauzimu ali ndi mwayi wothandiza ntchito za abale ake a Khristu, omwe ndi odzozedwa, komanso ntchito za a “khamu lalikulu” amene Yehova wawapatsa udindo wotsogolera. (Chiv. 7:9, 10) Njira yaikulu imene timawathandizira ndi kumvera ndi mtima wonse malangizo ochokera kwa kapolo wokhulupirika.
15, 16. (a) Kodi m’masomphenya a Ezekieli tingapezemo mfundo zina ziti zofunika? (b) Kodi tili ndi mwayi uti wogwira nawo ntchito yofanana ndi imeneyi?
15 Masomphenya a Ezekieliwa ali ndi mfundo inanso imene ikutiphunzitsa chinthu chofunika kwambiri chokhudza utumiki wathu. Kodi mfundo yake ndi yotani? Yehova ananena kuti anthu ochokera m’mafuko 12 amene si Alevi adzakhala akugwira ntchito m’malo awiri: m’bwalo la kachisi komanso m’malo odyetsera ziweto amumzindawo. Kodi ntchito yawo ndi yotani m’malo onsewo? Mafuko onse ‘amalowa [m’bwalo la kachisi] kudzalambira’ popereka nsembe kwa Yehova. (Ezek. 46:9, 24) Anthu ochokera m’mafuko onse amabwera kudzathandiza pa ntchito zimene zikuchitika mumzindawo pogwira ntchito yolima m’malo amumzindawo. Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amene akugwira ntchito zimenezi?
16 Masiku ano a khamu lalikulu ali ndi mwayi wogwira ntchito zofanana ndi zimene zikuchitika m’masomphenya a Ezekieliwa. Iwo amalambira Yehova “mʼkachisi wake,” popereka nsembe zotamanda. (Chiv. 7:9-15) Iwo amachita zimenezi pogwira nawo ntchito yolalikira komanso posonyeza chikhulupiriro chawo mwa kupereka ndemanga pamisonkhano ya Chikhristu. Iwo amaona kuti chofunika kwambiri kwa iwo ndi kutumikira Yehova mwa njira imeneyi. (1 Mbiri 16:29) Kuwonjezera pamenepo, anthu ambiri a Mulungu amathandiza gulu la Mulungu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amathandiza pa ntchito zomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu komanso maofesi a nthambi ndiponso amathandiza nawo ntchito zina zambiri zimene gulu la Yehova likuchita. Ena amathandiza pa ntchito zimenezi popereka ndalama. Iwo amagwira ntchito imeneyi, yomwe tinganene kuti ili ngati ntchito yolima, kuti abweretse “ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Iwo amagwira ntchito mwakhama komanso mosangalala chifukwa akudziwa kuti Yehova “amasangalala ndi nsembe zoterozo.” (Aheb. 13:16) Kodi mukugwira nawo mokwanira ntchito zimenezi?
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Ezekieli anafotokoza zokhudza ntchito zosiyanasiyana zimene zinkachitika mkati ndi kunja kwa mzinda? (Onani ndime 14-16)
“Pali Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano Zimene Ife Tikuyembekezera”
17. (a) Kodi m’tsogolo tidzaona kukwaniritsidwa kwakukulu kuti kwa masomphenya a Ezekieli? (b) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi ndi ndani amene adzapindule ndi oyang’anira amene ali ngati mzinda?
17 Kodi m’tsogolo tidzaona kukwaniritsidwa kwakukulu kwa masomphenya a Ezekieli a chopereka? Inde. Ganizirani mfundo iyi: Ezekieli anaona kuti gawo la dzikolo limene linapatsidwa dzina lakuti “chopereka chopatulika,” linali pakati pa dzikolo. (Ezek. 48:10) Mofanana ndi zimenezi, pambuyo pa Aramagedo Yehova adzakhala nafe kulikonse kumene tingakhale. (Chiv. 21:3) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, oyang’anira amene ali ngati mzinda, amene apatsidwa udindo wosamalira anthu a Mulungu padziko lapansi, adzathandiza kuti madalitso a ufumuwa afike padziko lonse lapansi. Iwo adzachita zimenezi popereka malangizo achikondi kwa onse amene adzapange “dziko lapansi latsopano,” omwe ndi anthu okhala padziko lapansi amene Mulungu azidzasangalala nawo.—2 Pet. 3:13.
18. (a) N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti oyang’anira amene ali ngati mzinda azidzachita zinthu mogwirizana ndi ulamuliro wa Mulungu? (b) Kodi dzina la mzindawo likutitsimikizira mfundo yofunika iti?
18 N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti oyang’anira amene ali ngati mzinda adzachita zinthu mogwirizana ndi ulamuliro wa Mulungu? Chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kuti mzinda wapadziko lapansi, womwe uli ndi mageti 12, ukusonyeza mmene mzinda wakumwamba wokhala ndi mageti 12, womwe ndi Yerusalemu Watsopano ulili. Mzinda umenewu wapangidwa ndi anthu 144,000 amene adzalamulire limodzi ndi Khristu. (Chiv. 21:2, 12, 21-27) Zimenezi zikusonyeza kuti oyang’anira apadziko lapansi azidzatsatira ndi kuchita zimene Ufumu wa Mulungu kumwamba wasankha. Inde, dzina la mzinda lakuti “Yehova ali Kumeneko” likutsimikizira aliyense wa ife kuti kulambira koyera kudzapitiriza mpaka kalekale m’Paradaiso. M’tsogolomutu muli zabwino kwambiri.
-