Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 5/1 tsamba 3
  • Mavuto Kenako Mtendere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mavuto Kenako Mtendere
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Ana Opanda Kokhala—Kodi Pali Yankho?
    Galamukani!—1990
  • Chiphunzitso Chothandiza M’nthaŵi Zathu Zoŵaŵitsa
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 5/1 tsamba 3

Mavuto Kenako Mtendere

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.”​—2 TIMOTEYO 3:1.

N’KUTHEKA kuti munamvapo kapena kuona zinthu zomvetsa chisoni ngati izi:

● Matenda oopsa amene anapha anthu ambirimbiri.

● Anthu miyandamiyanda amene anafa chifukwa cha njala.

● Chivomezi choopsa chomwe chinapha anthu ambiri n’kusiya enanso ochuluka alibe nyumba.

Mu nkhani zotsatirazi muwerenga mfundo zimene zingakuthandizeni kuganizira mofatsa za mavuto osiyanasiyana ngati amenewa. Muonanso kuti Baibulo linalosera kuti zinthu zimenezi zidzachitika “m’masiku otsiriza.”a

Nkhanizi cholinga chake sikukutsimikizirani kuti tikukhala m’dziko lamavuto. Zili choncho chifukwa inuyo muyenera kuti mukudziwa kale za mavuto amenewa. Koma cholinga chake ndi kukuthandizani kuti mukhale ndi chiyembekezo. Nkhanizi zikuthandizani kuona kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi 6 amene tikambirane ndi umboni wakuti “masiku otsiriza” atsala pang’ono kutha. Nkhani zimenezi zifotokozanso zimene anthu ambiri amanena potsutsa maulosiwa ndiponso zitithandiza kudziwa chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti posachedwapa zinthu zikhala bwino.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika, werengani mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Padzikoli Pakhale Mavuto?” patsamba 16 ndi 17 m’magazini ino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena