Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthufe timakumana ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa pa moyo wathu. Kodi mukuganiza kuti zimene Yesu ananena palemba ili ndi zothandiza masiku ano? [Werengani Mateyu 6:25 kenako yembekezerani kuti ayankhe.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuchepetsa nkhawa zimene zimayamba chifukwa chosowa ndalama, mavuto a m’banja komanso zinthu zina zoopsa.”
Galamukani! July
“Masiku ano anthu ambiri amada nkhawa chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo. Kodi inunso mumaona choncho? [Yembekezerani ayankhe.] Baibulo limanena kuti zimene timachita tikakumana ndi mavuto zikhoza kutithandiza kupirira kapena ayi. [Werengani Miyambo 24:10.] Magazini iyi ili ndi malangizo amene angatithandize ngati titakumana ndi mavuto aakulu. Komanso ikufotokoza zimene anthu ena akuchita kuti apirire mavuto amene akukumana nawo.”