MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzikumbukira Malemba
Kodi nthawi zina zimakuvutani kukumbukira lemba limene mumalikonda? Likhoza kukhala lemba limene limakulimbikitsani, limakuthandizani kupewa maganizo olakwika kapenanso limene mukufuna kufotokozera mnzanu. (Sal. 119:11, 111) Tiyeni tione zina zimene zingakuthandizeni kuti muzikumbukira malemba.
Muzigwiritsa ntchito matagi mu JW Library®. Mukhoza kukonza tagi n’kuilemba kuti “Malemba Amene Ndimakonda,” ndipo muzisungako malemba amene mukufuna muziwakumbukira.
Muzisunga malemba pamalo omwe mungathe kuwaona. Muzilemba papepala vesi limene mukufuna muzilikumbukira ndipo muziliika pamalo omwe mungathe kuliona mosavuta. Ena amaika pagalasi kapena pafiliji, pomwe ena amajambula lembalo n’kuliika ngati chithunzi kuti lizionekera akatsegula foni kapena kompyuta yawo.
Muzigwiritsa ntchito makadi. Muzilemba vesilo mbali ina n’kulemba mawu ake kuseri kwake. Kenako muziyesa kuona lembalo n’kutchula mawu ake kapena kuona mawuwo n’kutchula lemba lake.