Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/09 tsamba 2
  • Kugwiritsa Ntchito Baibulo Mwaluso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Baibulo Mwaluso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzikumbukira Malemba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 3:
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Kodi Mumadalira Mawu a Mulungu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kulimbikitsa Omvera Kuŵerenga Baibulo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 9/09 tsamba 2

Kugwiritsa Ntchito Baibulo Mwaluso

1. Kodi Baibulo ndi lofunika bwanji?

1 Kugwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tizilalikira ndi kuphunzitsa choonadi momveka bwino komanso kutsutsa ziphunzitso zonama ndi miyambo ya anthu.—2 Tim. 2:15; 1 Pet. 3:15.

2. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizitha kupeza malemba mosavuta?

2 Yesetsani Kulidziwa Bwino Baibulo: Kuti mudziwe kugwiritsa ntchito bwino chipangizo chinachake, mumafunikira kuchidziwa bwino. Kuwerenga Baibulo lonse kumathandiza kuti mukhale ndi chithunzi cha mutu wankhani wa Baibulo lonse. Kumathandizanso kuti muzikumbukira malemba ndi kuwapeza mosavuta. Mukadziwa bwino Malemba, mumatha kulankhula motsimikiza mukamalalikira ena mwamwayi kapena mukakhala mu utumiki wakumunda.—1 Ates. 1:5.

3, 4. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite kuti tilidziwe bwino Baibulo? (b) Kodi n’chiyani chimene chakuthandizani inuyo kuti muzidziwa kwambiri Malemba?

3 Yesetsani kukhala ndi chizolowezi chotsegula ndi kuwerenga Baibulo mukakhala pamisonkhano yampingo. Mukamaphunzira Baibulo panokha ndiponso mukamakonzekera misonkhano, muziwerenga Malemba a m’nkhanizo ndi kusinkhasinkha mmene mungawagwiritsire ntchito. Ena aona kuti kuwerenga malemba pogwiritsa ntchito Baibulo lenileni kumawathandiza kuti azitha kupeza malemba mosavuta akakhala mu utumiki kusiyana ndi kuwerenga Baibulo pakompyuta.—Yoh. 14:26.

4 Mabanja ena amakhala ndi nthawi yoloweza malemba. Amachita zimenezi pogwiritsa ntchito makadi okhala ndi lemba mbali imodzi ndi mawu a lembalo mbali ina. Amafunsana kuti wina atchule mawu a m’lemba linalake kapena amapatsidwa mawu kuti atchule lemba lake. Kukonzekera ulaliki ndiponso kuyankha mafunso pogwiritsa ntchito Baibulo kumathandizanso kuti mulidziwe bwino Baibulo.

5. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ndi luso logwiritsa ntchito Baibulo?

5 Palibe buku lina lililonse limene lingafanane ndi Baibulo, chifukwa Baibulo ndi buku lokhalo limene lingapatse munthu ‘nzeru za mmene angapezere chipulumutso.’ (2 Tim. 3:15) Popeza anthu ambiri sadziwa kuti m’Baibulo muli chuma chamtengo wapatali, ifeyo tiyenera kuyesetsa kukhala ndi luso logwiritsa ntchito Baibulo n’cholinga choti tiwasonyeze zinthu zimene zimapezeka m’bukuli.—Miy. 2:1-5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena