Macitidwe a Atumwi
2 Tsopano patsiku la cikondwelelo ca Pentekosite, onse anasonkhana pamalo amodzi. 2 Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka phokoso monga la mkokomo wa mphepo yamphamvu. Phokoso lake linadzaza nyumba yonse imene iwo analimo. 3 Ndiyeno iwo anaona malawi a moto ooneka ngati malilime ndipo anagawikana n’kukhala pa aliyense wa iwo limodzi limodzi. 4 Onse anadzazidwa ndi mzimu woyela, ndipo anayamba kukamba zinenelo zosiyanasiyana,* monga mmene mzimuwo unawacititsila kulankhula.
5 Panthawiyo, Ayuda oopa Mulungu ocokela m’mitundu yonse pa dziko lapansi, anali kukhala ku Yerusalemu. 6 Conco phokosolo litamveka, khamu la anthu linasonkhana, ndipo anadabwa kwambili cifukwa aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’cinenelo cake. 7 Iwo anadabwa kwambili cakuti anayamba kufunsana kuti: “Taonani, anthu onsewa amene akulankhula ndi Agalileya, si conco? 8 Nanga zikutheka bwanji kuti aliyense wa ife azimva cinenelo cake?* 9 Pakati pathu pali Apati, Amedi, Aelamu, anthu ocokela ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto, ndi ku cigawo ca Asia. 10 Palinso anthu ocokela ku Fulugiya, Pamfuliya, ku Iguputo, ndi kumadela a ku Libiya, amene ali pafupi ndi Kurene. Ndipo palinso alendo ocokela ku Roma ndi Ayuda, komanso anthu otembenukila ku Ciyuda, 11 Akerete, komanso a Arabu. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenelo zathu.” 12 Inde, onsewa anadabwa kwambili ndipo anathedwa nzelu, moti anali kufunsana kuti: “Kodi zocitika izi zikutanthauza ciyani?” 13 Koma ena anali kuwaseka ndipo anali kukamba kuti: “Amenewa aledzela ndi vinyo watsopano.”
14 Koma Petulo anaimilila pamodzi ndi atumwi 11 aja, n’kulankhula nawo mokweza mawu kuti: “Anthu inu a ku Yudeya, komanso onse okhala ku Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetselani mosamala mawu anga. 15 Anthu awa sanaledzele monga mmene mukuganizila, cifukwa apa ndi m’mawa ndipo nthawi ili ca m’ma 9 koloko.* 16 Koma zimene zacitikazi n’zimene mneneli Yoweli ananenelatu kuti: 17 ‘Mulungu anati, “Ndipo m’masiku otsiliza, ndidzapungulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse, ndipo ana anu aamuna komanso ana anu aakazi adzalosela. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna okalamba adzalota maloto. 18 Ndidzapungulilanso mzimu wanga ngakhale pa akapolo anga aamuna ndi akapolo anga aakazi m’masiku amenewo, ndipo iwo adzalosela. 19 Ndidzacita zodabwitsa* kumwamba, komanso zizindikilo pa dziko lapansi. Padzakhala magazi, moto, ndi utsi watolotolo. 20 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu komanso laulemelelo la Yehova lisanafike. 21 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”’
22 “Amuna inu a mu Isiraeli, mvelani mawu awa: Yesu Mnazareti, ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyela kudzela mu nchito za mphamvu, zodabwitsa, ndi zizindikilo zimene Mulungu anacita pakati panu kupitila mwa iye, monga mmene inu mukudziwila. 23 Mulungu anadziwilatu pasadakhale kuti Yesu adzapelekedwa. Conco, cinali cifunilo cake. Inu munamukhomelela pamtengo pogwilitsa nchito anthu osamvela malamulo, ndipo munamupha. 24 Koma Mulungu anamuukitsa pomumasula ku zowawa* za imfa cifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwile mwamphamvu. 25 Pakuti Davide anakamba za iye kuti: ‘Nthawi zonse ndimaika Yehova patsogolo panga,* cifukwa iye ali kudzanja langa lamanja kuti ndisagwedezeke. 26 Pa cifukwa cimeneci, mtima wanga unasangalala ndipo n’nalankhula mokondwela kwambili. Ndiponso ine ndidzakhala ndi ciyembekezo, 27 cifukwa simudzandisiya m’Manda,* kapena kulola kuti thupi la munthu wokhulupilika kwa inu liwole. 28 Mwandidziwitsa njila za moyo, ndipo ndikakhala nanu pafupi* mudzacititsa kuti ndisangalale kwambili.’
29 “Amuna inu, abale, ndiloleni ndilankhule mwaufulu za kholo lathu Davide. Iye anamwalila ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake tili nawo mpaka lelo. 30 Popeza iye anali mneneli, ndipo anali kudziwa kuti Mulungu anamulonjeza mwakucita kulumbila kuti pa mpando wake wacifumu adzaikapo mmodzi wa mbadwa zake, 31 anaonelatu pasadakhale ndipo anakambilatu za kuuka kwa Khristu kuti sadzasiyidwa m’Manda,* ndipo thupi lake silidzawola. 32 Mulungu anaukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife tonse ndife mboni za nkhani imeneyi. 33 Conco, cifukwa cakuti iye anakwezedwa n’kukhala kudzanja lamanja la Mulungu ndipo analandila mzimu woyela umene Atate analonjeza, iye ndiye watipatsa* mzimu woyela malinga ndi zimene mukuona ndi kumva. 34 Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35 kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’ 36 Conco nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphela pamtengo, Mulungu anamuika kukhala Ambuye komanso Khristu.”
37 Anthuwo atamva mawu amenewo anakhudzika mtima kwambili* moti anafunsa Petulo ndi atumwi ena onse kuti: “Amuna inu, abale, ndiye ticite ciyani?” 38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti macimo anu akhululukidwe. Mukacita izi, mudzalandila mphatso ya mzimu woyela kwaulele. 39 Cifukwa lonjezoli lipita kwa inu, kwa ana anu, komanso kwa anthu onse okhala kutali, onse amene Yehova Mulungu wathu angawaitane.” 40 Ndi mawu enanso ambili, Petulo anacitila umboni mokwanila, komanso anapitiliza kuwadandaulila kuti: “Dzipulumutseni ku m’badwo uwu wa maganizo opotoka.” 41 Cotelo amene analandila mawu ake mokondwela anabatizidwa. Moti pa tsikulo, anthu amene anawonjezekawo anali pafupifupi 3,000. 42 Iwo anapitiliza kutsatila zimene atumwi anali kuphunzitsa, ndipo anali kucezela pamodzi,* kudyela pamodzi, komanso kupemphela.
43 Anthu onse anayamba kucita mantha, ndipo atumwi anayamba kucita zodabwitsa ndi zizindikilo zambili. 44 Onse amene anakhala okhulupilila anali kukhala pamodzi ndipo anali kugawana zonse zimene anali nazo. 45 Iwo anali kugulitsa malo ndi zinthu zina zimene anali nazo, ndipo ndalama zake anali kugawila onse malinga ndi zosowa zawo. 46 Tsiku lililonse anali kusonkhana m’kacisi mogwilizana. Iwo anali kudyela pamodzi cakudya m’nyumba zawo. Ndipo anali kugawana cakudya cawo mokondwela kwambili komanso ndi mtima wonse. 47 Analinso kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda. Panthawi imodzimodzi, Yehova tsiku lililonse anapitiliza kuwonjezela anthu amene anali kuwapulumutsa.