Kwa Aefeso
5 Conco muzitengela Mulungu monga ana ake okondedwa. 2 Ndipo pitilizani kukondana ngati mmene Khristu anatikondela,* n’kudzipeleka yekha cifukwa ca ife* ngati copeleka, ndiponso ngati nsembe ya pfungo lokoma kwa Mulungu.
3 Nkhani za ciwelewele* komanso conyansa ca mtundu uliwonse, kapena umbombo, zisachulidwe n’komwe pakati panu, cifukwa anthu oyela sayenela kucita zimenezi. 4 Musachulenso nkhani zokhudza khalidwe locititsa manyazi, nkhani zopusa, kapena nthabwala zotukwana, cifukwa ndi zinthu zosayenela. M’malomwake, muziyamika Mulungu. 5 Pakuti mfundoyi mukuidziwa ndi kuimvetsa bwino, kuti munthu waciwelewele,* wodetsedwa, kapena waumbombo, kumene ndi kulambila mafano, sadzalowa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.
6 Munthu aliyense asakupusitseni ndi mau opanda pake, cifukwa ana osamvela amene akucita zinthu zimene ndachulazi, mkwiyo wa Mulungu udzawafikila. 7 Conco musamacite zimene iwo amacita.* 8 Cifukwa poyamba munali mdima, koma tsopano ndinu kuwala, popeza muli mu mgwilizano ndi Ambuye. Pitilizani kuyenda monga ana a kuwala. 9 Cifukwa zipatso za kuwala ndi ciliconse cabwino, colungama, ndi coona. 10 Nthawi zonse muzitsimikizila kuti cobvomelezeka kwa Ambuye n’citi. 11 Ndipo musiye kucita nao nchito zosapindulitsa za mumdima. M’malomwake, muzizibvumbulilatu kuti n’zoipa. 12 Cifukwa zimene iwo amacita mseli ndi zocititsa manyazi ngakhale kuzichula. 13 Tsopano zinthu zonse zimene zabvumbulidwa* zimaonekela poyela cifukwa ca kuwala, popeza ciliconse cimene caonekela cimakhala kuwala. 14 N’cifukwa cake pali mau akuti: “Uka, wogona iwe! Uka kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.”
15 Conco samalani kuti mmene mukuyendela, si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anthu anzelu. 16 Muziigwilitsa nchito bwino nthawi yanu* cifukwa masikuwa ndi oipa. 17 Pa cifukwa cimeneci, lekani kucita zinthu ngati anthu opanda nzelu, koma pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova. 18 Ndiponso musaledzele ndi vinyo, cifukwa m’kuledzela muli makhalidwe otayilila. Koma pitilizani kudzazidwa ndi mzimu. 19 Muziimbila limodzi masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba motsagana ndi malimba nyimbo zotamanda Yehova m’mitima yanu. 20 Nthawi zonse muziyamika Mulungu Atate wathu pa zinthu zonse m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.
21 Muzigonjelana poopa Khristu. 22 Akazi azigonjela amuna ao ngati kuti akugonjela Ambuye, 23 popeza mwamuna ndi mutu wa mkazi wake monga mmene Khristu alili mutu wa mpingo. Pajanso iye ndiye mpulumutsi wa thupi limeneli. 24 Ndipo monga mmene mpingo umagonjelela Khristu, naonso akazi azigonjela amuna ao pa ciliconse. 25 Inu amuna, pitilizani kukonda akazi anu ngati mmene Khristu anakondela mpingo mpaka kufika podzipeleka kaamba ka mpingowo, 26 kuti auyeletse pousambika m’madzi a mau a Mulungu. 27 Anatelo kuti iye alandile mpingowo uli wokongola ndiponso waulemelelo, wopanda banga, makwinya, kapenanso ciliconse cofanana ndi zimenezi, koma kuti ukhale woyela ndi wopanda ulemali.
28 Mofananamo, amuna azikonda akazi ao monga mmene amakondela matupi ao. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29 cifukwa palibe munthu amene anadanapo ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulicengeta, monga mmene Khristu amacitila ndi mpingo, 30 popeza ndife ziwalo za thupi lake. 31 “Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake ndi amai ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi.” 32 Cinsinsi copatulikaci n’cacikulu. Apa ndikunena za Khristu ndi mpingo. 33 Komabe, aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.