Ziŵelengelo Zonse za mu 2022
Nthambi za Mboni za Yehova: 86
Ciŵelengelo ca Maiko Ocitila Lipoti: 239
Ciŵelengelo ca Mipingo Yonse: 117,960
Opezeka pa Cikumbutso Padziko Lonse: 19,721,672
Amene Anadya Ziphiphilitso Padziko Lonse: 21,150
Ofalitsaa Onse Amene Anagwila Nchito Yolalikila: 8,699,048
Avaleji ya Ofalitsa Amene Anali kulalikila Mwezi Uliwonse: 8,514,983
Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Kucokela mu 2021: 0.4
Onse Amene Anabatizikab: 145,552
Avaleji ya Apainiyac Mwezi Uliwonse: 1,465,202
Avaleji ya Apainiya Othandiza Mwezi Uliwonse: 381,310
Maola Onse Amene Tinathela mu Utumiki: 1,501,797,703
Avaleji ya Maphunzilo a Baibod Mwezi Uliwonse: 5,666,996
M’caka ca utumiki ca 2022,e Mboni za Yehova zinaseŵenzetsa ndalama zoposa madola 242 miliyoni posamalila apainiya apadela, amishonale komanso oyang’anila madela pa utumiki wawo. Padziko lonse pali abale na alongo okwana 21,629, amene akutumikila m’maofesi a nthambi. Onse amenewa ali m’Gulu la Padziko Lonse la Atumiki Apadela a Nthawi Zonse a Mboni za Yehova.
a Wofalitsa ni munthu amene amalalikila mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuti mudziŵe mmene timapezela ciŵelengeloci, onani nkhani yakuti “Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?” pa jw.org ku Chichewa.
b Kuti mudziŵe zimene mungacite kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?” pa jw.org ku Chichewa.
c Mpainiya ni wa Mboni wacitsanzo cabwino amene amadzipeleka kuti azilalikila uthenga wabwino kwa maola ena ake mwezi uliwonse.
d Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani ya pa jw.org yakuti, “Kodi Phunzilo la Baibulo N’ciani?”
e Caka ca utumiki ca 2022 cinayamba pa September 1, 2021, ndipo cinasila pa August 31, 2022.