Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Tizilemba Tikapeza Anthu Acidwi
“Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:16) Uphungu wouzilidwa umenewu umene Mtumwi Paulo anapeleka kwa Timoteyo, umaonetsa kuti tiyenela kupita patsogolo kaya ndife atsopano kapena aciyamba kale. Potithandiza kucita zimenezo, nkhani zatsopano za mutu wakuti, “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki” zidzayamba kupezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nkhani iliyonse izifotokoza njila yofunika, ndipo izikhala ndi malangizo ofotokoza mmene tingakulitsile luso lathu. M’mwezi umenewo, tonse tidzalimbikitsidwa kugwilitsila nchito njila imeneyo mosamalitsa. Kumapeto kwa mwezi, Msonkhano wa Nchito uzikhala ndi nkhani imene izitipatsa mpata wofotokoza mmene tinapindulila cifukwa cogwilitsila nchito njila imeneyo. Mwezi uno tikulimbikitsidwa kugwilitsila nchito njila yakuti, tizilemba tikapeza anthu acidwi.
Cifukwa Cake N’kofunika: Kuti tikwanilitse nchito yathu tiyenela kucita zambili koposa kulalikila cabe. Tifunika kubwelelako kwa amene anaonetsa cidwi kuti tiwaphunzitse, ndi kuthilila mbeu za coonadi zimene tinabzala. (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 3:6-9) Zimenezo zitanthauza kupezanso munthuyo, kukambitsilana naye nkhawa zake, ndi kupitiliza makambilano athu. Conco, tikapeza anthu acidwi ndi bwino kulemba.
Mmene Tingacitile:
• Tsimikizilani kuti m’cola canu mwanyamula zonse zofunikila kuti muzilemba mukapeza anthu acidwi. Khalani ndi buku lolembamo labwino ndipo lembani zonse zofunikila mwadongosolo. Ndipo tizilemba tikangomaliza kukambitsilana.
• Lembani zonse zokhudza mwininyumba. Lembani dzina lake, adilesi, nambala ya foni, kapena imelo yake. Kodi n’ciani cimene mwaona cokhudza munthuyo ndi banja lake cimene mungalembe?
• Lembani zonse zimene munakambitsilana. Kodi munaŵelenga naye malemba ati? Kodi amakhulupilila zotani? Kodi munamugaŵila mabuku ati? Lembani nthawi, tsiku ndi deti limene munaceza naye.
• Lembani zimene mwalinganiza paulendo wotsatila. Kodi munapangana kuti mudzakambitsilana ciani? Kodi munalonjeza kuti mudzabwelelako liti?
• Nthawi iliyonse mukabwelelako muzilemba m’buku lanu. Palibe kulakwika kulikonse ngati mwalemba zinthu zambili zimene mufuna.
Yesani kucita izi mwezi uno:
• Polemba za munthu wacidwi, uzani amene mulalikila nao zimene mukulembazo.