Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda July-August
“Mukanakhala ndi mphamvu zothetsa mavuto m’dzikoli, kodi mukanathetsa vuto liti? [Yembekezani yankho.] Baibulo limanena kuti posacedwapa, Mulungu adzathetsa vuto limeneli ndi ena ambili. [Ŵelengani lemba logwilizana ndi vuto limene wakamba, monga Danieli 2:44; Miyambo 2:21, 22; Mateyu 7:21-23 kapena 2 Petulo 3:7.] Magazini iyi ifotokoza nthawi imene Mulungu adzathetsa mavuto pa dziko lapansi ndi mmene adzawathetsela.”
Galamukani! September
“Tonse timadziŵa kuti ndalama n’zofunika pa umoyo wathu. Koma kodi muganiza kuti pangakhale ngozi iliyonse ngati munthu amakonda kwambili ndalama? [Yembekezani yankho.] Onani cenjezo limene Baibulo limapeleka. [Ŵelengani 1 Timoteyo 6:9.] Magazini iyi ifotokoza mmene tingakhalile ndi maganizo oyenela pa nkhani ya ndalama.”