LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 July masa. 2-7
  • Khalani Wolimba Mtima Monga Zadoki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalani Wolimba Mtima Monga Zadoki
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KHALANI KUMBALI YA UFUMU WA MULUNGU
  • THANDIZANI ABALE NA ALONGO ANU
  • KHALANIBE WOKHULUPILIKA KWA YEHOVA
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 July masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 27

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

Khalani Wolimba Mtima Monga Zadoki

“Zadoki, [anali] mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima.”—1 MBIRI 12:28.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuona mmene citsanzo ca Zadoki cingatithandizile kukhala olimba mtima.

1-2. Kodi Zadoki anali ndani? (1 Mbiri 12:​22, 26-28)

YELEKEZANI kuti mukuciona cocitika cokopa cidwi ici: Namtindi wa amuna opitilila 340,000 anasonkhana ku mapili pafupi na mzinda wa Heburoni, pa mwambo womulonga ufumu Davide, kuti akhale mfumu ya mtundu wonse wa Aisiraeli. Kwa masiku atatu, phokoso la makambilano acisangalalo, nyimbo zokondwa komanso zacitamando, komanso la kuseka na kusekelela, linali kumveka mpaka kumapili ozungulila. (1 Mbiri 12:39) Pa gululo panali mnyamata wina dzina lake Zadoki, amene mwina sanali wodziŵika kwenikweni. Komabe, Yehova anafuna kuti tidziŵe kuti Zadoki analipo. (Ŵelengani 1 Mbiri 12:​22, 26-28.) Kodi Zadoki anali ndani?

2 Zadoki anali wansembe yemwe anali kuseŵenzela pamodzi na Mkulu wa Ansembe Abiyatara. Zadoki anali mneneli, ndipo Mulungu anam’patsa nzelu zapadela kuti athe kuzindikila cifunilo cake. (2 Sam. 15:27) Anthu anali kupita kwa Zadoki kukapezako ulangizi wanzelu. Cina, iye anali mwamuna wolimba mtima. Ili ndilo khalidwe lake limene tikambilane m’nkhani ino.

3. (a) N’cifukwa ciyani alambili a Yehova ayenela kukhala olimba mtima? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Masiku otsiliza ano, Satana akuyesetsa mwamphamvu kuti awononge cikhulupililo cathu mwa Mulungu. (1 Pet. 5:8) Tiyenela kukhala olimba mtima pamene tiyembekezela Yehova kuti akawononge Satana na dongosolo lake loipali. (Sal. 31:24) Tiyeni tikambilane njila zitatu zimene tingatengele kulimba mtima kwa Zadoki.

KHALANI KUMBALI YA UFUMU WA MULUNGU

4. N’cifukwa ciyani atumiki a Yehova ayenela kulimba mtima kuti akhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu? (Onaninso cithunzi.)

4 Monga anthu a Mulungu, timakhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu na mtima wonse. Koma kucita izi nthawi zambili kumalila kulimba mtima. (Mat. 6:33) Mwa citsanzo, timafunika kukhala olimba mtima kuti titsatile malamulo a Yehova na kulalikila uthenga wabwino m’dziko loipali. (1 Ates. 2:2) Ndipo nthawi zambili timafunika kulimba mtima kuti tisakhalile mbali m’zandale m’dongosolo logaŵikana lino. (Yoh. 18:36) Atumiki ambili a Yehova amakumana na mavuto azacuma, kumenyedwa, kapena kuponyedwa m’ndende cifukwa cokana kutengako mbali m’ndale kapena kuloŵa usilikali.

Pa nthawi yopuma ku nchito, m’bale ali na anchito anzake aŵili amene akufotokoza mwamphamvu maganizo awo. Mmodzi mwa anzakewo akuloza pa TV pomwe pakuonetsa zotulukapo za masankho.

Kodi mudzacita bwanji anthu ena akamakhalila mbali m’zandale? (Onani ndime 4)


5. N’cifukwa ciyani Zadoki anafunika kulimba mtima kuti athandize Davide?

5 Zadoki sanapite ku Heburoni kukangokondwelela kulongedwa ufumu kwa Davide. Iye anapita kumeneko atanyamula zida zake, ndipo anali wokonzeka kumenya nkhondo. (1 Mbiri 12:38) Iye anali wokonzeka kupita na Davide ku nkhondo kuti akateteze Isiraeli kwa adani ake. Ngakhale kuti Zadoki sanali ciyambakale pa zankhondo, anali munthu wolimba mtima kwambili.

6. Kodi Davide anapeleka motani citsanzo cabwino cokhala wolimba mtima kwa Zadoki? (Salimo 138:3)

6 Kodi wansembe Zadoki anaphunzila kwa ndani kukhala wolimba mtima? Iye anali kupezeka pakati pa amuna amphamvu komanso olimba mtima. Mosakaikila iye anaphunzila kwa iwo poona citsanzo cawo. Mwa citsanzo, cifukwa Davide anali ‘kutsogolela Aisiraeli ku nkhondo’ molimba mtima, Aisiraeli onse anafuna kumulonga ufumu. (1 Mbiri. 11:​1, 2) Davide nthawi zonse anali kudalila thandizo la Yehova kuti agonjetse adani ake. (Sal. 28:7; ŵelengani Salimo 138:3.) Zadoki anaphunzilanso ku zitsanzo za amuna ena olimba mtima monga Yehoyada na mwana wake Benaya amene anali msilikali. Anaphunzilanso zambili kwa atsogoleli 22 a m’nyumba ya bambo ake amene anali kumbali ya Davide. (1 Mbiri 11:​22-25; 12:​26-28) Amuna onsewa anacita zonse zotheka kuti athandize Davide kukhala mfumu.

7. (a) Ni zitsanzo ziti za kulimba mtima zimene tingatengeleko? (b) Kodi munaphunzila ciyani m’citsanzo ca M’bale Nsilu monga mmene munaonela mu vidiyo?

7 Timapeza mphamvu na kukhala olimba mtima tikaganizila zitsanzo za anthu omwe anakhala kumbali ya ufumu wa Mulungu molimba mtima. Mfumu yathu, Khristu Yesu, anakanilatu kumunyengelela kuti atengeko mbali m’zandale za m’dziko la Satanali. (Mat. 4:​8-11; Yoh. 6:​14, 15) Nthawi zonse anadalila Yehova kuti amupatse mphamvu. Masiku ano tilinso na zitsanzo za acinyamata amene akana molimba mtima kuloŵa usilikali kapena kutengako mbali m’zandale. Mungacite bwino kuonako zina mwa nkhanizi pa jw.org.a

THANDIZANI ABALE NA ALONGO ANU

8. Ni pa zocitika ziti pamene akulu afunika kulimba mtima kuti apeleke thandizo lofunikila kwa abale na alongo?

8 Anthu a Mulungu amakonda kuthandizana wina na mnzake. (2 Akor. 8:4) Komabe nthawi zina zimafunikila kulimba mtima kuti ticite zimenezi. Mwa citsanzo, nkhondo ikabuka, akulu amazindikila kuti abale na alongo awo amafunikila cilimbikitso, thandizo la kuthupi komanso lauzimu. Cifukwa ca cikondi cawo pa nkhosa, akulu amaika miyoyo yawo pa ciopsezo kuti apeleke zofunikila kwa nkhosazo. (Yoh. 15:​12, 13) Mwa kutelo, amatengela kulimba mtima kwa Zadoki.

9. Malinga na 2 Samueli 15:​27-29, kodi Davide anauza Zadoki kuti acite ciyani? (Onaninso cithunzi.)

9 Moyo wa Davide unali pa ciopsezo. Mwana wake Abisalomu anali atatsimikiza mtima kuti amulanda ufumu basi. (2 Sam. 15:​12, 13) Davide anafunika kuthaŵa kucoka mu Yerusalemu nthawi yomweyo! Iye anauza atumiki ake kuti: “Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithaŵe, cifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu.” (2 Sam. 15:14) Pomwe atumiki ake anali kucoka, Davide anazindikila kuti afunika kusiya m’mbuyo mmodzi wa atumiki ake kuti azimuuza mapulani a Abisalomu. Conco iye anatuma Zadoki na ansembe ena kuti abwelele mu mzinda kukakhala ngati akazitape. (Ŵelengani 2 Samueli 15:​27-29.) Iwo anafunika kugwila nchito imeneyi mosamala kwambili. Zimene Davide anauza ansembewo kucita zinali zoopsa ndipo zikanaika miyoyo yawo pa ciopsezo. Ganizilani zimene Abisalomu—amene anali munthu wankhanza, wodzikuza, komanso wodzikonda—akanacita kwa Zadoki na ansembe ena akanazindikila kuti iwo anali akazitape a Davide!

Mfumu Davide akulankhula na Zadoki pamene atumiki ake ena akucoka mu Yerusalemu.

Davide anatuma Zadoki kucita nchito yoopsa kwambili (Onani ndime 9)


10. Kodi Zadoki na amene anali naye, anateteza motani moyo wa Davide?

10 Davide anauza Zadoki komanso mnzake wina wokhulupilika Husai kuti amuthandize na pulani imene anapanga. (2 Sam. 15:​32-37) Potsatila pulaniyo Husai anakwanitsa kukhala phungu wodalilika wa Abisalomu, ndipo anamupatsa pulani ya mmene angam’thilile nkhondo Davide. Koma pulaniyo kwenikweni inali kupeleka mpata kwa Davide wokonzekela kuukilako. Kenako Husai anauza Zadoki komanso Abiyatara za pulani imene anauza Abisalomu. (2 Sam. 17:​8-16) Ndipo amuna aŵili amenewa anatumiza uthengawo kwa Davide. (2 Sam. 17:17) Na thandizo la Yehova, Zadoki komanso ansembe ena anacita mbali yaikulu poteteza moyo wa Davide.—2 Sam. 17:​21, 22.

11. Tingatsatile bwanji citsanzo ca kulimba mtima kwa Zadoki pamene tikuthandiza abale athu?

11 Kodi tingakhale bwanji olimba mtima monga Zadoki, akatipempha kuti tithandize abale m’nthawi yovuta? (1) Tsatilani malangizo. Pa nthawi zovuta ngati zimenezo tifunikila tizikhalabe ogwilizana. Tsatilani malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Akulu nthawi zonse ayenela kumabwelelamo m’malangizo kuti azikhala okonzeka komanso odziŵa mocitila tsoka likagwa. (1 Akor. 14:​33, 40) (2) Khalani olimba mtima komabe osamala. (Miy. 22:3) Ganizilani mofatsa musanacitepo kanthu. Musaike moyo wanu pa ciopsezo mwadala. (3) Dalilani Yehova. Kumbukilani kuti Yehova amasamala kwambili za moyo wanu komanso wa abale amene mufuna kuthandiza. Iye angakuthandizeni kuti mupeleke thandizo kwa abale anu muli otetezeka.

12-13. Mwaphunzilapo ciyani pa cocitika ca Viktor na Vitalii? (Onaninso cithunzi.)

12 Ganizilani za abale aŵili, Viktor na Vitalii, omwe ni akulu amene anathandiza abale na alongo awo ku Ukraine. Viktor anati, “Tinali kupita kukafuna-funa cakudya ku malo osiyana-siyana, ndipo nthawi zambili tinali kumva anthu akuwombelana mfuti pafupi nafe. M’bale wina anapeleka cakudya ca m’sitolo yake. Copeleka cimeneci cinathandiza abale na alongo ambili kwakanthawi ndithu kuti akhale na cakudya. Tikulongeza zakudyazo m’motoka yathu, bomba inaphulika pa mtundu wa mamita 20. Pa tsiku lonselo n’nacondelela Yehova kuti anithandize kukhala wolimba mtima kuti nipitilize kuthandiza abale na alongo.”

13 Vitalii anati, “Kucita izi kunafuna kulimba mtima zedi. Ulendo wanga woyamba unatenga maola 12. N’napemphela kwa Yehova paulendo wonsewo.” Vitalii anali wolimba mtima komanso wosamala. Iye anawonjezela kuti: “N’napitiliza kupempha kuti Yehova anipatse nzelu, na kutinso nikhale wodzicepetsa. Poyendetsa motoka n’nali kungoyenda m’misewu imene boma linavomeleza. Napindula ngako podzionela nekha mmene abale na alongo amaseŵenzela pamodzi mogwilizana. Iwo anali kucotsa zinthu zochinga m’misewu, kusonkhanitsa zakudya, zovala, na zinthu zina zofunika na kuzilonga m’motoka yathu.”

Abale aŵili akuyendetsa motoka kudela kumene kuli nkhondo. Kumbuyo kwawo kuli zinthu zowonongeka, utsi, komanso moto.

Khalani wolimba mtima koma wosamala pothandiza abale anu m’nthawi zoopsa (Onani ndime 12-13)


KHALANIBE WOKHULUPILIKA KWA YEHOVA

14. Timakhudzika bwanji munthu amene timakonda akaleka kutumikila Yehova?

14 Ena mwa mayeso ovuta kwambili kuwapilila, ni pamene wa m’banja mwathu kapena mnzathu wapamtima waleka kutumikila Yehova. (Sal. 78:40; Miy. 24:10) Ngati munthuyo tinali naye pa ubale wolimba, zimakhala zovuta kwambili kupilila. Za conco zikakucitikilani, kukumbukila citsanzo ca kukhulupilika ca Zadoki kungakulimbikitseni.

15. N’cifukwa ciyani Zadoki anafunikila kulimba mtima kuti akhalebe wokhulupilika kwa Yehova? (1 Maf. 1:​5-8)

15 Zadoki anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova pamene mnzake wapamtima Abiyatara anapandukila Yehova. Izi zinacitika ca kumapeto kwa ulamulilo wa Davide. Davide atakalamba komanso atatsala pang’ono kumwalila, mwana wake Adoniya anayesa kudzilonga yekha ufumu umene analonjeza Solomo. (1 Mbiri 22:​9, 10) Abiyatara anasankha kukhala kumbali ya Adoniya. (Ŵelengani 1 Mafumu 1:​5-8.) Mwa kutelo, Abiyatara anakhala wosakhulupilika kwa Davide komanso kwa Yehova! Izi ziyenela kuti zinam’pweteka ngako Zadoki. Kwa zaka 40, iye na Abiyatara anali ataseŵenzela pamodzi mogwilizana monga ansembe. (2 Sam. 8:17) Iwo anali kusamalila limodzi “Likasa la Mulungu woona.” (2 Sam. 15:29) Onse aŵili anacilikiza ulamulilo wa Davide, ndipo anacita zambili potumikila Yehova.—2 Sam. 19:​11-14.

16. N’ciyani cinathandiza Zadoki kukhalabe wokhulupilika?

16 Zadoki anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mosasamala kanthu za cisankho cimene Abiyatara anapanga. Davide anali kudziŵa kuti Zadoki ni munthu wokhulupilika. Ciwembu ca Adoniya citaululika, Davide anauza Zadoki, Natani, komanso Benaya kuti alonge Solomo kukhala mfumu. (1 Maf. 1:​32-34) Zadoki ayenela kuti analimbikitsidwa zedi kukhala na atumiki okhulupilika a Yehova monga Natani, komanso anthu ena omwe anali kumbali ya Mfumu Davide. (1 Maf. 1:​38, 39) Solomo atakhala mfumu, anasankha “wansembe Zadoki kuti aloŵe m’malo mwa Abiyatara.”—1 Maf. 2:35.

17. Mungatengele bwanji citsanzo ca Zadoki munthu amene mumamukonda akamusiya Yehova?

17 Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Zadoki? Khalanibe wokhulupilika kwa Yehova ngakhale kuti munthu amene mumam’konda wasankha kuleka kum’tumikila. (Yos. 24:15) Yehova adzakupatsani mphamvu ndipo adzakuthandizani kukhala wolimba mtima kuti mucite zoyenela. Dalilani Yehova mwa kupemphela kwa iye na kupitiliza kugwilizana nawo alambili anzanu okhulupilika. Yehova amakunyadilani cifukwa ca kukhulupilika kwanu, ndipo adzakufupani cifukwa ca zimenezi.—2 Sam. 22:26.

18. Mwaphunzilapo ciyani pa cocitika ca Marco na Sidse?

18 Ganizilani citsanzo ca Marco na mkazi wake Sidse, omwe atsikana awo aŵili anasiya coonadi. Marco anati: “Kucokela pamene ana ako abadwa umaŵakonda ngako. Ungacite zilizonse kuti uwateteze ku zoopsa. Conco, akasankha kusiya kutumikila Yehova zimapweteka mtima zedi.” Anapitiliza kuti: “Koma Yehova wakhala akutithandiza kupilila. Yehova waonetsetsa kuti nikakhala wofooka, mkazi wanga amakhala wolimba. Ndipo mkazi wanga akakhala wofooka, ine nimakhala wolimba kuti tizilimbikitsana.” Sidse anawonjezela kuti: “Tinakwanitsa kupilila cifukwa Yehova anatipatsa mphamvu zotithandiza kupilila. N’nali kuvutika na maganizo oona kuti ndine amene n’napangitsa kuti ana athu asiye kutumikila Yehova. Conco, n’namuuza Yehova mmene n’nali kumvela. Patapita kanthawi kocepa, mlongo wina amene sitinaonanepo kwa zaka anabwela kwa ine na kuika manja ake pa mapewa anga na kuniuza kuti: ‘Kumbukila Sidse, sikuti ndiwe unapangitsa zimenezi!’ Mwa thandizo la Yehova napitilizabe kukhala wacimwemwe pom’tumikila.”

19. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciyani?

19 Yehova afuna kuti alambili ake onse akhale olimba mtima ngati Zadoki. (2 Tim. 1:7) Komabe, Iye safuna kuti tizidalila mphamvu zathu. Amafuna kuti tizim’dalila. Conco, mukapezeka m’cocitika cofuna kulimba mtima, dalilani Yehova. Ndipo mosakaikila adzakuthandizani kukhala wolimba mtima monga mmene Zadoki analili!—1 Pet. 5:10.

MUNGATENGELE BWANJI KULIMBA MTIMA KWA ZADOKI . . .

  • pocilikiza Ufumu wa Mulungu?

  • pothandiza abale anu?

  • pokhalabe wokhulupilika kwa Yehova?

NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu

a Tambani vidiyo pa jw.org yakuti Cimene Akhristu Oona Afunikila Kukhala Olimba Mtima—Kuti Asamatengeko Mbali m’Zandale.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani