LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 December masa. 2-7
  • Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukakumana ndi Mabvuto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukakumana ndi Mabvuto
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MULUNGU ANALOLA YOBU KUKUMANA NDI MABVUTO
  • MMENE NKHANI YA YOBU INGATITHANDIZILE KUPILILA
  • GWILITSANI NCHITO BUKU LA YOBU POTHANDIZA ANTHU ENA
  • “Yembekezela Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukamapeleka Uphungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kodi Yobu Anali Ndani?
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 December masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 48

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukakumana ndi Mabvuto

“Ndithudi, Mulungu sacita zoipa.”​—YOBU 34:12.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tikambilane zimene tingaphunzile m’buku la Yobu ponena za cifukwa cake Mulungu walola mabvuto. Tikambilanenso zimene zingatithandize kuwapilila.

1-2. Kodi kuwelenga buku la Yobu kuli ndi ubwino wanji?

KODI munaliwelengapo buku la Yobu posacedwapa? Ngakhale kuti bukuli linalembedwa zaka pafupi-pafupi 3,500 zapitazo, anthu oculuka amaliona kuti ndi limodzi mwa mabuku olembedwa bwino kwambili. Buku lina linati munthu yemwe analemba buku la Yobu anali “katswili wa zolemba-lemba.” Linatelo poona kuti bukuli linalembedwa mwaluso, ndipo muli mau osabvuta kumva koma amphamvu. Mose ndiye analemba bukuli, koma uthenga wake ndi wocokela kwa Yehova Mulungu.​—2 Tim. 3:16.

2 Buku la Yobu ndi buku lofunika kwambili m’Baibo. Cifukwa cimodzi n’cakuti limafotokoza nkhani yaikulu imene imakhudza anthu ndi angelo onse. Nkhani yake ndi yokhudza kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova. Bukuli limatithandizanso kudziwa makhalidwe ocititsa cidwi a Yehova monga cikondi, nzelu, cilungamo, ndi mphamvu. Mwacitsanzo, m’buku la Yobu lokha, Yehova amachedwa “Wamphamvuyonse” maulendo 31. Ciwelengeloci ciposa ciwelengelo ca m’mabuku ena a m’Baibo tikawaphatikiza. Bukuli limayankhanso mafunso ambili amene anthu amadzifunsa monga lakuti: N’cifukwa ciani Mulungu walola kuti anthu azibvutika?

3. Ndi zinthu ziti zimene tingaphunzile m’buku la Yobu?

3 Kuwelenga buku la Yobu kuli ngati kukwela phili. Mukakhala pamwamba pa phili, mumatha kuona bwino-bwino malo onse okuzungulilani. Mofanana ndi zimenezi, tikamawelenga buku la Yobu timatha kuona bwino-bwino kapena kuti kumvetsa mmene Yehova amaonela mabvuto athu. M’nkhani ino, tiphunzila mmene nkhani ya Yobu ikanathandizila Aisiraeli m’nthawi yakale, komanso mmene ingatithandizile ife masiku ano. Tiphunzilanso mmene tingagwilitsile nchito bukuli pothandiza anthu ena.

MULUNGU ANALOLA YOBU KUKUMANA NDI MABVUTO

4. Ndi kusiyana kwakukulu kuti kumene kunalipo pakati pa Yobu ndi Aisiraeli amene anali ku Iguputo?

4 Pa nthawi imene Aisiraeli anali ku ukapolo ku Iguputo, mwamuna wina, dzina lake Yobu, anali kukhala m’dziko la Uzi. Mwacionekele, dziko la Uzi linali kum’mawa kwa Dziko Lolonjezedwa kufupi ndi cigao ca Arabiya. Pamene Aisiraeli anali ku Iguputo, ena mwa iwo anayamba kulambila mafano. Koma Yobu anali kutumikila Yehova mokhulupilika. (Yos. 24:14; Ezek. 20:8) Ponena za Yobu, Yehova anati: “Padziko lapansi palibe wina wofanana naye.”a (Yobu 1:8) Pa anthu onse a Kum’mawa, Yobu ndiye anali wolemela kwambili, komanso wolemekezeka kwambili. (Yobu 1:3) Satana anakwiya kwambili poona munthu wochuka ndi wolemekezekayu akutumikila Mulungu mokhulupilika.

5. N’cifukwa ciani Yehova analola Yobu kukumana ndi mabvuto? (Yobu 1:​20-22; 2:​9, 10)

5 Satana anati ngati Yobu angakumane ndi mabvuto, angasiye kulambila Yehova. (Yobu 1:​7-11; 2:​2-5) Yehova anali kum’konda kwambili Yobu. Ngakhale n’telo, Yehova analola Satana kuti ayese Yobu n’colinga coti Satanayo aonetse ngati zimene ananena zinalidi zoona. (Yobu 1:​12-19; 2:​6-8) Satana anapha ziweto zonse za Yobu. Anaphanso ana ake 10, ndipo anamuzunza ndi zilonda zowawa kwambili, kuyambila kuphazi mpaka kumutu. Ngakhale kuti Satana anazunza Yobu mwankhanza, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. (Welengani Yobu 1:​20-22; 2:​9, 10.) M’kupita kwa nthawi, Yehova anam’cilitsa. Anam’patsanso cuma ndi ana ena 10. Ndipo anthu anayambanso kumulemekeza. Yehova anam’dalitsanso ndi moyo wautali, ndipo anakhala ndi moyo zaka zina 140 moti anatha kuona zidzukulu za zidzukulu zake. (Yobu 42:​10-13, 16) Kodi nkhaniyi ikanawathandiza bwanji atumiki a Mulungu akale? Nanga ife ingatithandize bwanji masiku ano?

6. Kodi kudziwa nkhani ya Yobu kukanawathandiza bwanji Aisiraeli? (Onaninso cithunzi.)

6 Zimene Aisiraeli akanaphunzilapo. Nkhani ya Yobu iyenela kuti inawathandiza kwambili Aisiraeli amene anakumana ndi mabvuto aakulu ku Iguputo. Mwacitsanzo, Yoswa ndi Kalebe anali akapolo kwa zaka zambili. Kenako, anakhala m’cipululu zaka 40 cifukwa ca kusamvela kwa Aisiraeli ena. Ngati Aisiraeli anali kudziwa mabvuto amene Yobu anakumana nawo, komanso madalitso amene analandila, mosakaikila iwo ndi mbadwa zao zam’tsogolo anadziwa amene amacititsa mabvuto komanso cifukwa cake Mulungu amalola kuti anthu azibvutika. Sitikaikilanso kuti kudziwa nkhani ya Yobu kunawathandiza kudziwa kuti Mulungu amakonda anthu amene amakhalabe okhulupilika ngakhale pamene akukumana ndi mabvuto.

Mwamuna waciisiraeli akusinkha-sinkha pomwe akulongeza nchelwa. Capafupi pali Aiguputo omwe akumenya Aisiraeli ndi ndodo. Aisiraeliwo akugwila nchito mwakhama.

Aisiraeli anakhala mu ukapolo ku Iguputo kwa zaka zambili, ndipo akanalimbikitsidwa podziwa zimene zinacitikila Yobu (Onani ndime 6)


7-8. Kodi buku la Yobu lingawathandize bwanji amene akukumana ndi mabvuto? Fotokozani citsanzo.

7 Zimene ife tingaphunzilepo. N’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili masiku ano sakhulupilila Mulungu cifukwa samvetsa cifukwa cake zinthu zoipa zimacitikilanso anthu abwino. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitikila mai wina wa ku Rwanda, dzina lake Hazelb. Pamene anali mwana, anali kukhulupilila Mulungu. Koma zinthu pa umoyo wake zinasintha. Makolo ake anasudzulana, ndipo iye analeledwa ndi atate ake opeza. Iwo anali kum’zunza. Ali mtsikana, mwamuna wina anamugwilila. Komanso atapita kumalo ena olambilila kuti akalimbikitsidwe, sanapezeko cilimbikitso cimene anali kufuna. Kenako, analemba mau akuti: “Mulungu, ndakhala ndikupemphela kwa inu, ndipo ndimayesetsa kucita zabwino, koma mumandibwezela zoipa m’malo mwa zabwino. Kuyambila lelo, ndaleka kukulambilani. Tsopano ndiziyesetsa kucita zimene zingandisangalatse basi.” N’zomvetsa cisoni kuti pali anthu ambili monga Hazel amene cifukwa ca zimene apitamo, amakhulupilila kuti Mulungu ndiye amacititsa mabvuto.

8 Komabe, m’buku la Yobu taphunzila kuti si Yehova amene amacititsa mabvuto, koma Satana! Taphunzilanso kuti sitiyenela kuganiza kuti munthu akamakumana ndi mabvuto, ndiye kuti akukolola zimene anafesa. Malemba amatiuza kuti “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezeleka” zingagwele wina aliyense pa nthawi iliyonse. (Mlal. 9:11; Yobu 4:​1, 8) Tikamatumikila Yehova mokhulupilika ngakhale pamene tikukumana ndi mabvuto, timathandiza Yehova kuyankha Satana amene amam’tonza. (Yobu 2:3; Miy. 27:11) Timaona kuti ndi mwai kudziwa mfundo zimenezi cifukwa zimatithandiza kudziwa bwino cifukwa cake anthufe timakumana ndi mabvuto. Hazel, amene tachula m’ndime yapitayi, anayamba kuphunzila Baibo ndi Mboni za Yehova patapita nthawi, ndipo anamvetsa kuti Mulungu sindiye amene anali kucititsa kuti azikumana ndi mabvuto. Kenako, iye anati: “Ndinapemphelanso kwa Mulungu mocokela pansi pa mtima. Ndinauza Yehova kuti, ‘Pamene ndinanena kuti ndileka kukulambilani, sin’nali kufunadi kukusiyani. N’nakamba zimenezo cifukwa ndinali ndisanakudziweni.’ Panopa, ndimadziwa kuti Yehova amandikonda. Ndili ndi cimwemwe ndipo ndine wokhutila.” Ndife oyamikila kwambili kudziwa cifukwa cake Mulungu walola kuti anthu azikumana ndi mabvuto. Tsopano tiyeni tikambilane mmene nkhani ya Yobu ingathandizile aliyense wa ife pamene akukumana ndi mabvuto.

MMENE NKHANI YA YOBU INGATITHANDIZILE KUPILILA

9. Kodi umoyo wa Yobu unali bwanji atakumana ndi mabvuto? (Yakobo 5:11)

9 Yelekezelani kuti mukuona Yobu atakhala pa phulusa komanso ali yekha-yekha. Mutayang’ana thupi lake, mukuona kuti paliponse pali zilonda, ndipo wazyolika cifukwa ca ululu. Ndi woonda kwambili, ndipo khungu lake ndi lomyuka-myuka. Alibiletu mphamvu moti wangokhala n’kumadzikanda ndi phale, kwinaku akubuula ndi ululu. Yobu anapilila mavuto onsewa komanso anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. (Welengani Yakobo 5:11.) N’ciani cinamuthandiza kupilila?

10. Kodi n’ciani cionetsa kuti Yobu anali kumasuka pofotokoza zinthu kwa Yehova? Fotokozani.

10 Yobu anauza Yehova mmene anali kumvela. (Yobu 10:​1, 2; 16:20) Mwacitsanzo, caputala 3 cimati mowawidwa mtima, Yobu anadandaula cifukwa ca matsoka onse amene anam’gwela. Koma cifukwa cosadziwa, ananena kuti Yehova ndi amene anamugwetsela matsokawo. Kenako, anzake atatu ananena mobweleza-bweleza kuti Mulungu anali kumulanga cifukwa ca macimo ake. Koma nayenso mobweleza-bweleza anali kukamba kuti iye ndi wokhulupilika kwa Yehova. Mau a Yobu anaonetsa kuti, kwa kanthawi, anali kudziona ngati wolungama kuposa Mulungu. (Yobu 10:​1-3; 32:​1, 2; 35:​1, 2) Koma Yobu anabvomeleza kuti zina mwa zimene anakamba podziikila kumbuyo kuti anali wokhulupilika, zinali “zopanda pake.” (Yobu 6:​3, 26, mau a m’munsi.) M’caputala 31, Yobu ananena kuti anali kufuna kuti Mulungu amuyankhe n’kumuuza kuti analibe mlandu ulionse. (Yobu 31:35) Komabe, Yobu analakwitsa kuumilila kuti Mulungu amuyankhe n’kumuuza cifukwa cimene anali kubvutikila.

11. Kodi Yehova anacitapo ciani pa zimene Yobu anakamba?

11 Masiku ano, timatha kumvetsa kuti madandaulo a Yobu kwenikweni anaonetsa kuti iye anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ndipo anali kukhulupilila kuti Yehovayo adzaona kukhupilika kwake. Kenako, inafika nthawi yoti Yehova amuyankhe Yobu, ndipo anamuyankha kudzela mu mphepo yamkuntho. Koma, sanafotokoze zonse zimene zinali kucititsa kuti Yobu azibvutika. Komanso sanamuimbe mlandu cifukwa codandaula kapena cifukwa colankhula modzilungamitsa. M’malomwake, Yehova anamulangiza monga mmene tate angacitile ndi mwana wake. Ndipo imeneyi inali njila yabwino. Zotsatila zake zinali zakuti Yobu anadzicepetsa n’kubvomeleza kuti zimene anali kudziwa zinali zocepa kwambili. Kenako, anapepesa cifukwa colankhula mosaganiza bwino. (Yobu 31:6; 40:​4, 5; 42:​1-6) Kodi cocitika ici cikanawathandiza bwanji anthu akale? Nanga cingatithandize bwanji ife masiku ano?

12. Kodi Aisiraeli ayenela kuti anapindula bwanji ndi citsanzo ca Yobu?

12 Zimene Aisiraeli akanaphunzilapo. Aisiraeli akanaphunzilapo kanthu pa zimene zinacitikila Yobu. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitikila Mose. Pamene Mose anali kutsogolela mtundu wa Aisiraeli, anafunika kupilila zobvuta zosiyana-siyana, zofooketsa, komanso zokhumudwitsa. Nthawi zambili Aisiraeli anali kung’ung’udzila Yehova akakumana ndi mabvuto. Koma Mose anali kupemphela kwa Yehova kuti am’thandize pa nthawi zobvuta. (Eks. 16:​6-8; Num. 11:​10-14; 14:​1-4, 11; 16:​41, 49; 17:5) Citsanzo ca Yobu ciyenela kuti cinathandiza Mose kulandila uphungu wocokela kwa Yehova. Mwacitsanzo, Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa anamanga msasa ku Kadesi. Ali kumeneko, Mose “analankhula mosaganiza bwino” ndipo sanapeleke ulemelelo kwa Yehova. (Sal. 106:​32, 33) Pa cifukwa cimeneci, Yehova sanamulole kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 32:​50-52) Cilango cimeneci ciyenela kuti cinam’pweteka mtima Mose, koma anacilandila modzicepetsa. Nkhani ya Yobu ikanathandizanso Aisiraeli obwela mtsogolo. Kusinkha-sinkha nkhaniyi kukanathandiza Aisiraeli okhulupilika kudziwa mofotokozela nkhawa zao kwa Yehova ndi kupewa kudzilungamitsa pamaso pake. Akanaphunzilanso kufunika kobvomeleza cilango ca Yehova modzicepetsa.

13. Kodi citsanzo ca Yobu cingatithandize bwanji kupilila mabvuto? (Aheberi 10:36)

13 Zimene ife tingaphunzilepo. Masiku anonso, ife Akhristu, tifunika kupilila kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. (Welengani Aheberi 10:36.) Mwacitsanzo, mwina mukubvutika cifukwa ca kudwala matenda aakulu, kupanikizika maganizo, nkhawa yaikulu, mabvuto a m’banja, kufeledwa, kapenanso mabvuto ena aakulu. Ndipo nthawi zina, anthu ena angakambe kapena kucita zinthu zimene zingapangitse kuti cikhale cobvuta kupilila mabvutowa. (Miy. 12:18) Buku la Yobu limatiphunzitsa kuti tingathe kumufotokozela Yehova za mumtima mwathu, tili ndi cidalilo cakuti adzatimvela. (1 Yoh. 5:14) Nthawi zina, m’mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima tingalankhule mosaganiza bwino monga anacitila Yobu. Ngakhale n’telo, Yehova sangatikwiyile. M’malomwake, adzatipatsa mphamvu ndi nzelu zimene zidzatithandiza kupilila. (2 Mbiri 16:9; Yak. 1:5) Iye angatipatsenso uphungu monga anacitila kwa Yobu. Buku la Yobu limatiphunzitsanso zimene tingacite ngati talandila uphungu kapena cilango cocokela m’Mau a Yehova, ku gulu lake, kapena kwa bwenzi lokhwima kuuzimu. (Aheb. 12:​5-7) Monga mmene Yobu anapindulila atalandila uphungu modzicepetsa, ifenso tingapindule ngati tingayesetse kusintha maganizo athu pambuyo polandila uphungu. (2 Akor. 13:11) Izi ndi mfundo zothandiza kwambili zimene tingaphunzile m’buku la Yobu. Tsopano, tiyeni tikambilane mmene tingagwilitsile nchito buku la Yobu pothandiza anthu ena.

GWILITSANI NCHITO BUKU LA YOBU POTHANDIZA ANTHU ENA

14. Kodi tingamufotokozele bwanji munthu mu utumiki cifukwa cake padziko lapansi pali mabvuto?

14 Kodi munakumanapo ndi winawake mu ulaliki amene anakufunsani kuti n’cifukwa ciani anthu abwino amabvutika? Kodi munamuyankha bwanji? Mwina munamuuza zimene Baibo imakamba pa zimene zinacitika m’munda wa Edeni. Mwacionekele, munayamba mwa kufotokoza kuti Satana, yemwe ndi mngelo woipa, anapangitsa mwamuna ndi mkazi woyamba kupandukila Mulungu mwa kuwanamiza bodza. (Gen. 3:​1-6) Kenako, munamufotokozela kuti pambuyo pa kupanduka kwa Adamu ndi Hava, padziko lonse panadzadza mabvuto ndipo anthu anayamba kufa. (Aroma 5:12) N’kutheka kuti munamaliza mwa kufotokoza kuti Yehova walola kuti padutse nthawi yokwanila pofuna kutsimikizila kuti Satana ndi wabodza komanso kuti uthenga wabwino wakuti m’tsogolo anthu adzakhalanso angwilo ufalitsidwe. (Chiv. 21:​3, 4) Imeneyi ndi njila yabwino kwambili yoyankhila funsoli ndipo ingathandize anthu ambili kudziwa cifukwa cake timakumana ndi mabvuto.

15. Kodi tingagwilitse nchito bwanji buku la Yobu pothandiza munthu amene wafunsa kuti n’cifukwa ciani padzikoli pali mabvuto? (Onaninso zithunzi.)

15 Onaninso njila ina yopezeka m’buku la Yobu imenenso mungagwilitse nchito poyankha funsoli. Mungayambe mwa kumuyamikila munthuyo cifukwa cofunsa funso lofunika kwambili limeneli. Kenako, mungafotokoze kuti munthu wina wokhulupilika, dzina lake Yobu, amene anabvutika kwambili, anafunsa funso lofanana ndi limeneli. Anafika ngakhale poganiza kuti Yehova ndi amene anali kucititsa mabvuto ake. (Yobu 7:​17-21) Mwina munthuyo angacite cidwi podziwa kuti kuyambila kale-kale, anthu akhala akufunsa funso ngati lakelo. Kenako, mungamufotokozele kuti malinga n’zimene buku la Yobu limanena, si Mulungu amene anali kucititsa mabvuto a Yobu, koma Mdyelekezi. Mdyelekezi anacita zimenezi pofuna kutsimikizila zomwe anakamba zakuti anthu amatumikila Mulungu ndi zolinga zadyela. Amati ngati anthu angabvutike, angaleke kum’tumikila. Mungafotokozenso kuti, ngakhale kuti Mulungu sindiye anacititsa mabvuto a Yobu, iye analola zimenezi kucitika pofuna kuonetsa kuti Mdyelekezi ndi wabodza, komanso kuti anthu angatumikile Mulungu mokhulupilika, osati ndi zolinga zadyela. Ndipo mungamalize mwa kufotokoza kuti Mulungu anam’dalitsa Yobu cifukwa cokhalabe wokhulupilika. Conco, tingalimbikitse ena mwa kuwatsimikizila kuti si Yehova amene amacititsa mabvuto.

Zithunzi: 1. Mzimai wopanikizika maganizo wagwila cithunzi ali khale pamalo pomwe kale panali nyumba. Nyumbayo yapsyelatu ndi moto. 2. Pambuyo pake, mzimaiyo wapita pa kasitandi ka ulaliki ndipo akumvetsela pomwe mlongo akumuwelengela lemba. Pafupi ndi kasitandi ka ulalikiko pali malo pomwe akuthandizila anthu amene akhudzidwa ndi tsoka.

Kodi ndi motani mmene mungagwilitsile nchito buku la Yobu potsimikizila anthu kuti Mulungu sacita zoipa? (Onani ndime 15)


16. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene buku la Yobu lingathandizile munthu amene akukumana ndi mabvuto.

16 Ganizilani mmene buku la Yobu linathandizila munthu wina, dzina lake Mario. Tsiku lina mu 2021, mlongo wina anali kucita ulaliki wapafoni. Munthu woyamba kutumila foni anali Mario. Mlongoyo anamuwelengela vesi imene ionetsa kuti Mulungu amamvetsela mapemphelo athu komanso watilonjeza tsogolo labwino. Mlongoyo anapempha Mario kuti afotokoze mmene mfundo ya pa vesiyi yamukhudzila. Mario anauza mlongoyo kuti pamene iye anatuma foni, anali kulemba kalata yolaila a m’banja lake kuti kenako adziphe. Iye anati: “Ndimakhulupilila Mulungu. Koma m’mawa uno ndinali kuganiza kuti iye wanditaya.” Kenako, mlongoyo atatumanso foni, anakambilana naye nkhani ya Yobu komanso mabvuto amene anakumana nao. Mario anaganiza zowelenga buku lonse la Yobu. Kenako mlongoyo anam’tumizila linki ya Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Zotsatila zake, Mario anabvomela kuphunzila Baibo ndipo anasangalala kuphunzila zambili za Mulungu wacikondi amene amam’ganizila.

17. N’cifukwa ciani ndinu oyamikila kuti Yehova analemba nkhani ya Yobu m’Mau ake ouzilidwa? (Yobu 34:12)

17 Baibo ili ndi mphamvu yosintha anthu komanso yolimbikitsa amene akubvutika. (Aheb. 4:12) Ndife oyamikila kwambili kuti Yehova analemba nkhani ya Yobu m’Mau ake ouzilidwa! (Yobu 19:​23, 24) Buku la Yobu limatitsimikizila kuti, “Ndithudi, Mulungu sacita zoipa.” (Welengani Yobu 34:12.) Limatiphunzitsanso cifukwa cake Mulungu walola mabvuto komanso limatiuza zimene zingatithandize kuti tiwapilile. Ndipo limatithandiza kuti tizilimbikitsa amene akubvutika. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene buku la Yobu lingatithandizile tikamapeleka uphungu.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi kudziwa cifukwa cake Mulungu analola Yobu kubvutika kumatithandiza bwanji?

  • Kodi nkhani ya Yobu ingatithandize bwanji kupilila mabvuto?

  • Kodi tingasewenzetse bwanji buku la Yobu pothandiza anthu ena?

NYIMBO 156 Mwa Cikhulupililo

a Yosefe anamwalila m’caka ca 1657 B.C.E. Mose anasankhidwa kukhala m’tsogoleli wa Aisiraeli ca m’ma 1514 B.C.E. Mwacionekele, pakati pa zaka ziwilizi m’pamene Yehova ndi Satana anali kukambilana za Yobu, ndipo m’pamenenso Yobu anakumana ndi mabvuto.

b Maina ena asinthidwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani