NKHANI YOPHUNZILA 49
NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika
Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukamapeleka Uphungu
“Tsopano inu a Yobu, imvani mau anga.”—YOBU 33:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tiphunzila mmene buku la Yobu lingatithandizile kupeleka uphungu wogwila mtima.
1-2. N’cifukwa ciani zinali zobvuta kwa Elifazi, Bilidadi, Zofari ndi Elihu kuti alimbikitse Yobu?
YOBU atataikilidwa cuma cake conse, uthengawu unafalikilila mofulumilila kwambili ngati lupsya! Anzake atatu: Elifazi, Bilidadi ndi Zofari atamva zimene zinam’citikila, anapita ku Uzi kuti akam’tonthoze. Koma atafika n’kuona zimene zinacitika, anangoti kakasi.
2 Yelekezani kuti mukuona zimene zikucitika. Yobu wataikilidwa zinthu zake zonse. Anali ndi ziweto zambili: nkhosa, ng’ombe, ngamila, ndi abulu. Koma zonsezo kulibenso. Atumiki ake ambili aphedwa. Ana ake onse nyumba yawagwela, ndipo afelatu. Koma si zokhazi. Yobu iyemwini wayamba kudwala. Thupi lake lonse lili ndi zilonda zowawa. Apa n’kuti Yobu ali khale pa phulusa ali ndi cisoni cofa naco. Kenako, mukuona anzake atatu aja akubwela potelo. Kodi iwo adzacita ciani akaona zonsezi? Amunawa akukhala duu! kwa masiku 7 athunthu, sakukamba ciliconse kwa Yobu, ngakhale kuti akuona kuti mnzao akumva ululu waukulu. (Yobu 2:12, 13) Mnyamata wina, dzina lake Elihu, nayenso wabwela kudzaona Yobu ndipo wakhala capafupi nawo. Pambuyo pake, Yobu akutsegula pakamwa pake n’kuyamba kutembelela tsiku limene anabadwa ndipo akungolakalaka kufa. (Yobu 3:1-3, 11) Apa, n’zoonekelatu kuti Yobu akufunikila cilimbikitso. Koma n’zobvuta kwa anzakewo kuti amulimbikitse. Zimene iwo akambe zidzaonetsa ngati alidi mabwenzi ake eni-eni, komanso ngati amamudeladi nkhawa.
3. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino?
3 Yehova analamula Mose kulemba zimene Elihu komanso anzake atatu a Yobu anakamba ndi kucita. Zioneka kuti zina zimene Elifazi anakamba zinauzilidwa ndi ciwanda. Koma zimene Elihu anakamba zinali zouzilidwa ndi Yehova. (Yobu 4:12-16; 33:24, 25) N’cifukwa cake m’buku la Yobu muli malangizo ena abwino kwambili komanso ena oipa kwambili. M’nkhani ino, tikambilane mmene buku la Yobu lingatithandizile tikafuna kupeleka uphungu kwa mnzathu. Coyamba, tikambilana citsanzo coipa ca anzake atatu a Yobu pa nkhani yopeleka uphungu. Kenako, tikambilana citsanzo cabwino ca Elihu. Pa mbali iliyonse, tikambilane mmene Aisiraeli akanapindulila ndi citsanzo ca Yobu, komanso mmene ifeyo masiku ano tingapindulile.
MMENE ANZAKE ATATU A YOBU ANAPELEKELA UPHUNGU KWA IYE
4. N’cifukwa ciani anzake atatu a Yobu analephela kumulimbikitsa? (Onaninso cithunzi.)
4 Baibo imati anzake atatu a Yobu atamva zonse zimene zinamucitikila, anapita kuti akam’tonthoze ndi kumulimbikitsa. (Yobu 2:11) Komabe, iwo analephela kukwanilitsa colinga cao. Cifukwa ciani? Tiyeni tikambilane zifukwa zitatu. Coyamba, anafulumila kumuweluza Yobu, asanamvetse nkhani yonse. Mwacitsanzo, anaganiza kuti Yobu anali kulandila cilango cifukwa cakuti anacimwila Mulungu.a (Yobu 4:7; 11:14) Caciwili, uphungu woculuka umene amunawo anapatsa Yobu unali wosathandiza, wopanda cikondi, ndiponso wowawa. Mwacitsanzo, onse atatu analankhula mau amene anali kumveka ngati anzelu koma anali osathandiza. (Yobu 13:12) Kawili konse, Bilidadi anam’dzudzula Yobu mopanda cikondi mwa kumuuza kuti anali kulankhula kwambili. (Yobu 8:2; 18:2) Ndipo Zofari anakamba mau olasa amene anatanthauza kuti Yobu anali “munthu wopanda nzelu.” (Yobu 11:12) Cacitatu, ngakhale kuti mwina amunawo sanali kulankhula mozaza, mau ao kawili-kawili anali kukhala odzilungamitsa, olasa, ndiponso omuimba mlandu. (Yobu 15:7-11) Amuna amenewa anali kungofuna kutsimikizila Yobu kuti anacimwa, ndipo analephela kum’tonthoza komanso kumulimbikitsa.
Mukamapeleka uphungu kwa ena, musamalankhule ngati kuti inuyo mumacita bwino kuposa munthu amene mukupatsa uphunguyo. Colinga canu cizikhala kum’thandiza (Onani ndime 4)
5. Kodi uphungu wa anzake a Yobu unakhala ndi zotsatilapo zotani?
5 N’zosadabwitsa kuti uphungu wa anzake a Yobu sunakhale ndi zotsatilapo zabwino. Mau ao anam’fooketselatu. (Yobu 19:2) Tingamvetse cifukwa cake iye anali kudziteteza. Koma pocita zimenezi analephela kukhala woganiza bwino ndipo analankhula mopanda nzelu. (Yobu 6:3, 26) Zimene anzake a Yobu anakamba zinali zosagwilizana ndi maganizo a Yehova ndipo iwo analephela kum’citila cifundo. Conco, Satana anawagwilitsa nchito kuti afooketse Yobu. (Yobu 2:4, 6) Kodi nkhaniyi ikanawathandiza bwanji Aisiraeli? Nanga ingatithandize bwanji ife masiku ano?
6. Kodi akulu a mu Isiraeli akanaphunzilapo ciani pa citsanzo coipa ca anzake atatu a Yobu?
6 Zimene Aisiraeli akanaphunzilapo. Pambuyo pokhazikitsa mtundu wa Aisiraeli, Yehova anasankha akulu, omwe anali amuna oyenelela, kuti aziweluza mtunduwu mogwilizana ndi malamulo ake. (Deut. 1: 15-18; 27:1) Amuna amenewo anali kufunika kumvetsela mosamala asanapeleke uphungu kapena ciweluzo. (2 Mbiri 19:6) Anali kufunikanso kufunsa mafunso m’malo mongoganiza kuti anali kudziwa bwino nkhani yonse. (Deut. 19:18) Amunawo anafunika kulankhula mokoma mtima kwa anthu amene anali kubwela kwa iwo kudzapempha thandizo. Cifukwa cake n’cakuti kulankhula mau olasa kukanapangitsa anthuwo kulephela kufotokoza za kumtima kwao. (Eks. 22:22-24) Awa ndi ena mwa maphunzilo amene akulu a mu Isiraeli akanaphunzila pa nkhani ya Yobu.
7. Kupatulapo akulu mu Isiraeli, ndani ena anali ndi udindo wopeleka uphungu? Ndipo akanaphunzila ciani pa nkhani ya Yobu? (Miyambo 27:9)
7 Komabe, sunali udindo wa akulu okha kupeleka uphungu mu Isiraeli. Aliyense akanatha kupeleka malangizo kwa mnzake pofuna kum’thandiza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova kapena kumuongolela ngati walakwitsa zinazake. (Sal. 141:5) Izi n’zimene bwenzi labwino limacita. Ilo limakhala lokonzeka kupeleka malangizo mosapita m’mbali. (Welengani Miyambo 27:9.) Kuganizila citsanzo coipa ca anzake atatu a Yobu kuyenela kuti kunawathandiza Aisiraeli kudziwa zosayenela kukamba komanso zosayenela kucita akamapeleka uphungu.
8. Ndi zinthu ziti zimene tiyenela kupewa pamene tikupeleka uphungu kwa ena? (Onaninso zithunzi.)
8 Zimene ife tingaphunzilepo. Akhristufe timafuna kuthandiza abale ndi alongo athu akakumana ndi mabvuto. Komabe, pamene tikucita zimenezi, tiyenela kupewa kucita zinthu mmene anzake atatu a Yobu anacitila. Coyamba, tiyenela kupewa kupeleka uphungu tisanadziwe nkhani yonse. Caciwili, tikamapeleka uphungu tisamangokamba za m’mutu mwathu, ngati mmene Elifazi anacitila nthawi zambili. M’malomwake, uphungu wathu uzicokela m’Mau a Mulungu. (Yobu 4:8; 5:3, 27) Cacitatu, tizipewa kulankhula mwaukali kapena mosakoma mtima. Kumbukilani kuti zina zimene Elifazi ndi anzake anakamba zinali zoona, moti mtumwi Paulo anauzilidwa kugwila mau amene Elifazi anakamba. (Yelekezelani Yobu 5:13 ndi 1 Akorinto 3:19.) Koma zambili zimene anzake atatu a Yobu anakamba zokhudza Yehova zinali zomunamizila ndipo zinam’pweteka mtima Yobu. Conco, Yehova ananena kuti zimene anakambazo zinali zabodza. (Yobu 42:7, 8) Uphungu wabwino supangitsa munthu amene akuulandila kumva ngati Yehova samukonda kapena kumuganizila. Tsopano, tiyeni tikambilane zimene tikuphunzilapo pa citsanzo ca Elihu.
Mukamapeleka uphungu, (1) muziidziwa bwino nkhani yonse, (2) muzisewenzetsa Mau a Mulungu, ndipo (3) muzilankhula mwacikondi (Onani ndime 8)
MMENE ELIHU ANAPELEKELA UPHUNGU KWA YOBU
9. Fotokozani cifukwa cake Yobu anafunikila thandizo anzake atatu atasiya kulankhula. Nanga Yehova analipeleka motani?
9 Pamene Yobu ndi anzake atatu anasiya kukangana, aliyense wa iwo ayenela kuti anali wokwiya. Zimene amunawa anakamba n’zoculuka kwambili moti zikwana macaputala 28. Zimene iwo analankhula zionetsa kuti anali okwiya kwambili. N’cifukwa cake cisoni ca Yobu cinali cisanathe. Panafunika munthu wina kuti amulimbikitse ndi kumuongolela. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Yobu? Anam’patsa uphungu pogwilitsa nchito Elihu. N’cifukwa ciani Elihu sanalankhulepo maganizo ake mofulumila? Iyemwini ananena kuti: “Ine ndine wamng’ono ndipo amuna inu ndinu acikulile. N’cifukwa cake mwaulemu ndinakhala cete.” (Yobu 32:6, 7) Wacinyamata Elihu anazindikila mfundo imene anthu ambili amaidziwa bwino masiku ano yakuti: Cifukwa cakuti acikulile akhala zaka zambili, ali ndi nzelu komanso amadziwa zambili kuposa acinyamata. Koma atamvetsela zimene Yobu ndi anzake anakamba, Elihu sanathenso kugwila pakamwa. Iye anati: “Si zaka zokha zimene zimapangitsa kuti munthu akhale wanzelu ndipo si acikulile okha amene amadziwa zinthu zoyenela.” (Yobu 32:9) Kodi Elihu anakamba ciani pambuyo pake? Nanga analankhula motani?
10. Kodi Elihu anacitanji akalibe kupeleka uphungu kwa Yobu? (Yobu 33:6, 7)
10 Elihu asanapeleke uphungu kwa Yobu, coyamba anam’khazika mtima pansi kuti asabvutike kulandila uphunguwo. Kodi Elihu anacita bwanji zimenezi? Coyamba, anayesetsa kuugwila mtima. Tikutelo cifukwa Baibo imatiuza kuti poyamba Elihu anali wokwiya. (Yobu 32:2-5) Ngakhale n’telo, iye sanalankhulepo mau okhadzula kwa Yobu. M’malomwake, analankhula momulimbikitsa. Mwacitsanzo, anauza Yobu kuti: “Inetu n’cimodzi-modzi ndi inu pamaso pa Mulungu woona.” (Welengani Yobu 33:6, 7.) Kenako, Elihu anasonyeza kuti anamvetsa zokamba za Yobu cifukwa akalibe kum’patsa uphungu, anachulako mfundo zina zikulu-zikulu zimene Yobu anakamba. (Yobu 32:11; 33:8-11) Elihu anacitanso cimodzi-modzi pa nthawi ina pamene anali kupeleka uphungu kwa Yobu.—Yobu 34:5, 6, 9; 35:1-4.
11. Kodi Elihu anapeleka bwanji uphungu kwa Yobu? (Yobu 33:1)
11 Pamene Elihu anali kupeleka uphungu kwa munthu wokhulupilika Yobu, anaupeleka mwaulemu. Mwacitsanzo, Elihu anali kum’chula dzina Yobu polankhula naye, pomwe anzake atatu aja mwacionekele sanatelo. (Welengani Yobu 33:1.) Komanso, pamene anali kupatsa uphungu Yobu, anali kum’patsa mwai woti nayenso alankhulepo. Mwacionekele, Elihu anacita izi pokumbukila kuti nayenso anali kufunitsitsa kulankhulako pamene Yobu ndi anzake atatu aja anali kukangana. (Yobu 32:4; 33:32) Kuonjezela apo, Elihu anathandizanso Yobu kuzindikila kuti zina mwa zimene anakamba ndi kucita zinali zosayenela. Ndipo mokoma mtima, anamukumbutsa za nzelu za Yehova, mphamvu zake, cilungamo cake komanso cikondi cake cokhulupilika. (Yobu 36:18, 21-26; 37:23, 24) Uphungu wabwino umene Elihu anapeleka, mosakaikila unathandiza Yobu kukhala ndi maganizo oyenela, moti anakhala wokonzeka kulandila malangizo ena oonjezela kucokela kwa Mlengi wake. (Yobu 38:1-3) Kodi citsanzo ca Elihu, cikanawathandiza bwanji Aisiraeli? Nanga ife cingatithandize bwanji masiku ano?
12. Kodi Yehova anawagwilitsa nchito bwanji aneneli pothandiza anthu ake? Nanga Aisiraeli akanaphunzila ciani ku citsanzo cabwino ca Elihu?
12 Zimene Aisiraeli akanaphunzilapo. M’mbili yonse ya Aisiraeli, Yehova anali kusankha aneneli kuti azithandiza anthu ake kudziwa cifunilo cake. Mwacitsanzo, m’masiku a Oweluza, Yehova anagwilitsa nchito mneneli wamkazi Debora popeleka malangizo kwa anthu ake. Komanso Yehova anagwilitsa nchito Samueli kuyambila ali mwana popeleka malangizo kwa Aisiraeli. (Ower. 4:4-7; 5:7; 1 Sam. 3:19, 20) Kenako, m’nthawi ya mafumu, Yehova anali kutumiza aneneli ake mobweleza-bweleza kuti akathandize anthu ake mwauzimu komanso kuti apeleke uphungu kwa amene asiya kum’lambila m’njila yobvomelezeka. (2 Sam. 12:1-4; Mac. 3:24) Citsanzo ca Elihu, cimene cili m’buku la Yobu, cikanathandiza amuna ndi akazi okhulupilika amenewa kudziwa zimene anayenela kukamba komanso mmene anayenela kukambila popeleka uphungu.
13. Kodi Akhristu angawalimbikitse bwanji alambili anzao masiku ano?
13 Zimene ife tingaphunzilepo. Ifenso Akhristu tikamauza ena zimene zili m’Mau a Mulungu Baibo, timakhala kuti tikuwadziwitsa cifunilo cake. Njila ina imene timacitila zimenezi ndi kukamba mau olimbikitsa kwa alambili anzathu. (1 Akor. 14:3) Akulu maka-maka afunika kuyesetsa ‘kumalankhula molimbikitsa’ ngakhale kwa anthu amene apsyinjika maganizo, kapena kwa amene akulankhula “mosaganiza bwino.”—1 Ates. 5:14; Yobu 6:3.
14-15. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene mkulu angacitile potengela citsanzo ca Elihu pamene akupeleka uphungu.
14 Ganizilani cocitika ici congoyekezela: Mkulu wazindikila kuti mlongo wina mumpingo ndi wopanikizika maganizo. Iye ndi m’bale wina wayendela mlongoyo kuti akam’limbikitse. Ali kumeneko, mlongoyo akufotokoza kuti ngakhale kuti amapezeka pa misonkhano komanso kulalikila, sakhala wacimwemwe. Kodi mkuluyo ayenela kutani?
15 Coyamba, angafunike kudziwa cifukwa cake mlongoyo akumva conco. Kuti adziwe, afunika kumvetsela mosamala. Mwina mlongoyo akumva conco poganiza kuti Mulungu samukonda. Mwinanso zingakhale kuti nkhawa za moyo n’zimene zikum’fooketsa. (Luka 21:34) Caciwili, mkuluyo angafunike kuganizila zinthu zina zabwino zimene mlongoyo amacita ndi kumuyamikila pa zabwinozo. Mwacitsanzo, amapezekabe pa misonkhano ndi kulalikila ngakhale kuti ndi wopanikiza maganizo. Ndipo cacitatu, mkuluyo akamvetsa mmene zinthu zilili kwa mlongoyo, komanso zimene zikum’pangitsa kuti asamasangalale, angagwilitse nchito Baibo pom’limbikitsa ndi kum’thandiza kuti adziwe kuti Mulungu amam’konda.—Agal. 2:20.
PITILIZANI KUPHUNZILA ZAMBILI M’BUKU LA YOBU
16. Kodi tingatani kuti tipitilize kuphunzila mfundo za m’buku la Yobu?
16 Kukamba zoona, pali zambili zimene tingaphunzile m’buku la Yobu. Monga tinaonela m’nkhani yapita, buku la Yobu silimangotiphunzitsa cifukwa cake Mulungu walola mabvuto, koma limatiphunzitsanso zimene zingatithandize kuwapilila. Ndipo m’nkhani ino, taphunzila kuti tonsefe tingapeleke uphungu wogwila mtima mwa kutsatila citsanzo cabwino ca Elihu osati citsanzo coipa ca anzake atatu a Yobu. Bwanji osadzabwelelamo m’maphunzilo a m’buku la Yobu mukadzafunika kupeleka uphungu kwa winawake? Ndipo ngati papita nthawi kucokela pamene munaliwelenga buku lonse la Yobu, dziikileni colinga coti mukaliwelengenso. Mudzaona kuti likali lopindulitsa kwambili monga mmene linalili litangolembedwa!
NYIMBO 125 ‘Acifundo ni Acimwemwe!’
a Zioneka kuti ciwanda n’cimene cinapangitsa Elifazi kukamba kuti Yehova saona anthu kukhala olungama, ndipo palibe munthu angakondweletse Mulungu. Elifazi anaikhulupilila kwambili mfundo yopotoka imeneyi ndipo nthawi zonse akamalankhula ndi Yobu, anali kuibweleza.—Yobu 4:17; 15:15, 16; 22:2.