LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 113
  • Makhalidwe Aloŵa Pansi—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makhalidwe Aloŵa Pansi—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
  • Nkhani Zina
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa ciyani makhalidwe aloŵa pansi?
  • Gwelo lodalilika pa nkhani ya makhalidwe abwino
  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
  • N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kufunika kwa Makhalidwe Abwino
    Galamuka!—2019
  • Tonsefe Timafuna Malangizo Odalilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
Onaninso Zina
Nkhani Zina
mrt nkhani 113
Mtsikana akuthandiza mayi wacikulile mokoma mtima kupeza pokhala m’basi.

KHALANI MASO!

Makhalidwe Aloŵa Pansi—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Makhalidwe akuloŵa pansi. Odwala amwano amalalatila madokotala; makasitomala opanda ulemu amakalipila ogwila nchito m’malesitilanti; okwela ndeke osalamulilika amacitila nkhanza ogwila nchito m’ndeke; ana okonda kuphwanya malamulo amaseka aphunzitsi awo, kuwaopseza, ngakhale kuwaukila kumene; andale ena amacita zinthu zocititsa manyazi, pomwe ena amadzionetsela kuti ali na makhalidwe abwino.

Baibo ni gwelo lodalilika lotionetsa makhalidwe abwino. Imafotokozanso cifukwa cake anthu alibe makhalidwe abwino masiku ano.

N’cifukwa ciyani makhalidwe aloŵa pansi?

Kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino kukuonekela kwambili kuzungulila dziko lonse lapansi.

  • Malinga na kafukufuku wina wodalilika wa posacedwapa, anthu a ku America amaona kuti m’dziko lawo makhalidwe aloŵa pansi kwambili kuposa mmene zinalili pa zaka 22 zapitazi.

  • Pa kafukufuku winanso amene anacitika pa anthu 32,000 m’maiko 28, anthu opitilila hafu anakamba kuti makhalidwe aloŵa pansi kwambili kuposa n’kale lonse.

Baibo inakambilatu za makhalidwe amene timaona masiku ano.

  • “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, . . . osadziletsa, [komanso] oopsa.”—2 Timoteyo 3:1-3.

Kuti mudziŵe zambili zokhudza mmene ulosiwu ukukwanilitsikila masiku ano, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?”

Gwelo lodalilika pa nkhani ya makhalidwe abwino

M’dziko limene makhalidwe akuloŵa pansi, anthu mamiliyoni apeza kuti Baibo ni gwelo lodalilika la makhalidwe abwino. Malangizo ake pa nkhani ya makhalidwe ni “odalilika nthawi zonse, kuyambila panopa mpaka kalekale.” (Salimo 111:8) Onan’koni zitsanzo zingapo:

  • Zimene Baibo imanena: “Zinthu zonse zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”—Mateyo 7:12.

    Tanthauzo lake: Tizicitila ena zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu, monga tingafunile kuti ena aziticitila.

  • Zimene Baibo imanena: “Popeza tsopano mwataya cinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake.”—Aefeso 4:25.

    Tanthauzo lake: Tizikhala oona mtima pa zonse zimene timakamba na kucita.

Kuti mudziŵe zambili pa nkhani imeneyi, conde ŵelengani:

  • Nsanja ya Mlonda ya mutu wakuti “Kodi Tingawapeze Kuti Malangizo Odalilika?”

  • Nkhani yakuti “Kodi Baibo Imathandiza Bwanji Anthu Kukhala Ololela?.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani