Webu Saiti Yathu—Igwilitsileni Nchito Polalikila
Limbikitsani Anthu Kupita pa Webu Saiti Yathu: Anthu ena amene safuna kukamba nafe kapena kulandila mabuku athu, angafune kufufuza za Mboni za Yehova paokha kudzela pa jw.org. Conco, muziuzako ena za Webu saiti yathu pamene kuli koyenela kutelo.
Yankhani Mafunso: Nthawi zina mwininyumba, munthu wacidwi kapena mnzanu angafunse funso ponena za Mboni za Yehova kapena zikhulupililo zathu. Muyankheni nthawi yomweyo mwa kugwilitsila nchito foni kapena kompyuta. Nthawi zambili ndi bwino kuŵelenga malemba osagwidwa mau m’Baibo. Ngati mulibe foni imene ili ndi intaneti, mufotokozeleni mmene angagwilitsilile nchito jw.org kuti apeze yekha yankho.—Pitani pa tumitu takuti “Bible Teachings/Bible Questions Answered” kapena kakuti “About Us/Frequently Asked Questions.”
Tumizani Nkhani Kapena Cofalitsa kwa Munthu Amene Mumam’dziŵa: Tengani faelo ya PDF kapena ya EPUB ndi kuitumiza pa imelo. Kapena tengani zofalitsa zimene mungalize ndi kuziika pa CD. Nthawi iliyonse mukatumizila munthu wosabatizika cofalitsa cathunthu ca pa Intaneti, kaya ndi buku, kabuku, kapena magazini, mungalembe kuti mwagaŵila. Potumiza zofalitsa zimenezi musamaiwale kulemba dzina lanu kapena adilesi yanu, ndipo musamatuze zambili panthawi imodzi. Ndiponso musaike zofalitsa zimenezi pa Webu saiti ina iliyonse.—Pitani pa kamutu kakuti “Publications.”
Aonetseni Nkhani Zatsopano Zokhudza Mboni za Yehova: Zimenezi zingathandize ophunzila Baibo ndi ena amene timawalalikila kuti adziŵe za nchito yathu ya padziko lonse ndi mgwilizano wathu. (Sal. 133:1)—Pitani pa kamutu kakuti “News.”
[Cithunzi papeji 5]
(Kuti muone mau onse, pitani ku cofalitsa)
Iyeseni
1 Pa kamutu kakuti “Publications,” onani cofalitsa cimene mufuna kutenga, ndiyeno dinizani batani pa nkhani kapena cofalitsa comvetsela cimene mufuna.
2 Dinizani batani la MP3 kuti muone m’ndandanda wa nkhani zosiyana-siyana. Dinizani pa mutu wa nkhani imene mukufuna kuti muitenge kapena ▸ kuimvetsela pa intaneti.
3 Sankhani cinenelo cina pa m’ndandanda umenewu ngati mufuna kutenga cofalitsa ca cinenelo cimeneco.