Mmene Tingagwilitsile Nchito Zinthu Zongomvetsela za pa jw.org
1. Kuonjezela pa mabuku amene amalembedwa, n’ciani cina cimene cingatipindulitse?
1 Anthu ambili amakonda kuŵelenga mau okoma ndi olondola a coonadi pa jw.org. (Mlal. 12:10) Kodi inuyo munamvetselapo zinthu zongomvetsela cabe? Kumvetsela zinthu zimenezi kumatithandiza kudziŵa nkhani zambili zimene zipezeka pa webusaiti yathu. Kodi zinthu zongomvetsela zimenezi zingatipindulitse bwanji?
2. Kodi tingaseŵenzetse bwanji zinthu zongomvetsela pa phunzilo laumwini kapena pa phunzilo labanja?
2 Pa Phunzilo Laumwini Kapena Labanja: Kumvetsela zinthu zojambulidwa monga Baibulo, magazini, kapena cofalitsa ciliconse pamene tili paulendo kapena tikugwila nchito za tsiku ndi tsiku, kungatithandize kuseŵenzetsa bwino nthawi yathu. (Aef. 5:15, 16) Pa kulambila kwathu kwa pabanja, tingamvetsele kuŵelengedwa kwa cofalitsa cinacake uku tikutsatila m’kope lathu. Kumvetsela zinthu zimenezi pa phunzilo laumwini n’kothandiza kwambili, makamaka ngati tikufuna kukulitsa luso lathu loŵelenga, kapena ngati tikuphunzila cinenelo cina.
3. Ndi anthu otani amene angapindule ndi zinthu zongomvetsela m’gawo lathu?
3 Mu Ulaliki: Anthu a m’gawo lathu amene amaona kuti alibe nthawi yoŵelenga zofalitsa zathu, angakonde kumvetsela zinthu zojambulidwa. Mwina tingapeze anthu amene amakamba cinenelo cina, amene mwacionekele angamvetsele uthenga wa Ufumu ‘m’cinenelo cimene anabadwa naco.’ (Mac. 2:6-8) M’maiko ena, pa cikhalidwe, kumvetsela n’kofunika kwambili. Mwacitsanzo, anthu a cikhalidwe ca Cihomongi, amasimbila ana ao mbili yakale, ndipo anawo amakumbukila bwinobwino zimene amva. Maiko ambili mu Africa muno, pa cikhalidwe amakonda kuphunzitsa mwa nthano.
4. Tingadzifunse mafunso ati pankhani yothandiza anthu a m’gawo lathu?
4 Kodi pali wina amene angapindule m’gawo lanu mutamulizila nkhani imodzi yojambulidwa m’cinenelo cake? Kodi pali wina amene angapindule ngati mwam’tumizila cofalitsa congomvetsela cabe pa imelo? Kodi tingacite daunilodi cofalitsa congomvetsela ndi kuika pa CD, n’kupatsa munthu wacidwi pamodzi ndi kope lenileni la cofalitsaco? Tikagaŵila buku, kabuku, magazini kapena kapepala kauthenga kwa winawake mu ulaliki kupitila pa intaneti, tingalembe zimenezo monga zogaŵila. Zinthu zongomvetsela za pa webusaiti yathu zinakonzedwa kuti zitithandize pocita phunzilo laumwini, ndiponso pobzala mbeu za coonadi ca Ufumu.—1 Akor. 3:6.