Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu May
“Ife tonse timafanana pa cinthu cimodzi, timaphophonya. Kodi munayamba mwaganizapo ngati Mulungu amakhululuka zolakwa zazikulu?” [Yembekezani yankho.] M’patseni Nsanja ya Olonda ya May 1, ndi kumuonetsa nkhani ili patsamba 15. Ndiyeno kambilanani naye nkhani ili pa funso loyamba ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova May 1
“Tingakonde kumvako maganizo anu pa mau awa. [Ŵelengani 1 Yohane 4:8.] Anthu ambili amavomeleza mau awa, koma ena amaganiza kuti Mulungu ndi wankhanza cifukwa amacititsa kapena kulola masoka acilengedwe. Kodi inu muganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi zifukwa zomveka zimene zitionetsa cifukwa cake sitiyenela kuweluza Mulungu kuti ndi wankhanza.”
Galamukani! May
“Tikucezela anansi athu n’colinga cokambilana nao za vuto limene limativutitsa maganizo kwambili. Vuto limeneli ndi upandu. Ena amaganiza kuti njila yothetsela vuto limeneli ndi kukhala ndi apolisi ambili. Kodi inu muganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mudziŵa kuti Baibo imalonjeza kuti upandu udzatha? [Ŵelengani Salimo 37:10, 11.] Magazini iyi ifotokoza lonjezo limeneli ndipo itionetsa mfundo zothandiza zimene tingatsatile kuti tiziteteze ku upandu.”