Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu July
“Pafupi-fupi munthu aliyense m’dela lathu angakonde kukhala ndi umoyo wa zaka zambili komanso wosangalatsa. Conco tingakonde kumvako maganizo anu pa funso ili: Kodi muganiza kuti sayansi ndi mankhwala zidzatithandiza kuti tsiku lina tidzakhale kwamuyaya? [Yembekezani yankho.] Onani zimene panena apa.” Muonetseni nkhani ili pacikuto cothela ca Nsanja ya Olonda ya July 1. Ndiyeno kambilanani naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga lemba limodzi. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Cidziŵitso: Muyenela kucita citsanzo ici pa kukumana kokonzekela ulaliki pa July 6.
Nsanja ya Olonda July 1
“Anthu ambili amene timakambitsilana nao, ali ndi cipembedzo cao. Koma ena amakamba kuti asiya kukhulupilila cipembedzo ciliconse. Kodi inu mumaciona motani cipembedzo? [Yembekezani yankho.] Yesu anapeleka mfundo imene ingatithandize kufufuza bwino cipembedzo. [Ŵelengani Luka 6:44a.] Magazini iyi ifotokoza zipatso zina zoipa zimene cipembedzo cabeleka. Ikuyankhanso funso lakuti, kodi pali cipembedzo cimene mungakhulupilile?”
Galamukani! July
“Tikucezela anansi athu n’colinga cokambilana nao za vuto limene limativutitsa maganizo kwambili. Vuto limeneli ndi kupanda cilungamo. Ena amafuna kuthetsa vuto limeneli mwa kucita zionetselo zankhanza. Kodi muganiza kuti anthu amene amacita zionetselo amasinthadi zinthu? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Baibo imanena kuti zidzasinthadi zinthu padziko lapansi. [Welengani Mateyu 6:9, 10.] Magazini iyi iyankha funso lakuti, Kodi kucita zionetselo zankhanza n’kumene kungasinthe zinthu?”
Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
“Tikucezela mabanja m’gawo lino kuti tikambilane nao kanthu kena kocokela m’Baibo. Anthu ambili amene takamba nao akudabwa cifukwa cake Mulungu wacikondi angalolele mavuto conco padziko lapansi. Kodi muganiza kuti kuvutika kunali mbali ya colinga ca Mulungu ca padziko lapansi?” Yembekezani yankho. Ndiyeno pitani pa Phunzilo 5, ndi kuŵelenga komanso kukambilana ndime zoyambilila ziŵili ndi malemba ali m’zilembo zopendeka. M’gaŵileni kabuku ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila lili m’zilembo zakuda.”