Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu July
“Kodi muganiza kuti mapemphelo athu Mulungu amawaona bwanji? Kodi amawaona kukhala ofunika kapena amangowavomeleza cabe?” Yembekezani ayankhe. Kenako muonetseni kucikuto comaliza ca Nsanja ya Mlonda ya July 1, ndiyeno ŵelengelani pamodzi ndime imene ili munsi mwa funso loyamba ndi lemba limodzi limene lili pamenepo. Mugaŵileni magazini ndi kupangana zakuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda July 1
“Popeza kuti Mulungu ndi wamphamvuyonse, kodi muganiza kuti ndiye amacititsa zinthu zoipa zonse zimene zimacitika padziko lapansi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵelengani Yakobo 1:13.] Magazini iyi ifotokoza cifukwa cake zinthu zoipa zimacitika, ndi zimene Mulungu adzacita kuti athetse zinthu zoipa ndi kuvutika.”
Galamukani! July
“Nthawi iliyonse, pafupifupi munthu aliyense amakumana ndi zovuta zosiyanasiyana monga ngozi zacilengedwe, matenda oika moyo paciswe kapena imfa ya wokondedwa wathu. Zinthu zimenezi zikacitika, kodi muganiza kuti m’pofunika kukhala ndi maganizo oyenela? [Yembekezani ayankhe.] Ambili apeza kuti Baibulo lawathandiza kwambili polimbana ndi zovuta. [Ŵelengani Aroma 15:4.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Baibulo lingatithandizile tikakumana ndi zovuta.”