Tumapepala Twauthenga Twatsopano Topangidwa Mosangalatsa!
1. N’zogaŵila ziti za mu ulaliki zimene zili ndi mapangidwe atsopano osangalatsa?
1 Pamsonkhano wa Cigawo wa 2013 wa mutu wakuti “Mau a Mulungu ndi Coonadi” panatulutsidwa tumapepala twauthenga twatsopano tusanu. Kuonjezela pa tumapepala tumenetu, palinso Kapepala Kauthenga wa Ufumu Na. 38 kamutu wakuti “Kodi N’zoona kuti Akufa Angakhalenso Ndi Moyo?” Tumapepala tonse 6 twapangidwa m’njila yatsopano yosangalatsa. N’cifukwa ciani tunapangidwa m’njila yatsopano? Nanga tingagwilitsile nchito bwanji mapangidwe ake tikamatugaŵila ku nyumba ndi nyumba?
2. Kodi colinga ca mapangidwe atsopano n’ciani?
2 Cifukwa Cake Tuli ndi Mapangidwe Atsopano: Kuti ticite ulaliki wa kunyumba ndi nyumba wogwila mtima, nthawi zambili timafunika kutsatila njila zinai zotsatilazi: (1) Funsani funso n’colinga cakuti muyambe makambilano. (2) Afotokozeleni mfundo ya m’Malemba. (3) Gaŵilani mwininyumba cofalitsa cakuti aŵelenge. (4) Siyani funso kuti mukayankhe ulendo wotsatila, ndipo pangani makonzedwe akuti mukabwelenso. Mpangidwe watsopano wa tumapepala twauthenga tumenetu umatithandiza kutsatila mosavuta njila zonse zinai.
3. Tingagaŵile bwanji tumapepala twatsopano mu ulaliki?
3 Mmene Mungatugwilitsile Nchito: (1) Mukapatsana moni ndi mwininyumba muonetseni funso ndi mayankho ocita kusankhapo opezeka patsogolo pa kapepala kameneka. Ndipo m’funseni zimene iye aganiza. (2) Tsegulani kapepala ndikuona pa mutu wakuti “Zimene Baibulo limanena.” Ngati n’kotheka ŵelengani malemba mwacindunji m’Baibulo. Ngati mwininyumba ali ndi nthawi mungakambilane kamutu kakuti “Mapindu Okhulupilila kuti Akufa Adzauka.” (3) M’gaŵileni kapepala ndi kumulimbikitsa kuti apeze nthawi yabwino yokaŵelenga konse. (4) Musanacoke, muonetseni funso limene lili pansi pa kamutu kakuti “Ganizilani Funso lli” ndipo panganani zakuti mudzakambilane yankho lake m’Baibulo ulendo wotsatila.
4. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji tumapepala twauthenga twatsopano paulendo wobwelelako?
4 Kupanga maulendo obwelelako n’kosavuta. Kuti muyankhe funso limene munasiyalo, gwilitsilani nchito Malemba amene sanagwidwe mau amene apezeka kumbuyo kwa kapepala kauthenga kameneka. Musanacoke onetsani mwininyumba cithunzi ca bulosha la Uthenga Wabwino kenako muonetseni bulosha lenilenilo ndi kumusonyeza nkhani zake ndipo m’gaŵileni buloshalo. Ngati wavomeleza, pangani makonzedwe akuti ulendo wotsatila mudzakambilane za bulosha limenelo. Mukatelo ndiye kuti basi mwayambitsa phunzilo la Baibulo. Mwinanso m’malo mogaŵila bulosha, mungagaŵile kapepala kauthenga kena ndi kupanga makonzedwe akuti mudzakambilane ndi mwininyumba ulendo wina.
5. Kodi tumapepala twauthenga ndi tofunika bwanji tikamacita ulaliki?
5 Kwa zaka zoposa 130 takhala tikugwilitsila nchito tumapepala twauthenga mu ulaliki. Ngakhale kuti ndi tosiyana mkapangidwe kake, twakhala zida zothandiza kwambili pocitila umboni. Tiyeni titugwilitsile nchito bwino tumapepala twauthenga twatsopanotu popitiliza kufalitsa cidziŵitso ca m’Baibulo pa dziko lonse.—Miy. 15:7a.