Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Phunzilo la Baibulo Pogwilitsila Nchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Kuti tipange ophunzila, tiyenela kukhala aphunzitsi a Mau a Mulungu. (Mat. 28:19, 20) Tonse tingaphunzitse coonadi mogwila mtima pogwilitsila nchito zida zimene tili nazo. Kabuku ka Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu kanakonzedwa kuti katithandize pophunzitsa ena coonadi. Tingakagwilitsile nchito paulendo woyamba poyambitsa phunzilo la Baibulo.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kuyambitsa phunzilo la Baibulo ndi kuphunzitsa coonadi mogwila mtima.—Afil. 2:13.
Pa kulambila kwanu kwa pabanja kapena pa phunzilo lanu laumwini, ŵelengani ndi kumvetsetsa ulaliki wacitsanzo. Zimenezi zidzakuthandizani kuyambitsa phunzilo la Baibulo ndi kulankhula mogwila mtima mu ulaliki.