LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsa. 11
  • Kambani Mwaumoyo Pophunzitsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kambani Mwaumoyo Pophunzitsa
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kukamba Mwaumoyo
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Afikeni Pamtima Anthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 May tsa. 11
M’bale amwetulila na kucita magesica pamene aphunzitsa Baibo wacikulile.

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Kambani Mwaumoyo Pophunzitsa

Anthu amakhudzidwa ngati tikamba mwaumoyo. Kukamba mwaumoyo kumasonkhezela anthu kumvetsela zimene tikamba. Kumaonetsanso kuti timaona uthenga wathu kukhala wofunika. Tingakwanitse kukamba mwaumoyo mosasamala kanthu za cikhalidwe cathu kapena cibadwa cathu. (Aroma 12:11) Motani?

Coyamba, ganizilani za kufunika kwa uthenga wanu. Muli na mwayi ‘wolengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’ (Aroma 10:15) Caciŵili, ganizilani mmene uthenga wabwino udzapindulitsila omvela anu. Uthenga wanu ni wofunika kwambili kwa iwo. (Aroma 10:13, 14) Cotsiliza, kambani mwaumoyo, pangani magesica mwacibadwa, ndipo khope yanu izionetsa mmene mumvelela.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUKAMBA MWAUMOYO POPHUNZITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kukamba Mwaumoyo Pophunzitsa.’ Neeta aoneka wosasangalala Rose atamuuza kuti asaphunzile Baibo.

    N’ciani cinacititsa kuti cidwi ca Neeta cotsogoza phunzilo la Baibo kwa Rose cicepe?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kukamba Mwaumoyo Pophunzitsa.’ Rose aoneka wosasangalala pamene aphunzila Baibo.

    N’ciani cinapangitsa kuti Neeta akhalenso na cidwi cotsogoza phunzilo kwa Rose?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kukamba Mwaumoyo Pophunzitsa.’ Rose na Neeta akukambilana mosangalala pambuyo pa phunzilo la Baibo.

    Anthu amakhudzidwa ngati tikamba mwaumoyo

    N’cifukwa ciani tiyenela kusumika maganizo athu pa makhalidwe abwino a omvela athu?

  • Kodi kukamba mwaumoyo kungakhudze bwanji ophunzila Baibo athu na ena?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani