CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Landilani Thandizo la Anchito Anzanu
Pofuna kutithandiza, Yehova watipatsa “gulu lonse” la abale na alongo. (1 Pet. 5:9) Iwo angatithandize kugonjetsa zopinga zimene tingakumane nazo mu ulaliki. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anapindula na thandizo la Akula na Purisikila, Sila, Timoteyo, komanso ena.—Mac. 18:1-5.
Kodi anchito anzanu angakuthandizeni bwanji mu ulaliki? Angakuthandizeni kudziŵa mmene mungayankhile anthu okana kuwalalikila. Angakuthandizeninso kupanga maulendo obwelelako, komanso kuyambitsa maphunzilo a Baibo na kuwatsogoza. Ganizilani wofalitsa mumpingo amene angakuthandizeni pa mbali imene mufunika thandizo. Ndiyeno, m’pempheni kuti akuthandizeni. Mosakayikila, nonse mudzapindula, ndipo mudzapeza cimwemwe.—Afil. 1:25.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—LANDILANI THANDIZO LA YEHOVA—ABALE ATHU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi mlongo Neeta anam’limbikitsa bwanji Rose kuti azipezeka ku misonkhano?
N’cifukwa ciani tiyenela kumatengako ofalitsa ena pokatsogoza phunzilo la Baibo?
Ni udindo wa mpingo wonse kuthandiza munthu kuti akhale wophunzila
Kodi Rose na mlongo Abigay anali kukonda zinthu ziti zofanana?
Ni maluso ati a mu ulaliki amene mungaphunzile kwa anchito anzanu?