CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kudzikweza Kumanyazitsa Munthu
Mfumu Sauli anaona kuti wathedwa nzelu (1 Sam. 13:5-7)
M’malo motsatila malangizo a Yehova modzicepetsa, Sauli anacita zinthu modzikweza (1 Sam. 13:8,9; w00 8/1 13 ¶17)
Yehova anamulanga Sauli (1 Sam. 13:13, 14; w07 6/15 27 ¶8)
Kumakhala kudzikweza komanso kupanda nzelu ngati munthu afulumila kucita cinthu popanda cilolezo. Kudzikweza kumasiyana na kudzicepetsa. Ni zocitika monga ziti zimene zingapangitse munthu kudzikweza?