LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 May tsa. 13
  • Kodi Mumaigwilitsa Nchito Mofikapo Baibo Yongomvetsela?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumaigwilitsa Nchito Mofikapo Baibo Yongomvetsela?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Zinthu Zongomvetsela za pa jw.org
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zimene Mungacite Kuti Muziwelenga Baibo Tsiku Lililonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Webu Saiti Yathu—Igwilitsileni Nchito Kuthandiza Munthu Amene Amalankhula Cinenelo Cina
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Kodi Munadzifunsapo?
    Galamuka!—2019
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 May tsa. 13
Zithunzi: Kumvetsela Baibo. 1. M’bale ali panja, ndipo akumvetsela Baibo pafoni yake atavala mahedifoni. 2. Mayi na mwana wake wamkazi akumvetsela Baibo poseŵenzetsa kawailesi kwinaku akutsatila m’Baibo yawo yosindikizidwa. 3. Mlongo wavala tumahedifoni ndipo akumvetsela Baibo pafoni yake ali pa ulendo m’sitima.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumaigwilitsa Nchito Mofikapo Baibo Yongomvetsela?

Kodi Baibo yongomvetsela ni yotani? Baibo yongomvetsela ni Baibo ya Dziko Latsopano yokonzedwanso imene mawu ake anajambulidwa. Ikutulutsidwa pang’ono-pang’ono m’zinenelo zambili. Cimodzi cocititsa cidwi na Baiboyi n’cakuti mawu a munthu aliyense m’Baibo anaŵelengedwa na munthu wosiyana. Mawu ake anaŵelengedwa motsindika komanso na mzimu wake pofuna kumveketsa molondola uthenga wa m’Baibo.

Kodi ena apindula bwanji na Baibo yongomvetsela? Anthu ambili amene amakonda kumvetsela Baibo imeneyi aona kuti imawathandiza kumvetsa Mawu a Mulungu mosavuta. Iwo aona kuti kumvetsela mawu a anthu a m’Baibo akuŵelengedwa na anthu osiyana-siyana, kumawathandiza kuona m’maganizo mwawo zocitika za m’Baibo na kumvetsetsa zimene zinalembedwazo. (Miy. 4:5) Enanso ambili amaona kuti kumvetsela Baibo imeneyi kumawatsitsimula akakhala na nkhawa.—Sal. 94:19.

Kumvetsela Mawu a Mulungu akuŵelengedwa mokweza kungasinthe kwambili umoyo wathu. (2 Mbiri 34:19-21) Ngati Baibo yongomvetsela, kaya mbali yake kapena yathunthu, ipezeka m’cinenelo cimene mumamva, bwanji osakonza zakuti muziimvetsela nthawi zonse pa pulogilamu yanu yauzimu?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI NCHITO YOPANGA BAIBO YONGOMVETSELA—MBALI YAKE, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

N’ciyani cakucititsani cidwi pa nchito yopanga Baibo yongomvetsela?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani