LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Mbum
  • Lelo

Sondo, July 27

[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.​—Tito 1:9.

Kuti mukhale Mkhristu wokhwima, muyenela kukulitsa maluso othandiza. Izi zidzakuthandizani kusenza maudindo mu mpingo, kupeza nchito yokuthandizani inuyo na banja lanu, komanso kukhala paubwenzi wabwino na anthu ena. Mwacitsanzo, phunzilani kuŵelenga na kulemba bwino. Baibo imati mwamuna wacimwemwe komanso wopambana amaseŵenzetsa nthawi yake kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. (Sal. 1:1-3) Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse kumam’thandiza kudziŵa bwino kaganizidwe ka Yehova, zimene zimamuthandiza kukhala woganiza bwino. (Miy. 1:3, 4) Abale na alongo athu amayang’ana kwa amuna oyenelela akafuna malangizo. Ngati mumatha kuŵelenga na kulemba, mudzakwanitsa kukonzekela nkhani na ndemanga zogwila mtima komanso zolimbikitsa cikhulupililo. Mudzakwanitsanso kulemba manotsi atanthauzo amenewa adzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu komanso kulimbikitsa ena. w23.12 26-27 ¶9-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Mande, July 28

Amene ali wogwilizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwilizana ndi dziko.​—1 Yoh. 4:4.

Mukakhala na mantha, muzisinkhasinkha zimene Yehova adzacita m’tsogolo Satana akadzacotsedwapo. Msonkhano wa cigawo wa mu 2014 unali na citsanzo coonetsa tate akukambilana na banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likanalembedwela cikanakhala kuti linali kulosela mmene Paradaiso adzakhalile. Analiŵelenga motele: “Masiku a m’dziko latsopano adzakhala nthawi yapadela komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambila Mulungu, odzicepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvela makolo, oyamika, okhulupilika, okonda acibale awo, ofuna kugwilizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalilika, oganizila ena, osadzitukumula, ndiponso osanyada, okonda Mulungu m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odzipelekadi kwa Mulungu, anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambilana nawo a m’banja lanu kapena alambili anzanu za mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵili, July 29

Umandisangalatsa kwambili.​—Luka 3:22.

N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda gulu lonse la anthu ake! Baibo imati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe, nthawi zina ena amalefuka moti amafika podzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amakondwela nane?’ Ena mwa alambili okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Baibo anavutikapo na maganizo otelo. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibo imakamba momveka bwino kuti anthu opanda ungwilo angapeze ciyanjo ca Yehova. Motani? Mwa kukhulupilila Yesu Khristu na kubatizika. (Yoh. 3:16) Mwa kutelo, timaonetsa poyela kuti tinalapa macimo athu, komanso kuti tinapanga lonjezo kwa Mulungu lakuti tidzacita cifunilo cake. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amakondwela ngati tapanga masitepe amenewa kuti tikhale naye pa ubale. Kuwonjezela apo, amakondwela nafe ngati tipitiliza kucita zonse zimene tingathe posunga lumbilo lathu la kudzipatulila. Ndipo amationa kukhala mabwenzi ake a pamtima.​—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani