Citatu, July 30
Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.—Mac. 4:20.
Tingatengele citsanzo ca ophunzila mwa kupitiliza kulalikila ngakhale pamene maboma atilamula kuti tileke kulalikila. Tili na cidalilo kuti Yehova adzatithandiza kukwanilitsa utumiki wathu. Conco mupemphani kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima, akupatseni nzelu komanso kuti akuthandizeni kuthana na mavuto. Ambili a ife tikulimbana na mavuto monga matenda, kupsinjika maganizo, kutaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa, mavuto a m’banja, mazunzo, kapena vuto lina. Ndipo zinthu monga milili na nkhondo, zapangitsa kuti cikhale covuta kwambili kuthana na mavuto ngati amenewa. Conco, m’khuthulileni za kumtima kwanu Yehova. Muuzeni za vuto lanu mmene mungauzile bwenzi lanu lapamtima. Khalani wotsimikiza kuti Yehova “adzakuthandizani.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikila kupemphela kudzatithandiza ‘kupilila mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziŵa mavuto amene atumiki ake amakumana nawo, “amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15
Cinayi, July 31
Nthawi zonse muzitsimikizila kuti covomelezeka kwa Ambuye nʼciti.—Aef. 5:10.
Tikafunika kupanga cisankho cofunika kwambili, tiyenela “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco. (Aef. 5:17) Tikamafufuza na kupeza mfundo za m’Baibo zothandiza pa cisankho cimene tifuna kupanga, kwenikweni timakhala tikufunafuna maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndipo tikagwilitsa nchito mfundo zake, timapanga zisankho zabwino. Mdani wathu Satana, “Woipayo,” amafuna kuticenjeneka na kufuna-funa zinthu za m’dzikoli n’colinga cakuti tizisoŵelatu nthawi yotumikila Mulungu. (1 Yoh. 5:19) Cingakhale capafupi kwa Mkhristu kutsogoza zakuthupi, maphunzilo, kapena nchito m’malo moseŵenzetsa mipata imene ilipo yotumikila Yehova. Zotelezi zikacitika, zingaonetse kuti munthu wayamba kuyendela maganizo a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Koma si ndiye zomwe tiyenela kutsogoza pa umoyo wathu. w24.03 24 ¶16-17
Cisanu, August 1
Mavuto a munthu wolungama ndi ambili, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.—Sal. 34:19.
Onani mfundo ziŵili izi zimene zili pa salimo lili pamwambapa: (1) Anthu olungama amakumana na mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa ku mavutowo. Kodi amatipulumutsa bwanji? Njila imodzi ni kutithandiza kuona umoyo moyenela m’dzikoli. N’zoona kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala acimwemwe pom’tumikila. Koma sanatiuze kuti palipano tidzakhala na umoyo wopanda mavuto. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuganizila za tsogolo lathu, pamene tidzasangalala na moyo kwamuyaya. (2 Akor. 4:16-18) Koma pakali pano, iye amatithandiza kuti tisaleke kum’tumikila. (Maliro 3:22-24) Tiphunzilapo ciyani pa zitsanzo za alambili a Yehova okhulupilika ochulidwa m’Baibo, komanso amakono? Tingakumane na mavuto mosayembekezela. Koma tikam’dalila Yehova, sadzalephela kutithandiza.—Sal. 55:22. w23.04 14-15 ¶3-4